Numbers 15 (BOGWICC)

1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupatsanilo, 3 ndipo mukamadzapereka kwa Yehova, nsembe yotentha pa moto ya ngʼombe kapena nkhosa monga fungo lokoma kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena nsembe zina, nsembe yapadera chifukwa cha lumbiro kapena nsembe yoperekedwa mwaufulu kapenanso yoperekedwa pa chikondwerero, 4 munthu amene akubweretsa zopereka zake, azikapereka kwa Yehova chopereka chachakudya cholemera kilogalamu imodzi ya ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta wokwana lita imodzi. 5 Pamodzi ndi mwana wankhosa aliyense wa nsembe yopsereza kapena nsembe ina, muzikakonzanso lita imodzi la vinyo ngati chopereka cha chakumwa.’ ” 6 “Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, muzikakonzanso chopereka cha chakudya cholemera makilogalamu awiri a ufa wosalala, wosakaniza ndi mafuta okwanira lita imodzi ndi theka, 7 ndi vinyo wokwanira lita imodzi ndi theka ngati chopereka cha chakumwa. Muzikapereka monga nsembe yopereka fungo lokoma kwa Yehova. 8 “ ‘Pamene mukukonza mwana wangʼombe wamwamuna kuti akhale nsembe yopsereza kapena nsembe ina iliyonse: ya lumbiro lapadera kapena nsembe yachiyanjano kwa Yehova, 9 pamodzi ndi mwana wangʼombe wamwamunayo muzibweretsa nsembe yachakudya yolemera makilogalamu atatu a ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta okwana malita awiri. 10 Komanso muzibweretsa vinyo wokwanira malita awiri monga chopereka chachakumwa. Imeneyi idzakhala chopereka chotentha pa moto kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova. 11 Ngʼombe yayimuna iliyonse kapena nkhosa yayimuna iliyonse, mwana wankhosa aliyense kapena mbuzi yayingʼono, zizikonzedwa motere. 12 Ngakhale zingachuluke chotani, chitani izi kwa iliyonse ya nyamazo. 13 “ ‘Mbadwa iliyonse ya mu Israeli izichita zimenezi pamene ibweretsa nsembe yotentha pa moto kuti ikhale fungo lokoma kwa Yehova. 14 Ku mibado yanu yonse ya mʼtsogolo, pamene mlendo kapena wina aliyense wokhala pakati panu apereka chopereka chotentha pa moto kuti chikhale fungo lokoma kwa Yehova, azichita mofanana ndi momwe inu mumachitira. 15 Gulu lonse likhale ndi malamulo ofanana a inu kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli ndi lamulo lamuyaya kwa mibado imene ikubwera. Inuyo ndi mlendo mudzakhala wofanana pamaso pa Yehova. 16 Mudzakhale ndi malamulo ndi miyambo yofanana, inuyo ndi mlendo wokhala pakati panu.’ ” 17 Yehova anawuza Mose kuti, 18 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo unene kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukutengeraniko 19 ndipo mukakadya chakudya cha mʼdzikolo, mukapereke gawo lina kwa Yehova monga chopereka. 20 Pa buledi wanu woyamba, mukapereke mmodzi monga nsembe, ngati chopereka chochokera ku malo wopunthira tirigu. 21 Pa mibado yanu yonse muzidzapereka chopereka ichi kwa Yehova kuchokera ku zakudya zanu zoyamba za mʼnthaka. 22 “ ‘Ndipo ngati muchimwa mosadziwa posasunga ena mwa malamulo awa amene Yehova wapereka kwa Mose, 23 lina lililonse mwa malamulo a Yehova amene wapereka kwa inu kudzera mwa Mose, kuyambira tsiku limene Yehova anawapereka mpaka mibado ya mʼtsogolo, 24 ndipo ngati zimenezi zachitika osati mwadala ndipo gulu lonse silinadziwe, zikatero gulu lonselo lipereke mwana wangʼombe wamwamuna monga nsembe yopsereza kuti likhale fungo lokoma kwa Yehova pamodzinso ndi chopereka chachakudya ndi chopereka cha chakumwa ndi mbuzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo potsata zimene zinalamulidwa. 25 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimo a gulu lonse la Aisraeli, ndipo adzakhululukidwa, pakuti linali tchimo lochita mosadziwa. Ndipo chifukwa cha tchimo lawolo, abweretse kwa Yehova nsembe yotentha pa moto ndi nsembe yopepesera machimo. 26 Gulu lonse la Aisraeli ndi alendo okhala pakati pawo adzakhululukidwa chifukwa anthu onsewo anachimwa mosadziwa. 27 “ ‘Koma ngati munthu mmodzi achimwa mosadziwa, ayenera kubweretsa mbuzi yayikazi ya chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopepesera machimo. 28 Wansembe apereke nsembe yopepesera machimowo pamaso pa Yehova chifukwa cha munthu yemwe anachimwa mosadziwayo. Nsembe yopepesera tchimo lakelo ikaperekedwa, munthuyo adzakhululukidwa. 29 Lamulo lomweli ligwiritsidwe ntchito kwa aliyense wochimwa mosadziwa, kaya ndi mbadwa ya mu Israeli kapena mlendo. 30 “ ‘Koma aliyense amene achimwa mwadala, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, nachitira chipongwe Yehova, ameneyo achotsedwe ndithu pakati pa anthu ake. 31 Popeza wanyoza mawu a Yehova ndi kuphwanya malamulo ake. Munthu ameneyo achotsedwe ndithu, kuchimwa kwake kudzakhala pa iyeyo.’ ” 32 Aisraeli ali mʼchipululu, munthu wina anapezeka akutola nkhuni tsiku la Sabata. 33 Amene anamupeza akutola nkhunizo anabwera naye kwa Mose ndi Aaroni ndi kwa gulu lonse 34 ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa sankadziwa choti achite naye. 35 Pamenepo Yehova anawuza Mose kuti, “Munthu ameneyu ayenera kuphedwa. Gulu lonse liyenera kumugenda ndi miyala kunja kwa msasa.” 36 Choncho gululo linamutengera kunja kwa msasa ndi kumupha pomugenda ndi miyala, monga momwe Yehova analamulira Mose. 37 Yehova anawuza Mose kuti, 38 “Yankhula ndi Aisraeli ndipo uwawuze kuti, ‘Pa mibado yanu yonse muzisokerera mphonje pa ngodya za zovala zanu ndipo pa ngodya ya mphonje iliyonse azisokererapo chingwe chobiriwira. 39 Mudzakhala ndi mphonje zimenezi kuti mukaziona muzikakumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwamvera kuti musamatsatenso zilakolako za mʼmitima mwanu ndi za maso anu. 40 Motero mudzakumbukira kumvera malamulo anga ndipo mudzakhala opatulikira a Mulungu wanu. 41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto kuti ndikhale Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ ”

In Other Versions

Numbers 15 in the ANGEFD

Numbers 15 in the ANTPNG2D

Numbers 15 in the AS21

Numbers 15 in the BAGH

Numbers 15 in the BBPNG

Numbers 15 in the BBT1E

Numbers 15 in the BDS

Numbers 15 in the BEV

Numbers 15 in the BHAD

Numbers 15 in the BIB

Numbers 15 in the BLPT

Numbers 15 in the BNT

Numbers 15 in the BNTABOOT

Numbers 15 in the BNTLV

Numbers 15 in the BOATCB

Numbers 15 in the BOATCB2

Numbers 15 in the BOBCV

Numbers 15 in the BOCNT

Numbers 15 in the BOECS

Numbers 15 in the BOHCB

Numbers 15 in the BOHCV

Numbers 15 in the BOHLNT

Numbers 15 in the BOHNTLTAL

Numbers 15 in the BOICB

Numbers 15 in the BOILNTAP

Numbers 15 in the BOITCV

Numbers 15 in the BOKCV

Numbers 15 in the BOKCV2

Numbers 15 in the BOKHWOG

Numbers 15 in the BOKSSV

Numbers 15 in the BOLCB

Numbers 15 in the BOLCB2

Numbers 15 in the BOMCV

Numbers 15 in the BONAV

Numbers 15 in the BONCB

Numbers 15 in the BONLT

Numbers 15 in the BONUT2

Numbers 15 in the BOPLNT

Numbers 15 in the BOSCB

Numbers 15 in the BOSNC

Numbers 15 in the BOTLNT

Numbers 15 in the BOVCB

Numbers 15 in the BOYCB

Numbers 15 in the BPBB

Numbers 15 in the BPH

Numbers 15 in the BSB

Numbers 15 in the CCB

Numbers 15 in the CUV

Numbers 15 in the CUVS

Numbers 15 in the DBT

Numbers 15 in the DGDNT

Numbers 15 in the DHNT

Numbers 15 in the DNT

Numbers 15 in the ELBE

Numbers 15 in the EMTV

Numbers 15 in the ESV

Numbers 15 in the FBV

Numbers 15 in the FEB

Numbers 15 in the GGMNT

Numbers 15 in the GNT

Numbers 15 in the HARY

Numbers 15 in the HNT

Numbers 15 in the IRVA

Numbers 15 in the IRVB

Numbers 15 in the IRVG

Numbers 15 in the IRVH

Numbers 15 in the IRVK

Numbers 15 in the IRVM

Numbers 15 in the IRVM2

Numbers 15 in the IRVO

Numbers 15 in the IRVP

Numbers 15 in the IRVT

Numbers 15 in the IRVT2

Numbers 15 in the IRVU

Numbers 15 in the ISVN

Numbers 15 in the JSNT

Numbers 15 in the KAPI

Numbers 15 in the KBT1ETNIK

Numbers 15 in the KBV

Numbers 15 in the KJV

Numbers 15 in the KNFD

Numbers 15 in the LBA

Numbers 15 in the LBLA

Numbers 15 in the LNT

Numbers 15 in the LSV

Numbers 15 in the MAAL

Numbers 15 in the MBV

Numbers 15 in the MBV2

Numbers 15 in the MHNT

Numbers 15 in the MKNFD

Numbers 15 in the MNG

Numbers 15 in the MNT

Numbers 15 in the MNT2

Numbers 15 in the MRS1T

Numbers 15 in the NAA

Numbers 15 in the NASB

Numbers 15 in the NBLA

Numbers 15 in the NBS

Numbers 15 in the NBVTP

Numbers 15 in the NET2

Numbers 15 in the NIV11

Numbers 15 in the NNT

Numbers 15 in the NNT2

Numbers 15 in the NNT3

Numbers 15 in the PDDPT

Numbers 15 in the PFNT

Numbers 15 in the RMNT

Numbers 15 in the SBIAS

Numbers 15 in the SBIBS

Numbers 15 in the SBIBS2

Numbers 15 in the SBICS

Numbers 15 in the SBIDS

Numbers 15 in the SBIGS

Numbers 15 in the SBIHS

Numbers 15 in the SBIIS

Numbers 15 in the SBIIS2

Numbers 15 in the SBIIS3

Numbers 15 in the SBIKS

Numbers 15 in the SBIKS2

Numbers 15 in the SBIMS

Numbers 15 in the SBIOS

Numbers 15 in the SBIPS

Numbers 15 in the SBISS

Numbers 15 in the SBITS

Numbers 15 in the SBITS2

Numbers 15 in the SBITS3

Numbers 15 in the SBITS4

Numbers 15 in the SBIUS

Numbers 15 in the SBIVS

Numbers 15 in the SBT

Numbers 15 in the SBT1E

Numbers 15 in the SCHL

Numbers 15 in the SNT

Numbers 15 in the SUSU

Numbers 15 in the SUSU2

Numbers 15 in the SYNO

Numbers 15 in the TBIAOTANT

Numbers 15 in the TBT1E

Numbers 15 in the TBT1E2

Numbers 15 in the TFTIP

Numbers 15 in the TFTU

Numbers 15 in the TGNTATF3T

Numbers 15 in the THAI

Numbers 15 in the TNFD

Numbers 15 in the TNT

Numbers 15 in the TNTIK

Numbers 15 in the TNTIL

Numbers 15 in the TNTIN

Numbers 15 in the TNTIP

Numbers 15 in the TNTIZ

Numbers 15 in the TOMA

Numbers 15 in the TTENT

Numbers 15 in the UBG

Numbers 15 in the UGV

Numbers 15 in the UGV2

Numbers 15 in the UGV3

Numbers 15 in the VBL

Numbers 15 in the VDCC

Numbers 15 in the YALU

Numbers 15 in the YAPE

Numbers 15 in the YBVTP

Numbers 15 in the ZBP