Malachi 1 (BOGWICC)
1 Uthenga: Mawu a Yehova kwa Israeli kudzera mwa Malaki. 2 Yehova akuti, “Ine ndakukondani. Koma inu mukufunsa kuti, ‘Kodi mwatikonda motani?’ ”Yehova akuti, “Kodi Esau sanali mʼbale wake wa Yakobo? Komatu Ine ndinakonda Yakobo, 3 koma ndinamuda Esau, ndipo dziko lake lamapiri ndalisandutsa chipululu ndipo cholowa chake ndasiyira ankhandwe a mʼchipululu.” 4 Mwina Edomu nʼkunena kuti, “Ngakhale taphwanyidwa, tidzamanganso mʼmabwinja.”Koma Yehova Wamphamvuzonse akuti, “Iwo angathe kumanganso, koma Ine ndidzazigwetsanso. Iwo adzatchedwa dziko loyipa, la anthu amene Yehova wayipidwa nawo mpaka muyaya. 5 Inu mudzaziona zimenezi ndi maso anu ndipo mudzati, ‘Yehova ndi Wamkulu, ukulu wake umafika ngakhale kunja kwa malire a Israeli!’ 6 “Mwana amalemekeza abambo ake, ndipo wantchito amaopa abwana ake. Ngati Ine ndine abambo anu, ulemu wanga uli kuti? Ngati ndine mbuye wanu, nanga kundiopa kuli kuti?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse.“Ndinu, inu ansembe, amene mumanyoza dzina langa.“Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi timanyoza dzina lanu bwanji?’ 7 “Inu mwanyoza dzina langa popereka chakudya chodetsedwa pa guwa langa lansembe.“Komatu mukufunsa kuti, ‘Kodi ife takunyozani bwanji?’“Mwandinyoza ponena kuti tebulo la Yehova ndi lonyozeka. 8 Mukamapereka nsembe nyama zosaona, kodi sicholakwa? Mukamapereka nsembe nyama zachilema kapena zodwala, kodi sicholakwa? Kayeseni kuzipereka kwa bwanamkubwa wanu! Kodi akasangalatsidwa nanu? Kodi akazilandira? Akutero Yehova Wamphamvuzonse. 9 “Tsopano tayesani kupempha Mulungu kuti akuchitireni chifundo. Kodi ndi zopereka zotere mʼmanja mwanu, Iye angakulandireni?” Akutero Yehova Wamphamvuzonse. 10 “Ndikulakalaka mmodzi wa inu akanatseka zitseko za Nyumba ya Mulungu, kuti musayatsemo moto pachabe pa guwa langa lansembe! Ine sindikukondwera nanu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse, “ndipo Ine sindidzalandira zopereka za mʼmanja mwanu. 11 Dzina langa lidzalemekezedwa pakati pa mitundu ya anthu, kuchokera kummawa mpaka kumadzulo. Mʼmalo monse adzapereka nsembe zofukiza ndi zopereka zangwiro mʼdzina langa, chifukwa dzina langa lidzakhala lalikulu pakati pa mitundu ya anthu,” akutero Yehova Wamphamvuzonse. 12 “Koma inu mumalinyoza ponena kuti tebulo la Ambuye, ‘ndi lodetsedwa,’ ndipo chakudya chake, ‘nʼchonyozeka!’ 13 Ndipo inu mumati, ‘Ndi zotopetsa zimenezi!’ Ndipo mumandinyogodola Ine,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.“Pamene inu mubweretsa nyama zakuba, zolumala kapena zodwala ndi kupereka nsembe, kodi Ine ndizilandire kuchokera mʼmanja mwanu?” Akutero Yehova. 14 “Atembereredwe munthu wachinyengo amene ali ndi nyama yayimuna yabwino mʼgulu la ziweto zake ndipo analumbira kuyipereka, koma mʼmalo mwake nʼkupereka nsembe kwa Ambuye nyama yosayenera. Yehova Wamphamvuzonse akuti, ‘Pakuti ndine mfumu yayikulu, dzina langa liyenera kuopedwa pakati pa anthu a mitundu yonse.’ ”
In Other Versions
Malachi 1 in the ANGEFD
Malachi 1 in the ANTPNG2D
Malachi 1 in the AS21
Malachi 1 in the BAGH
Malachi 1 in the BBPNG
Malachi 1 in the BBT1E
Malachi 1 in the BDS
Malachi 1 in the BEV
Malachi 1 in the BHAD
Malachi 1 in the BIB
Malachi 1 in the BLPT
Malachi 1 in the BNT
Malachi 1 in the BNTABOOT
Malachi 1 in the BNTLV
Malachi 1 in the BOATCB
Malachi 1 in the BOATCB2
Malachi 1 in the BOBCV
Malachi 1 in the BOCNT
Malachi 1 in the BOECS
Malachi 1 in the BOHCB
Malachi 1 in the BOHCV
Malachi 1 in the BOHLNT
Malachi 1 in the BOHNTLTAL
Malachi 1 in the BOICB
Malachi 1 in the BOILNTAP
Malachi 1 in the BOITCV
Malachi 1 in the BOKCV
Malachi 1 in the BOKCV2
Malachi 1 in the BOKHWOG
Malachi 1 in the BOKSSV
Malachi 1 in the BOLCB
Malachi 1 in the BOLCB2
Malachi 1 in the BOMCV
Malachi 1 in the BONAV
Malachi 1 in the BONCB
Malachi 1 in the BONLT
Malachi 1 in the BONUT2
Malachi 1 in the BOPLNT
Malachi 1 in the BOSCB
Malachi 1 in the BOSNC
Malachi 1 in the BOTLNT
Malachi 1 in the BOVCB
Malachi 1 in the BOYCB
Malachi 1 in the BPBB
Malachi 1 in the BPH
Malachi 1 in the BSB
Malachi 1 in the CCB
Malachi 1 in the CUV
Malachi 1 in the CUVS
Malachi 1 in the DBT
Malachi 1 in the DGDNT
Malachi 1 in the DHNT
Malachi 1 in the DNT
Malachi 1 in the ELBE
Malachi 1 in the EMTV
Malachi 1 in the ESV
Malachi 1 in the FBV
Malachi 1 in the FEB
Malachi 1 in the GGMNT
Malachi 1 in the GNT
Malachi 1 in the HARY
Malachi 1 in the HNT
Malachi 1 in the IRVA
Malachi 1 in the IRVB
Malachi 1 in the IRVG
Malachi 1 in the IRVH
Malachi 1 in the IRVK
Malachi 1 in the IRVM
Malachi 1 in the IRVM2
Malachi 1 in the IRVO
Malachi 1 in the IRVP
Malachi 1 in the IRVT
Malachi 1 in the IRVT2
Malachi 1 in the IRVU
Malachi 1 in the ISVN
Malachi 1 in the JSNT
Malachi 1 in the KAPI
Malachi 1 in the KBT1ETNIK
Malachi 1 in the KBV
Malachi 1 in the KJV
Malachi 1 in the KNFD
Malachi 1 in the LBA
Malachi 1 in the LBLA
Malachi 1 in the LNT
Malachi 1 in the LSV
Malachi 1 in the MAAL
Malachi 1 in the MBV
Malachi 1 in the MBV2
Malachi 1 in the MHNT
Malachi 1 in the MKNFD
Malachi 1 in the MNG
Malachi 1 in the MNT
Malachi 1 in the MNT2
Malachi 1 in the MRS1T
Malachi 1 in the NAA
Malachi 1 in the NASB
Malachi 1 in the NBLA
Malachi 1 in the NBS
Malachi 1 in the NBVTP
Malachi 1 in the NET2
Malachi 1 in the NIV11
Malachi 1 in the NNT
Malachi 1 in the NNT2
Malachi 1 in the NNT3
Malachi 1 in the PDDPT
Malachi 1 in the PFNT
Malachi 1 in the RMNT
Malachi 1 in the SBIAS
Malachi 1 in the SBIBS
Malachi 1 in the SBIBS2
Malachi 1 in the SBICS
Malachi 1 in the SBIDS
Malachi 1 in the SBIGS
Malachi 1 in the SBIHS
Malachi 1 in the SBIIS
Malachi 1 in the SBIIS2
Malachi 1 in the SBIIS3
Malachi 1 in the SBIKS
Malachi 1 in the SBIKS2
Malachi 1 in the SBIMS
Malachi 1 in the SBIOS
Malachi 1 in the SBIPS
Malachi 1 in the SBISS
Malachi 1 in the SBITS
Malachi 1 in the SBITS2
Malachi 1 in the SBITS3
Malachi 1 in the SBITS4
Malachi 1 in the SBIUS
Malachi 1 in the SBIVS
Malachi 1 in the SBT
Malachi 1 in the SBT1E
Malachi 1 in the SCHL
Malachi 1 in the SNT
Malachi 1 in the SUSU
Malachi 1 in the SUSU2
Malachi 1 in the SYNO
Malachi 1 in the TBIAOTANT
Malachi 1 in the TBT1E
Malachi 1 in the TBT1E2
Malachi 1 in the TFTIP
Malachi 1 in the TFTU
Malachi 1 in the TGNTATF3T
Malachi 1 in the THAI
Malachi 1 in the TNFD
Malachi 1 in the TNT
Malachi 1 in the TNTIK
Malachi 1 in the TNTIL
Malachi 1 in the TNTIN
Malachi 1 in the TNTIP
Malachi 1 in the TNTIZ
Malachi 1 in the TOMA
Malachi 1 in the TTENT
Malachi 1 in the UBG
Malachi 1 in the UGV
Malachi 1 in the UGV2
Malachi 1 in the UGV3
Malachi 1 in the VBL
Malachi 1 in the VDCC
Malachi 1 in the YALU
Malachi 1 in the YAPE
Malachi 1 in the YBVTP
Malachi 1 in the ZBP