Judges 21 (BOGWICC)

1 Aisraeli anali atalumbira ku Mizipa kuti, “Palibe mmodzi wa ife adzapereke mwana wake wamkazi kuti akwatiwe ndi mwamuna wa fuko la Benjamini.” 2 Anthu anapita ku Beteli kumene anakakhala pansi pamaso pa Mulungu mpaka madzulo. Iwo anakweza mawu nalira kwambiri. 3 Iwo ankanena kuti, “Yehova Mulungu wa Israeli, nʼchifukwa chiyani izi zachitika mʼdziko la Israeli kuti lero fuko limodzi lisowe mu Israeli?” 4 Mmawa mwake anthu anadzuka namanga guwa lansembe ndi kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. 5 Kenaka Aisraeli anafunsa kuti, “Kodi ndani pakati pa mafuko a Israeli sanafike ku msonkhano wa Yehova?” Anatero chifukwa anachita malumbiro aakulu okhudza munthu amene alephere kupita ku Mizipa ndi kuti woteroyo ayenera kuphedwa. 6 Tsono Aisraeli anamva chisoni chifukwa cha abale awo, Abenjamini. Iwo anati, “Lero fuko limodzi lachotsedwa mu Israeli. 7 Kodi tingawapezere bwanji anthu otsalawa akazi woti awakwatire? Paja ife tinalumbira kwa Yehova kuti sitidzapereka ana anthu aakazi kuti awakwatire. 8 Kenaka anafunsa kuti, ‘Kodi mu fuko la Israeli ndani amene sanabwere pamaso pa Yehova ku Mizipa?’ ” Tsono panapezeka kuti panalibe ndi mmodzi yemwe wochokera ku Yabesi Giliyadi amene anapita ku msonkhano ku misasa kuja. 9 Pamene anthu anawerengana anangoona kuti anthu a ku Yabesi Giliyadi palibe. 10 Choncho msonkhano unatumiza anthu ankhondo 12,000 ndi kuwalamula kuti, “Mukaphe anthu onse okhala ku Yabesi Giliyadi, kuphatikizapo akazi ndi ana.” 11 Izi ndi zimene mukachite. “Mukaphe mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense amene anadziwapo mwamuna.” 12 Iwo anapeza atsikana 400 pakati pa anthu okhala mu Yabesi Giliyadi amene anali asanadziwepo mwamuna ndipo anabwera nawo ku misasa ku Silo mʼdziko la Kanaani. 13 Kenaka msonkhano wonse unatumiza uthenga kwa Abenjamini amene ankakhala ku thanthwe la Rimoni kuwawuza kuti nkhondo yatha. 14 Choncho Abenjamini anabwera nthawi imeneyo ndipo Aisraeli anawapatsa akazi a ku Yabesi Giliyadi amene sanaphedwe. Koma sanapezeke owakwanira. 15 Aisraeli anamvera chisoni Abenjamini, chifukwa Yehova anachita ngati waligwerula dzino fuko la Israeli. 16 Choncho akuluakulu a msonkhano anati, “Kodi tikawapezera kuti akazi anthu otsalirawa kuti awakwatire popeza kuti akazi a fuko la Benjamini anaphedwa?” 17 Iwo anati, “Abenjamini amene anapulumukawa ayenera kukhala ndi zidzukulu, kuti mtundu wa Israeli usafafanizike. 18 Ife sitingathe kuwapatsa ana anthu aakazi kuti akwatire. Paja tinalumbira kuti, ‘Akhale wotembereredwa aliyense amene adzapereka mwana wake wamkazi kwa mwamuna wa fuko la Benjamini kuti akwatire.’ 19 Ndipo anati, ‘Paja ku Silo kuli chikondwerero cha chaka ndi chaka cholemekeza Yehova. Tsono Silo ali kumpoto kwa Beteli, kummawa kwa msewu wochokera ku Beteli kupita ku Sekemu, ndiponso kummwera kwa Lebona.’ ” 20 Choncho anawalamulira Abenjamini aja kuti, “Pitani mukabisale mʼminda ya mpesa 21 ndipo mukakhale tcheru. Ana aakazi a ku Silo akadzatulukira kudzavina nawo magule, pomwepo inu mutuluke minda ya mpesa ndi kukawagwira aliyense wake ndi kupita nawo ku dziko la Benjamini. 22 Ngati abambo awo kapena alongo awo adzabwera kudzadandaula kwa ife, tidzawawuza kuti, ‘Chonde, tikomereni mtima powalola kuti atenga ana anu aakaziwo popeza kuti ife sitinawapezere akazi pomenya nkhondo. Inunso simunachite kuwapatsa. Mukanatero ndiye mukanapalamula.’ ” 23 Abenjamini anachitadi zimenezi. Mwa akazi amene ankavina aja anagwirapo ena, malingana ndi chiwerengero chawo, nawatenga kuti akhale akazi awo. Kenaka ananyamuka kubwerera ku dziko la kwawo, nakamanganso mizinda yawo ndi kumakhalamo. 24 Pambuyo pake Aisraeli anachoka kumeneko ndi kubwerera kwawo, ku mafuko ndi ku mabanja awo, aliyense ku dera la cholowa chake. 25 Masiku amenewo kunalibe mfumu ku Israeli. Aliyense ankangochita zimene zomukomera yekha.

In Other Versions

Judges 21 in the ANGEFD

Judges 21 in the ANTPNG2D

Judges 21 in the AS21

Judges 21 in the BAGH

Judges 21 in the BBPNG

Judges 21 in the BBT1E

Judges 21 in the BDS

Judges 21 in the BEV

Judges 21 in the BHAD

Judges 21 in the BIB

Judges 21 in the BLPT

Judges 21 in the BNT

Judges 21 in the BNTABOOT

Judges 21 in the BNTLV

Judges 21 in the BOATCB

Judges 21 in the BOATCB2

Judges 21 in the BOBCV

Judges 21 in the BOCNT

Judges 21 in the BOECS

Judges 21 in the BOHCB

Judges 21 in the BOHCV

Judges 21 in the BOHLNT

Judges 21 in the BOHNTLTAL

Judges 21 in the BOICB

Judges 21 in the BOILNTAP

Judges 21 in the BOITCV

Judges 21 in the BOKCV

Judges 21 in the BOKCV2

Judges 21 in the BOKHWOG

Judges 21 in the BOKSSV

Judges 21 in the BOLCB

Judges 21 in the BOLCB2

Judges 21 in the BOMCV

Judges 21 in the BONAV

Judges 21 in the BONCB

Judges 21 in the BONLT

Judges 21 in the BONUT2

Judges 21 in the BOPLNT

Judges 21 in the BOSCB

Judges 21 in the BOSNC

Judges 21 in the BOTLNT

Judges 21 in the BOVCB

Judges 21 in the BOYCB

Judges 21 in the BPBB

Judges 21 in the BPH

Judges 21 in the BSB

Judges 21 in the CCB

Judges 21 in the CUV

Judges 21 in the CUVS

Judges 21 in the DBT

Judges 21 in the DGDNT

Judges 21 in the DHNT

Judges 21 in the DNT

Judges 21 in the ELBE

Judges 21 in the EMTV

Judges 21 in the ESV

Judges 21 in the FBV

Judges 21 in the FEB

Judges 21 in the GGMNT

Judges 21 in the GNT

Judges 21 in the HARY

Judges 21 in the HNT

Judges 21 in the IRVA

Judges 21 in the IRVB

Judges 21 in the IRVG

Judges 21 in the IRVH

Judges 21 in the IRVK

Judges 21 in the IRVM

Judges 21 in the IRVM2

Judges 21 in the IRVO

Judges 21 in the IRVP

Judges 21 in the IRVT

Judges 21 in the IRVT2

Judges 21 in the IRVU

Judges 21 in the ISVN

Judges 21 in the JSNT

Judges 21 in the KAPI

Judges 21 in the KBT1ETNIK

Judges 21 in the KBV

Judges 21 in the KJV

Judges 21 in the KNFD

Judges 21 in the LBA

Judges 21 in the LBLA

Judges 21 in the LNT

Judges 21 in the LSV

Judges 21 in the MAAL

Judges 21 in the MBV

Judges 21 in the MBV2

Judges 21 in the MHNT

Judges 21 in the MKNFD

Judges 21 in the MNG

Judges 21 in the MNT

Judges 21 in the MNT2

Judges 21 in the MRS1T

Judges 21 in the NAA

Judges 21 in the NASB

Judges 21 in the NBLA

Judges 21 in the NBS

Judges 21 in the NBVTP

Judges 21 in the NET2

Judges 21 in the NIV11

Judges 21 in the NNT

Judges 21 in the NNT2

Judges 21 in the NNT3

Judges 21 in the PDDPT

Judges 21 in the PFNT

Judges 21 in the RMNT

Judges 21 in the SBIAS

Judges 21 in the SBIBS

Judges 21 in the SBIBS2

Judges 21 in the SBICS

Judges 21 in the SBIDS

Judges 21 in the SBIGS

Judges 21 in the SBIHS

Judges 21 in the SBIIS

Judges 21 in the SBIIS2

Judges 21 in the SBIIS3

Judges 21 in the SBIKS

Judges 21 in the SBIKS2

Judges 21 in the SBIMS

Judges 21 in the SBIOS

Judges 21 in the SBIPS

Judges 21 in the SBISS

Judges 21 in the SBITS

Judges 21 in the SBITS2

Judges 21 in the SBITS3

Judges 21 in the SBITS4

Judges 21 in the SBIUS

Judges 21 in the SBIVS

Judges 21 in the SBT

Judges 21 in the SBT1E

Judges 21 in the SCHL

Judges 21 in the SNT

Judges 21 in the SUSU

Judges 21 in the SUSU2

Judges 21 in the SYNO

Judges 21 in the TBIAOTANT

Judges 21 in the TBT1E

Judges 21 in the TBT1E2

Judges 21 in the TFTIP

Judges 21 in the TFTU

Judges 21 in the TGNTATF3T

Judges 21 in the THAI

Judges 21 in the TNFD

Judges 21 in the TNT

Judges 21 in the TNTIK

Judges 21 in the TNTIL

Judges 21 in the TNTIN

Judges 21 in the TNTIP

Judges 21 in the TNTIZ

Judges 21 in the TOMA

Judges 21 in the TTENT

Judges 21 in the UBG

Judges 21 in the UGV

Judges 21 in the UGV2

Judges 21 in the UGV3

Judges 21 in the VBL

Judges 21 in the VDCC

Judges 21 in the YALU

Judges 21 in the YAPE

Judges 21 in the YBVTP

Judges 21 in the ZBP