Genesis 8 (BOGWICC)
1 Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera. 2 Tsono akasupe a madzi ambiri a pansi pa dziko ndi zitseko za madzi a kumwamba zinatsekedwa, ndipo mvula inaleka kugwa. 3 Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, 4 ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati. 5 Madzi anapitirira kuphwa mpaka mwezi wa khumi, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wa khumiwo msonga za mapiri zinayamba kuonekera. 6 Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo 7 natulutsa khwangwala, koma khwangwalayo ankangowuluka uku ndi uku mpaka madzi anawuma pa dziko lapansi. 8 Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko. 9 Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. 10 Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja. 11 Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. 12 Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye. 13 Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. 14 Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu. 15 Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, 16 “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. 17 Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.” 18 Nowa anatuluka pamodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake. 19 Nyama zonse, zokwawa zonse, mbalame zonse, chilichonse choyenda pa dziko lapansi, zinatuluka mʼchombo motsogozana monga mwa mitundu yawo. 20 Pamenepo Nowa anamanga guwa lansembe la Yehova ndipo anatengako mtundu uliwonse wa nyama zoti nʼkudya ndi mbalame zoti nʼkudya naperekapo nsembe yopsereza. 21 Yehova atamva fungo labwino anati mu mtima mwake: “Sindidzatembereranso nthaka chifukwa cha munthu, ngakhale kuti maganizo a mu mtima mwake ndi oyipa kuyambira ubwana wake. Ndipo sindidzawononganso zolengedwa zonse zamoyo monga ndachitiramu. 22 “Nthawi zonse mmene dziko lapansi lidzakhalire,nthawi yodzala ndi nthawi yokololayozizira ndi yotentha,dzinja ndi chilimwe,usana ndi usiku,sizidzatha.”
In Other Versions
Genesis 8 in the ANGEFD
Genesis 8 in the ANTPNG2D
Genesis 8 in the AS21
Genesis 8 in the BAGH
Genesis 8 in the BBPNG
Genesis 8 in the BBT1E
Genesis 8 in the BDS
Genesis 8 in the BEV
Genesis 8 in the BHAD
Genesis 8 in the BIB
Genesis 8 in the BLPT
Genesis 8 in the BNT
Genesis 8 in the BNTABOOT
Genesis 8 in the BNTLV
Genesis 8 in the BOATCB
Genesis 8 in the BOATCB2
Genesis 8 in the BOBCV
Genesis 8 in the BOCNT
Genesis 8 in the BOECS
Genesis 8 in the BOHCB
Genesis 8 in the BOHCV
Genesis 8 in the BOHLNT
Genesis 8 in the BOHNTLTAL
Genesis 8 in the BOICB
Genesis 8 in the BOILNTAP
Genesis 8 in the BOITCV
Genesis 8 in the BOKCV
Genesis 8 in the BOKCV2
Genesis 8 in the BOKHWOG
Genesis 8 in the BOKSSV
Genesis 8 in the BOLCB
Genesis 8 in the BOLCB2
Genesis 8 in the BOMCV
Genesis 8 in the BONAV
Genesis 8 in the BONCB
Genesis 8 in the BONLT
Genesis 8 in the BONUT2
Genesis 8 in the BOPLNT
Genesis 8 in the BOSCB
Genesis 8 in the BOSNC
Genesis 8 in the BOTLNT
Genesis 8 in the BOVCB
Genesis 8 in the BOYCB
Genesis 8 in the BPBB
Genesis 8 in the BPH
Genesis 8 in the BSB
Genesis 8 in the CCB
Genesis 8 in the CUV
Genesis 8 in the CUVS
Genesis 8 in the DBT
Genesis 8 in the DGDNT
Genesis 8 in the DHNT
Genesis 8 in the DNT
Genesis 8 in the ELBE
Genesis 8 in the EMTV
Genesis 8 in the ESV
Genesis 8 in the FBV
Genesis 8 in the FEB
Genesis 8 in the GGMNT
Genesis 8 in the GNT
Genesis 8 in the HARY
Genesis 8 in the HNT
Genesis 8 in the IRVA
Genesis 8 in the IRVB
Genesis 8 in the IRVG
Genesis 8 in the IRVH
Genesis 8 in the IRVK
Genesis 8 in the IRVM
Genesis 8 in the IRVM2
Genesis 8 in the IRVO
Genesis 8 in the IRVP
Genesis 8 in the IRVT
Genesis 8 in the IRVT2
Genesis 8 in the IRVU
Genesis 8 in the ISVN
Genesis 8 in the JSNT
Genesis 8 in the KAPI
Genesis 8 in the KBT1ETNIK
Genesis 8 in the KBV
Genesis 8 in the KJV
Genesis 8 in the KNFD
Genesis 8 in the LBA
Genesis 8 in the LBLA
Genesis 8 in the LNT
Genesis 8 in the LSV
Genesis 8 in the MAAL
Genesis 8 in the MBV
Genesis 8 in the MBV2
Genesis 8 in the MHNT
Genesis 8 in the MKNFD
Genesis 8 in the MNG
Genesis 8 in the MNT
Genesis 8 in the MNT2
Genesis 8 in the MRS1T
Genesis 8 in the NAA
Genesis 8 in the NASB
Genesis 8 in the NBLA
Genesis 8 in the NBS
Genesis 8 in the NBVTP
Genesis 8 in the NET2
Genesis 8 in the NIV11
Genesis 8 in the NNT
Genesis 8 in the NNT2
Genesis 8 in the NNT3
Genesis 8 in the PDDPT
Genesis 8 in the PFNT
Genesis 8 in the RMNT
Genesis 8 in the SBIAS
Genesis 8 in the SBIBS
Genesis 8 in the SBIBS2
Genesis 8 in the SBICS
Genesis 8 in the SBIDS
Genesis 8 in the SBIGS
Genesis 8 in the SBIHS
Genesis 8 in the SBIIS
Genesis 8 in the SBIIS2
Genesis 8 in the SBIIS3
Genesis 8 in the SBIKS
Genesis 8 in the SBIKS2
Genesis 8 in the SBIMS
Genesis 8 in the SBIOS
Genesis 8 in the SBIPS
Genesis 8 in the SBISS
Genesis 8 in the SBITS
Genesis 8 in the SBITS2
Genesis 8 in the SBITS3
Genesis 8 in the SBITS4
Genesis 8 in the SBIUS
Genesis 8 in the SBIVS
Genesis 8 in the SBT
Genesis 8 in the SBT1E
Genesis 8 in the SCHL
Genesis 8 in the SNT
Genesis 8 in the SUSU
Genesis 8 in the SUSU2
Genesis 8 in the SYNO
Genesis 8 in the TBIAOTANT
Genesis 8 in the TBT1E
Genesis 8 in the TBT1E2
Genesis 8 in the TFTIP
Genesis 8 in the TFTU
Genesis 8 in the TGNTATF3T
Genesis 8 in the THAI
Genesis 8 in the TNFD
Genesis 8 in the TNT
Genesis 8 in the TNTIK
Genesis 8 in the TNTIL
Genesis 8 in the TNTIN
Genesis 8 in the TNTIP
Genesis 8 in the TNTIZ
Genesis 8 in the TOMA
Genesis 8 in the TTENT
Genesis 8 in the UBG
Genesis 8 in the UGV
Genesis 8 in the UGV2
Genesis 8 in the UGV3
Genesis 8 in the VBL
Genesis 8 in the VDCC
Genesis 8 in the YALU
Genesis 8 in the YAPE
Genesis 8 in the YBVTP
Genesis 8 in the ZBP