Joshua 4 (BOGWICC)
1 Anthu onse atatha kuwoloka Yorodani, Yehova anati kwa Yoswa, 2 “Sankha amuna khumi ndi awiri, mmodzi pa fuko lililonse. 3 Tsono uwalamule kuti, ‘Tengani miyala khumi ndi iwiri pakati penipeni pa mtsinje wa Yorodani, pamalo pamene ansembe anayimirirapo. Miyalayo muwoloke nayo ndi kudzayitula pamalo pamene mukagone usiku uno.’ ” 4 Choncho Yoswa anayitana amuna khumi ndi awiri amene anawasankha aja kuchokera pakati pa Aisraeli, mmodzi pa fuko lililonse, 5 ndipo anawawuza kuti, “Lowani pakati pa mtsinje wa Yorodani, patsogolo pa Bokosi la Yehova Mulungu wanu. Ndipo aliyense wa inu atenge mwala pa phewa lake, monga mwa chiwerengero cha mafuko a Aisraeli, 6 kuti ikhale chizindikiro kwa inu. Mʼtsogolo muno ana anu akamadzakufunsani kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’ 7 Muzidzawawuza kuti, ‘Madzi a Yorodani analeka kuyenda pamene Bokosi la Chipangano la Yehova linkawoloka mtsinjewo. Miyala iyi idzakhala chikumbutso kwa anthu a Israeli kwa muyaya.’ ” 8 Aisraeli anachitadi monga Yoswa anawalamulira. Iwo ananyamula miyala khumi ndi iwiri kuchokera pakati pa Yorodani, fuko lililonse la Israeli mwala wake, monga Yehova analamulira Yoswa. Miyalayo anapita nayo ku misasa yawo nakayikhazika kumeneko. 9 Yoswa anayimika miyala khumi ndi iwiri imene inali pakati pa Yorodani pamalo pamene ansembe onyamula Bokosi la Chipangano anayimapo. Ndipo miyalayo ili pamalo pomwepo mpaka lero lino. 10 Ansembe onyamula Bokosi lija anayimirirabe pakati pa Yorodani mpaka zonse zimene Yehova analamulira Yoswa kuti awuze anthu zinatha. Zimenezi zinali monga momwe Mose anamufotokozera Yoswa. Tsono anthu anawoloka mtsinjewo mofulumira. 11 Anthu atatha kuwoloka, ansembe anatsogolera anthuwo atanyamula Bokosi la Yehova. 12 Anthu a fuko la Rubeni, Gadi ndi theka la fuko la Manase anawoloka patsogolo pa Aisraeli ali ndi zida, monga momwe Mose anawalamulira. 13 Asilikali pafupifupi 40,000 anawoloka napita kukayima mʼchigwa cha Yeriko kukonzekera nkhondo. 14 Zimene Yehova anachita tsiku limeneli zinapatsa anthu mtima wolemekeza Yoswa. Ndipo anamulemekeza masiku onse a moyo wake, monga momwe analemekezera Mose. 15 Kenaka Yehova anati kwa Yoswa, 16 “Lamula ansembe onyamula Bokosi la Chipanganowo kuti atuluke mu Yorodani.” 17 Choncho Yoswa anawalamuladi ansembe aja kuti atuluke mu Yorodani muja. 18 Ansembe onyamula Bokosi la Chipangano la Yehova aja atangotuluka mu mtsinje muja nʼkuponda powuma, madzi a mu Yorodani anayambanso kuyenda ngati poyamba mpaka kumasefukira. 19 Aisraeli anawoloka Yorodani tsiku lakhumi la mwezi woyamba ndipo anakamanga misasa yawo ku Giligala mbali ya kummawa kwa Yeriko. 20 Ku Giligala, Yoswa anayimikako miyala khumi ndi iwiri imene anayitenga mu Yorodani ija. 21 Ndipo iye anati kwa Aisraeli, “Mʼtsogolo muno pamene adzukulu anu adzafunsa makolo awo kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’ 22 Muzidzawawuza kuti, ‘Aisraeli anawoloka Yorodani pansi pali powuma.’ 23 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndiye anawumitsa Yorodani pamaso panu mpaka inu mutawoloka. Yehova Mulungu wanu anaphwetsa madzi a Yorodani monga mmene anachitira ndi Nyanja Yofiira mpaka ife tinawoloka powuma. 24 Iye anachita zimenezi kuti anthu onse pa dziko lapansi adziwe kuti dzanja la Yehova ndi lamphamvu, ndi kuti inu muziopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.”
In Other Versions
Joshua 4 in the ANGEFD
Joshua 4 in the ANTPNG2D
Joshua 4 in the AS21
Joshua 4 in the BAGH
Joshua 4 in the BBPNG
Joshua 4 in the BBT1E
Joshua 4 in the BDS
Joshua 4 in the BEV
Joshua 4 in the BHAD
Joshua 4 in the BIB
Joshua 4 in the BLPT
Joshua 4 in the BNT
Joshua 4 in the BNTABOOT
Joshua 4 in the BNTLV
Joshua 4 in the BOATCB
Joshua 4 in the BOATCB2
Joshua 4 in the BOBCV
Joshua 4 in the BOCNT
Joshua 4 in the BOECS
Joshua 4 in the BOHCB
Joshua 4 in the BOHCV
Joshua 4 in the BOHLNT
Joshua 4 in the BOHNTLTAL
Joshua 4 in the BOICB
Joshua 4 in the BOILNTAP
Joshua 4 in the BOITCV
Joshua 4 in the BOKCV
Joshua 4 in the BOKCV2
Joshua 4 in the BOKHWOG
Joshua 4 in the BOKSSV
Joshua 4 in the BOLCB
Joshua 4 in the BOLCB2
Joshua 4 in the BOMCV
Joshua 4 in the BONAV
Joshua 4 in the BONCB
Joshua 4 in the BONLT
Joshua 4 in the BONUT2
Joshua 4 in the BOPLNT
Joshua 4 in the BOSCB
Joshua 4 in the BOSNC
Joshua 4 in the BOTLNT
Joshua 4 in the BOVCB
Joshua 4 in the BOYCB
Joshua 4 in the BPBB
Joshua 4 in the BPH
Joshua 4 in the BSB
Joshua 4 in the CCB
Joshua 4 in the CUV
Joshua 4 in the CUVS
Joshua 4 in the DBT
Joshua 4 in the DGDNT
Joshua 4 in the DHNT
Joshua 4 in the DNT
Joshua 4 in the ELBE
Joshua 4 in the EMTV
Joshua 4 in the ESV
Joshua 4 in the FBV
Joshua 4 in the FEB
Joshua 4 in the GGMNT
Joshua 4 in the GNT
Joshua 4 in the HARY
Joshua 4 in the HNT
Joshua 4 in the IRVA
Joshua 4 in the IRVB
Joshua 4 in the IRVG
Joshua 4 in the IRVH
Joshua 4 in the IRVK
Joshua 4 in the IRVM
Joshua 4 in the IRVM2
Joshua 4 in the IRVO
Joshua 4 in the IRVP
Joshua 4 in the IRVT
Joshua 4 in the IRVT2
Joshua 4 in the IRVU
Joshua 4 in the ISVN
Joshua 4 in the JSNT
Joshua 4 in the KAPI
Joshua 4 in the KBT1ETNIK
Joshua 4 in the KBV
Joshua 4 in the KJV
Joshua 4 in the KNFD
Joshua 4 in the LBA
Joshua 4 in the LBLA
Joshua 4 in the LNT
Joshua 4 in the LSV
Joshua 4 in the MAAL
Joshua 4 in the MBV
Joshua 4 in the MBV2
Joshua 4 in the MHNT
Joshua 4 in the MKNFD
Joshua 4 in the MNG
Joshua 4 in the MNT
Joshua 4 in the MNT2
Joshua 4 in the MRS1T
Joshua 4 in the NAA
Joshua 4 in the NASB
Joshua 4 in the NBLA
Joshua 4 in the NBS
Joshua 4 in the NBVTP
Joshua 4 in the NET2
Joshua 4 in the NIV11
Joshua 4 in the NNT
Joshua 4 in the NNT2
Joshua 4 in the NNT3
Joshua 4 in the PDDPT
Joshua 4 in the PFNT
Joshua 4 in the RMNT
Joshua 4 in the SBIAS
Joshua 4 in the SBIBS
Joshua 4 in the SBIBS2
Joshua 4 in the SBICS
Joshua 4 in the SBIDS
Joshua 4 in the SBIGS
Joshua 4 in the SBIHS
Joshua 4 in the SBIIS
Joshua 4 in the SBIIS2
Joshua 4 in the SBIIS3
Joshua 4 in the SBIKS
Joshua 4 in the SBIKS2
Joshua 4 in the SBIMS
Joshua 4 in the SBIOS
Joshua 4 in the SBIPS
Joshua 4 in the SBISS
Joshua 4 in the SBITS
Joshua 4 in the SBITS2
Joshua 4 in the SBITS3
Joshua 4 in the SBITS4
Joshua 4 in the SBIUS
Joshua 4 in the SBIVS
Joshua 4 in the SBT
Joshua 4 in the SBT1E
Joshua 4 in the SCHL
Joshua 4 in the SNT
Joshua 4 in the SUSU
Joshua 4 in the SUSU2
Joshua 4 in the SYNO
Joshua 4 in the TBIAOTANT
Joshua 4 in the TBT1E
Joshua 4 in the TBT1E2
Joshua 4 in the TFTIP
Joshua 4 in the TFTU
Joshua 4 in the TGNTATF3T
Joshua 4 in the THAI
Joshua 4 in the TNFD
Joshua 4 in the TNT
Joshua 4 in the TNTIK
Joshua 4 in the TNTIL
Joshua 4 in the TNTIN
Joshua 4 in the TNTIP
Joshua 4 in the TNTIZ
Joshua 4 in the TOMA
Joshua 4 in the TTENT
Joshua 4 in the UBG
Joshua 4 in the UGV
Joshua 4 in the UGV2
Joshua 4 in the UGV3
Joshua 4 in the VBL
Joshua 4 in the VDCC
Joshua 4 in the YALU
Joshua 4 in the YAPE
Joshua 4 in the YBVTP
Joshua 4 in the ZBP