Nehemiah 6 (BOGWICC)
1 Pamenepo Sanibalati, Tobiya, Gesemu Mwarabu ndi adani athu anamva kuti ndatsiriza ntchito yomanganso khoma ndi kuti palibe mpata umene watsala ngakhale kuti pa nthawi imeneyi ndinali ndisanayike zitseko pa zipata. 2 Sanibalati ndi Gesemu, ananditumizira uthenga uwu: “Bwerani tidzakumane pa mudzi wina ku chigwa cha Ono.”Koma iwo anakonzekera kuti akandichite chiwembu kumeneko. 3 Choncho ine ndinatuma amithenga ndi yankho ili: “Ine ndikugwira ntchito yayikulu kuno ndipo sindingathe kubwera kumeneko. Kodi ntchito iyime pofuna kuti ndibwere kumeneko?” 4 Ananditumizira uthenga umodzimodzi omwewu kanayi ndipo ndinawayankha chimodzimodzi. 5 Tsono kachisanu, Sanibalati anatumiza wantchito wake ndi kalata yosamata. 6 Mu kalatamo munali mawu akuti,“Pali mphekesera pakati pa mitundu ya anthu, ndiponso Gesemu akunena zomwezo kuti inu ndi Ayuda onse mufuna kuwukira boma. Nʼchifukwa chake mukumanga khoma. Mphekeserazo zikutinso inu mukufuna kudzakhala mfumu yawo. 7 Mwayikanso kale aneneri amene adzalengeza za iwe mu Yerusalemu kuti ‘Mu Yuda muli mfumu!’ Tsono nkhani iyi imveka ndithu kwa mfumu. Choncho bwerani kuti tidzakambirane.” 8 Ine ndinatumiza yankho ili: “Pa zimene mukunenazo, palibe chimene chinachitikapo. Inu mukungozipeka mʼmutu mwanu.” 9 Apa adani athu onsewa ankangofuna kutiopseza. Iwo ankaganiza kuti “Tichita mantha ndi kuleka kugwira ntchito.”Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu ndilimbitseni mtima.” 10 Tsiku lina ndinapita ku nyumba ya Semaya mwana wa Delaya mwana wa Mehatabeli. Tsono anandiwuza kuti, “Tiyeni tikakumanire ku Nyumba ya Mulungu. Tikabisale mʼmenemo ndi kutseka zitseko chifukwa akubwera kudzakuphani. Ndithu usiku uno akubwera kudzakuphani.” 11 Koma ndinayankha kuti, “Kodi munthu ngati ine nʼkuthawa? Kapena munthu wofanana ndi ine nʼkupita ku Nyumba ya Mulungu kuti apulumutse moyo wake? Ayi, ine sindipita!” 12 Ndinazindikira kuti Mulungu sanamutume koma kuti anayankhula mawu oloserawa motsutsana nane chifukwa Tobiya ndi Sanibalati anamulemba ntchitoyi. 13 Iye analembedwa ntchitoyi ndi cholinga choti ine ndichite mantha, ndithawe. Ndikanatero ndiye kuti ndikanachimwira Yehova ndiponso iwowo akanandiyipitsira mbiri yanga ndi kumandinyoza. 14 Tsono ndinapemphera kuti, “Inu Mulungu wanga, kumbukirani Tobiya ndi Sanibalati chifukwa cha zimene achita. Kumbukiraninso mneneri wamkazi Nowadiya ndi aneneri amene akhala akufuna kundiopseza.” 15 Ndipo khoma linatsirizidwa kumanga pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli. Linamangidwa pa masiku okwana 52. 16 Adani athu onse atamva izi, mitundu yonse ya anthu yozungulira inachita mantha ndi kuchita manyazi. Iwo anazindikira kuti ntchitoyo inachitika ndi thandizo la Mulungu wathu. 17 Komanso masiku amenewo anthu olemekezeka a ku Yuda ankalemberana naye makalata ambiri ndi Tobiyayo, 18 pakuti anthu ambiri a ku Yuda anali atalumbira kale kuti adzagwira naye ntchito popeza anali mkamwini wa Sekaniya mwana wa Ara, ndipo mwana wake Yehohanani anakwatira mwana wamkazi wa Mesulamu mwana wa Berekiya. 19 Kuwonjezera apo, anthu ankasimba za ntchito zake zabwino ine ndili pomwepo ndipo anakamuwululira mawu anga. Choncho Tobiyayo ankatumiza makalata ondiopseza.
In Other Versions
Nehemiah 6 in the ANGEFD
Nehemiah 6 in the ANTPNG2D
Nehemiah 6 in the AS21
Nehemiah 6 in the BAGH
Nehemiah 6 in the BBPNG
Nehemiah 6 in the BBT1E
Nehemiah 6 in the BDS
Nehemiah 6 in the BEV
Nehemiah 6 in the BHAD
Nehemiah 6 in the BIB
Nehemiah 6 in the BLPT
Nehemiah 6 in the BNT
Nehemiah 6 in the BNTABOOT
Nehemiah 6 in the BNTLV
Nehemiah 6 in the BOATCB
Nehemiah 6 in the BOATCB2
Nehemiah 6 in the BOBCV
Nehemiah 6 in the BOCNT
Nehemiah 6 in the BOECS
Nehemiah 6 in the BOHCB
Nehemiah 6 in the BOHCV
Nehemiah 6 in the BOHLNT
Nehemiah 6 in the BOHNTLTAL
Nehemiah 6 in the BOICB
Nehemiah 6 in the BOILNTAP
Nehemiah 6 in the BOITCV
Nehemiah 6 in the BOKCV
Nehemiah 6 in the BOKCV2
Nehemiah 6 in the BOKHWOG
Nehemiah 6 in the BOKSSV
Nehemiah 6 in the BOLCB
Nehemiah 6 in the BOLCB2
Nehemiah 6 in the BOMCV
Nehemiah 6 in the BONAV
Nehemiah 6 in the BONCB
Nehemiah 6 in the BONLT
Nehemiah 6 in the BONUT2
Nehemiah 6 in the BOPLNT
Nehemiah 6 in the BOSCB
Nehemiah 6 in the BOSNC
Nehemiah 6 in the BOTLNT
Nehemiah 6 in the BOVCB
Nehemiah 6 in the BOYCB
Nehemiah 6 in the BPBB
Nehemiah 6 in the BPH
Nehemiah 6 in the BSB
Nehemiah 6 in the CCB
Nehemiah 6 in the CUV
Nehemiah 6 in the CUVS
Nehemiah 6 in the DBT
Nehemiah 6 in the DGDNT
Nehemiah 6 in the DHNT
Nehemiah 6 in the DNT
Nehemiah 6 in the ELBE
Nehemiah 6 in the EMTV
Nehemiah 6 in the ESV
Nehemiah 6 in the FBV
Nehemiah 6 in the FEB
Nehemiah 6 in the GGMNT
Nehemiah 6 in the GNT
Nehemiah 6 in the HARY
Nehemiah 6 in the HNT
Nehemiah 6 in the IRVA
Nehemiah 6 in the IRVB
Nehemiah 6 in the IRVG
Nehemiah 6 in the IRVH
Nehemiah 6 in the IRVK
Nehemiah 6 in the IRVM
Nehemiah 6 in the IRVM2
Nehemiah 6 in the IRVO
Nehemiah 6 in the IRVP
Nehemiah 6 in the IRVT
Nehemiah 6 in the IRVT2
Nehemiah 6 in the IRVU
Nehemiah 6 in the ISVN
Nehemiah 6 in the JSNT
Nehemiah 6 in the KAPI
Nehemiah 6 in the KBT1ETNIK
Nehemiah 6 in the KBV
Nehemiah 6 in the KJV
Nehemiah 6 in the KNFD
Nehemiah 6 in the LBA
Nehemiah 6 in the LBLA
Nehemiah 6 in the LNT
Nehemiah 6 in the LSV
Nehemiah 6 in the MAAL
Nehemiah 6 in the MBV
Nehemiah 6 in the MBV2
Nehemiah 6 in the MHNT
Nehemiah 6 in the MKNFD
Nehemiah 6 in the MNG
Nehemiah 6 in the MNT
Nehemiah 6 in the MNT2
Nehemiah 6 in the MRS1T
Nehemiah 6 in the NAA
Nehemiah 6 in the NASB
Nehemiah 6 in the NBLA
Nehemiah 6 in the NBS
Nehemiah 6 in the NBVTP
Nehemiah 6 in the NET2
Nehemiah 6 in the NIV11
Nehemiah 6 in the NNT
Nehemiah 6 in the NNT2
Nehemiah 6 in the NNT3
Nehemiah 6 in the PDDPT
Nehemiah 6 in the PFNT
Nehemiah 6 in the RMNT
Nehemiah 6 in the SBIAS
Nehemiah 6 in the SBIBS
Nehemiah 6 in the SBIBS2
Nehemiah 6 in the SBICS
Nehemiah 6 in the SBIDS
Nehemiah 6 in the SBIGS
Nehemiah 6 in the SBIHS
Nehemiah 6 in the SBIIS
Nehemiah 6 in the SBIIS2
Nehemiah 6 in the SBIIS3
Nehemiah 6 in the SBIKS
Nehemiah 6 in the SBIKS2
Nehemiah 6 in the SBIMS
Nehemiah 6 in the SBIOS
Nehemiah 6 in the SBIPS
Nehemiah 6 in the SBISS
Nehemiah 6 in the SBITS
Nehemiah 6 in the SBITS2
Nehemiah 6 in the SBITS3
Nehemiah 6 in the SBITS4
Nehemiah 6 in the SBIUS
Nehemiah 6 in the SBIVS
Nehemiah 6 in the SBT
Nehemiah 6 in the SBT1E
Nehemiah 6 in the SCHL
Nehemiah 6 in the SNT
Nehemiah 6 in the SUSU
Nehemiah 6 in the SUSU2
Nehemiah 6 in the SYNO
Nehemiah 6 in the TBIAOTANT
Nehemiah 6 in the TBT1E
Nehemiah 6 in the TBT1E2
Nehemiah 6 in the TFTIP
Nehemiah 6 in the TFTU
Nehemiah 6 in the TGNTATF3T
Nehemiah 6 in the THAI
Nehemiah 6 in the TNFD
Nehemiah 6 in the TNT
Nehemiah 6 in the TNTIK
Nehemiah 6 in the TNTIL
Nehemiah 6 in the TNTIN
Nehemiah 6 in the TNTIP
Nehemiah 6 in the TNTIZ
Nehemiah 6 in the TOMA
Nehemiah 6 in the TTENT
Nehemiah 6 in the UBG
Nehemiah 6 in the UGV
Nehemiah 6 in the UGV2
Nehemiah 6 in the UGV3
Nehemiah 6 in the VBL
Nehemiah 6 in the VDCC
Nehemiah 6 in the YALU
Nehemiah 6 in the YAPE
Nehemiah 6 in the YBVTP
Nehemiah 6 in the ZBP