Isaiah 1 (BOGWICC)

1 Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda. 2 Tamverani, miyamba inu! Tchera khutu, iwe dziko lapansi!Pakuti Yehova wanena kuti,“Ndinabala ana ndi kuwalera,koma anawo andiwukira Ine. 3 Ngʼombe imadziwa mwini wake,bulu amadziwa kumene kuli gome la mbuye wake,koma Israeli sadziwa,anthu anga samvetsa konse.” 4 Haa, mtundu wochimwa,anthu olemedwa ndi machimo,obadwa kwa anthu ochita zoyipa,ana odzipereka ku zoyipa!Iwo asiya Yehova;anyoza Woyerayo wa Israelindipo afulatira Iyeyo. 5 Chifukwa chiyani mukufuna kuti muzingolangidwabe?Chifukwa chiyani mukupitirira kukhala mʼmoyo wowukira?Mutu wanu wonse uli ndi mabala,mtima wanu wonse wafowokeratu. 6 Kuchokera ku phazi mpaka ku mutupalibe pabwino,paliponse pali mikwingwirima ndi zilonda,mabala ali magazi chuchuchu,mabala ake ngosatsuka, ngosamangandiponso ngosapaka mafuta ofewetsa. 7 Dziko lanu lasanduka bwinja,mizinda yanu yatenthedwa ndi moto;minda yanu ikukololedwa ndi alendoinu muli pomwepo,dziko lanu lasanduka bwinja monga ngati lagonjetsedwa ndi alendo. 8 Mwana wamkazi wa Ziyoni watsala yekhangati nsanja mʼmunda wampesa,ngati chisimba mʼmunda wa minkhaka,ngati mzinda wozingidwa ndi nkhondo. 9 Yehova Wamphamvuzonse akanapandakutisiyira opulumuka,tikanawonongeka ngati Sodomu,tikanakhala ngati anthu a ku Gomora. 10 Imvani mawu a Yehova,inu olamulira Sodomu;mverani lamulo la Mulungu wathu,inu anthu a ku Gomora! 11 Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyaninsembe zanu zochuluka?”“Zandikola nsembe zanu zopserezaza nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa;sindikusangalatsidwansondi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna. 12 Ndani anakulamulirani kutimubwere nazo pamaso panga?Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga? 13 Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo!Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine.Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa,kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata. 14 Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulikandimadana nazo.Zasanduka katundu wondilemera;ndatopa kuzinyamula. 15 Mukamatambasula manja anu popemphera,Ine sindidzakuyangʼanani;ngakhale muchulukitse mapemphero anu,sindidzakumverani.Manja anu ndi odzaza ndi magazi; 16 sambani, dziyeretseni.Chotsani pamaso panuntchito zanu zoyipa!Lekani kuchita zoyipa, 17 phunzirani kuchita zabwino!Funafunani chilungamo,thandizani oponderezedwa.Tetezani ana amasiye,muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.” 18 Yehova akuti,“Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu.Ngakhale machimo anu ali ofiira,adzayera ngati thonje.Ngakhale ali ofiira ngati kapezi,adzayera ngati ubweya wankhosa. 19 Ngati muli okonzeka kundimveramudzadya zinthu zabwino za mʼdziko; 20 koma mukakana ndi kuwukiramudzaphedwa ndi lupanga.”Pakuti Yehova wayankhula. 21 Taonani momwe mzinda wokhulupirikawasandukira wadama!Mzinda umene kale unali wodzaza ndi chiweruzo cholungama;mu mzindamo munali chilungamo,koma tsopano muli anthu opha anzawo! 22 Siliva wako wasanduka wachabechabe,vinyo wako wabwino wasungunulidwa ndi madzi. 23 Atsogoleri ako ndi owukira,anthu ogwirizana ndi mbala;onse amakonda ziphuphundipo amathamangira mphatso.Iwo sateteza ana amasiye;ndipo samvera madandawulo a akazi amasiye. 24 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova Wamphamvu,Wamphamvuyo wa Israeli, akunena kuti,“Haa, odana nane ndidzawatha,ndipo ndidzawabwezera ndekha adani anga. 25 Ndidzatambasula dzanja langa kuti ndilimbane nawe;ndidzasungunula machimo ako nʼkuwachotsa,monga mmene amachotsera dzimbiri ndi mankhwala. 26 Ndidzabwezeretsa oweruza ako ngati masiku amakedzana,aphungu ako ndidzawabwezeretsa ngati poyamba paja.Kenaka iweyo udzatchedwamzinda wolungama,mzinda wokhulupirika.” 27 Ziyoni adzawomboledwa mwa chiweruzo cholungama,anthu ake olapadi adzapulumutsidwa mwachilungamo. 28 Koma owukira ndi ochimwa adzawawonongera pamodzi,ndipo amene asiya Yehova adzatheratu. 29 “Mudzachita nayo manyazi mitengo ya thunduimene inkakusangalatsani;mudzagwetsa nkhope chifukwa cha mindaimene munayipatula. 30 Mudzakhala ngati mtengo wa thundu umene masamba ake akufota,mudzakhala ngati munda wopanda madzi. 31 Munthu wamphamvu adzasanduka ngati udzu wowuma,ndipo ntchito zake zidzakhala ngati mbaliwali;motero zonse zidzayakira limodzi,popanda woti azimitse motowo.”

In Other Versions

Isaiah 1 in the ANGEFD

Isaiah 1 in the ANTPNG2D

Isaiah 1 in the AS21

Isaiah 1 in the BAGH

Isaiah 1 in the BBPNG

Isaiah 1 in the BBT1E

Isaiah 1 in the BDS

Isaiah 1 in the BEV

Isaiah 1 in the BHAD

Isaiah 1 in the BIB

Isaiah 1 in the BLPT

Isaiah 1 in the BNT

Isaiah 1 in the BNTABOOT

Isaiah 1 in the BNTLV

Isaiah 1 in the BOATCB

Isaiah 1 in the BOATCB2

Isaiah 1 in the BOBCV

Isaiah 1 in the BOCNT

Isaiah 1 in the BOECS

Isaiah 1 in the BOHCB

Isaiah 1 in the BOHCV

Isaiah 1 in the BOHLNT

Isaiah 1 in the BOHNTLTAL

Isaiah 1 in the BOICB

Isaiah 1 in the BOILNTAP

Isaiah 1 in the BOITCV

Isaiah 1 in the BOKCV

Isaiah 1 in the BOKCV2

Isaiah 1 in the BOKHWOG

Isaiah 1 in the BOKSSV

Isaiah 1 in the BOLCB

Isaiah 1 in the BOLCB2

Isaiah 1 in the BOMCV

Isaiah 1 in the BONAV

Isaiah 1 in the BONCB

Isaiah 1 in the BONLT

Isaiah 1 in the BONUT2

Isaiah 1 in the BOPLNT

Isaiah 1 in the BOSCB

Isaiah 1 in the BOSNC

Isaiah 1 in the BOTLNT

Isaiah 1 in the BOVCB

Isaiah 1 in the BOYCB

Isaiah 1 in the BPBB

Isaiah 1 in the BPH

Isaiah 1 in the BSB

Isaiah 1 in the CCB

Isaiah 1 in the CUV

Isaiah 1 in the CUVS

Isaiah 1 in the DBT

Isaiah 1 in the DGDNT

Isaiah 1 in the DHNT

Isaiah 1 in the DNT

Isaiah 1 in the ELBE

Isaiah 1 in the EMTV

Isaiah 1 in the ESV

Isaiah 1 in the FBV

Isaiah 1 in the FEB

Isaiah 1 in the GGMNT

Isaiah 1 in the GNT

Isaiah 1 in the HARY

Isaiah 1 in the HNT

Isaiah 1 in the IRVA

Isaiah 1 in the IRVB

Isaiah 1 in the IRVG

Isaiah 1 in the IRVH

Isaiah 1 in the IRVK

Isaiah 1 in the IRVM

Isaiah 1 in the IRVM2

Isaiah 1 in the IRVO

Isaiah 1 in the IRVP

Isaiah 1 in the IRVT

Isaiah 1 in the IRVT2

Isaiah 1 in the IRVU

Isaiah 1 in the ISVN

Isaiah 1 in the JSNT

Isaiah 1 in the KAPI

Isaiah 1 in the KBT1ETNIK

Isaiah 1 in the KBV

Isaiah 1 in the KJV

Isaiah 1 in the KNFD

Isaiah 1 in the LBA

Isaiah 1 in the LBLA

Isaiah 1 in the LNT

Isaiah 1 in the LSV

Isaiah 1 in the MAAL

Isaiah 1 in the MBV

Isaiah 1 in the MBV2

Isaiah 1 in the MHNT

Isaiah 1 in the MKNFD

Isaiah 1 in the MNG

Isaiah 1 in the MNT

Isaiah 1 in the MNT2

Isaiah 1 in the MRS1T

Isaiah 1 in the NAA

Isaiah 1 in the NASB

Isaiah 1 in the NBLA

Isaiah 1 in the NBS

Isaiah 1 in the NBVTP

Isaiah 1 in the NET2

Isaiah 1 in the NIV11

Isaiah 1 in the NNT

Isaiah 1 in the NNT2

Isaiah 1 in the NNT3

Isaiah 1 in the PDDPT

Isaiah 1 in the PFNT

Isaiah 1 in the RMNT

Isaiah 1 in the SBIAS

Isaiah 1 in the SBIBS

Isaiah 1 in the SBIBS2

Isaiah 1 in the SBICS

Isaiah 1 in the SBIDS

Isaiah 1 in the SBIGS

Isaiah 1 in the SBIHS

Isaiah 1 in the SBIIS

Isaiah 1 in the SBIIS2

Isaiah 1 in the SBIIS3

Isaiah 1 in the SBIKS

Isaiah 1 in the SBIKS2

Isaiah 1 in the SBIMS

Isaiah 1 in the SBIOS

Isaiah 1 in the SBIPS

Isaiah 1 in the SBISS

Isaiah 1 in the SBITS

Isaiah 1 in the SBITS2

Isaiah 1 in the SBITS3

Isaiah 1 in the SBITS4

Isaiah 1 in the SBIUS

Isaiah 1 in the SBIVS

Isaiah 1 in the SBT

Isaiah 1 in the SBT1E

Isaiah 1 in the SCHL

Isaiah 1 in the SNT

Isaiah 1 in the SUSU

Isaiah 1 in the SUSU2

Isaiah 1 in the SYNO

Isaiah 1 in the TBIAOTANT

Isaiah 1 in the TBT1E

Isaiah 1 in the TBT1E2

Isaiah 1 in the TFTIP

Isaiah 1 in the TFTU

Isaiah 1 in the TGNTATF3T

Isaiah 1 in the THAI

Isaiah 1 in the TNFD

Isaiah 1 in the TNT

Isaiah 1 in the TNTIK

Isaiah 1 in the TNTIL

Isaiah 1 in the TNTIN

Isaiah 1 in the TNTIP

Isaiah 1 in the TNTIZ

Isaiah 1 in the TOMA

Isaiah 1 in the TTENT

Isaiah 1 in the UBG

Isaiah 1 in the UGV

Isaiah 1 in the UGV2

Isaiah 1 in the UGV3

Isaiah 1 in the VBL

Isaiah 1 in the VDCC

Isaiah 1 in the YALU

Isaiah 1 in the YAPE

Isaiah 1 in the YBVTP

Isaiah 1 in the ZBP