Matthew 17 (BOGWICC)
1 Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali. 2 Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu. 3 Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu. 4 Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.” 5 Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!” 6 Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba. 7 Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.” 8 Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha. 9 Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.” 10 Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?” 11 Yesu anayankha kuti, “Kunena zoona, Eliya adzayenera kubwera ndipo adzakonza zinthu zonse. 12 Koma Ine ndikuwuzani inu kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anachita naye chilichonse chimene anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa Munthu.” 13 Pamenepo ophunzira anazindikira kuti amawawuza za Yohane Mʼbatizi. 14 Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake. 15 Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi. 16 Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.” 17 Yesu anayankha nati, “Haa, mʼbado wosakhulupirira ndi wokhota maganizo! Kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Ndidzapirira nanu mpaka liti? Bwera nayeni kwa Ine mnyamatayo.” 18 Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo. 19 Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?” 20 Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani. 21 Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.” 22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu. 23 Iwo adzamupha koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chisoni. 24 Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?” 25 Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.”Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?” 26 Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.”Yesu ananena kwa iye kuti, “Ndiye kuti ana sapereka.” 27 Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.
In Other Versions
Matthew 17 in the ANGEFD
Matthew 17 in the ANTPNG2D
Matthew 17 in the AS21
Matthew 17 in the BAGH
Matthew 17 in the BBPNG
Matthew 17 in the BBT1E
Matthew 17 in the BDS
Matthew 17 in the BEV
Matthew 17 in the BHAD
Matthew 17 in the BIB
Matthew 17 in the BLPT
Matthew 17 in the BNT
Matthew 17 in the BNTABOOT
Matthew 17 in the BNTLV
Matthew 17 in the BOATCB
Matthew 17 in the BOATCB2
Matthew 17 in the BOBCV
Matthew 17 in the BOCNT
Matthew 17 in the BOECS
Matthew 17 in the BOHCB
Matthew 17 in the BOHCV
Matthew 17 in the BOHLNT
Matthew 17 in the BOHNTLTAL
Matthew 17 in the BOICB
Matthew 17 in the BOILNTAP
Matthew 17 in the BOITCV
Matthew 17 in the BOKCV
Matthew 17 in the BOKCV2
Matthew 17 in the BOKHWOG
Matthew 17 in the BOKSSV
Matthew 17 in the BOLCB
Matthew 17 in the BOLCB2
Matthew 17 in the BOMCV
Matthew 17 in the BONAV
Matthew 17 in the BONCB
Matthew 17 in the BONLT
Matthew 17 in the BONUT2
Matthew 17 in the BOPLNT
Matthew 17 in the BOSCB
Matthew 17 in the BOSNC
Matthew 17 in the BOTLNT
Matthew 17 in the BOVCB
Matthew 17 in the BOYCB
Matthew 17 in the BPBB
Matthew 17 in the BPH
Matthew 17 in the BSB
Matthew 17 in the CCB
Matthew 17 in the CUV
Matthew 17 in the CUVS
Matthew 17 in the DBT
Matthew 17 in the DGDNT
Matthew 17 in the DHNT
Matthew 17 in the DNT
Matthew 17 in the ELBE
Matthew 17 in the EMTV
Matthew 17 in the ESV
Matthew 17 in the FBV
Matthew 17 in the FEB
Matthew 17 in the GGMNT
Matthew 17 in the GNT
Matthew 17 in the HARY
Matthew 17 in the HNT
Matthew 17 in the IRVA
Matthew 17 in the IRVB
Matthew 17 in the IRVG
Matthew 17 in the IRVH
Matthew 17 in the IRVK
Matthew 17 in the IRVM
Matthew 17 in the IRVM2
Matthew 17 in the IRVO
Matthew 17 in the IRVP
Matthew 17 in the IRVT
Matthew 17 in the IRVT2
Matthew 17 in the IRVU
Matthew 17 in the ISVN
Matthew 17 in the JSNT
Matthew 17 in the KAPI
Matthew 17 in the KBT1ETNIK
Matthew 17 in the KBV
Matthew 17 in the KJV
Matthew 17 in the KNFD
Matthew 17 in the LBA
Matthew 17 in the LBLA
Matthew 17 in the LNT
Matthew 17 in the LSV
Matthew 17 in the MAAL
Matthew 17 in the MBV
Matthew 17 in the MBV2
Matthew 17 in the MHNT
Matthew 17 in the MKNFD
Matthew 17 in the MNG
Matthew 17 in the MNT
Matthew 17 in the MNT2
Matthew 17 in the MRS1T
Matthew 17 in the NAA
Matthew 17 in the NASB
Matthew 17 in the NBLA
Matthew 17 in the NBS
Matthew 17 in the NBVTP
Matthew 17 in the NET2
Matthew 17 in the NIV11
Matthew 17 in the NNT
Matthew 17 in the NNT2
Matthew 17 in the NNT3
Matthew 17 in the PDDPT
Matthew 17 in the PFNT
Matthew 17 in the RMNT
Matthew 17 in the SBIAS
Matthew 17 in the SBIBS
Matthew 17 in the SBIBS2
Matthew 17 in the SBICS
Matthew 17 in the SBIDS
Matthew 17 in the SBIGS
Matthew 17 in the SBIHS
Matthew 17 in the SBIIS
Matthew 17 in the SBIIS2
Matthew 17 in the SBIIS3
Matthew 17 in the SBIKS
Matthew 17 in the SBIKS2
Matthew 17 in the SBIMS
Matthew 17 in the SBIOS
Matthew 17 in the SBIPS
Matthew 17 in the SBISS
Matthew 17 in the SBITS
Matthew 17 in the SBITS2
Matthew 17 in the SBITS3
Matthew 17 in the SBITS4
Matthew 17 in the SBIUS
Matthew 17 in the SBIVS
Matthew 17 in the SBT
Matthew 17 in the SBT1E
Matthew 17 in the SCHL
Matthew 17 in the SNT
Matthew 17 in the SUSU
Matthew 17 in the SUSU2
Matthew 17 in the SYNO
Matthew 17 in the TBIAOTANT
Matthew 17 in the TBT1E
Matthew 17 in the TBT1E2
Matthew 17 in the TFTIP
Matthew 17 in the TFTU
Matthew 17 in the TGNTATF3T
Matthew 17 in the THAI
Matthew 17 in the TNFD
Matthew 17 in the TNT
Matthew 17 in the TNTIK
Matthew 17 in the TNTIL
Matthew 17 in the TNTIN
Matthew 17 in the TNTIP
Matthew 17 in the TNTIZ
Matthew 17 in the TOMA
Matthew 17 in the TTENT
Matthew 17 in the UBG
Matthew 17 in the UGV
Matthew 17 in the UGV2
Matthew 17 in the UGV3
Matthew 17 in the VBL
Matthew 17 in the VDCC
Matthew 17 in the YALU
Matthew 17 in the YAPE
Matthew 17 in the YBVTP
Matthew 17 in the ZBP