Jeremiah 52 (BOGWICC)

1 Zedekiya anali wa zaka 21 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Amayi ake anali Hamutali mwana wa Yeremiya wa ku Libina. 2 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Yehoyakimu. 3 Chifukwa cha zonse zimene zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda Yehova anakwiyira anthu ake mpaka kuwachotsa pamaso pake.Tsono Zedekiya anawukira mfumu ya ku Babuloni. 4 Choncho mʼchaka cha chisanu ndi chinayi cha ulamuliro wa Zedekiya, mwezi wakhumi, pa tsiku la khumi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni anabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo Yerusalemu. Anamanga misasa ndi mitumbira yankhondo kunja kuzungulira mzindawo. 5 Mzindawo unazingidwa mpaka chaka cha khumi ndi chimodzi cha ulamuliro wa Mfumu Zedekiya. 6 Pa tsiku lachisanu ndi chinayi la mwezi wachinayi njala inakula kwambiri mu mzindamo kotero kuti munalibe chakudya choti anthu nʼkudya. 7 Tsono linga la mzindawo linabowoledwa, ndipo ankhondo onse anathawa. Iwo anatuluka mu mzindamo usiku kudzera pa chipata cha pakati pa makoma awiri a pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababuloni anali atazinga mzindawo. Ndipo anathawira ku Araba, 8 koma gulu la ankhondo la ku Babuloni linalondola mfumu Zedekiya ndi kumupeza mʼchigwa cha ku Yeriko. Ankhondo onse anamusiya yekha nabalalika. 9 Anagwidwa napita naye kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula mʼdziko la Hamati, kumene anagamula mlandu wake. 10 Ku Ribulako mfumu ya ku Babuloni inapha ana aamuna a Zedekiya iyeyo akuona; ndiponso inapha akuluakulu onse a ku Yuda. 11 Ndipo inamukolowola maso Zedekiya, ndi kumumanga ndi maunyolo a mkuwa nʼkupita naye ku Babuloni kumene inakamuyika mʼndende kuti akhalemo moyo wake wonse. 12 Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi, chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni, Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo a mfumu, amene amatumikira mfumu ya ku Babuloni, anabwera ku Yerusalemu. 13 Ndipo anatentha Nyumba ya Yehova, nyumba ya mfumu ndi nyumba zonse za mu Yerusalemu. Anatentha nyumba iliyonse. 14 Tsono gulu lonse lankhondo la Ababuloni limene linali ndi mtsogoleri wa ankhondo a mfumu uja linagwetsa malinga onse ozungulira Yerusalemu. 15 Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anatenga anthu amene anatsala mu mzindamo, anthu aluso pamodzi ndi amene anadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babuloni kupita nawo ku ukapolo ku Babuloni. 16 Komabe Nebuzaradani mtsogoleri wa ankhondo anasiya anthu ena onse osaukitsitsa a mʼdzikomo kuti azigwira ntchito mʼminda ya mpesa ndi minda ina. 17 Ababuloni anaphwanya nsanamira za mkuwa, maphaka ndi chimbiya chamkuwa zimene zinali mʼNyumba ya Yehova. Anatenga mkuwa wonsewo nʼkupita nazo ku Babuloni. 18 Ankhondowo anatenganso mbiya, zochotsera phulusa, zozimitsira nyale, mbale zofukizira lubani, zikho pamodzi ndi ziwiya zina zonse za mkuwa zimene ankagwiritsira ntchito mʼNyumba ya Yehova. 19 Nebuzaradani uja anatenganso mabeseni, ziwiya zosonkhapo moto, mbale zowazira madzi, zoyikapo nyale, zipande zofukizira lubani ndi zikho ndi zina zonse zagolide ndi siliva. 20 Nsanamira ziwiri zija, chimbiya, maphaka ndi ngʼombe khumi ndi ziwiri za mkuwa zochirikizira chimbiyacho zimene mfumu Solomoni anapangira Nyumba ya Yehova kulemera kwake kunali kosawerengeka. 21 Nsanamira imodzi kutalika kwake kunali mamita asanu ndi atatu, akazunguliza chingwe inali mamita asanu ndi theka; mʼkati mwake munali bowo ndipo kuchindikala kwake kunali zala zinayi. 22 Pamwamba pa nsanamira iliyonse panali mutu wamkuwa umene kutalika kwake kunali mamita awiri. Pozungulira pake panali ukonde ndi makangadza, zonsezo za mkuwa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangadza ake ndipo inali yofanana ndi inzake ija. 23 Mʼmbali mwake munali makangadza 96; makangadza onse pamodzi analipo 100 kuzungulira ukonde onse. 24 Mtsogoleri wa ankhondo uja, anagwira Seraya mkulu wa ansembe ndi Zefaniya, wachiwiri wa mkulu wa ansembe ndi alonda atatu apachipata. 25 Mu mzindamo anagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndi alangizi amfumu asanu ndi awiri. Anagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu mʼdzikomo, pamodzi ndi anthu ena 60 amene anali mu mzindamo. 26 Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondoyo anawatenga onse napita nawo kwa mfumu ya ku Babuloni ku Ribula. 27 Ku Ribulako, mʼdziko la Hamati, mfumu ya ku Babuloniyo inalamula kuti anthuwo aphedwe.Motero anthu a ku Yuda anapita ku ukapolo, kutali ndi dziko lawo. 28 Chiwerengero cha anthu amene Nebukadinezara anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi ichi: Mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023; 29 mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,anatenga anthu 832 kuchokera mu Yerusalemu; 30 mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,Nebuzaradani, mtsogoleri wa ankhondo a mfumu anagwira Ayuda 745 kupita ku ukapolo.Onse pamodzi analipo anthu 4,600. 31 Mʼchaka chimene Evili-Merodaki analowa ufumu wa Babuloni, iye anakomera mtima Yehoyakini mfumu ya ku Yuda, namutulutsa mʼndende. Izi zinachitika pa tsiku la 25 la mwezi wa khumi ndi chiwiri zitatha zaka 37 chitengedwere Yehoyakimu ku ukapolo. 32 Evili-Merodaki anakomera mtima Yehoyakini, namupatsa malo aulemu kuposa mafumu ena amene anali naye ku Babuloni. 33 Choncho Yehoyakini analoledwa kuvula zovala zake za ku ndende ndipo tsiku ndi tsiku ankadya ndi mfumu pa moyo wake wonse. 34 Tsiku ndi tsiku mfumu ya ku Babuloni inkamupatsa Yehoyakini phoso lake nthawi yonse ya moyo wake, mpaka pa nthawi ya imfa yake.

In Other Versions

Jeremiah 52 in the ANGEFD

Jeremiah 52 in the ANTPNG2D

Jeremiah 52 in the AS21

Jeremiah 52 in the BAGH

Jeremiah 52 in the BBPNG

Jeremiah 52 in the BBT1E

Jeremiah 52 in the BDS

Jeremiah 52 in the BEV

Jeremiah 52 in the BHAD

Jeremiah 52 in the BIB

Jeremiah 52 in the BLPT

Jeremiah 52 in the BNT

Jeremiah 52 in the BNTABOOT

Jeremiah 52 in the BNTLV

Jeremiah 52 in the BOATCB

Jeremiah 52 in the BOATCB2

Jeremiah 52 in the BOBCV

Jeremiah 52 in the BOCNT

Jeremiah 52 in the BOECS

Jeremiah 52 in the BOHCB

Jeremiah 52 in the BOHCV

Jeremiah 52 in the BOHLNT

Jeremiah 52 in the BOHNTLTAL

Jeremiah 52 in the BOICB

Jeremiah 52 in the BOILNTAP

Jeremiah 52 in the BOITCV

Jeremiah 52 in the BOKCV

Jeremiah 52 in the BOKCV2

Jeremiah 52 in the BOKHWOG

Jeremiah 52 in the BOKSSV

Jeremiah 52 in the BOLCB

Jeremiah 52 in the BOLCB2

Jeremiah 52 in the BOMCV

Jeremiah 52 in the BONAV

Jeremiah 52 in the BONCB

Jeremiah 52 in the BONLT

Jeremiah 52 in the BONUT2

Jeremiah 52 in the BOPLNT

Jeremiah 52 in the BOSCB

Jeremiah 52 in the BOSNC

Jeremiah 52 in the BOTLNT

Jeremiah 52 in the BOVCB

Jeremiah 52 in the BOYCB

Jeremiah 52 in the BPBB

Jeremiah 52 in the BPH

Jeremiah 52 in the BSB

Jeremiah 52 in the CCB

Jeremiah 52 in the CUV

Jeremiah 52 in the CUVS

Jeremiah 52 in the DBT

Jeremiah 52 in the DGDNT

Jeremiah 52 in the DHNT

Jeremiah 52 in the DNT

Jeremiah 52 in the ELBE

Jeremiah 52 in the EMTV

Jeremiah 52 in the ESV

Jeremiah 52 in the FBV

Jeremiah 52 in the FEB

Jeremiah 52 in the GGMNT

Jeremiah 52 in the GNT

Jeremiah 52 in the HARY

Jeremiah 52 in the HNT

Jeremiah 52 in the IRVA

Jeremiah 52 in the IRVB

Jeremiah 52 in the IRVG

Jeremiah 52 in the IRVH

Jeremiah 52 in the IRVK

Jeremiah 52 in the IRVM

Jeremiah 52 in the IRVM2

Jeremiah 52 in the IRVO

Jeremiah 52 in the IRVP

Jeremiah 52 in the IRVT

Jeremiah 52 in the IRVT2

Jeremiah 52 in the IRVU

Jeremiah 52 in the ISVN

Jeremiah 52 in the JSNT

Jeremiah 52 in the KAPI

Jeremiah 52 in the KBT1ETNIK

Jeremiah 52 in the KBV

Jeremiah 52 in the KJV

Jeremiah 52 in the KNFD

Jeremiah 52 in the LBA

Jeremiah 52 in the LBLA

Jeremiah 52 in the LNT

Jeremiah 52 in the LSV

Jeremiah 52 in the MAAL

Jeremiah 52 in the MBV

Jeremiah 52 in the MBV2

Jeremiah 52 in the MHNT

Jeremiah 52 in the MKNFD

Jeremiah 52 in the MNG

Jeremiah 52 in the MNT

Jeremiah 52 in the MNT2

Jeremiah 52 in the MRS1T

Jeremiah 52 in the NAA

Jeremiah 52 in the NASB

Jeremiah 52 in the NBLA

Jeremiah 52 in the NBS

Jeremiah 52 in the NBVTP

Jeremiah 52 in the NET2

Jeremiah 52 in the NIV11

Jeremiah 52 in the NNT

Jeremiah 52 in the NNT2

Jeremiah 52 in the NNT3

Jeremiah 52 in the PDDPT

Jeremiah 52 in the PFNT

Jeremiah 52 in the RMNT

Jeremiah 52 in the SBIAS

Jeremiah 52 in the SBIBS

Jeremiah 52 in the SBIBS2

Jeremiah 52 in the SBICS

Jeremiah 52 in the SBIDS

Jeremiah 52 in the SBIGS

Jeremiah 52 in the SBIHS

Jeremiah 52 in the SBIIS

Jeremiah 52 in the SBIIS2

Jeremiah 52 in the SBIIS3

Jeremiah 52 in the SBIKS

Jeremiah 52 in the SBIKS2

Jeremiah 52 in the SBIMS

Jeremiah 52 in the SBIOS

Jeremiah 52 in the SBIPS

Jeremiah 52 in the SBISS

Jeremiah 52 in the SBITS

Jeremiah 52 in the SBITS2

Jeremiah 52 in the SBITS3

Jeremiah 52 in the SBITS4

Jeremiah 52 in the SBIUS

Jeremiah 52 in the SBIVS

Jeremiah 52 in the SBT

Jeremiah 52 in the SBT1E

Jeremiah 52 in the SCHL

Jeremiah 52 in the SNT

Jeremiah 52 in the SUSU

Jeremiah 52 in the SUSU2

Jeremiah 52 in the SYNO

Jeremiah 52 in the TBIAOTANT

Jeremiah 52 in the TBT1E

Jeremiah 52 in the TBT1E2

Jeremiah 52 in the TFTIP

Jeremiah 52 in the TFTU

Jeremiah 52 in the TGNTATF3T

Jeremiah 52 in the THAI

Jeremiah 52 in the TNFD

Jeremiah 52 in the TNT

Jeremiah 52 in the TNTIK

Jeremiah 52 in the TNTIL

Jeremiah 52 in the TNTIN

Jeremiah 52 in the TNTIP

Jeremiah 52 in the TNTIZ

Jeremiah 52 in the TOMA

Jeremiah 52 in the TTENT

Jeremiah 52 in the UBG

Jeremiah 52 in the UGV

Jeremiah 52 in the UGV2

Jeremiah 52 in the UGV3

Jeremiah 52 in the VBL

Jeremiah 52 in the VDCC

Jeremiah 52 in the YALU

Jeremiah 52 in the YAPE

Jeremiah 52 in the YBVTP

Jeremiah 52 in the ZBP