Joshua 15 (BOGWICC)

1 Chigawo cha dzikolo chimene mabanja a fuko la Yuda analandira chinafika ku malire ndi Edomu mpaka ku chipululu cha Zini kummwera kwenikweni. 2 Malire awo a kummwera anayambira kummwera kwenikweni kwa Nyanja ya Mchere, 3 kudutsa cha kummwera ku Akirabimu, nʼkupitirira mpaka ku Zini. Kuchokera pamenepo nʼkumapita cha kummwera kwa Kadesi Barinea, kudutsa Hezironi mpaka ku Adari ndi kutembenuka mpaka ku Karika. 4 Anapitirira mpaka ku Azimoni motsata mtsinje umene uli malire a Igupto mpaka ku nyanja. Awa ndiwo malire awo a kummwera. 5 Malire a kummawa anali Nyanja Yakufa mpaka kumene Yorodani amathira mu Nyanja ya Mchere.Malire a kumpoto anayambira kumene Yorodani amathirira nyanjayo, 6 napitirira mpaka ku Beti-Hogila ndi kupitirira kumpoto mpaka ku Beti-Araba. Anapitirira mpaka anakafika ku Mwala wa Bohani. 7 Ndipo malirewo anachokeranso ku chigwa cha Akori mpaka ku Debri, kuchokera ku chigwa cha Akori ndi kutembenukira kumpoto ku Giligala, dera limene linayangʼanana ndi msewu wa Adumimu kummwera kwa chigwa. Anapitirira mpaka ku madzi a ku Eni Semesi ndi kutulukira ku Eni Rogeli. 8 Ndipo anapitirira mpaka ku chigwa cha Hinomu mbali ya kummwera kwa mzinda wa Ayebusi (mzinda wa Yerusalemu). Kuchokera kumeneko anakwera mpaka pamwamba pa phiri kumadzulo kwa chigwa cha Hinomu cha kumpoto kwenikweni kwa chigwa cha Refaimu. 9 Ndipo anachokeranso pamwamba pa phiri, kukafika mpaka ku akasupe a ku Nepitowa, nadzatulukira ku mizinda ya phiri la Efroni, ndi kutsikira ku Baalahi (ndiye Kiriati Yearimu). 10 Kuchokera kumeneko anazungulira cha kumadzulo ku Baalahi mpaka ku phiri la Seiri. Anapitirira cha kumpoto kutsata phiri la Yearimu (lomwe ndi Kesaloni). Anapitirirabe kutsika ku Beti Semesi ndi kuwolokera ku Timna. 11 Malirewo anapitirira kumatsitso a mapiri chakumpoto kwa Ekroni, ndi kukhotera ku Sikeroni. Malirewo anadutsa phiri la Baalahi ndi kufika ku Yabineeli. Malirewo anathera ku nyanja. 12 Malire a mbali ya kumadzulo anali Nyanja Yayikulu. Awa ndi malire ozungulira malo amene anapatsidwa kwa mabanja a fuko la Yuda. 13 Potsata lamulo la Yehova, Yoswa anapereka kwa Kalebe mwana wa Yefune gawo lina la dziko la Yuda dera la Kiriati Ariba, limene ndi Hebroni. (Ariba anali gogo wa Aanaki). 14 Kuchokera ku Hebroni, Kalebe anathamangitsamo mafuko a Aanaki awa: Sesai, Ahimani ndi Talimai, zidzukulu za Aanaki. 15 Kuchokera kumeneko, Kalebe anakathira nkhondo anthu amene ankakhala ku Debri (mzindawu poyamba unkatchedwa Kiriati Seferi). 16 Tsono Kalebe anati, “Munthu amene angathire nkhondo mzinda wa Kiriati Seferi ndi kuwulanda, ndidzamupatsa mwana wanga Akisa kuti akhale mkazi wake.” 17 Otanieli, mwana wa mʼbale wa Kalebe, Kenazi, ndiye anawulanda. Choncho Kalebe anamupatsa mwana wake Akisa kuti akhale mkazi wake. 18 Tsiku lina atafika Akisayo, Otanieli anamuwumiriza mkazi wakeyo kuti apemphe munda kwa Kalebe abambo ake. Pamene Akisa anatsika pa bulu wake, Kalebe anamufunsa kuti, “Kodi ukufuna ndikuchitire chiyani.” 19 Iye anayankha kuti “Mundikomere mtima. Popeza mwandipatsa ku Negevi, kumalo kumene kulibe madzi, mundipatsenso akasupe amadzi.” Choncho Kalebe anamupatsa akasupe a kumtunda ndi a kumunsi. 20 Dziko limene mabanja a fuko la Yuda analandira ngati cholowa chawo ndi ili: 21 Mizinda yakummwera kwenikweni kwa fuko la Yuda yoyandikana ndi malire a Edomu anali:Kabizeeli, Ederi, Yaguri 22 Kina, Dimona, Adada 23 Kedesi, Hazori, Itinani 24 Zifi, Telemu, Bealoti, 25 Hazori-Hadata, Keriyoti Hezironi (ndiye kuti Hazori) 26 Amamu, Sema, Molada 27 Hazari-Gada, Hesimoni, Beti-Peleti 28 Hazari-Suwali, Beeriseba, Biziotiya, 29 Baalahi, Iyimu, Ezemu 30 Elitoladi, Kesili, Horima 31 Zikilagi, Madimena, Sanisana, 32 Lebaoti, Silihimu, Aini ndi Rimoni. Mizinda yonse inalipo 29 pamodzi ndi midzi yake yozungulira. 33 Mizinda ya ku chigwa cha kumadzulo ndi iyi:Esitaoli, Zora, Asina 34 Zanowa, Eni-Ganimu, Tapuwa, Enamu, 35 Yarimuti, Adulamu, Soko, Azeka, 36 Saaraimu, Aditaimu, ndi Gederi (kapena Gederotaimu). Mizinda yonse inalipo 14 pamodzi ndi midzi yake yozungulira. 37 Mizinda ina inali iyi: Zenani, Hadasa, Migidali-Gadi, 38 Dileani, Mizipa, Yokiteeli, 39 Lakisi, Bozikati, Egiloni, 40 Kaboni, Lahimasi, Kitilisi, 41 Gederoti, Beti-Dagoni, Naama ndi Makeda. Mizinda yonse pamodzi inalipo 16 pamodzi ndi midzi yake yozungulira. 42 Mizinda ina inali iyi: Libina, Eteri, Asani, 43 Ifita, Asina, Nezibu, 44 Keila, Akizibu ndi Maresa, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake. 45 Panalinso Ekroni pamodzi ndi midzi yake; 46 komanso yonse imene inali mʼmbali mwa Asidodi ndi midzi yake kuyambira ku Ekroni mpaka ku Nyanja Yayikulu. 47 Panalinso mizinda ya Asidodi ndi Gaza pamodzi ndi midzi yawo. Malire ake anafika ku mtsinje wa Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. 48 Mizinda ya kumapiri inali:Samiri, Yatiri, Soko, 49 Dana, Kiriati-Sana, (ndiye kuti Debri) 50 Anabu, Esitemo, Animu, 51 Goseni, Holoni ndi Gilo. Mizinda yonse pamodzi inali khumi ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake. 52 Analandiranso mizinda iyi: Arabu, Duma, Esani, 53 Yanumu, Beti-Tapuwa, Afeki 54 Humita, Kiriati-Ariba (ndiye kuti Hebroni) ndi Ziori, mizinda isanu ndi inayi pamodzi ndi midzi yake. 55 Panalinso Maoni, Karimeli, Zifi, Yuta 56 Yezireeli, Yokideamu, Zanowa, 57 Kaini, Gibeya ndi Timna, mizinda khumi ndi midzi yake. 58 Mizinda ina inali: Halihuli, Beti Zuri, Gedori, 59 Maarati, Beti-Anoti ndi Elitekoni, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake 60 Panalinso Kiriati Baala (ndiye kuti Kiriati Yearimu) ndi Raba; mizinda iwiri pamodzi ndi midzi yake. 61 Mizinda ya ku chipululu inali iyi:Beti-Araba, Midini, Sekaka, 62 Nibisani, Mzinda wa Mchere ndi Eni Gedi, mizinda isanu ndi umodzi pamodzi ndi midzi yake. 63 Koma Yuda sanathe kuthamangitsa Ayebusi amene amakhala ku Yerusalemu, ndipo mpaka lero Ayebusi akukhala komweko pamodzi ndi Ayudawo.

In Other Versions

Joshua 15 in the ANGEFD

Joshua 15 in the ANTPNG2D

Joshua 15 in the AS21

Joshua 15 in the BAGH

Joshua 15 in the BBPNG

Joshua 15 in the BBT1E

Joshua 15 in the BDS

Joshua 15 in the BEV

Joshua 15 in the BHAD

Joshua 15 in the BIB

Joshua 15 in the BLPT

Joshua 15 in the BNT

Joshua 15 in the BNTABOOT

Joshua 15 in the BNTLV

Joshua 15 in the BOATCB

Joshua 15 in the BOATCB2

Joshua 15 in the BOBCV

Joshua 15 in the BOCNT

Joshua 15 in the BOECS

Joshua 15 in the BOHCB

Joshua 15 in the BOHCV

Joshua 15 in the BOHLNT

Joshua 15 in the BOHNTLTAL

Joshua 15 in the BOICB

Joshua 15 in the BOILNTAP

Joshua 15 in the BOITCV

Joshua 15 in the BOKCV

Joshua 15 in the BOKCV2

Joshua 15 in the BOKHWOG

Joshua 15 in the BOKSSV

Joshua 15 in the BOLCB

Joshua 15 in the BOLCB2

Joshua 15 in the BOMCV

Joshua 15 in the BONAV

Joshua 15 in the BONCB

Joshua 15 in the BONLT

Joshua 15 in the BONUT2

Joshua 15 in the BOPLNT

Joshua 15 in the BOSCB

Joshua 15 in the BOSNC

Joshua 15 in the BOTLNT

Joshua 15 in the BOVCB

Joshua 15 in the BOYCB

Joshua 15 in the BPBB

Joshua 15 in the BPH

Joshua 15 in the BSB

Joshua 15 in the CCB

Joshua 15 in the CUV

Joshua 15 in the CUVS

Joshua 15 in the DBT

Joshua 15 in the DGDNT

Joshua 15 in the DHNT

Joshua 15 in the DNT

Joshua 15 in the ELBE

Joshua 15 in the EMTV

Joshua 15 in the ESV

Joshua 15 in the FBV

Joshua 15 in the FEB

Joshua 15 in the GGMNT

Joshua 15 in the GNT

Joshua 15 in the HARY

Joshua 15 in the HNT

Joshua 15 in the IRVA

Joshua 15 in the IRVB

Joshua 15 in the IRVG

Joshua 15 in the IRVH

Joshua 15 in the IRVK

Joshua 15 in the IRVM

Joshua 15 in the IRVM2

Joshua 15 in the IRVO

Joshua 15 in the IRVP

Joshua 15 in the IRVT

Joshua 15 in the IRVT2

Joshua 15 in the IRVU

Joshua 15 in the ISVN

Joshua 15 in the JSNT

Joshua 15 in the KAPI

Joshua 15 in the KBT1ETNIK

Joshua 15 in the KBV

Joshua 15 in the KJV

Joshua 15 in the KNFD

Joshua 15 in the LBA

Joshua 15 in the LBLA

Joshua 15 in the LNT

Joshua 15 in the LSV

Joshua 15 in the MAAL

Joshua 15 in the MBV

Joshua 15 in the MBV2

Joshua 15 in the MHNT

Joshua 15 in the MKNFD

Joshua 15 in the MNG

Joshua 15 in the MNT

Joshua 15 in the MNT2

Joshua 15 in the MRS1T

Joshua 15 in the NAA

Joshua 15 in the NASB

Joshua 15 in the NBLA

Joshua 15 in the NBS

Joshua 15 in the NBVTP

Joshua 15 in the NET2

Joshua 15 in the NIV11

Joshua 15 in the NNT

Joshua 15 in the NNT2

Joshua 15 in the NNT3

Joshua 15 in the PDDPT

Joshua 15 in the PFNT

Joshua 15 in the RMNT

Joshua 15 in the SBIAS

Joshua 15 in the SBIBS

Joshua 15 in the SBIBS2

Joshua 15 in the SBICS

Joshua 15 in the SBIDS

Joshua 15 in the SBIGS

Joshua 15 in the SBIHS

Joshua 15 in the SBIIS

Joshua 15 in the SBIIS2

Joshua 15 in the SBIIS3

Joshua 15 in the SBIKS

Joshua 15 in the SBIKS2

Joshua 15 in the SBIMS

Joshua 15 in the SBIOS

Joshua 15 in the SBIPS

Joshua 15 in the SBISS

Joshua 15 in the SBITS

Joshua 15 in the SBITS2

Joshua 15 in the SBITS3

Joshua 15 in the SBITS4

Joshua 15 in the SBIUS

Joshua 15 in the SBIVS

Joshua 15 in the SBT

Joshua 15 in the SBT1E

Joshua 15 in the SCHL

Joshua 15 in the SNT

Joshua 15 in the SUSU

Joshua 15 in the SUSU2

Joshua 15 in the SYNO

Joshua 15 in the TBIAOTANT

Joshua 15 in the TBT1E

Joshua 15 in the TBT1E2

Joshua 15 in the TFTIP

Joshua 15 in the TFTU

Joshua 15 in the TGNTATF3T

Joshua 15 in the THAI

Joshua 15 in the TNFD

Joshua 15 in the TNT

Joshua 15 in the TNTIK

Joshua 15 in the TNTIL

Joshua 15 in the TNTIN

Joshua 15 in the TNTIP

Joshua 15 in the TNTIZ

Joshua 15 in the TOMA

Joshua 15 in the TTENT

Joshua 15 in the UBG

Joshua 15 in the UGV

Joshua 15 in the UGV2

Joshua 15 in the UGV3

Joshua 15 in the VBL

Joshua 15 in the VDCC

Joshua 15 in the YALU

Joshua 15 in the YAPE

Joshua 15 in the YBVTP

Joshua 15 in the ZBP