Matthew 28 (BOGWICC)

1 Litapita tsiku la Sabata, mmawa wa tsiku loyamba la Sabata, Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina anapita kukaona manda. 2 Kunachitika chivomerezi chachikulu, pakuti mngelo wa Ambuye anabwera kuchokera kumwamba ndipo anapita ku manda, nakagubuduza mwala nawukhalira. 3 Maonekedwe ake anali ngati mphenzi ndipo zovala zake zinali mbuu ngati matalala. 4 Alondawo anachita naye mantha kwambiri kotero kuti ananjenjemera ndi kuwuma ngati akufa. 5 Mngelo anati kwa amayiwo, “Musachite mantha popeza ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anapachikidwa. 6 Iye muno mulibe, wauka monga mmene ananenera. Bwerani, dzaoneni malo amene anagona. 7 Ndipo pitani msanga kawuzeni ophunzira ake kuti, ‘Wauka kwa akufa ndipo watsogola kupita ku Galileya. Mukamuona Iye kumeneko.’ Taonani ndakuwuzani.” 8 Pamenepo amayiwo anachoka mofulumira ku mandako ali ndi mantha komabe atadzaza ndi chimwemwe, ndipo anathamanga kukawuza ophunzira ake. 9 Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nati, “Moni.” Iwo anabwera kwa Iye, nagwira mapazi ake namulambira. 10 Ndipo Yesu anawawuza kuti, “Musachite mantha, pitani kawuzeni abale anga kuti apite ku Galileya ndipo kumeneko akandiona Ine.” 11 Amayi aja akupita, ena mwa alonda aja anapita ku mzinda nafotokozera akulu a ansembe zonse zimene zinachitika. 12 Akulu a ansembe atakumana ndi akuluakulu anapangana zochita. Anapatsa alonda aja ndalama zambiri, 13 nawawuza kuti, “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku ndipo amuba ife tili mtulo.’ 14 Ngati nkhani iyi imupeze bwanamkubwa, ife tidzamukhazika mtima pansi ndipo simudzakhala mʼmavuto.” 15 Pamenepo alondawo anatenga ndalamazo nachita monga mmene anawuzidwira. Ndipo mbiri iyi inawanda pakati pa Ayuda mpaka lero lino. 16 Ndipo ophunzira khumi ndi mmodzi aja anapita ku Galileya, ku phiri limene Yesu anawawuza kuti apite. 17 Atamuona Iye, anamulambira; koma ena anakayika. 18 Kenaka Yesu anabwera kwa iwo nati, “Ulamuliro wonse kumwamba ndi dziko lapansi wapatsidwa kwa Ine. 19 Chifukwa chake, pitani kaphunzitseni anthu a mitundu yonse, ndi kuwabatiza mʼdzina la Atate ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera, 20 ndi kuwaphunzitsa amvere zonse zimene ndinakulamulirani. Ndipo onani, Ine ndidzakhala pamodzi ndi inu kufikira kutha kwa dziko lapansi pano.”

In Other Versions

Matthew 28 in the ANGEFD

Matthew 28 in the ANTPNG2D

Matthew 28 in the AS21

Matthew 28 in the BAGH

Matthew 28 in the BBPNG

Matthew 28 in the BBT1E

Matthew 28 in the BDS

Matthew 28 in the BEV

Matthew 28 in the BHAD

Matthew 28 in the BIB

Matthew 28 in the BLPT

Matthew 28 in the BNT

Matthew 28 in the BNTABOOT

Matthew 28 in the BNTLV

Matthew 28 in the BOATCB

Matthew 28 in the BOATCB2

Matthew 28 in the BOBCV

Matthew 28 in the BOCNT

Matthew 28 in the BOECS

Matthew 28 in the BOHCB

Matthew 28 in the BOHCV

Matthew 28 in the BOHLNT

Matthew 28 in the BOHNTLTAL

Matthew 28 in the BOICB

Matthew 28 in the BOILNTAP

Matthew 28 in the BOITCV

Matthew 28 in the BOKCV

Matthew 28 in the BOKCV2

Matthew 28 in the BOKHWOG

Matthew 28 in the BOKSSV

Matthew 28 in the BOLCB

Matthew 28 in the BOLCB2

Matthew 28 in the BOMCV

Matthew 28 in the BONAV

Matthew 28 in the BONCB

Matthew 28 in the BONLT

Matthew 28 in the BONUT2

Matthew 28 in the BOPLNT

Matthew 28 in the BOSCB

Matthew 28 in the BOSNC

Matthew 28 in the BOTLNT

Matthew 28 in the BOVCB

Matthew 28 in the BOYCB

Matthew 28 in the BPBB

Matthew 28 in the BPH

Matthew 28 in the BSB

Matthew 28 in the CCB

Matthew 28 in the CUV

Matthew 28 in the CUVS

Matthew 28 in the DBT

Matthew 28 in the DGDNT

Matthew 28 in the DHNT

Matthew 28 in the DNT

Matthew 28 in the ELBE

Matthew 28 in the EMTV

Matthew 28 in the ESV

Matthew 28 in the FBV

Matthew 28 in the FEB

Matthew 28 in the GGMNT

Matthew 28 in the GNT

Matthew 28 in the HARY

Matthew 28 in the HNT

Matthew 28 in the IRVA

Matthew 28 in the IRVB

Matthew 28 in the IRVG

Matthew 28 in the IRVH

Matthew 28 in the IRVK

Matthew 28 in the IRVM

Matthew 28 in the IRVM2

Matthew 28 in the IRVO

Matthew 28 in the IRVP

Matthew 28 in the IRVT

Matthew 28 in the IRVT2

Matthew 28 in the IRVU

Matthew 28 in the ISVN

Matthew 28 in the JSNT

Matthew 28 in the KAPI

Matthew 28 in the KBT1ETNIK

Matthew 28 in the KBV

Matthew 28 in the KJV

Matthew 28 in the KNFD

Matthew 28 in the LBA

Matthew 28 in the LBLA

Matthew 28 in the LNT

Matthew 28 in the LSV

Matthew 28 in the MAAL

Matthew 28 in the MBV

Matthew 28 in the MBV2

Matthew 28 in the MHNT

Matthew 28 in the MKNFD

Matthew 28 in the MNG

Matthew 28 in the MNT

Matthew 28 in the MNT2

Matthew 28 in the MRS1T

Matthew 28 in the NAA

Matthew 28 in the NASB

Matthew 28 in the NBLA

Matthew 28 in the NBS

Matthew 28 in the NBVTP

Matthew 28 in the NET2

Matthew 28 in the NIV11

Matthew 28 in the NNT

Matthew 28 in the NNT2

Matthew 28 in the NNT3

Matthew 28 in the PDDPT

Matthew 28 in the PFNT

Matthew 28 in the RMNT

Matthew 28 in the SBIAS

Matthew 28 in the SBIBS

Matthew 28 in the SBIBS2

Matthew 28 in the SBICS

Matthew 28 in the SBIDS

Matthew 28 in the SBIGS

Matthew 28 in the SBIHS

Matthew 28 in the SBIIS

Matthew 28 in the SBIIS2

Matthew 28 in the SBIIS3

Matthew 28 in the SBIKS

Matthew 28 in the SBIKS2

Matthew 28 in the SBIMS

Matthew 28 in the SBIOS

Matthew 28 in the SBIPS

Matthew 28 in the SBISS

Matthew 28 in the SBITS

Matthew 28 in the SBITS2

Matthew 28 in the SBITS3

Matthew 28 in the SBITS4

Matthew 28 in the SBIUS

Matthew 28 in the SBIVS

Matthew 28 in the SBT

Matthew 28 in the SBT1E

Matthew 28 in the SCHL

Matthew 28 in the SNT

Matthew 28 in the SUSU

Matthew 28 in the SUSU2

Matthew 28 in the SYNO

Matthew 28 in the TBIAOTANT

Matthew 28 in the TBT1E

Matthew 28 in the TBT1E2

Matthew 28 in the TFTIP

Matthew 28 in the TFTU

Matthew 28 in the TGNTATF3T

Matthew 28 in the THAI

Matthew 28 in the TNFD

Matthew 28 in the TNT

Matthew 28 in the TNTIK

Matthew 28 in the TNTIL

Matthew 28 in the TNTIN

Matthew 28 in the TNTIP

Matthew 28 in the TNTIZ

Matthew 28 in the TOMA

Matthew 28 in the TTENT

Matthew 28 in the UBG

Matthew 28 in the UGV

Matthew 28 in the UGV2

Matthew 28 in the UGV3

Matthew 28 in the VBL

Matthew 28 in the VDCC

Matthew 28 in the YALU

Matthew 28 in the YAPE

Matthew 28 in the YBVTP

Matthew 28 in the ZBP