Jeremiah 41 (BOGWICC)
1 Pa mwezi wachisanu ndi chiwiri Ismaeli mwana wa Netaniya, mdzukulu wa Elisama amene anali wa banja laufumu ndiponso mmodzi wa atsogoleri a ankhondo a mfumu, anabwera ku Mizipa kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ndi anthu khumi. Pamene ankadya naye kumeneko, 2 Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu khumi aja anayimirira ndi kupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mdzukulu wa Safani. Choncho anapha munthu amene mfumu ya ku Babuloni inamusankha kukhala bwanamkubwa wa dzikolo. 3 Ismaeli anaphanso Ayuda onse amene anali pamodzi ndi Gedaliya ku Mizipa, kuphatikizanso asilikali a Ababuloni amene anali ku Mizipako. 4 Mmawa mwake, anthu asanadziwe kuti Gedaliya waphedwa, 5 kunafika anthu 80 ochekera ku Sekemu, Silo ndi Samariya, amene anali atameta ndevu zawo, atangʼamba zovala zawo ndi kudzichekacheka. Iwowa anatenga chopereka cha ufa ndi lubani kuti adzapereke ku Nyumba ya Yehova. 6 Ismaeli mwana wa Netaniya anachoka ku Mizipa akulira kupita kukakumana nawo. Atakumana nawo, iye anati, “Bwerani mudzaonane ndi Gedaliya mwana wa Ahikamu.” 7 Atafika pakati pa mzinda, Ismaeli mwana wa Netaniya pamodzi ndi anthu amene anali naye anawapha anthuwo ndi kuwaponya mʼchitsime. 8 Koma anthu khumi a gululo anawuza Ismaeli kuti, “Musatiphe! Tili ndi tirigu ndi barele, mafuta ndi uchi, zimene tabisa mʼmunda.” Choncho anawasiya ndipo sanawaphere pamodzi ndi anzawo aja. 9 Tsono chitsime chimene anaponyamo mitembo ya anthu amene anawaphawo pamodzi ndi mtembo wa Gedaliya chinali chimene mfumu Asa anachikumba poopsedwa ndi Baasa mfumu ya Israeli. Ismaeli mwana wa Netaliya anachidzaza ndi mitembo. 10 Pambuyo pake Ismaeli anatenga ukapolo anthu ena onse amene anali ku Mizipa: ana aakazi a mfumu pamodzi ndi ena onse amene anatsalira kumeneko, amene Nebuzaradani mtsogoleri wa asilikali olonda mfumu anapatsa Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale bwanamkubwa wawo. Ismaeli mwana wa Netaliya anatenga ukapolo anthuwa ndi kuwoloka nawo kumapita ku dziko la Aamoni. 11 Pamene Yohanani mwana wa Kareya ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye pamodzi anamva zoyipa zonse zimene Ismaeli mwana wa Netaniya anachita, 12 anatenga ankhondo awo onse kupita kukamenyana ndi Ismaeli mwana wa Netaniya. Anakamupeza kufupi ndi chidziwe chachikulu cha ku Gibiyoni. 13 Pamene anthu onse amene Ismaeli anawagwira anaona Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo amene anali naye, anasangalala. 14 Anthu onse amene Ismaeli anawagwira ukapolo ku Mizipa anabwerera ndi kupita kwa Yohanani mwana wa Kareya. 15 Koma Ismaeli pamodzi ndi anthu ake asanu ndi atatu, anathawa Yohanani ndi kuthawira kwa Aamoni. 16 Kenaka Yohanani mwana wa Kareya pamodzi ndi atsogoleri onse a ankhondo amene anali naye anatsogolera anthu onse otsala a ku Mizipa amene anawapulumutsa kwa Ismaeli mwana wa Netaniya atapha Gedaliya mwana wa Ahikamu. Anthu amenewa anali: asilikali, akazi, ana ndi amuna ofulidwa otumikira mfumu amene anawatenga ku Gibiyoni. 17 Ndipo ananyamuka nayima ku Geruti Kimuhamu pafupi ndi Betelehemu pa ulendo wawo wopita ku Igupto 18 kuthawa Ababuloni. Iwo anaopa Ababuloniwo chifukwa Ismaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya ku Babuloni inamuyika kukhala bwanamkubwa wa dzikolo.
In Other Versions
Jeremiah 41 in the ANGEFD
Jeremiah 41 in the ANTPNG2D
Jeremiah 41 in the AS21
Jeremiah 41 in the BAGH
Jeremiah 41 in the BBPNG
Jeremiah 41 in the BBT1E
Jeremiah 41 in the BDS
Jeremiah 41 in the BEV
Jeremiah 41 in the BHAD
Jeremiah 41 in the BIB
Jeremiah 41 in the BLPT
Jeremiah 41 in the BNT
Jeremiah 41 in the BNTABOOT
Jeremiah 41 in the BNTLV
Jeremiah 41 in the BOATCB
Jeremiah 41 in the BOATCB2
Jeremiah 41 in the BOBCV
Jeremiah 41 in the BOCNT
Jeremiah 41 in the BOECS
Jeremiah 41 in the BOHCB
Jeremiah 41 in the BOHCV
Jeremiah 41 in the BOHLNT
Jeremiah 41 in the BOHNTLTAL
Jeremiah 41 in the BOICB
Jeremiah 41 in the BOILNTAP
Jeremiah 41 in the BOITCV
Jeremiah 41 in the BOKCV
Jeremiah 41 in the BOKCV2
Jeremiah 41 in the BOKHWOG
Jeremiah 41 in the BOKSSV
Jeremiah 41 in the BOLCB
Jeremiah 41 in the BOLCB2
Jeremiah 41 in the BOMCV
Jeremiah 41 in the BONAV
Jeremiah 41 in the BONCB
Jeremiah 41 in the BONLT
Jeremiah 41 in the BONUT2
Jeremiah 41 in the BOPLNT
Jeremiah 41 in the BOSCB
Jeremiah 41 in the BOSNC
Jeremiah 41 in the BOTLNT
Jeremiah 41 in the BOVCB
Jeremiah 41 in the BOYCB
Jeremiah 41 in the BPBB
Jeremiah 41 in the BPH
Jeremiah 41 in the BSB
Jeremiah 41 in the CCB
Jeremiah 41 in the CUV
Jeremiah 41 in the CUVS
Jeremiah 41 in the DBT
Jeremiah 41 in the DGDNT
Jeremiah 41 in the DHNT
Jeremiah 41 in the DNT
Jeremiah 41 in the ELBE
Jeremiah 41 in the EMTV
Jeremiah 41 in the ESV
Jeremiah 41 in the FBV
Jeremiah 41 in the FEB
Jeremiah 41 in the GGMNT
Jeremiah 41 in the GNT
Jeremiah 41 in the HARY
Jeremiah 41 in the HNT
Jeremiah 41 in the IRVA
Jeremiah 41 in the IRVB
Jeremiah 41 in the IRVG
Jeremiah 41 in the IRVH
Jeremiah 41 in the IRVK
Jeremiah 41 in the IRVM
Jeremiah 41 in the IRVM2
Jeremiah 41 in the IRVO
Jeremiah 41 in the IRVP
Jeremiah 41 in the IRVT
Jeremiah 41 in the IRVT2
Jeremiah 41 in the IRVU
Jeremiah 41 in the ISVN
Jeremiah 41 in the JSNT
Jeremiah 41 in the KAPI
Jeremiah 41 in the KBT1ETNIK
Jeremiah 41 in the KBV
Jeremiah 41 in the KJV
Jeremiah 41 in the KNFD
Jeremiah 41 in the LBA
Jeremiah 41 in the LBLA
Jeremiah 41 in the LNT
Jeremiah 41 in the LSV
Jeremiah 41 in the MAAL
Jeremiah 41 in the MBV
Jeremiah 41 in the MBV2
Jeremiah 41 in the MHNT
Jeremiah 41 in the MKNFD
Jeremiah 41 in the MNG
Jeremiah 41 in the MNT
Jeremiah 41 in the MNT2
Jeremiah 41 in the MRS1T
Jeremiah 41 in the NAA
Jeremiah 41 in the NASB
Jeremiah 41 in the NBLA
Jeremiah 41 in the NBS
Jeremiah 41 in the NBVTP
Jeremiah 41 in the NET2
Jeremiah 41 in the NIV11
Jeremiah 41 in the NNT
Jeremiah 41 in the NNT2
Jeremiah 41 in the NNT3
Jeremiah 41 in the PDDPT
Jeremiah 41 in the PFNT
Jeremiah 41 in the RMNT
Jeremiah 41 in the SBIAS
Jeremiah 41 in the SBIBS
Jeremiah 41 in the SBIBS2
Jeremiah 41 in the SBICS
Jeremiah 41 in the SBIDS
Jeremiah 41 in the SBIGS
Jeremiah 41 in the SBIHS
Jeremiah 41 in the SBIIS
Jeremiah 41 in the SBIIS2
Jeremiah 41 in the SBIIS3
Jeremiah 41 in the SBIKS
Jeremiah 41 in the SBIKS2
Jeremiah 41 in the SBIMS
Jeremiah 41 in the SBIOS
Jeremiah 41 in the SBIPS
Jeremiah 41 in the SBISS
Jeremiah 41 in the SBITS
Jeremiah 41 in the SBITS2
Jeremiah 41 in the SBITS3
Jeremiah 41 in the SBITS4
Jeremiah 41 in the SBIUS
Jeremiah 41 in the SBIVS
Jeremiah 41 in the SBT
Jeremiah 41 in the SBT1E
Jeremiah 41 in the SCHL
Jeremiah 41 in the SNT
Jeremiah 41 in the SUSU
Jeremiah 41 in the SUSU2
Jeremiah 41 in the SYNO
Jeremiah 41 in the TBIAOTANT
Jeremiah 41 in the TBT1E
Jeremiah 41 in the TBT1E2
Jeremiah 41 in the TFTIP
Jeremiah 41 in the TFTU
Jeremiah 41 in the TGNTATF3T
Jeremiah 41 in the THAI
Jeremiah 41 in the TNFD
Jeremiah 41 in the TNT
Jeremiah 41 in the TNTIK
Jeremiah 41 in the TNTIL
Jeremiah 41 in the TNTIN
Jeremiah 41 in the TNTIP
Jeremiah 41 in the TNTIZ
Jeremiah 41 in the TOMA
Jeremiah 41 in the TTENT
Jeremiah 41 in the UBG
Jeremiah 41 in the UGV
Jeremiah 41 in the UGV2
Jeremiah 41 in the UGV3
Jeremiah 41 in the VBL
Jeremiah 41 in the VDCC
Jeremiah 41 in the YALU
Jeremiah 41 in the YAPE
Jeremiah 41 in the YBVTP
Jeremiah 41 in the ZBP