Leviticus 22 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Uza Aaroni ndi ana ake kuti azilemekeza zinthu zopatulika zimene Aisraeli azipereka kwa Ine, kuti asayipitse dzina langa loyera. Ine ndine Yehova. 3 “Uwawuze kuti ngati wina aliyense mwa zidzukulu zawo mʼmibado yonse imene ikubwera adzayandikira zinthu zopatulika zimene ana a Israeli apereka kwa Yehova, ali wodetsedwa, ameneyo achotsedwe pamaso pa Yehova. Ine ndine Yehova. 4 “Munthu aliyense mwa zidzukulu za Aaroni amene ali ndi khate kapena amatulutsa zoyipa mʼthupi mwake, asadye zinthu zopatulika mpaka atayeretsedwa. Wansembe angakhale wodetsedwa atakhudzana ndi chinthu chimene chadetsedwa ndi chinthu chakufa kapena kukhudza munthu amene wataya umuna, 5 kapena kukhudza chilichonse chokwawa chomwe chimadetsa munthu, kapena kukhudza munthu amene angamudetse, kapenanso kukhudza kanthu kena kalikonse kodetsedwa. 6 Tsono ngati wansembe angakhudze chilichonse mwa zimenezi ndiye kuti adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. Asadye chopereka chilichonse chopatulika mpaka atasamba thupi lake lonse. 7 Munthuyo adzakhala woyeretsedwa pamene dzuwa lalowa, ndipo angathe kudya chopereka chopatulikacho popeza ndi chakudya chake. 8 Wansembe sayenera kudya chinthu chofa chokha kapena chojiwa ndi chirombo kuopa kuti angadzidetse ndi chakudyacho. Ine ndine Yehova. 9 “ ‘Choncho ansembe azisunga malamulo angawa kuti asapezeke wolakwa ndi kufa chifukwa chopeputsa malamulowa. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa. 10 “ ‘Aliyense amene si wabanja la wansembe, kaya ndi mlendo wa wansembe, kapena wantchito wake, asadye chopereka chopatulika. 11 Koma kapolo amene wagulidwa ndi ndalama kapena kubadwira mʼbanja la wansembe angathe kudya chakudya cha wansembeyo. 12 Mwana wamkazi wa wansembe amene wakwatiwa ndi munthu amene si wansembe, asadyeko nsembe zopatulikazo. 13 Koma mwana wamkazi wa wansembe amene ali wamasiye kapena wosudzulidwa, ndipo alibe mwana, komanso anabwerera ku nyumba ya abambo ake monga pa nthawi ya utsikana wake, angathe kudya chakudya cha abambo ake. Mlendo asadye chakudya chopatulika. 14 “ ‘Ngati munthu wina aliyense adya chopereka chopatulika mosadziwa, munthuyo amubwezere wansembe chinthu chopatulikacho ndipo awonjezerepo limodzi la magawo asanu a chinthucho. 15 Choncho ansembe asayipitse zopereka zopatulika za Aisraeli zimene apereka kwa Yehova 16 ndipo asachimwitse ndi kupalamulitsa Aisraeli powalola kudya zakudya zawo zopatulika. Ine ndine Yehova amene ndimawayeretsa.’ ” 17 Yehova anawuza Mose kuti, 18 “Yankhula ndi Aaroni, ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse, ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati wina aliyense wa inu, Mwisraeli kapena mlendo amene akukhala mu Israeli abwera ndi mphatso ya nsembe yopsereza kwa Yehova, kupereka chimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, 19 ndiye kuti abwere ndi ngʼombe yayimuna, nkhosa yayimuna kapena mbuzi yayimuna. Izi zikhale zopanda chilema kuti zilandiridwe. 20 Musapereke nyama iliyonse yokhala ndi chilema chifukwa sidzalandiridwa mʼmalo mwanu. 21 Pamene wina aliyense abweretsa ngʼombe kapena nkhosa kuti ikhale nsembe yachiyanjano kwa Yehova, kukwaniritsa zimene analumbira kapena kuti ikhale nsembe yaufulu, nyamayo iyenera kukhala yangwiro ndi yopanda chilema kuti ilandiridwe. 22 Musapereke kwa Yehova nyama zakhungu, zovulala kapena zolumala, kapena nyama zimene zikutulutsa mafinya mʼthupi mwake, kapena zimene zili ndi nthenda yonyerenyetsa, kapena zimene zili ndi mphere. Nyama zotere musaziyike pa guwa kuti zikhale nsembe yopsereza kwa Yehova. 23 Koma mungathe kupereka ngʼombe yayimuna kapena nkhosa imene ili ndi chiwalo chachitali kapena chachifupi kukhala nsembe yaufulu. Koma simungayipereke ngati nsembe yoperekera zimene munalumbirira chifukwa sidzalandiridwa. 24 Nyama iliyonse imene mavalo ake ndi onyuka kapena ophwanyika, ongʼambika kapena oduka, musamayipereke kwa Yehova mʼdziko lanu. 25 Ndipo musalandire nyama zotere kuchokera kwa mlendo ndi kuzipereka kukhala zakudya za Mulungu wanu. Zimenezi sizidzalandiridwa mʼmalo mwanu chifukwa zili ndi chilema ndipo ndi zolumala.’ ” 26 Yehova anawuza Mose kuti, 27 “Pamene mwana wangʼombe, mwana wankhosa kapena mwana wambuzi wabadwa, akhale ndi make kwa masiku asanu ndi awiri. Kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu mpaka mʼtsogolo mwake, angathe kulandiridwa kuti akhale nsembe yopsereza ya kwa Yehova. 28 Musaphe ngʼombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzi. Muyidye pa tsiku lomwelo; musasiyeko ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova. 29 “Pamene mupereka nsembe yoyamika kwa Yehova, muyipereke mwakufuna kwanu mu njira yoti ilandiridwe mʼmalo mwanu. 30 Muyidye pa tsiku lomwelo, wosasiyako ina mpaka mmawa. Ine ndine Yehova. 31 “Choncho sungani malamulo anga ndi kuwatsatira. Ine ndine Yehova. 32 Musanyoze dzina langa loyera. Koma lilemekezedwe pakati pa Aisraeli. Ine ndine Yehova amene ndimakuyeretsani 33 ndipo ndine amene ndinakutulutsani mu Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova.”

In Other Versions

Leviticus 22 in the ANGEFD

Leviticus 22 in the ANTPNG2D

Leviticus 22 in the AS21

Leviticus 22 in the BAGH

Leviticus 22 in the BBPNG

Leviticus 22 in the BBT1E

Leviticus 22 in the BDS

Leviticus 22 in the BEV

Leviticus 22 in the BHAD

Leviticus 22 in the BIB

Leviticus 22 in the BLPT

Leviticus 22 in the BNT

Leviticus 22 in the BNTABOOT

Leviticus 22 in the BNTLV

Leviticus 22 in the BOATCB

Leviticus 22 in the BOATCB2

Leviticus 22 in the BOBCV

Leviticus 22 in the BOCNT

Leviticus 22 in the BOECS

Leviticus 22 in the BOHCB

Leviticus 22 in the BOHCV

Leviticus 22 in the BOHLNT

Leviticus 22 in the BOHNTLTAL

Leviticus 22 in the BOICB

Leviticus 22 in the BOILNTAP

Leviticus 22 in the BOITCV

Leviticus 22 in the BOKCV

Leviticus 22 in the BOKCV2

Leviticus 22 in the BOKHWOG

Leviticus 22 in the BOKSSV

Leviticus 22 in the BOLCB

Leviticus 22 in the BOLCB2

Leviticus 22 in the BOMCV

Leviticus 22 in the BONAV

Leviticus 22 in the BONCB

Leviticus 22 in the BONLT

Leviticus 22 in the BONUT2

Leviticus 22 in the BOPLNT

Leviticus 22 in the BOSCB

Leviticus 22 in the BOSNC

Leviticus 22 in the BOTLNT

Leviticus 22 in the BOVCB

Leviticus 22 in the BOYCB

Leviticus 22 in the BPBB

Leviticus 22 in the BPH

Leviticus 22 in the BSB

Leviticus 22 in the CCB

Leviticus 22 in the CUV

Leviticus 22 in the CUVS

Leviticus 22 in the DBT

Leviticus 22 in the DGDNT

Leviticus 22 in the DHNT

Leviticus 22 in the DNT

Leviticus 22 in the ELBE

Leviticus 22 in the EMTV

Leviticus 22 in the ESV

Leviticus 22 in the FBV

Leviticus 22 in the FEB

Leviticus 22 in the GGMNT

Leviticus 22 in the GNT

Leviticus 22 in the HARY

Leviticus 22 in the HNT

Leviticus 22 in the IRVA

Leviticus 22 in the IRVB

Leviticus 22 in the IRVG

Leviticus 22 in the IRVH

Leviticus 22 in the IRVK

Leviticus 22 in the IRVM

Leviticus 22 in the IRVM2

Leviticus 22 in the IRVO

Leviticus 22 in the IRVP

Leviticus 22 in the IRVT

Leviticus 22 in the IRVT2

Leviticus 22 in the IRVU

Leviticus 22 in the ISVN

Leviticus 22 in the JSNT

Leviticus 22 in the KAPI

Leviticus 22 in the KBT1ETNIK

Leviticus 22 in the KBV

Leviticus 22 in the KJV

Leviticus 22 in the KNFD

Leviticus 22 in the LBA

Leviticus 22 in the LBLA

Leviticus 22 in the LNT

Leviticus 22 in the LSV

Leviticus 22 in the MAAL

Leviticus 22 in the MBV

Leviticus 22 in the MBV2

Leviticus 22 in the MHNT

Leviticus 22 in the MKNFD

Leviticus 22 in the MNG

Leviticus 22 in the MNT

Leviticus 22 in the MNT2

Leviticus 22 in the MRS1T

Leviticus 22 in the NAA

Leviticus 22 in the NASB

Leviticus 22 in the NBLA

Leviticus 22 in the NBS

Leviticus 22 in the NBVTP

Leviticus 22 in the NET2

Leviticus 22 in the NIV11

Leviticus 22 in the NNT

Leviticus 22 in the NNT2

Leviticus 22 in the NNT3

Leviticus 22 in the PDDPT

Leviticus 22 in the PFNT

Leviticus 22 in the RMNT

Leviticus 22 in the SBIAS

Leviticus 22 in the SBIBS

Leviticus 22 in the SBIBS2

Leviticus 22 in the SBICS

Leviticus 22 in the SBIDS

Leviticus 22 in the SBIGS

Leviticus 22 in the SBIHS

Leviticus 22 in the SBIIS

Leviticus 22 in the SBIIS2

Leviticus 22 in the SBIIS3

Leviticus 22 in the SBIKS

Leviticus 22 in the SBIKS2

Leviticus 22 in the SBIMS

Leviticus 22 in the SBIOS

Leviticus 22 in the SBIPS

Leviticus 22 in the SBISS

Leviticus 22 in the SBITS

Leviticus 22 in the SBITS2

Leviticus 22 in the SBITS3

Leviticus 22 in the SBITS4

Leviticus 22 in the SBIUS

Leviticus 22 in the SBIVS

Leviticus 22 in the SBT

Leviticus 22 in the SBT1E

Leviticus 22 in the SCHL

Leviticus 22 in the SNT

Leviticus 22 in the SUSU

Leviticus 22 in the SUSU2

Leviticus 22 in the SYNO

Leviticus 22 in the TBIAOTANT

Leviticus 22 in the TBT1E

Leviticus 22 in the TBT1E2

Leviticus 22 in the TFTIP

Leviticus 22 in the TFTU

Leviticus 22 in the TGNTATF3T

Leviticus 22 in the THAI

Leviticus 22 in the TNFD

Leviticus 22 in the TNT

Leviticus 22 in the TNTIK

Leviticus 22 in the TNTIL

Leviticus 22 in the TNTIN

Leviticus 22 in the TNTIP

Leviticus 22 in the TNTIZ

Leviticus 22 in the TOMA

Leviticus 22 in the TTENT

Leviticus 22 in the UBG

Leviticus 22 in the UGV

Leviticus 22 in the UGV2

Leviticus 22 in the UGV3

Leviticus 22 in the VBL

Leviticus 22 in the VDCC

Leviticus 22 in the YALU

Leviticus 22 in the YAPE

Leviticus 22 in the YBVTP

Leviticus 22 in the ZBP