Leviticus 8 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Tenga Aaroni ndi ana ake, zovala zawo, mafuta wodzozera, ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziwiri zazimuna ndi dengu la buledi wopanda yisiti, 3 ndipo usonkhanitse gulu la anthu pa khomo la tenti ya msonkhano.” 4 Mose anachita zomwe Yehova anamulamula ndipo gulu la anthu linasonkhana pa khomo la tenti ya msonkhano. 5 Mose anawuza gulu la anthuwo kuti, “Izi ndi zimene Yehova walamulira kuti zichitike.” 6 Pamenepo Mose anabwera ndi Aaroni ndi ana ake nawasambitsa ndi madzi. 7 Anamuveka Aaroni mwinjiro, ndi kumumanga lamba mʼchiwuno. Anamuvekanso mkanjo wa efodi ndi efodiyo. Anamangira lamba efodiyo amene analukidwa mwaluso uja, motero efodiyo analimba mʼchiwunomo. 8 Anamuvekanso chovala chapachifuwa ndipo mʼchovalacho anayikamo Urimu ndi Tumimu. 9 Kenaka anamuveka Aaroniyo nduwira kumutu ndipo patsogolo pa nduwirayo anayikapo duwa lagolide, chizindikiro chopatulika monga momwe Yehova analamulira Mose. 10 Pamenepo Mose anatenga mafuta wodzozera nadzoza tenti ya msonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali mʼmenemo, ndipo potero anazipatula. 11 Anawaza mafuta ena pa guwa kasanu ndi kawiri, nalidzoza guwalo pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso beseni ndi tsinde lake, nazipatula. 12 Anathira mafuta wodzozera ena pamutu pa Aaroni ndipo anamudzoza ndi kumupatula. 13 Kenaka anabwera ndi ana a Aaroni. Anawaveka minjiro, ndi kuwamanga malamba mʼchiwuno ndi kuwaveka nduwira kumutu monga momwe Yehova analamulira Mose. 14 Kenaka Mose anabwera ndi ngʼombe yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aaroni ndi ana ake anasanjika manja awo pamutu pa ngʼombeyo. 15 Mose anapha ngʼombeyo, ndi kutenga magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chake pa nyanga zaguwa lansembe, naliyeretsa. Magazi otsalawo anawakhuthulira pa tsinde laguwalo. Motero anachita mwambo wopepesera machimo. 16 Mose anatenganso mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi, ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake, nazitentha pa guwapo. 17 Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake anaziwotcha kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose. 18 Kenaka anabwera ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopsereza, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake. 19 Ndipo Mose anapha nkhosayo ndi kuwaza magazi ake mbali zonse zaguwalo. 20 Anayidula nkhosayo nthulinthuli ndipo anatentha mutu wake, nthulizo ndi mafuta. 21 Anatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, ndi kutentha nkhosa yonseyo pa guwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yachakudya yoperekedwa kwa Yehova monga Yehovayo analamulira Mose. 22 Kenaka Mose anapereka nkhosa yayimuna ina pamwambo wodzoza ansembe, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake. 23 Mose anayipha nkhosayo ndipo anatenga magazi ake ena ndi kupaka ndewere za khutu la kudzanja lamanja la Aaroni, pa chala chake chachikulu cha kudzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha phazi lakumanja. 24 Pambuyo pake Mose anabwera ndi ana aamuna a Aaroni ndi kupaka magazi pa ndewere za makutu awo akumanja, pa zala zawo zazikulu za dzanja lamanja, ndiponso pa zala zawo zazikulu za kuphazi lakumanja. Kenaka iye anawaza magazi otsalawo mbali zonse za guwalo. 25 Anatenganso mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake ndiponso ntchafu yakumanja. 26 Ndipo mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo buledi mmodzi, buledi mmodzi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. Zonsezi anaziyika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija. 27 Mose anapereka zonsezi mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake amene anazipereka kwa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula. 28 Kenaka Mose anazitenga mʼmanja mwawo ndipo anazipsereza pa guwa lansembe pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza ija kuti ikhale nsembe yopereka pamwambo wodzoza ansembe, kuti ipereke fungo lokoma, chopereka chachakudya kwa Yehova. 29 Mose anatenga chidale cha nkhosa yayimuna, chomwe ndi gawo lake pamwambo wodzoza ansembe, ndipo anachiweyula pamaso pa Yehova kuti chikhale nsembe yoweyula monga momwe Yehova analamulira Mose. 30 Kenaka Mose anatenga mafuta wodzozera ansembe ndi magazi amene anali pa guwa nawaza pa Aaroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zawo. Motero Mose anapatula Aaroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zawo. 31 Mose anawuza Aaroni ndi ana ake kuti, “Phikani nyamayo pa khomo la tenti ya msonkhano, ndipo mudyere pomwepo pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu la zopereka za pamwambo wodzoza ansembe monga Yehova analamulira kuti, ‘Aaroni ndi ana ake azidya zimenezi.’ 32 Ndipo nyama ndi buledi zotsalazo, muziwotche. 33 Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano kwa masiku asanu ndi awiri mpaka masiku amwambo wokudzozani unsembe atatha, pakuti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi awiri. 34 Zimene zachitika lerozi analamula ndi Yehova kuti zichitike ngati nsembe yopepesera machimo anu. 35 Muzikhala pa khomo la tenti ya msonkhano usana ndi usiku kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo muzichita zimene Yehova wakulamulani kuti musafe, pakuti zimenezi ndi zomwe Yehova wandilamulira.” 36 Choncho Aaroni ndi ana ake anachita zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.

In Other Versions

Leviticus 8 in the ANGEFD

Leviticus 8 in the ANTPNG2D

Leviticus 8 in the AS21

Leviticus 8 in the BAGH

Leviticus 8 in the BBPNG

Leviticus 8 in the BBT1E

Leviticus 8 in the BDS

Leviticus 8 in the BEV

Leviticus 8 in the BHAD

Leviticus 8 in the BIB

Leviticus 8 in the BLPT

Leviticus 8 in the BNT

Leviticus 8 in the BNTABOOT

Leviticus 8 in the BNTLV

Leviticus 8 in the BOATCB

Leviticus 8 in the BOATCB2

Leviticus 8 in the BOBCV

Leviticus 8 in the BOCNT

Leviticus 8 in the BOECS

Leviticus 8 in the BOHCB

Leviticus 8 in the BOHCV

Leviticus 8 in the BOHLNT

Leviticus 8 in the BOHNTLTAL

Leviticus 8 in the BOICB

Leviticus 8 in the BOILNTAP

Leviticus 8 in the BOITCV

Leviticus 8 in the BOKCV

Leviticus 8 in the BOKCV2

Leviticus 8 in the BOKHWOG

Leviticus 8 in the BOKSSV

Leviticus 8 in the BOLCB

Leviticus 8 in the BOLCB2

Leviticus 8 in the BOMCV

Leviticus 8 in the BONAV

Leviticus 8 in the BONCB

Leviticus 8 in the BONLT

Leviticus 8 in the BONUT2

Leviticus 8 in the BOPLNT

Leviticus 8 in the BOSCB

Leviticus 8 in the BOSNC

Leviticus 8 in the BOTLNT

Leviticus 8 in the BOVCB

Leviticus 8 in the BOYCB

Leviticus 8 in the BPBB

Leviticus 8 in the BPH

Leviticus 8 in the BSB

Leviticus 8 in the CCB

Leviticus 8 in the CUV

Leviticus 8 in the CUVS

Leviticus 8 in the DBT

Leviticus 8 in the DGDNT

Leviticus 8 in the DHNT

Leviticus 8 in the DNT

Leviticus 8 in the ELBE

Leviticus 8 in the EMTV

Leviticus 8 in the ESV

Leviticus 8 in the FBV

Leviticus 8 in the FEB

Leviticus 8 in the GGMNT

Leviticus 8 in the GNT

Leviticus 8 in the HARY

Leviticus 8 in the HNT

Leviticus 8 in the IRVA

Leviticus 8 in the IRVB

Leviticus 8 in the IRVG

Leviticus 8 in the IRVH

Leviticus 8 in the IRVK

Leviticus 8 in the IRVM

Leviticus 8 in the IRVM2

Leviticus 8 in the IRVO

Leviticus 8 in the IRVP

Leviticus 8 in the IRVT

Leviticus 8 in the IRVT2

Leviticus 8 in the IRVU

Leviticus 8 in the ISVN

Leviticus 8 in the JSNT

Leviticus 8 in the KAPI

Leviticus 8 in the KBT1ETNIK

Leviticus 8 in the KBV

Leviticus 8 in the KJV

Leviticus 8 in the KNFD

Leviticus 8 in the LBA

Leviticus 8 in the LBLA

Leviticus 8 in the LNT

Leviticus 8 in the LSV

Leviticus 8 in the MAAL

Leviticus 8 in the MBV

Leviticus 8 in the MBV2

Leviticus 8 in the MHNT

Leviticus 8 in the MKNFD

Leviticus 8 in the MNG

Leviticus 8 in the MNT

Leviticus 8 in the MNT2

Leviticus 8 in the MRS1T

Leviticus 8 in the NAA

Leviticus 8 in the NASB

Leviticus 8 in the NBLA

Leviticus 8 in the NBS

Leviticus 8 in the NBVTP

Leviticus 8 in the NET2

Leviticus 8 in the NIV11

Leviticus 8 in the NNT

Leviticus 8 in the NNT2

Leviticus 8 in the NNT3

Leviticus 8 in the PDDPT

Leviticus 8 in the PFNT

Leviticus 8 in the RMNT

Leviticus 8 in the SBIAS

Leviticus 8 in the SBIBS

Leviticus 8 in the SBIBS2

Leviticus 8 in the SBICS

Leviticus 8 in the SBIDS

Leviticus 8 in the SBIGS

Leviticus 8 in the SBIHS

Leviticus 8 in the SBIIS

Leviticus 8 in the SBIIS2

Leviticus 8 in the SBIIS3

Leviticus 8 in the SBIKS

Leviticus 8 in the SBIKS2

Leviticus 8 in the SBIMS

Leviticus 8 in the SBIOS

Leviticus 8 in the SBIPS

Leviticus 8 in the SBISS

Leviticus 8 in the SBITS

Leviticus 8 in the SBITS2

Leviticus 8 in the SBITS3

Leviticus 8 in the SBITS4

Leviticus 8 in the SBIUS

Leviticus 8 in the SBIVS

Leviticus 8 in the SBT

Leviticus 8 in the SBT1E

Leviticus 8 in the SCHL

Leviticus 8 in the SNT

Leviticus 8 in the SUSU

Leviticus 8 in the SUSU2

Leviticus 8 in the SYNO

Leviticus 8 in the TBIAOTANT

Leviticus 8 in the TBT1E

Leviticus 8 in the TBT1E2

Leviticus 8 in the TFTIP

Leviticus 8 in the TFTU

Leviticus 8 in the TGNTATF3T

Leviticus 8 in the THAI

Leviticus 8 in the TNFD

Leviticus 8 in the TNT

Leviticus 8 in the TNTIK

Leviticus 8 in the TNTIL

Leviticus 8 in the TNTIN

Leviticus 8 in the TNTIP

Leviticus 8 in the TNTIZ

Leviticus 8 in the TOMA

Leviticus 8 in the TTENT

Leviticus 8 in the UBG

Leviticus 8 in the UGV

Leviticus 8 in the UGV2

Leviticus 8 in the UGV3

Leviticus 8 in the VBL

Leviticus 8 in the VDCC

Leviticus 8 in the YALU

Leviticus 8 in the YAPE

Leviticus 8 in the YBVTP

Leviticus 8 in the ZBP