Numbers 30 (BOGWICC)
1 Mose anawuza Aisraeli onse zonse zimene Yehova anamulamula. Iye anati, “Zimene Yehova walamula ndi izi: 2 Munthu wamwamuna ngati walonjeza kwa Yehova kapena kulumbira kuti adzachita zimene walumbirazo, asaphwanye mawuwo koma ayenera kuchita chilichonse chimene wanena. 3 “Pamene munthu wamkazi amene akukhalabe mʼnyumba ya abambo ake alumbira kwa Yehova kuti adzachita zimene walonjeza pa ubwana wake, 4 abambo ake namva kulumbira kwakeko kapena kulonjeza kwake kuti adzachitadi, ndipo abambo akewo wosayankhula kanthu, mkaziyo achitedi zomwe analumbirazo. Ayenera kudzachita zonse zimene walonjeza zija. 5 Koma ngati abambo akewo amva kulumbira kwake ndi kumukaniza, palibe lamulo lomukakamiza mkaziyo kuchita zimene walonjeza. Yehova adzamukhululukira chifukwa abambo ake anamukaniza. 6 “Ngati akwatiwa atalumbira kale kapena ngati alonjeza mofulumira ndi pakamwa pake, 7 mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma wosanenapo kanthu, mkaziyo achitedi zomwe walumbirazo. Achite ndithu zomwe walonjeza zija. 8 Koma ngati mwamuna wake amuletsa atamva kulumbira kwakeko, pamenepo amumasula mayiyo ku zimene analumbira komanso ku zimene analonjeza mosaganiza bwinozo ndipo Yehova adzamukhululukira. 9 “Mayi wamasiye kapena wosiyidwa ukwati akalumbira kapena kulonjeza kuti adzachita kanthu kalikonse, ayenera kukachitadi. 10 “Koma ngati mayi wokwatiwa alumbira nalonjeza kuti adzachitadi zimene walonjeza, 11 mwamuna wake ndi kumva kulumbira kwakeko koma osayankhulapo kanthu, osamuletsa, ayenera kuchitadi zonse zimene walumbira ndi zonse zimene walonjeza. 12 Koma ngati mwamuna wake amva ndi kumuletsa kuti asachite zomwe walumbirazo, palibe lamulo lomukakamiza mayiyo kuchita zomwe walumbirazo kapenanso zimene walonjeza. Popeza mwamuna wake wamuletsa, Yehova adzamukhululukira mayiyo. 13 Mwamuna wake ali ndi mphamvu zovomereza kapena kukana zimene mayiyo walumbira kapena zimene walonjeza zokhudza kudzilanga yekha. 14 Ndipo ngati mmawa mwake ndi masiku otsatira mwamuna wake sanenapo kanthu atamva zimenezi, mayiyo achitedi zimene walumbira kapena zimene walonjeza. Mwamunayo wavomereza zimenezo, chifukwa sanamuwuze kanthu mayiyo pa tsiku limene anamva akulonjeza kapena kulumbira. 15 Koma ngati mwamunayo amukaniza patapita kanthawi atazimva kale, iyeyo ndiye wochimwa mʼmalo mwa mayiyo.” 16 Awa ndiwo malamulo amene Yehova analamula Mose za mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso abambo ndi mwana wawo wamkazi amene akanali mtsikana wokhalabe mʼnyumba ya abambo akewo.
In Other Versions
Numbers 30 in the ANGEFD
Numbers 30 in the ANTPNG2D
Numbers 30 in the AS21
Numbers 30 in the BAGH
Numbers 30 in the BBPNG
Numbers 30 in the BBT1E
Numbers 30 in the BDS
Numbers 30 in the BEV
Numbers 30 in the BHAD
Numbers 30 in the BIB
Numbers 30 in the BLPT
Numbers 30 in the BNT
Numbers 30 in the BNTABOOT
Numbers 30 in the BNTLV
Numbers 30 in the BOATCB
Numbers 30 in the BOATCB2
Numbers 30 in the BOBCV
Numbers 30 in the BOCNT
Numbers 30 in the BOECS
Numbers 30 in the BOHCB
Numbers 30 in the BOHCV
Numbers 30 in the BOHLNT
Numbers 30 in the BOHNTLTAL
Numbers 30 in the BOICB
Numbers 30 in the BOILNTAP
Numbers 30 in the BOITCV
Numbers 30 in the BOKCV
Numbers 30 in the BOKCV2
Numbers 30 in the BOKHWOG
Numbers 30 in the BOKSSV
Numbers 30 in the BOLCB
Numbers 30 in the BOLCB2
Numbers 30 in the BOMCV
Numbers 30 in the BONAV
Numbers 30 in the BONCB
Numbers 30 in the BONLT
Numbers 30 in the BONUT2
Numbers 30 in the BOPLNT
Numbers 30 in the BOSCB
Numbers 30 in the BOSNC
Numbers 30 in the BOTLNT
Numbers 30 in the BOVCB
Numbers 30 in the BOYCB
Numbers 30 in the BPBB
Numbers 30 in the BPH
Numbers 30 in the BSB
Numbers 30 in the CCB
Numbers 30 in the CUV
Numbers 30 in the CUVS
Numbers 30 in the DBT
Numbers 30 in the DGDNT
Numbers 30 in the DHNT
Numbers 30 in the DNT
Numbers 30 in the ELBE
Numbers 30 in the EMTV
Numbers 30 in the ESV
Numbers 30 in the FBV
Numbers 30 in the FEB
Numbers 30 in the GGMNT
Numbers 30 in the GNT
Numbers 30 in the HARY
Numbers 30 in the HNT
Numbers 30 in the IRVA
Numbers 30 in the IRVB
Numbers 30 in the IRVG
Numbers 30 in the IRVH
Numbers 30 in the IRVK
Numbers 30 in the IRVM
Numbers 30 in the IRVM2
Numbers 30 in the IRVO
Numbers 30 in the IRVP
Numbers 30 in the IRVT
Numbers 30 in the IRVT2
Numbers 30 in the IRVU
Numbers 30 in the ISVN
Numbers 30 in the JSNT
Numbers 30 in the KAPI
Numbers 30 in the KBT1ETNIK
Numbers 30 in the KBV
Numbers 30 in the KJV
Numbers 30 in the KNFD
Numbers 30 in the LBA
Numbers 30 in the LBLA
Numbers 30 in the LNT
Numbers 30 in the LSV
Numbers 30 in the MAAL
Numbers 30 in the MBV
Numbers 30 in the MBV2
Numbers 30 in the MHNT
Numbers 30 in the MKNFD
Numbers 30 in the MNG
Numbers 30 in the MNT
Numbers 30 in the MNT2
Numbers 30 in the MRS1T
Numbers 30 in the NAA
Numbers 30 in the NASB
Numbers 30 in the NBLA
Numbers 30 in the NBS
Numbers 30 in the NBVTP
Numbers 30 in the NET2
Numbers 30 in the NIV11
Numbers 30 in the NNT
Numbers 30 in the NNT2
Numbers 30 in the NNT3
Numbers 30 in the PDDPT
Numbers 30 in the PFNT
Numbers 30 in the RMNT
Numbers 30 in the SBIAS
Numbers 30 in the SBIBS
Numbers 30 in the SBIBS2
Numbers 30 in the SBICS
Numbers 30 in the SBIDS
Numbers 30 in the SBIGS
Numbers 30 in the SBIHS
Numbers 30 in the SBIIS
Numbers 30 in the SBIIS2
Numbers 30 in the SBIIS3
Numbers 30 in the SBIKS
Numbers 30 in the SBIKS2
Numbers 30 in the SBIMS
Numbers 30 in the SBIOS
Numbers 30 in the SBIPS
Numbers 30 in the SBISS
Numbers 30 in the SBITS
Numbers 30 in the SBITS2
Numbers 30 in the SBITS3
Numbers 30 in the SBITS4
Numbers 30 in the SBIUS
Numbers 30 in the SBIVS
Numbers 30 in the SBT
Numbers 30 in the SBT1E
Numbers 30 in the SCHL
Numbers 30 in the SNT
Numbers 30 in the SUSU
Numbers 30 in the SUSU2
Numbers 30 in the SYNO
Numbers 30 in the TBIAOTANT
Numbers 30 in the TBT1E
Numbers 30 in the TBT1E2
Numbers 30 in the TFTIP
Numbers 30 in the TFTU
Numbers 30 in the TGNTATF3T
Numbers 30 in the THAI
Numbers 30 in the TNFD
Numbers 30 in the TNT
Numbers 30 in the TNTIK
Numbers 30 in the TNTIL
Numbers 30 in the TNTIN
Numbers 30 in the TNTIP
Numbers 30 in the TNTIZ
Numbers 30 in the TOMA
Numbers 30 in the TTENT
Numbers 30 in the UBG
Numbers 30 in the UGV
Numbers 30 in the UGV2
Numbers 30 in the UGV3
Numbers 30 in the VBL
Numbers 30 in the VDCC
Numbers 30 in the YALU
Numbers 30 in the YAPE
Numbers 30 in the YBVTP
Numbers 30 in the ZBP