Judges 14 (BOGWICC)

1 Samsoni anapita ku Timna ndipo kumeneko anaonako mtsikana wa Chifilisiti. 2 Atabwerera kwawo, anawuza abambo ndi amayi ake kuti, “Ine ndaona mtsikana wa Chifilisiti ku Timna, tsono mukanditengere ameneyo kuti akhale mkazi wanga.” 3 Koma abambo ndi amayi ake anayankha kuti, “Kodi palibe mkazi pakati pa abale akowa kapena pakati pa anthu a mtundu wako, kuti iwe upite kukapeza mkazi kwa Afilisti anthu osachita mdulidwe?”Koma Samsoni anawuza abambo ake kuti, “Kanditengereni ameneyu basi, pakuti ndamukonda.” 4 (Abambo ndi amayi ake sankadziwa kuti zimenezi zinali zochokera kwa Yehova, pakuti Yehova amafuna powapezera chifukwa Afilistiwo. Nthawi imeneyo nʼkuti Afilisti akulamulira Aisraeli). 5 Choncho Samsoni pamodzi ndi abambo ake anapita ku Timna. Akuyandikira minda ya mpesa ya ku Timna, mwadzidzidzi anamva kubuma kwa mkango waungʼono ukubwera kumene kunali iye. 6 Tsono Mzimu wa Yehova unafika ndi mphamvu pa Samsoni ndipo ngakhale analibe chida mʼmanja mwake, iye anakadzula mkangowo ngati akukadzula mwana wambuzi. Koma sanawuze abambo kapena amayi ake zimene anachitazo. 7 Kenaka Samsoni anapita kukakambirana ndi mkaziyo, ndipo anamukonda mtsikanayo. 8 Patapita nthawi, Samsoni anabwerera kukatenga mtsikana uja. Panjira anapatuka kukaona mkango unawupha uja, ndipo anangoona njuchi zili mu mkangowo pamodzi ndi uchi wake. 9 Tsono anakomberako uchi uja mʼmanja mwake ndi kumapita akudya. Atabwereranso kwa abambo ndi amayi ake, anawapatsako uchiwo ndipo anadya. Koma sanawawuze kuti uchi umenewo anawufula mu mkango wakufa. 10 Tsopano Samsoni anapita ku nyumba kwa mtsikanayo. Ndipo kumeneko Samsoni anakonza phwando monga ankachitira anyamata. 11 Makolo a mkwatibwiyo atamuona, anasankha anyamata makumi atatu kuti akhale naye. 12 Samsoni anawawuza kuti, “Bwanji ndikuphereni mwambi. Mukandiwuza tanthauzo lake asanathe masiku asanu ndi awiri aphwandowa, ndidzakupatsani zovala makumi atatu za bafuta ndi zina makumi atatu za tsiku la chikondwerero. 13 Koma ngati simutha kundiwuza tanthauzo lake, inuyo mudzandipatsa zovala makumi atatu zabafuta ndi zina za tsiku la chikondwerero.”Iwo anamuyankha kuti, “Tiwuze mwambi wakowo tiwumve.” 14 Iye anati,“Chakudya chinatuluka mu chinthu chodya chinzake;ndipo chozuna chinatuluka mu chinthu champhamvu.”Panapita masiku atatu anthuwo akulephera kumasulira mwambiwo. 15 Tsiku lachinayi anthuwo anawuza mkazi wa Samsoni kuti, “Umunyengerere mwamuna wako kuti akuwuze tanthauzo la mwambiwu. Ngati sutero tikutentha iweyo pamodzi ndi nyumba ya abambo ako. Kodi unatiyitana kuti mudzatilande zinthu zathu?” 16 Kenaka mkazi wa Samsoni anayamba kulira pamaso pake namuwuza kuti, “Inu mumandida ndipo simundikonda. Mwaphera anyamata a mtundu wathu mwambi, koma ine wosandiwuza tanthauzo lake.”Samsoni anamuyankha kuti, “Taona sindinawuze abambo kapena amayi anga, ndiye ndiwuze iweyo?” 17 Mkaziyo anamulirira masiku onse asanu ndi awiri aphwandowo. Choncho pa tsiku lachisanu ndi chiwiri anamuwuza tanthauzo lake popeza amamukakamiza. Ndipo mkaziyo anakawuza abale ake aja tanthauzo la mwambiwo. 18 Pambuyo pake anthu a mu mzinda aja anamuwuza Samsoni pa tsiku lachisanu ndi chiwiri dzuwa lisanalowe kuti,“Chozuna nʼchiyani choposa uchi?Champhamvu nʼchiyani choposa mkango?”Samsoni anawawuza kuti,“Mukanapanda kutipula ndi ngʼombe yanga yayingʼono,simukanatha kumasulira mwambi wangawu.” 19 Ndipo Mzimu wa Yehova unafika pa iye mwamphamvu. Choncho anatsikira ku Asikeloni naphako anthu makumi atatu, natenga zovala zawo za tsiku la chikondwerero napereka kwa anthu amene anamasulira mwambi wake. Kenaka anabwerera ku nyumba ya abambo ake ndi mkwiyo waukulu. 20 Ndipo mkazi wa Samsoniyo anamukwatitsa kwa amene anali mnzake womuperekeza pa ukwati paja.

In Other Versions

Judges 14 in the ANGEFD

Judges 14 in the ANTPNG2D

Judges 14 in the AS21

Judges 14 in the BAGH

Judges 14 in the BBPNG

Judges 14 in the BBT1E

Judges 14 in the BDS

Judges 14 in the BEV

Judges 14 in the BHAD

Judges 14 in the BIB

Judges 14 in the BLPT

Judges 14 in the BNT

Judges 14 in the BNTABOOT

Judges 14 in the BNTLV

Judges 14 in the BOATCB

Judges 14 in the BOATCB2

Judges 14 in the BOBCV

Judges 14 in the BOCNT

Judges 14 in the BOECS

Judges 14 in the BOHCB

Judges 14 in the BOHCV

Judges 14 in the BOHLNT

Judges 14 in the BOHNTLTAL

Judges 14 in the BOICB

Judges 14 in the BOILNTAP

Judges 14 in the BOITCV

Judges 14 in the BOKCV

Judges 14 in the BOKCV2

Judges 14 in the BOKHWOG

Judges 14 in the BOKSSV

Judges 14 in the BOLCB

Judges 14 in the BOLCB2

Judges 14 in the BOMCV

Judges 14 in the BONAV

Judges 14 in the BONCB

Judges 14 in the BONLT

Judges 14 in the BONUT2

Judges 14 in the BOPLNT

Judges 14 in the BOSCB

Judges 14 in the BOSNC

Judges 14 in the BOTLNT

Judges 14 in the BOVCB

Judges 14 in the BOYCB

Judges 14 in the BPBB

Judges 14 in the BPH

Judges 14 in the BSB

Judges 14 in the CCB

Judges 14 in the CUV

Judges 14 in the CUVS

Judges 14 in the DBT

Judges 14 in the DGDNT

Judges 14 in the DHNT

Judges 14 in the DNT

Judges 14 in the ELBE

Judges 14 in the EMTV

Judges 14 in the ESV

Judges 14 in the FBV

Judges 14 in the FEB

Judges 14 in the GGMNT

Judges 14 in the GNT

Judges 14 in the HARY

Judges 14 in the HNT

Judges 14 in the IRVA

Judges 14 in the IRVB

Judges 14 in the IRVG

Judges 14 in the IRVH

Judges 14 in the IRVK

Judges 14 in the IRVM

Judges 14 in the IRVM2

Judges 14 in the IRVO

Judges 14 in the IRVP

Judges 14 in the IRVT

Judges 14 in the IRVT2

Judges 14 in the IRVU

Judges 14 in the ISVN

Judges 14 in the JSNT

Judges 14 in the KAPI

Judges 14 in the KBT1ETNIK

Judges 14 in the KBV

Judges 14 in the KJV

Judges 14 in the KNFD

Judges 14 in the LBA

Judges 14 in the LBLA

Judges 14 in the LNT

Judges 14 in the LSV

Judges 14 in the MAAL

Judges 14 in the MBV

Judges 14 in the MBV2

Judges 14 in the MHNT

Judges 14 in the MKNFD

Judges 14 in the MNG

Judges 14 in the MNT

Judges 14 in the MNT2

Judges 14 in the MRS1T

Judges 14 in the NAA

Judges 14 in the NASB

Judges 14 in the NBLA

Judges 14 in the NBS

Judges 14 in the NBVTP

Judges 14 in the NET2

Judges 14 in the NIV11

Judges 14 in the NNT

Judges 14 in the NNT2

Judges 14 in the NNT3

Judges 14 in the PDDPT

Judges 14 in the PFNT

Judges 14 in the RMNT

Judges 14 in the SBIAS

Judges 14 in the SBIBS

Judges 14 in the SBIBS2

Judges 14 in the SBICS

Judges 14 in the SBIDS

Judges 14 in the SBIGS

Judges 14 in the SBIHS

Judges 14 in the SBIIS

Judges 14 in the SBIIS2

Judges 14 in the SBIIS3

Judges 14 in the SBIKS

Judges 14 in the SBIKS2

Judges 14 in the SBIMS

Judges 14 in the SBIOS

Judges 14 in the SBIPS

Judges 14 in the SBISS

Judges 14 in the SBITS

Judges 14 in the SBITS2

Judges 14 in the SBITS3

Judges 14 in the SBITS4

Judges 14 in the SBIUS

Judges 14 in the SBIVS

Judges 14 in the SBT

Judges 14 in the SBT1E

Judges 14 in the SCHL

Judges 14 in the SNT

Judges 14 in the SUSU

Judges 14 in the SUSU2

Judges 14 in the SYNO

Judges 14 in the TBIAOTANT

Judges 14 in the TBT1E

Judges 14 in the TBT1E2

Judges 14 in the TFTIP

Judges 14 in the TFTU

Judges 14 in the TGNTATF3T

Judges 14 in the THAI

Judges 14 in the TNFD

Judges 14 in the TNT

Judges 14 in the TNTIK

Judges 14 in the TNTIL

Judges 14 in the TNTIN

Judges 14 in the TNTIP

Judges 14 in the TNTIZ

Judges 14 in the TOMA

Judges 14 in the TTENT

Judges 14 in the UBG

Judges 14 in the UGV

Judges 14 in the UGV2

Judges 14 in the UGV3

Judges 14 in the VBL

Judges 14 in the VDCC

Judges 14 in the YALU

Judges 14 in the YAPE

Judges 14 in the YBVTP

Judges 14 in the ZBP