Numbers 32 (BOGWICC)

1 Arubeni ndi Agadi amene anali ndi ngʼombe zambiri ndi ziweto zina anaona dziko la Yazeri ndi la Giliyadi kuti linali labwino kwa ziwetozo. 2 Choncho Arubeni ndi Agadi anapita kwa Mose ndi kwa wansembe Eliezara ndi kwa atsogoleri a anthu ndi kunena kuti, 3 “Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni, Eleali, Sebamu, Nebo ndi Beoni, 4 dziko lomwe Yehova anagonjetsa pamaso pa Aisraeli, ndiwo malo woyenera ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto. 5 Iwo anati, ‘Ngati tapeza ufulu pamaso panu atumiki anufe, mutipatse dziko limeneli kuti likhale lathu. Tisawoloke nanu Yorodani.’ ” 6 Ndipo Mose anati kwa Agadi ndi Arubeni, “Kodi anthu a mtundu wanu apite ku nkhondo inu mutangokhala kuno? 7 Chifukwa chiyani mukufowoketsa Aisraeli kupita mʼdziko limene Yehova wawapatsa? 8 Izi ndi zimene makolo anu anachita pamene ndinawatuma kuchokera ku Kadesi kukaona dzikolo. 9 Atapita ku chigwa cha Esikolo, ndi kuliona dzikolo, anafowoketsa Aisraeli kuti asalowe mʼdziko limene Yehova anawapatsa. 10 Yehova anakwiya tsiku limenelo ndipo analumbira kuti, 11 ‘Chifukwa sananditsatire ndi mtima wonse, palibe ndi mmodzi yemwe mwa amuna a zaka makumi awiri kapena kuposa pamenepo, amene anachokera ku Igupto, amene adzaone dziko limene ndinalonjeza mwa lumbiro kwa Abrahamu, Isake ndi Yakobo. 12 Palibe ndi mmodzi yemwe kupatula Kalebe mwana wa Yefune, Mkeni, ndi Yoswa mwana wa Nuni chifukwa anatsatira Yehova ndi mtima wonse.’ 13 Yehova anakwiyira Aisraeli kwambiri ndipo anawachititsa kuyenda mʼchipululu zaka makumi anayi, mpaka mʼbado wonse wa anthu amene anachita choyipa pamaso pake unatha. 14 “Ndipo onani tsopano, inu mʼbado wochimwa, mwalowa mʼmalo mwa makolo anu ndipo mwachititsa kuti Yehova akwiyire Israeli kwambiri. 15 Ngati muleka kumutsata, Iye adzawasiyiranso anthu onsewa mʼchipululu ndipo mudzawonongetsa anthu onsewa.” 16 Ndipo iwo anabwera kwa Mose namuwuza kuti, “Ife tikufuna kumanga makola a ziweto zathu kuno ndi mizinda yokhalamo akazi athu ndi ana athu. 17 Koma ndife okonzeka kutenga zida za nkhondo ndi kupita pamodzi ndi Aisraeli mpaka titakawafikitsa ku malo awo. Panopa, akazi ndi ana athu akhala mʼmizinda yotetezedwa, kuwateteza kwa anthu okhala mʼdzikoli. 18 Sitidzabwerera ku midzi yathu mpaka Mwisraeli aliyense atalandira cholowa chake. 19 Sitidzalandira cholowa chilichonse pamodzi nawo ku tsidya lina la Yorodani, chifukwa cholowa chathu tachipezera ku tsidya lino la kummawa kwa Yorodani.” 20 Tsono Mose anati kwa anthuwo, “Ngati inu mudzachita zimenezi, kutenga zida zankhondo pamaso pa Yehova kuti muchite nkhondo, 21 ndipo ngati nonsenu mudzapita ndi zida kuwoloka Yorodani pamaso pa Yehova mpaka atachotsa adani ake pamaso pake, 22 dzikolo nʼkugonja pamaso pa Yehova, mudzabwera ndi kukhala mfulu pamaso pa Yehova ndi Aisraeli. Ndipo dziko lino lidzakhala lanu pamaso pa Yehova. 23 “Koma mukalephera kuchita izi, mudzakhala mukuchimwira Yehova. Ndipo dziwani kuti tchimo lanu lidzakupezani. 24 Amangireni akazi ndi ana anu mizinda, mangani makola a ziweto zanu, koma chitani zomwe mwalonjeza.” 25 Agadi ndi Arubeni anati kwa Mose, “Ife antchito anu tidzachita monga mbuye wathu mwalamulira. 26 Ana ndi akazi athu, ziweto zathu zina ndi ngʼombe zidzatsala kuno ku mizinda ya Giliyadi, 27 koma antchito anufe, mwamuna aliyense amene ali ndi chida cha nkhondo, adzawoloka kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova monga mbuye wathu wanenera.” 28 Choncho Mose anapereka malamulo awa kwa wansembe Eliezara, kwa Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa akulu a mafuko a Aisraeli. 29 Mose anawawuza kuti, ngati Agadi ndi Arubeni, mwamuna aliyense wokonzekera nkhondo, awoloka Yorodani pamodzi ndi inu pamaso pa Yehova, ndipo dzikolo nʼkugonjetsedwa pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kukhala lawo. 30 Koma ngati sawoloka pamodzi nanu ndi zida zankhondo, ayenera kulandira cholowa chawo pamodzi ndi inu ku Kanaani. 31 Agadi ndi Arubeni anayankha kuti, “Antchito anu adzachita zimene Yehova wanena. 32 Tidzawoloka pamaso pa Yehova ndipo tidzalowa mu Kanaani ndi zida zankhondo, koma cholowa chathu chidzakhala ku tsidya lino la Yorodani.” 33 Choncho Mose anapatsa Agadi, Arubeni ndi theka la fuko la Manase mwana wa Yosefe dziko la Sihoni mfumu ya Aamori ndi dziko la Ogi, mfumu ya ku Basani, dziko lonse, mizinda yake ndi midzi yowazungulira. 34 Agadi anamanga Diboni, Ataroti, Aroeri, 35 Atiroti-Sofani, Yazeri, Yogibeha, 36 Beti-Nimira ndi Beti-Harani mizinda ya malinga. Anamanganso makola a ziweto zawo. 37 Ndipo Arubeni anamanga Hesiboni, Eleali, Kiriataimu, 38 Nebo ndi Baala-Meoni (mayina awa anasinthidwa) ndi Sibima. Anapereka mayina ku mizinda ina yomwe anamangayo. 39 Zidzukulu za Makiri mwana wa Manase zinapita ku Giliyadi kulanda mzindawo ndi kuthamangitsira kunja Aamori omwe anali kumeneko. 40 Tsono Mose anapereka Giliyadi kwa Amakiri, ana a Manase, ndipo anakhala kumeneko. 41 Yairi, mwana wa Manase analanda midzi yambiri ya Giliyadi ndi kuyitcha kuti Havoti-Yairi. 42 Ndipo Noba analanda Kenati ndi midzi yozungulira ndi kuyitcha Noba, kutengera dzina la iye mwini.

In Other Versions

Numbers 32 in the ANGEFD

Numbers 32 in the ANTPNG2D

Numbers 32 in the AS21

Numbers 32 in the BAGH

Numbers 32 in the BBPNG

Numbers 32 in the BBT1E

Numbers 32 in the BDS

Numbers 32 in the BEV

Numbers 32 in the BHAD

Numbers 32 in the BIB

Numbers 32 in the BLPT

Numbers 32 in the BNT

Numbers 32 in the BNTABOOT

Numbers 32 in the BNTLV

Numbers 32 in the BOATCB

Numbers 32 in the BOATCB2

Numbers 32 in the BOBCV

Numbers 32 in the BOCNT

Numbers 32 in the BOECS

Numbers 32 in the BOHCB

Numbers 32 in the BOHCV

Numbers 32 in the BOHLNT

Numbers 32 in the BOHNTLTAL

Numbers 32 in the BOICB

Numbers 32 in the BOILNTAP

Numbers 32 in the BOITCV

Numbers 32 in the BOKCV

Numbers 32 in the BOKCV2

Numbers 32 in the BOKHWOG

Numbers 32 in the BOKSSV

Numbers 32 in the BOLCB

Numbers 32 in the BOLCB2

Numbers 32 in the BOMCV

Numbers 32 in the BONAV

Numbers 32 in the BONCB

Numbers 32 in the BONLT

Numbers 32 in the BONUT2

Numbers 32 in the BOPLNT

Numbers 32 in the BOSCB

Numbers 32 in the BOSNC

Numbers 32 in the BOTLNT

Numbers 32 in the BOVCB

Numbers 32 in the BOYCB

Numbers 32 in the BPBB

Numbers 32 in the BPH

Numbers 32 in the BSB

Numbers 32 in the CCB

Numbers 32 in the CUV

Numbers 32 in the CUVS

Numbers 32 in the DBT

Numbers 32 in the DGDNT

Numbers 32 in the DHNT

Numbers 32 in the DNT

Numbers 32 in the ELBE

Numbers 32 in the EMTV

Numbers 32 in the ESV

Numbers 32 in the FBV

Numbers 32 in the FEB

Numbers 32 in the GGMNT

Numbers 32 in the GNT

Numbers 32 in the HARY

Numbers 32 in the HNT

Numbers 32 in the IRVA

Numbers 32 in the IRVB

Numbers 32 in the IRVG

Numbers 32 in the IRVH

Numbers 32 in the IRVK

Numbers 32 in the IRVM

Numbers 32 in the IRVM2

Numbers 32 in the IRVO

Numbers 32 in the IRVP

Numbers 32 in the IRVT

Numbers 32 in the IRVT2

Numbers 32 in the IRVU

Numbers 32 in the ISVN

Numbers 32 in the JSNT

Numbers 32 in the KAPI

Numbers 32 in the KBT1ETNIK

Numbers 32 in the KBV

Numbers 32 in the KJV

Numbers 32 in the KNFD

Numbers 32 in the LBA

Numbers 32 in the LBLA

Numbers 32 in the LNT

Numbers 32 in the LSV

Numbers 32 in the MAAL

Numbers 32 in the MBV

Numbers 32 in the MBV2

Numbers 32 in the MHNT

Numbers 32 in the MKNFD

Numbers 32 in the MNG

Numbers 32 in the MNT

Numbers 32 in the MNT2

Numbers 32 in the MRS1T

Numbers 32 in the NAA

Numbers 32 in the NASB

Numbers 32 in the NBLA

Numbers 32 in the NBS

Numbers 32 in the NBVTP

Numbers 32 in the NET2

Numbers 32 in the NIV11

Numbers 32 in the NNT

Numbers 32 in the NNT2

Numbers 32 in the NNT3

Numbers 32 in the PDDPT

Numbers 32 in the PFNT

Numbers 32 in the RMNT

Numbers 32 in the SBIAS

Numbers 32 in the SBIBS

Numbers 32 in the SBIBS2

Numbers 32 in the SBICS

Numbers 32 in the SBIDS

Numbers 32 in the SBIGS

Numbers 32 in the SBIHS

Numbers 32 in the SBIIS

Numbers 32 in the SBIIS2

Numbers 32 in the SBIIS3

Numbers 32 in the SBIKS

Numbers 32 in the SBIKS2

Numbers 32 in the SBIMS

Numbers 32 in the SBIOS

Numbers 32 in the SBIPS

Numbers 32 in the SBISS

Numbers 32 in the SBITS

Numbers 32 in the SBITS2

Numbers 32 in the SBITS3

Numbers 32 in the SBITS4

Numbers 32 in the SBIUS

Numbers 32 in the SBIVS

Numbers 32 in the SBT

Numbers 32 in the SBT1E

Numbers 32 in the SCHL

Numbers 32 in the SNT

Numbers 32 in the SUSU

Numbers 32 in the SUSU2

Numbers 32 in the SYNO

Numbers 32 in the TBIAOTANT

Numbers 32 in the TBT1E

Numbers 32 in the TBT1E2

Numbers 32 in the TFTIP

Numbers 32 in the TFTU

Numbers 32 in the TGNTATF3T

Numbers 32 in the THAI

Numbers 32 in the TNFD

Numbers 32 in the TNT

Numbers 32 in the TNTIK

Numbers 32 in the TNTIL

Numbers 32 in the TNTIN

Numbers 32 in the TNTIP

Numbers 32 in the TNTIZ

Numbers 32 in the TOMA

Numbers 32 in the TTENT

Numbers 32 in the UBG

Numbers 32 in the UGV

Numbers 32 in the UGV2

Numbers 32 in the UGV3

Numbers 32 in the VBL

Numbers 32 in the VDCC

Numbers 32 in the YALU

Numbers 32 in the YAPE

Numbers 32 in the YBVTP

Numbers 32 in the ZBP