Genesis 9 (BOGWICC)
1 Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake aamuna nati kwa iwo, “Berekanani ndipo muchulukane ndi kudzaza dziko lapansi. 2 Nyama zonse za dziko lapansi, ndi mbalame zonse za mlengalenga, ndi chamoyo chilichonse chokwawa, ndiponso nsomba zonse za ku nyanja; zidzakuopani ndipo ndazipereka kuti muzilamulire. 3 Tsopano chamoyo chilichonse chidzakhala chakudya chanu. Monga momwe ndinakupatsirani ndiwo zamasamba, tsopano ndikupatsaninso nyama iliyonse. 4 “Koma musamadye nyama imene ikanali ndi magazi oyenda. 5 Aliyense wopha munthu adzaphedwa, nyama iliyonse yopha munthu idzaphedwa, munthu aliyense wopha munthu mnzake, adzaphedwa. 6 “Aliyense wopha munthu,adzaphedwanso ndi munthu;pakuti Mulungu analenga munthumʼchifanizo chake. 7 Inu muberekane ndi kuchulukana kuti mudzaze dziko lonse lapansi ndi kuligonjetsa.” 8 Mulungu anawuza Nowa ndi ana ake kuti, 9 “Tsopano Ine ndapangana ndi iwe ndi zidzukulu zako zamʼtsogolomo, 10 pamodzi ndi zamoyo zonse, mbalame, ziweto ndi nyama zonse za kuthengo, ndi zonse zimene zinatuluka mʼchombo pamodzi ndi iwe. 11 Pangano langa ndi ili: Ine ndilonjeza kuti sindidzawononganso zamoyo ndi madzi a chigumula. Chigumula sichidzawononganso dziko lapansi.” 12 Ndipo Mulungu anati, “Ine ndikupereka chizindikiro ichi cha pangano langa la pakati pa Ine ndi iwe, ana ako, zamoyo zonse, pamodzi ndi mibado ya mʼtsogolo. 13 Ndayika utawaleza wanga mʼmitambo, ndipo chidzakhala chizindikiro cha pangano langa ndi dziko lapansi. 14 Nthawi zonse pakakhala mitambo mu mlengalenga ndipo utawaleza uwoneka, 15 ndizikumbukira pangano langa pakati pa Ine ndi inu ndi zolengedwa zonse. Madzi sadzakhalanso chigumula chowononga dziko lapansi. 16 Utawaleza ukamadzaoneka mʼmitambo, ndidzawuona ndi kukumbukira pangano losatha pakati pa Mulungu ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.” 17 Choncho Mulungu anati kwa Nowa, “Ichi ndiye chizindikiro cha pangano limene ndalichita pakati pa Ine ndi zamoyo zonse pa dziko lapansi.” 18 Ana aamuna a Nowa amene anatuluka mʼchombo muja anali Semu, Hamu ndi Yafeti. Hamu anali abambo ake a Kanaani. 19 Ana aamuna a Nowa amenewa ndiwo anali makolo a anthu onse pa dziko lapansi. 20 Nowa anali munthu woyamba kulima munda wamphesa. 21 Tsiku lina pamene Nowa anamwako vinyo wa zipatso za mʼmundawo analedzera ndipo anavula zovala zake zonse ndi kugona mu tenti yake ali maliseche. 22 Hamu, abambo ake a Kanaani ataona kuti abambo ake ali maliseche anakawuza abale ake awiri aja omwe anali panja. 23 Koma Semu ndi Yafeti anatenga chofunda nachiyika pa mapewa awo; ndipo anayenda chamʼmbuyo naphimba umaliseche wa abambo awo. Anafulatira kuti asaone umaliseche wa abambo awo. 24 Nowa atadzuka, kuledzera kutatha, ndikudziwa zimene mwana wake wamngʼono wamwamuna uja anamuchitira, 25 anati,“Atembereredwe Kanaani!Adzakhala kapolowa pansi kwenikweni kwa abale ake.” 26 Anatinso,“Atamandike Yehova, Mulungu wa Semu!Kanaani akhale kapolo wa Semu. 27 Mulungu akulitse dziko la Yafeti;Yafeti alandire madalitso pamodzi ndi Semu,ndipo Kanaani akhale kapolo wawo.” 28 Chitatha chigumula, Nowa anakhala ndi moyo zaka 350. 29 Anamwalira ali ndi zaka 950.
In Other Versions
Genesis 9 in the ANGEFD
Genesis 9 in the ANTPNG2D
Genesis 9 in the AS21
Genesis 9 in the BAGH
Genesis 9 in the BBPNG
Genesis 9 in the BBT1E
Genesis 9 in the BDS
Genesis 9 in the BEV
Genesis 9 in the BHAD
Genesis 9 in the BIB
Genesis 9 in the BLPT
Genesis 9 in the BNT
Genesis 9 in the BNTABOOT
Genesis 9 in the BNTLV
Genesis 9 in the BOATCB
Genesis 9 in the BOATCB2
Genesis 9 in the BOBCV
Genesis 9 in the BOCNT
Genesis 9 in the BOECS
Genesis 9 in the BOHCB
Genesis 9 in the BOHCV
Genesis 9 in the BOHLNT
Genesis 9 in the BOHNTLTAL
Genesis 9 in the BOICB
Genesis 9 in the BOILNTAP
Genesis 9 in the BOITCV
Genesis 9 in the BOKCV
Genesis 9 in the BOKCV2
Genesis 9 in the BOKHWOG
Genesis 9 in the BOKSSV
Genesis 9 in the BOLCB
Genesis 9 in the BOLCB2
Genesis 9 in the BOMCV
Genesis 9 in the BONAV
Genesis 9 in the BONCB
Genesis 9 in the BONLT
Genesis 9 in the BONUT2
Genesis 9 in the BOPLNT
Genesis 9 in the BOSCB
Genesis 9 in the BOSNC
Genesis 9 in the BOTLNT
Genesis 9 in the BOVCB
Genesis 9 in the BOYCB
Genesis 9 in the BPBB
Genesis 9 in the BPH
Genesis 9 in the BSB
Genesis 9 in the CCB
Genesis 9 in the CUV
Genesis 9 in the CUVS
Genesis 9 in the DBT
Genesis 9 in the DGDNT
Genesis 9 in the DHNT
Genesis 9 in the DNT
Genesis 9 in the ELBE
Genesis 9 in the EMTV
Genesis 9 in the ESV
Genesis 9 in the FBV
Genesis 9 in the FEB
Genesis 9 in the GGMNT
Genesis 9 in the GNT
Genesis 9 in the HARY
Genesis 9 in the HNT
Genesis 9 in the IRVA
Genesis 9 in the IRVB
Genesis 9 in the IRVG
Genesis 9 in the IRVH
Genesis 9 in the IRVK
Genesis 9 in the IRVM
Genesis 9 in the IRVM2
Genesis 9 in the IRVO
Genesis 9 in the IRVP
Genesis 9 in the IRVT
Genesis 9 in the IRVT2
Genesis 9 in the IRVU
Genesis 9 in the ISVN
Genesis 9 in the JSNT
Genesis 9 in the KAPI
Genesis 9 in the KBT1ETNIK
Genesis 9 in the KBV
Genesis 9 in the KJV
Genesis 9 in the KNFD
Genesis 9 in the LBA
Genesis 9 in the LBLA
Genesis 9 in the LNT
Genesis 9 in the LSV
Genesis 9 in the MAAL
Genesis 9 in the MBV
Genesis 9 in the MBV2
Genesis 9 in the MHNT
Genesis 9 in the MKNFD
Genesis 9 in the MNG
Genesis 9 in the MNT
Genesis 9 in the MNT2
Genesis 9 in the MRS1T
Genesis 9 in the NAA
Genesis 9 in the NASB
Genesis 9 in the NBLA
Genesis 9 in the NBS
Genesis 9 in the NBVTP
Genesis 9 in the NET2
Genesis 9 in the NIV11
Genesis 9 in the NNT
Genesis 9 in the NNT2
Genesis 9 in the NNT3
Genesis 9 in the PDDPT
Genesis 9 in the PFNT
Genesis 9 in the RMNT
Genesis 9 in the SBIAS
Genesis 9 in the SBIBS
Genesis 9 in the SBIBS2
Genesis 9 in the SBICS
Genesis 9 in the SBIDS
Genesis 9 in the SBIGS
Genesis 9 in the SBIHS
Genesis 9 in the SBIIS
Genesis 9 in the SBIIS2
Genesis 9 in the SBIIS3
Genesis 9 in the SBIKS
Genesis 9 in the SBIKS2
Genesis 9 in the SBIMS
Genesis 9 in the SBIOS
Genesis 9 in the SBIPS
Genesis 9 in the SBISS
Genesis 9 in the SBITS
Genesis 9 in the SBITS2
Genesis 9 in the SBITS3
Genesis 9 in the SBITS4
Genesis 9 in the SBIUS
Genesis 9 in the SBIVS
Genesis 9 in the SBT
Genesis 9 in the SBT1E
Genesis 9 in the SCHL
Genesis 9 in the SNT
Genesis 9 in the SUSU
Genesis 9 in the SUSU2
Genesis 9 in the SYNO
Genesis 9 in the TBIAOTANT
Genesis 9 in the TBT1E
Genesis 9 in the TBT1E2
Genesis 9 in the TFTIP
Genesis 9 in the TFTU
Genesis 9 in the TGNTATF3T
Genesis 9 in the THAI
Genesis 9 in the TNFD
Genesis 9 in the TNT
Genesis 9 in the TNTIK
Genesis 9 in the TNTIL
Genesis 9 in the TNTIN
Genesis 9 in the TNTIP
Genesis 9 in the TNTIZ
Genesis 9 in the TOMA
Genesis 9 in the TTENT
Genesis 9 in the UBG
Genesis 9 in the UGV
Genesis 9 in the UGV2
Genesis 9 in the UGV3
Genesis 9 in the VBL
Genesis 9 in the VDCC
Genesis 9 in the YALU
Genesis 9 in the YAPE
Genesis 9 in the YBVTP
Genesis 9 in the ZBP