Leviticus 6 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Ngati munthu wina aliyense achimwa, nachita zinthu mosakhulupirika kwa Yehova chifukwa cha kunyenga mnzake pokana kumubwezera zimene anamusungitsa, kapena kumubera kapenanso kumulanda, 3 kapena ndi kunama kuti sanatole chinthu chimene chinatayika, kapena kulumbira mwachinyengo pa chinthu chilichonse chimene munthu akachita amachimwa nacho, 4 ndi wopalamula ndithu, ndipo ayenera kubweza zimene anabazo, zimene analanda mwachinyengozo, zimene anamusungitsazo, zimene anatolazo 5 kapena zimene analumbira monyengazo. Pa tsiku limene apezeke kuti wapalamuladi, iye ayenera kumubwezera mwini wake zinthu zonsezi ndi kuwonjezerapo chimodzi mwa zigawo zisanu zilizonse. 6 Pambuyo pake apereke kwa Yehova nsembe yopalamula. Nsembe yake ikhale nkhosa yayimuna yopanda chilema ndipo mtengo wake wogwirizana ndi nsembe yopepesera machimo. 7 Kenaka wansembe achite mwambo wopepesera tchimo la munthuyo pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa chilichonse chomwe anachita kuti akhale wopalamula.” 8 Yehova anawuza Mose kuti, 9 “Lamula Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Lamulo la nsembe yopsereza ndi ili: Nsembe yopserezayo izikhala pa moto pa guwa usiku wonse mpaka mmawa, ndipo moto wa paguwapo uzikhala ukuyaka nthawi zonse. 10 Tsono wansembe avale mkanjo wake wa nsalu yofewa ndi yosalala. Mʼkati avalenso kabudula wofewa, wosalala. Pambuyo pake atenge phulusa la nyama imene yatenthedwa pa guwa lansembe paja ndi kulithira pambali pa guwa lomwelo. 11 Akatero avule zovala zakezo ndi kuvala zovala zina. Kenaka atulutse phulusalo ndi kukaliyika pa malo woyeretsedwa kunja kwa chithando. 12 Moto wa pa guwa uzikhala ukuyaka nthawi zonse, usamazime. Mmawa uliwonse wansembe aziwonjezerapo nkhuni pa motopo ndi kukonza nsembe yopsereza, ndi kutentha mafuta a nsembe yachiyanjano pamenepo. 13 Moto uzikhala ukuyaka pa guwa nthawi zonse ndipo usazimepo. 14 “ ‘Lamulo la nsembe yachakudya ndi ili: ana a Aaroni azibwera nayo nsembeyo pamaso pa Yehova, patsogolo pa guwa. 15 Wansembe mmodzi atapeko dzanja limodzi la ufa wosalala wa nsembe yachakudya ija kuti ukhala ufa wachikumbutso ndi mafuta pamodzi ndi lubani yense amene ali pa nsembe ya chakudyacho, ndipo azitenthe pa guwa kuti zilandiridwe ndi Yehova mʼmalo mwa nsembe yonse kuti zikhale nsembe ya fungo lokomera Yehova. 16 Aaroni ndi ana ake azidya zimene zatsala koma azidya zopanda yisiti ku malo wopatulika, ku bwalo la tenti ya msonkhano. 17 Poziphika asathire yisiti. Ndawapatsa zotsalazo kuti zikhale gawo lawo la nsembe zanga zopsereza. Zonsezi ndi zopatulika kwambiri monga nsembe yopepesera tchimo ndiponso nsembe yopepesera machimo. 18 Mwana aliyense wamwamuna wa Aaroni azidyako za nsembe zopsereza zopereka kwa Yehova. Ndi gawo lake lokhazikika la chopereka chopsereza kwa Yehova pa mibado yanu yonse. Chilichonse chimene chidzakhudza nsembezo chidzakhala chopatulika.’ ” 19 Yehova anawuzanso Mose kuti, 20 “Nsembe imene Aaroni ndi ana ake ayenera kupereka kwa Yehova pa tsiku limene wansembe akudzozedwa ndi iyi: ufa wosalala kilogalamu imodzi ngati chopereka chachakudya cha nthawi zonse. Azipereka theka limodzi mmawa ndipo theka linalo madzulo. 21 Ipangidwe ndi mafuta pa chiwaya ndipo ubwere nayo ili yosakaniza bwino, yophikidwa mitandamitanda monga amachitira ndi nsembe yachakudya. Iphikidwe moti itulutse fungo lokomera Yehova. 22 Mwana wa fuko la Aaroni amene adzadzozedwe kukhala wansembe kulowa mʼmalo mwa Aaroni ndiye amene azidzakonza ndi kupereka nsembeyi kwa Yehova nthawi zonse monga kunalembedwera. 23 Nsembe iliyonse yachakudya ya wansembe izitenthedwa kwathunthu, isamadyedwe.” 24 Yehova anawuza Mose kuti 25 “Uza Aaroni ndi ana ake kuti, ‘Malamulo a nsembe ya tchimo ndi awa: Nsembeyi iziphedwa pamaso pa Yehova pa malo pamene mumaphera nsembe yopsereza popeza ndi nsembe yopatulika. 26 Wansembe amene apereke nsembeyi adyere ku malo wopatulika ndiye kuti mʼbwalo la tenti ya msonkhano. 27 Chilichonse chimene chidzakhudza nsembeyo chidzakhala chopatulika, ndipo ngati magazi ake agwera pa chovala, muchape chovalacho pa malo opatulika. 28 Mʼphika wadothi umene aphikira nyamayo auphwanye. Koma ngati yaphikidwa mu mʼphika wa mkuwa, awukweche ndi kuwutsukuluza ndi madzi. 29 Munthu wamwamuna aliyense wa mʼbanja la wansembe angathe kuyidya popeza nsembeyi ndi yopatulika kwambiri. 30 Koma nsembe yopepesera tchimo imene magazi ake amabwera nawo mu tenti ya msonkhano kudzachita mwambo wopepesera tchimo ku malo opatulika isadyedwe, mʼmalo mwake itenthedwe.’ ”

In Other Versions

Leviticus 6 in the ANGEFD

Leviticus 6 in the ANTPNG2D

Leviticus 6 in the AS21

Leviticus 6 in the BAGH

Leviticus 6 in the BBPNG

Leviticus 6 in the BBT1E

Leviticus 6 in the BDS

Leviticus 6 in the BEV

Leviticus 6 in the BHAD

Leviticus 6 in the BIB

Leviticus 6 in the BLPT

Leviticus 6 in the BNT

Leviticus 6 in the BNTABOOT

Leviticus 6 in the BNTLV

Leviticus 6 in the BOATCB

Leviticus 6 in the BOATCB2

Leviticus 6 in the BOBCV

Leviticus 6 in the BOCNT

Leviticus 6 in the BOECS

Leviticus 6 in the BOHCB

Leviticus 6 in the BOHCV

Leviticus 6 in the BOHLNT

Leviticus 6 in the BOHNTLTAL

Leviticus 6 in the BOICB

Leviticus 6 in the BOILNTAP

Leviticus 6 in the BOITCV

Leviticus 6 in the BOKCV

Leviticus 6 in the BOKCV2

Leviticus 6 in the BOKHWOG

Leviticus 6 in the BOKSSV

Leviticus 6 in the BOLCB

Leviticus 6 in the BOLCB2

Leviticus 6 in the BOMCV

Leviticus 6 in the BONAV

Leviticus 6 in the BONCB

Leviticus 6 in the BONLT

Leviticus 6 in the BONUT2

Leviticus 6 in the BOPLNT

Leviticus 6 in the BOSCB

Leviticus 6 in the BOSNC

Leviticus 6 in the BOTLNT

Leviticus 6 in the BOVCB

Leviticus 6 in the BOYCB

Leviticus 6 in the BPBB

Leviticus 6 in the BPH

Leviticus 6 in the BSB

Leviticus 6 in the CCB

Leviticus 6 in the CUV

Leviticus 6 in the CUVS

Leviticus 6 in the DBT

Leviticus 6 in the DGDNT

Leviticus 6 in the DHNT

Leviticus 6 in the DNT

Leviticus 6 in the ELBE

Leviticus 6 in the EMTV

Leviticus 6 in the ESV

Leviticus 6 in the FBV

Leviticus 6 in the FEB

Leviticus 6 in the GGMNT

Leviticus 6 in the GNT

Leviticus 6 in the HARY

Leviticus 6 in the HNT

Leviticus 6 in the IRVA

Leviticus 6 in the IRVB

Leviticus 6 in the IRVG

Leviticus 6 in the IRVH

Leviticus 6 in the IRVK

Leviticus 6 in the IRVM

Leviticus 6 in the IRVM2

Leviticus 6 in the IRVO

Leviticus 6 in the IRVP

Leviticus 6 in the IRVT

Leviticus 6 in the IRVT2

Leviticus 6 in the IRVU

Leviticus 6 in the ISVN

Leviticus 6 in the JSNT

Leviticus 6 in the KAPI

Leviticus 6 in the KBT1ETNIK

Leviticus 6 in the KBV

Leviticus 6 in the KJV

Leviticus 6 in the KNFD

Leviticus 6 in the LBA

Leviticus 6 in the LBLA

Leviticus 6 in the LNT

Leviticus 6 in the LSV

Leviticus 6 in the MAAL

Leviticus 6 in the MBV

Leviticus 6 in the MBV2

Leviticus 6 in the MHNT

Leviticus 6 in the MKNFD

Leviticus 6 in the MNG

Leviticus 6 in the MNT

Leviticus 6 in the MNT2

Leviticus 6 in the MRS1T

Leviticus 6 in the NAA

Leviticus 6 in the NASB

Leviticus 6 in the NBLA

Leviticus 6 in the NBS

Leviticus 6 in the NBVTP

Leviticus 6 in the NET2

Leviticus 6 in the NIV11

Leviticus 6 in the NNT

Leviticus 6 in the NNT2

Leviticus 6 in the NNT3

Leviticus 6 in the PDDPT

Leviticus 6 in the PFNT

Leviticus 6 in the RMNT

Leviticus 6 in the SBIAS

Leviticus 6 in the SBIBS

Leviticus 6 in the SBIBS2

Leviticus 6 in the SBICS

Leviticus 6 in the SBIDS

Leviticus 6 in the SBIGS

Leviticus 6 in the SBIHS

Leviticus 6 in the SBIIS

Leviticus 6 in the SBIIS2

Leviticus 6 in the SBIIS3

Leviticus 6 in the SBIKS

Leviticus 6 in the SBIKS2

Leviticus 6 in the SBIMS

Leviticus 6 in the SBIOS

Leviticus 6 in the SBIPS

Leviticus 6 in the SBISS

Leviticus 6 in the SBITS

Leviticus 6 in the SBITS2

Leviticus 6 in the SBITS3

Leviticus 6 in the SBITS4

Leviticus 6 in the SBIUS

Leviticus 6 in the SBIVS

Leviticus 6 in the SBT

Leviticus 6 in the SBT1E

Leviticus 6 in the SCHL

Leviticus 6 in the SNT

Leviticus 6 in the SUSU

Leviticus 6 in the SUSU2

Leviticus 6 in the SYNO

Leviticus 6 in the TBIAOTANT

Leviticus 6 in the TBT1E

Leviticus 6 in the TBT1E2

Leviticus 6 in the TFTIP

Leviticus 6 in the TFTU

Leviticus 6 in the TGNTATF3T

Leviticus 6 in the THAI

Leviticus 6 in the TNFD

Leviticus 6 in the TNT

Leviticus 6 in the TNTIK

Leviticus 6 in the TNTIL

Leviticus 6 in the TNTIN

Leviticus 6 in the TNTIP

Leviticus 6 in the TNTIZ

Leviticus 6 in the TOMA

Leviticus 6 in the TTENT

Leviticus 6 in the UBG

Leviticus 6 in the UGV

Leviticus 6 in the UGV2

Leviticus 6 in the UGV3

Leviticus 6 in the VBL

Leviticus 6 in the VDCC

Leviticus 6 in the YALU

Leviticus 6 in the YAPE

Leviticus 6 in the YBVTP

Leviticus 6 in the ZBP