Proverbs 26 (BOGWICC)

1 Ngati chisanu choti mbee nthawi yachilimwe kapena mvula nthawi yokolola,ndi momwe zilili ndi ulemu wowulandira chitsiru. 2 Ngati timba wokhalira kuwuluka kapena namzeze wokhalira kuzungulirazungulira,ndi mmenenso limachitira temberero lopanda chifukwa, silichitika. 3 Mkwapulo ndi wokwapulira kavalo, chitsulo ndi cha mʼkamwa mwa bulu,choncho ndodo ndi yoyenera ku msana wa chitsiru. 4 Usayankhe chitsiru monga mwa uchitsiru wake,kuopa kuti ungadzakhale ngati chitsirucho. 5 Koma nthawi zina umuyankhe monga mwa uchitsiru wake,kuopa kuti angamadziyese yekha wanzeru. 6 Kutuma chitsiru kuti akapereke uthengakuli ngati kudzidula mapazi ndipo kumakuyitanira mavuto. 7 Monga miyendo ya munthu wolumala imene ilibe mphamvundi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru. 8 Kupereka ulemu kwa chitsiruzili ngati kukulunga mwala mʼlegeni. 9 Monga umachitira mtengo waminga wobaya mʼdzanja la chidakwandi mmene ulili mwambi mʼkamwa mwa chitsiru. 10 Munthu amene amalemba ntchito chitsiru chongoyendayenda,ali ngati woponya mivi amene angolasa anthu chilaselase. 11 Chitsiru chimene chimabwerezabwereza uchitsiru wakechili ngati galu amene amabwerera ku masanzi ake. 12 Munthu wa uchitsiru aliko bwino popeza pali chiyembekezokuposana ndi munthu amene amadziyesa yekha kuti ndi wanzeru. 13 Munthu waulesi amati, “Mu msewu muli mkango,mkango woopsa ukuyendayenda mʼmisewu!” 14 Monga chitseko chimapita uku ndi uku pa zolumikizira zake,momwemonso munthu waulesi amangotembenukatembenuka pa bedi lake. 15 Munthu waulesi akapisa dzanja lake mu mʼbale;zimamutopetsa kuti alifikitse pakamwa pake. 16 Munthu waulesi amadziyesa yekha wanzerukuposa anthu asanu ndi awiri amene amayankha mochenjera. 17 Munthu wongolowera mikangano imene si yakeali ngati munthu wogwira makutu a galu wongodziyendera. 18 Monga munthu wamisala ameneakuponya sakali zamoto kapena mivi yoopsa, 19 ndi momwe alili munthu wonamiza mnzake,amene amati, “Ndimangoseka chabe!” 20 Pakasowa nkhuni, moto umazima;chomwechonso pakasowa anthu amiseche mkangano umatha. 21 Monga alili makala pa moto wonyeka kapena mmene zimachitira nkhuni pa moto,ndi mmene alili munthu wolongolola poyambitsa mikangano. 22 Mawu a munthu wamiseche ali ngati chakudya chokoma;chimene chimatsikira mʼmimba mwa munthu. 23 Monga mmene chiziro chimakutira chiwiya chadothindi mmene mawu oshashalika amabisira mtima woyipa. 24 Munthu wachidani amayankhula zabwinopamene mu mtima mwake muli chinyengo. 25 Ngakhale wotereyu mawu ake ali okoma, koma usamukhulupirire,pakuti mu mtima mwake mwadzaza zonyansa. 26 Ngakhale amabisa chidani mochenjera,koma kuyipa kwakeko kudzaonekera poyera pa gulu la anthu. 27 Ngati munthu akumba dzenje, adzagweramo yekha;ngati munthu agubuduza mwala, udzamupsinja iye mwini. 28 Munthu wonama amadana ndi amene anawapweteka,ndipo pakamwa poshashalika pamabweretsa chiwonongeko.

In Other Versions

Proverbs 26 in the ANGEFD

Proverbs 26 in the ANTPNG2D

Proverbs 26 in the AS21

Proverbs 26 in the BAGH

Proverbs 26 in the BBPNG

Proverbs 26 in the BBT1E

Proverbs 26 in the BDS

Proverbs 26 in the BEV

Proverbs 26 in the BHAD

Proverbs 26 in the BIB

Proverbs 26 in the BLPT

Proverbs 26 in the BNT

Proverbs 26 in the BNTABOOT

Proverbs 26 in the BNTLV

Proverbs 26 in the BOATCB

Proverbs 26 in the BOATCB2

Proverbs 26 in the BOBCV

Proverbs 26 in the BOCNT

Proverbs 26 in the BOECS

Proverbs 26 in the BOHCB

Proverbs 26 in the BOHCV

Proverbs 26 in the BOHLNT

Proverbs 26 in the BOHNTLTAL

Proverbs 26 in the BOICB

Proverbs 26 in the BOILNTAP

Proverbs 26 in the BOITCV

Proverbs 26 in the BOKCV

Proverbs 26 in the BOKCV2

Proverbs 26 in the BOKHWOG

Proverbs 26 in the BOKSSV

Proverbs 26 in the BOLCB

Proverbs 26 in the BOLCB2

Proverbs 26 in the BOMCV

Proverbs 26 in the BONAV

Proverbs 26 in the BONCB

Proverbs 26 in the BONLT

Proverbs 26 in the BONUT2

Proverbs 26 in the BOPLNT

Proverbs 26 in the BOSCB

Proverbs 26 in the BOSNC

Proverbs 26 in the BOTLNT

Proverbs 26 in the BOVCB

Proverbs 26 in the BOYCB

Proverbs 26 in the BPBB

Proverbs 26 in the BPH

Proverbs 26 in the BSB

Proverbs 26 in the CCB

Proverbs 26 in the CUV

Proverbs 26 in the CUVS

Proverbs 26 in the DBT

Proverbs 26 in the DGDNT

Proverbs 26 in the DHNT

Proverbs 26 in the DNT

Proverbs 26 in the ELBE

Proverbs 26 in the EMTV

Proverbs 26 in the ESV

Proverbs 26 in the FBV

Proverbs 26 in the FEB

Proverbs 26 in the GGMNT

Proverbs 26 in the GNT

Proverbs 26 in the HARY

Proverbs 26 in the HNT

Proverbs 26 in the IRVA

Proverbs 26 in the IRVB

Proverbs 26 in the IRVG

Proverbs 26 in the IRVH

Proverbs 26 in the IRVK

Proverbs 26 in the IRVM

Proverbs 26 in the IRVM2

Proverbs 26 in the IRVO

Proverbs 26 in the IRVP

Proverbs 26 in the IRVT

Proverbs 26 in the IRVT2

Proverbs 26 in the IRVU

Proverbs 26 in the ISVN

Proverbs 26 in the JSNT

Proverbs 26 in the KAPI

Proverbs 26 in the KBT1ETNIK

Proverbs 26 in the KBV

Proverbs 26 in the KJV

Proverbs 26 in the KNFD

Proverbs 26 in the LBA

Proverbs 26 in the LBLA

Proverbs 26 in the LNT

Proverbs 26 in the LSV

Proverbs 26 in the MAAL

Proverbs 26 in the MBV

Proverbs 26 in the MBV2

Proverbs 26 in the MHNT

Proverbs 26 in the MKNFD

Proverbs 26 in the MNG

Proverbs 26 in the MNT

Proverbs 26 in the MNT2

Proverbs 26 in the MRS1T

Proverbs 26 in the NAA

Proverbs 26 in the NASB

Proverbs 26 in the NBLA

Proverbs 26 in the NBS

Proverbs 26 in the NBVTP

Proverbs 26 in the NET2

Proverbs 26 in the NIV11

Proverbs 26 in the NNT

Proverbs 26 in the NNT2

Proverbs 26 in the NNT3

Proverbs 26 in the PDDPT

Proverbs 26 in the PFNT

Proverbs 26 in the RMNT

Proverbs 26 in the SBIAS

Proverbs 26 in the SBIBS

Proverbs 26 in the SBIBS2

Proverbs 26 in the SBICS

Proverbs 26 in the SBIDS

Proverbs 26 in the SBIGS

Proverbs 26 in the SBIHS

Proverbs 26 in the SBIIS

Proverbs 26 in the SBIIS2

Proverbs 26 in the SBIIS3

Proverbs 26 in the SBIKS

Proverbs 26 in the SBIKS2

Proverbs 26 in the SBIMS

Proverbs 26 in the SBIOS

Proverbs 26 in the SBIPS

Proverbs 26 in the SBISS

Proverbs 26 in the SBITS

Proverbs 26 in the SBITS2

Proverbs 26 in the SBITS3

Proverbs 26 in the SBITS4

Proverbs 26 in the SBIUS

Proverbs 26 in the SBIVS

Proverbs 26 in the SBT

Proverbs 26 in the SBT1E

Proverbs 26 in the SCHL

Proverbs 26 in the SNT

Proverbs 26 in the SUSU

Proverbs 26 in the SUSU2

Proverbs 26 in the SYNO

Proverbs 26 in the TBIAOTANT

Proverbs 26 in the TBT1E

Proverbs 26 in the TBT1E2

Proverbs 26 in the TFTIP

Proverbs 26 in the TFTU

Proverbs 26 in the TGNTATF3T

Proverbs 26 in the THAI

Proverbs 26 in the TNFD

Proverbs 26 in the TNT

Proverbs 26 in the TNTIK

Proverbs 26 in the TNTIL

Proverbs 26 in the TNTIN

Proverbs 26 in the TNTIP

Proverbs 26 in the TNTIZ

Proverbs 26 in the TOMA

Proverbs 26 in the TTENT

Proverbs 26 in the UBG

Proverbs 26 in the UGV

Proverbs 26 in the UGV2

Proverbs 26 in the UGV3

Proverbs 26 in the VBL

Proverbs 26 in the VDCC

Proverbs 26 in the YALU

Proverbs 26 in the YAPE

Proverbs 26 in the YBVTP

Proverbs 26 in the ZBP