Jeremiah 36 (BOGWICC)

1 Chaka chachinayi cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 2 “Tenga buku ndipo ulembemo mawu onse amene ndayankhula nawe otsutsa Israeli, Yuda ndi mitundu yonse ya anthu, kuyambira nthawi imene ndinayamba kuyankhula nawe pa nthawi ya ulamuliro wa Yosiya mpaka lero lino. 3 Mwina mwake anthu a ku Yuda adzamva za zoopsa zonse zimene ndakonza kuti ndiwachitire, ndipo munthu aliyense adzatembenuka ndi kusiya ntchito zake zoyipa. Motero ndidzawakhululukira zoyipa zawo ndi machimo awo.” 4 Tsono Yeremiya anayitana Baruki mwana wa Neriya. Baruki analemba mʼbuku mawu onse amene Yeremiya ankamuwuza, mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya. 5 Kenaka Yeremiya anawuza Baruki kuti, “Ine andiletsa kupita ku Nyumba ya Mulungu. 6 Tsono iwe upite ku Nyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya ndipo ukawerenge mawu a Yehova ochokera mʼbukumu amene ndinakulembetsa anthu onse akumva. Ukawawerengere anthu onse a ku Yuda amene amabwera ku Nyumba ya Mulungu kuchokera ku mizinda yawo. 7 Mwina mwake adzapempha kwa Yehova ndipo aliyense adzatembenuka ndi kusiya makhalidwe ake oyipa pakuti mkwiyo ndi ukali wa Yehova pa anthu awa ndi woopsa kwambiri.” 8 Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamuwuza kuti achite. Mʼnyumba ya Yehova, iye anawerenga mawu a Yehova ochokera mʼbukulo. 9 Pa mwezi wachisanu ndi chinayi wa chaka chachisanu cha Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya Yuda, anthu onse a mu Yerusalemu ndi onse amene anabwera kumeneko kuchokera ku mizinda ya Yuda, anapangana za kusala kudya kuti apepese Yehova. 10 Atayima pa chipinda cha Gemariya mwana wa mlembi Safani, chimene chinali mʼbwalo lapamwamba, pafupi ndi Chipata Chatsopano cholowera ku Nyumba ya Yehova, Baruki anawerenga mawu onse a Yeremiya amene anali mʼbuku muja kwa anthu onse amene anali ku Nyumba ya Yehova. 11 Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, atamva mawu onse a Yehova ochokera mʼbukumo, 12 anapita ku nyumba ya mfumu nakalowa ku chipinda cha mlembi. Akuluakulu, mlembi Elisama, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani mwana wa Akibori, Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya pamodzi ndi akuluakulu ena onse, anali atasonkhana kumeneko. 13 Tsono Mikaya anawafotokozera mawu onse amene anamva pamene Baruki ankawerenga buku lija anthu onse akumva. 14 Pambuyo pake akuluakulu onsewo anatuma Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusi, kwa Baruki kukamuwuza kuti, “Bwera ndi buku limene unawerenga kwa anthu.” Ndipo Baruki mwana wa Neriya anapita nalo bukulo kwa anthuwo. 15 Iwo anati, “Khala pansi, ndipo tiwerengere bukuli.”Ndipo Baruki anawawerengera. 16 Atamva mawu onsewo, anayangʼanana mwa mantha ndipo anamuwuza Baruki kuti, “Ndithudi tikafotokozera mfumu mawu onsewa.” 17 Tsono anamufunsa Baruki kuti, “Tatiwuze, unalemba bwanji mawu onsewa? Kodi ndi Yeremiya anakulembetsa zimenezi?” 18 Baruki anayankha kuti, “Inde, ndi Yeremiya amene anandiwuza mawu onsewa, ndipo ine ndinawalemba ndi utoto mʼbukumu.” 19 Kenaka akuluakuluwo anamuwuza Baruki kuti, “Iweyo ndi Yeremiya, pitani mukabisale. Munthu aliyense asadziwe kumene muli.” 20 Atayika bukulo mʼchipinda cha mlembi Elisama, analowa mʼbwalo, napita kwa mfumu ndi kukayifotokozera zonse. 21 Itamva zimenezi mfumu inatuma Yehudi kuti akatenge bukulo, ndipo Yehudi anakalitenga ku chipinda cha mlembi Elisama ndipo anawerengera mfumu pamodzi ndi akuluakulu ake amene anali naye. 22 Unali mwezi wachisanu ndi chinayi ndipo mfumu inali mʼnyumba ya pa nyengo yozizira, ikuwotha moto umene anasonkha. 23 Yehudi ankati akawerenga masamba atatu kapena anayi a bukulo, mfumu inkawangʼamba ndi mpeni ndi kuwaponya pa moto ndipo anapitiriza kuchita zimenezi mpaka buku lonse linapsa. 24 Mfumu pamodzi ndi omutumikira ake onse amene anamva mawu onsewa sanachite mantha kapena kungʼamba zovala zawo. 25 Ngakhale kuti Elinatani, Delaya, ndi Gemariya anapempha mfumu kuti isatenthe bukulo, mfumuyo sinawamvere. 26 Mʼmalo mwake, mfumu inalamula Yerahimeeli mwana wake, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti agwire mlembi Baruki ndi mneneri Yeremiya. Koma pamenepo nʼkuti Yehova atawabisa. 27 Mfumu itatentha buku limene linali ndi mawu amene Yeremiya anamulembetsa Baruki, Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, 28 “Tenganso buku lina ndipo ulembe mawu onse amene anali mʼbuku loyamba lija, limene Yehoyakimu analitentha. 29 Ndiponso akamuwuze Yehoyakimu mfumu ya Yuda kuti, ‘Yehova akuti: Iwe unatentha buku lija ndipo unati: Nʼchifukwa chiyani unalemba kuti mfumu ya ku Babuloni idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndi kupha anthu pamodzi ndi nyama zomwe?’ 30 Nʼchifukwa chake kunena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda Yehova akuti sipadzaoneka munthu wina wolowa mʼmalo mwake pa mpando wa Davide. Akadzafa mtembo wake udzaponyedwa kunja ndipo udzakhala pa dzuwa masana, ndi pachisanu chowundana usiku. 31 Ndidzamulanga pamodzi ndi ana ake ndiponso omutumikira ake chifukwa cha zoyipa zawo; ndidzagwetsa pa iwo ndi pa onse amene akukhala mu Yerusalemu ndiponso pa anthu a ku Yuda masautso onse amene ndinawanena, chifukwa sanamvere.” 32 Choncho Yeremiya anatenga buku lina napatsa mlembi Baruki mwana wa Neriya, ndipo Yeremiya anamulembetsa mawu onse amene anali mʼbuku limene Yehoyakimu mfumu ya Yuda anatentha. Ndipo anawonjezerapo mawu ambiri monga omwewo.

In Other Versions

Jeremiah 36 in the ANGEFD

Jeremiah 36 in the ANTPNG2D

Jeremiah 36 in the AS21

Jeremiah 36 in the BAGH

Jeremiah 36 in the BBPNG

Jeremiah 36 in the BBT1E

Jeremiah 36 in the BDS

Jeremiah 36 in the BEV

Jeremiah 36 in the BHAD

Jeremiah 36 in the BIB

Jeremiah 36 in the BLPT

Jeremiah 36 in the BNT

Jeremiah 36 in the BNTABOOT

Jeremiah 36 in the BNTLV

Jeremiah 36 in the BOATCB

Jeremiah 36 in the BOATCB2

Jeremiah 36 in the BOBCV

Jeremiah 36 in the BOCNT

Jeremiah 36 in the BOECS

Jeremiah 36 in the BOHCB

Jeremiah 36 in the BOHCV

Jeremiah 36 in the BOHLNT

Jeremiah 36 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 36 in the BOICB

Jeremiah 36 in the BOILNTAP

Jeremiah 36 in the BOITCV

Jeremiah 36 in the BOKCV

Jeremiah 36 in the BOKCV2

Jeremiah 36 in the BOKHWOG

Jeremiah 36 in the BOKSSV

Jeremiah 36 in the BOLCB

Jeremiah 36 in the BOLCB2

Jeremiah 36 in the BOMCV

Jeremiah 36 in the BONAV

Jeremiah 36 in the BONCB

Jeremiah 36 in the BONLT

Jeremiah 36 in the BONUT2

Jeremiah 36 in the BOPLNT

Jeremiah 36 in the BOSCB

Jeremiah 36 in the BOSNC

Jeremiah 36 in the BOTLNT

Jeremiah 36 in the BOVCB

Jeremiah 36 in the BOYCB

Jeremiah 36 in the BPBB

Jeremiah 36 in the BPH

Jeremiah 36 in the BSB

Jeremiah 36 in the CCB

Jeremiah 36 in the CUV

Jeremiah 36 in the CUVS

Jeremiah 36 in the DBT

Jeremiah 36 in the DGDNT

Jeremiah 36 in the DHNT

Jeremiah 36 in the DNT

Jeremiah 36 in the ELBE

Jeremiah 36 in the EMTV

Jeremiah 36 in the ESV

Jeremiah 36 in the FBV

Jeremiah 36 in the FEB

Jeremiah 36 in the GGMNT

Jeremiah 36 in the GNT

Jeremiah 36 in the HARY

Jeremiah 36 in the HNT

Jeremiah 36 in the IRVA

Jeremiah 36 in the IRVB

Jeremiah 36 in the IRVG

Jeremiah 36 in the IRVH

Jeremiah 36 in the IRVK

Jeremiah 36 in the IRVM

Jeremiah 36 in the IRVM2

Jeremiah 36 in the IRVO

Jeremiah 36 in the IRVP

Jeremiah 36 in the IRVT

Jeremiah 36 in the IRVT2

Jeremiah 36 in the IRVU

Jeremiah 36 in the ISVN

Jeremiah 36 in the JSNT

Jeremiah 36 in the KAPI

Jeremiah 36 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 36 in the KBV

Jeremiah 36 in the KJV

Jeremiah 36 in the KNFD

Jeremiah 36 in the LBA

Jeremiah 36 in the LBLA

Jeremiah 36 in the LNT

Jeremiah 36 in the LSV

Jeremiah 36 in the MAAL

Jeremiah 36 in the MBV

Jeremiah 36 in the MBV2

Jeremiah 36 in the MHNT

Jeremiah 36 in the MKNFD

Jeremiah 36 in the MNG

Jeremiah 36 in the MNT

Jeremiah 36 in the MNT2

Jeremiah 36 in the MRS1T

Jeremiah 36 in the NAA

Jeremiah 36 in the NASB

Jeremiah 36 in the NBLA

Jeremiah 36 in the NBS

Jeremiah 36 in the NBVTP

Jeremiah 36 in the NET2

Jeremiah 36 in the NIV11

Jeremiah 36 in the NNT

Jeremiah 36 in the NNT2

Jeremiah 36 in the NNT3

Jeremiah 36 in the PDDPT

Jeremiah 36 in the PFNT

Jeremiah 36 in the RMNT

Jeremiah 36 in the SBIAS

Jeremiah 36 in the SBIBS

Jeremiah 36 in the SBIBS2

Jeremiah 36 in the SBICS

Jeremiah 36 in the SBIDS

Jeremiah 36 in the SBIGS

Jeremiah 36 in the SBIHS

Jeremiah 36 in the SBIIS

Jeremiah 36 in the SBIIS2

Jeremiah 36 in the SBIIS3

Jeremiah 36 in the SBIKS

Jeremiah 36 in the SBIKS2

Jeremiah 36 in the SBIMS

Jeremiah 36 in the SBIOS

Jeremiah 36 in the SBIPS

Jeremiah 36 in the SBISS

Jeremiah 36 in the SBITS

Jeremiah 36 in the SBITS2

Jeremiah 36 in the SBITS3

Jeremiah 36 in the SBITS4

Jeremiah 36 in the SBIUS

Jeremiah 36 in the SBIVS

Jeremiah 36 in the SBT

Jeremiah 36 in the SBT1E

Jeremiah 36 in the SCHL

Jeremiah 36 in the SNT

Jeremiah 36 in the SUSU

Jeremiah 36 in the SUSU2

Jeremiah 36 in the SYNO

Jeremiah 36 in the TBIAOTANT

Jeremiah 36 in the TBT1E

Jeremiah 36 in the TBT1E2

Jeremiah 36 in the TFTIP

Jeremiah 36 in the TFTU

Jeremiah 36 in the TGNTATF3T

Jeremiah 36 in the THAI

Jeremiah 36 in the TNFD

Jeremiah 36 in the TNT

Jeremiah 36 in the TNTIK

Jeremiah 36 in the TNTIL

Jeremiah 36 in the TNTIN

Jeremiah 36 in the TNTIP

Jeremiah 36 in the TNTIZ

Jeremiah 36 in the TOMA

Jeremiah 36 in the TTENT

Jeremiah 36 in the UBG

Jeremiah 36 in the UGV

Jeremiah 36 in the UGV2

Jeremiah 36 in the UGV3

Jeremiah 36 in the VBL

Jeremiah 36 in the VDCC

Jeremiah 36 in the YALU

Jeremiah 36 in the YAPE

Jeremiah 36 in the YBVTP

Jeremiah 36 in the ZBP