Leviticus 27 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Ngati munthu anachita lumbiro lapadera loti adzapereka munthu mnzake kwa Yehova ndipo akufuna kuti amuwombole, 3 mtengo wake ukhale masekeli a siliva makumi asanu, molingana ndi kawerengedwe ka ku Nyumba ya Mulungu, ngati munthuyo ndi wamwamuna wa zaka zapakati pa 20 ndi 60. 4 Ndipo ngati ndi wamkazi, mtengo wake ukhale masekeli makumi atatu. 5 Mtengo wa munthu wamwamuna wa zaka zapakati pa zisanu ndi makumi awiri ukhale masekeli makumi awiri ndipo munthu wamkazi ukhale masekeli khumi. 6 Ngati ndi munthu wamwamuna wa pakati pa mwezi umodzi ndi zaka zisanu, mtengo wa munthu wamwamuna ukhale masekeli asanu a siliva ndipo ngati ndi wamkazi, ukhale masekeli atatu a siliva. 7 Ngati ndi munthu wa zaka makumi asanu ndi limodzi kapena kuposerapo, mtengo wa wamwamuna ukhale masekeli khumi ndi asanu, ndipo wamkazi ukhale masekeli khumi. 8 Ngati munthu amene anachita lumbiro ndi wosauka kwambiri kuti sangathe kulipira ndalama zimenezo, abwere ndi munthu woperekedwa uja kwa wansembe, ndipo wansembeyo ayike mtengo woti munthu wolumbirayo angathe kulipira. 9 “ ‘Ngati chimene anachitira lumbiro kuti apereke ndi nyama imene amapereka kukhala nsembe kwa Yehova, zonse zimene amapereka kwa Yehova nʼzopatulika. 10 Munthu asasinthanitse ndi ina kapena kupereka ina yabwino mʼmalo mwa yoyipa, kapena yoyipa mʼmalo mwa yabwino. Ngati asinthitsa nyama ina mʼmalo mwa ina, nyamayo pamodzi ndi inzake wasinthitsayo zikhala zopatulika. 11 Ngati chimene anachitira lumbiro ndi nyama yodetsedwa, nyama imene siloledwa kuyipereka kukhala nsembe kwa Yehova, nyamayo abwere nayo kwa wansembe, 12 ndipo wansembeyo atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake. 13 Ngati mwini wakeyo akufuna kuwombola nyamayo, awonjezere pa mtengo wake wa nyamayo chimodzi mwa zigawo zisanu zamtengowo. 14 “ ‘Ngati munthu apereka nyumba yake kuti ikhale yopatulika kwa Yehova, wansembe atchule mtengo wake poona ngati ndi yabwino kapena ndi yoyipa. Mtengo umene wansembe atchule ndiwo udzakhale mtengo wake. 15 Ngati munthu amene wapereka nyumbayo afuna kuyiwombola nyumbayo, awonjezere pamtengo wake wa nyumbayo, limodzi mwa magawo asanu amtengowo. Ndipo nyumbayo idzakhalanso yake. 16 “ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova mbali ina ya malo a makolo ake, mtengo umene awuyike ukhale wolingana ndi mtengo wa mbewu zimene zimadzabzalidwamo. Zikhale mbewu za barele za makilogalamu makumi awiri ndipo mtengo wake ukhale masekeli makumi asanu. 17 Ngati munthu apereka munda wake kuyambira chaka chokondwerera zaka makumi asanu, mtengo wake ukhale umene unakhazikitsidwa. 18 Koma ngati apereka mundawo chaka chokondwerera zaka makumi asanu chitapita, wansembe adzatchula mtengo molingana ndi zaka zomwe zatsala kuti chifike chaka china chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo mtengo wake udzakhala wotsikirapo. 19 Ngati munthu amene wapereka munda afuna kuwuwombola, ayenera kuwonjezera pa mtengo wake wa mundawo, limodzi mwa magawo asanu a mtengowo. Ndipo mundawo udzakhalanso wake. 20 Koma ngati sawuwombola mundawo, kapena ngati waugulitsa kwa munthu wina, mundawo sudzawomboledwanso. 21 Mwini mundawo akawusiya mʼchaka chokondwerera zaka makumi asanu ndiye kuti mundawo udzakhala wopatulika monga woperekedwa kwa Yehova: udzakhala munda wa ansembe. 22 “ ‘Ngati munthu apereka kwa Yehova munda umene anagula, umene si malo a makolo ake, 23 wansembe atchule mtengo wake kufikira pa chaka chokondwerera zaka makumi asanu, ndipo munthuyo apereke ndalama zokwanira mtengo wake pa tsikulo monga ndalama zopatulika kwa Yehova. 24 Pa chaka chokondwerera zaka makumi asanu, mundawo udzabwezedwa kwa munthu amene anawugulitsayo, amene malowo anali ake. 25 Potchula mtengo uliwonse wansembe awerengere molingana ndi mtengo wa sekeli wa ku Nyumba ya Mulungu: magera makumi awiri pa sekeli imodzi. 26 “ ‘Koma pasapezeke munthu wopereka mwana woyamba kubadwa wa nyama, popeza mwana woyamba kubadwa ali kale wa Yehova, kaya ndi ngʼombe kapena nkhosa, zimenezi ndi za Yehova. 27 Ngati ili nyama yodetsedwa, ayiwombole pa mtengo umene wansembe wawuyika, ndi kuwonjezeranso pa mtengo wake wa nyamayo, limodzi mwa magawo asanu amtengowo. Ngati sayiwombola, igulitsidwe pa mtengo umene wansembe awuyike. 28 “ ‘Koma chinthu chilichonse choperekedwa kwa Yehova, kaya ndi munthu, nyama, kaya ndi malo a makolo, chimenechi chisagulitsidwe kapena kuwomboledwa. Choperekedwa kwa Yehova motere nʼchopatulika kwambiri. 29 “ ‘Munthu amene waperekedwa kotheratu sangawomboledwe. Munthuyo ayenera kuphedwa. 30 “ ‘Chakhumi chilichonse chochokera mʼdziko, kaya ndi tirigu wochokera mʼnthaka kapena chipatso cha mʼmitengo ndi za Yehova. Chimenecho ndi chopatulika kwa Yehova. 31 Ngati munthu afuna kuwombola chakhumi chilichonse, awonjezere pamtengo wake chimodzi mwa zigawo zisanu za mtengowo. 32 Chakhumi cha ngʼombe ndi nkhosa, kapena kuti nyama iliyonse ya khumi imene mʼbusa wayiwerenga idzakhala yopatulikira kwa Yehova. 33 Palibe amene adzaloledwa kusankha nyama yomwe ili yabwino kapena kusinthitsa. Ngati asinthitsa, nyamayo pamodzi ndi inzakeyo zidzakhala zopatulika ndipo sangaziwombole.’ ” 34 Amenewa ndi malamulo amene Yehova anamupatsa Mose pa Phiri la Sinai kuti awuze Aisraeli.

In Other Versions

Leviticus 27 in the ANGEFD

Leviticus 27 in the ANTPNG2D

Leviticus 27 in the AS21

Leviticus 27 in the BAGH

Leviticus 27 in the BBPNG

Leviticus 27 in the BBT1E

Leviticus 27 in the BDS

Leviticus 27 in the BEV

Leviticus 27 in the BHAD

Leviticus 27 in the BIB

Leviticus 27 in the BLPT

Leviticus 27 in the BNT

Leviticus 27 in the BNTABOOT

Leviticus 27 in the BNTLV

Leviticus 27 in the BOATCB

Leviticus 27 in the BOATCB2

Leviticus 27 in the BOBCV

Leviticus 27 in the BOCNT

Leviticus 27 in the BOECS

Leviticus 27 in the BOHCB

Leviticus 27 in the BOHCV

Leviticus 27 in the BOHLNT

Leviticus 27 in the BOHNTLTAL

Leviticus 27 in the BOICB

Leviticus 27 in the BOILNTAP

Leviticus 27 in the BOITCV

Leviticus 27 in the BOKCV

Leviticus 27 in the BOKCV2

Leviticus 27 in the BOKHWOG

Leviticus 27 in the BOKSSV

Leviticus 27 in the BOLCB

Leviticus 27 in the BOLCB2

Leviticus 27 in the BOMCV

Leviticus 27 in the BONAV

Leviticus 27 in the BONCB

Leviticus 27 in the BONLT

Leviticus 27 in the BONUT2

Leviticus 27 in the BOPLNT

Leviticus 27 in the BOSCB

Leviticus 27 in the BOSNC

Leviticus 27 in the BOTLNT

Leviticus 27 in the BOVCB

Leviticus 27 in the BOYCB

Leviticus 27 in the BPBB

Leviticus 27 in the BPH

Leviticus 27 in the BSB

Leviticus 27 in the CCB

Leviticus 27 in the CUV

Leviticus 27 in the CUVS

Leviticus 27 in the DBT

Leviticus 27 in the DGDNT

Leviticus 27 in the DHNT

Leviticus 27 in the DNT

Leviticus 27 in the ELBE

Leviticus 27 in the EMTV

Leviticus 27 in the ESV

Leviticus 27 in the FBV

Leviticus 27 in the FEB

Leviticus 27 in the GGMNT

Leviticus 27 in the GNT

Leviticus 27 in the HARY

Leviticus 27 in the HNT

Leviticus 27 in the IRVA

Leviticus 27 in the IRVB

Leviticus 27 in the IRVG

Leviticus 27 in the IRVH

Leviticus 27 in the IRVK

Leviticus 27 in the IRVM

Leviticus 27 in the IRVM2

Leviticus 27 in the IRVO

Leviticus 27 in the IRVP

Leviticus 27 in the IRVT

Leviticus 27 in the IRVT2

Leviticus 27 in the IRVU

Leviticus 27 in the ISVN

Leviticus 27 in the JSNT

Leviticus 27 in the KAPI

Leviticus 27 in the KBT1ETNIK

Leviticus 27 in the KBV

Leviticus 27 in the KJV

Leviticus 27 in the KNFD

Leviticus 27 in the LBA

Leviticus 27 in the LBLA

Leviticus 27 in the LNT

Leviticus 27 in the LSV

Leviticus 27 in the MAAL

Leviticus 27 in the MBV

Leviticus 27 in the MBV2

Leviticus 27 in the MHNT

Leviticus 27 in the MKNFD

Leviticus 27 in the MNG

Leviticus 27 in the MNT

Leviticus 27 in the MNT2

Leviticus 27 in the MRS1T

Leviticus 27 in the NAA

Leviticus 27 in the NASB

Leviticus 27 in the NBLA

Leviticus 27 in the NBS

Leviticus 27 in the NBVTP

Leviticus 27 in the NET2

Leviticus 27 in the NIV11

Leviticus 27 in the NNT

Leviticus 27 in the NNT2

Leviticus 27 in the NNT3

Leviticus 27 in the PDDPT

Leviticus 27 in the PFNT

Leviticus 27 in the RMNT

Leviticus 27 in the SBIAS

Leviticus 27 in the SBIBS

Leviticus 27 in the SBIBS2

Leviticus 27 in the SBICS

Leviticus 27 in the SBIDS

Leviticus 27 in the SBIGS

Leviticus 27 in the SBIHS

Leviticus 27 in the SBIIS

Leviticus 27 in the SBIIS2

Leviticus 27 in the SBIIS3

Leviticus 27 in the SBIKS

Leviticus 27 in the SBIKS2

Leviticus 27 in the SBIMS

Leviticus 27 in the SBIOS

Leviticus 27 in the SBIPS

Leviticus 27 in the SBISS

Leviticus 27 in the SBITS

Leviticus 27 in the SBITS2

Leviticus 27 in the SBITS3

Leviticus 27 in the SBITS4

Leviticus 27 in the SBIUS

Leviticus 27 in the SBIVS

Leviticus 27 in the SBT

Leviticus 27 in the SBT1E

Leviticus 27 in the SCHL

Leviticus 27 in the SNT

Leviticus 27 in the SUSU

Leviticus 27 in the SUSU2

Leviticus 27 in the SYNO

Leviticus 27 in the TBIAOTANT

Leviticus 27 in the TBT1E

Leviticus 27 in the TBT1E2

Leviticus 27 in the TFTIP

Leviticus 27 in the TFTU

Leviticus 27 in the TGNTATF3T

Leviticus 27 in the THAI

Leviticus 27 in the TNFD

Leviticus 27 in the TNT

Leviticus 27 in the TNTIK

Leviticus 27 in the TNTIL

Leviticus 27 in the TNTIN

Leviticus 27 in the TNTIP

Leviticus 27 in the TNTIZ

Leviticus 27 in the TOMA

Leviticus 27 in the TTENT

Leviticus 27 in the UBG

Leviticus 27 in the UGV

Leviticus 27 in the UGV2

Leviticus 27 in the UGV3

Leviticus 27 in the VBL

Leviticus 27 in the VDCC

Leviticus 27 in the YALU

Leviticus 27 in the YAPE

Leviticus 27 in the YBVTP

Leviticus 27 in the ZBP