Psalms 12 (BOGWICC)
undefined Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe seminiti. Salimo la Davide. 1 Thandizeni Yehova pakuti palibe munthu wokhulupirika;okhulupirika akusowa pakati pa anthu. 2 Aliyense amanamiza mʼbale wake;ndi pakamwa pawo pabodza amayankhula zachinyengo. 3 Inu Yehova tsekani milomo yonse yachinyengondi pakamwa paliponse podzikuza. 4 Pakamwa pamene pamati, “Ife tidzapambana ndi kuyankhula kwathu;pakamwapa ndi pathupathu, tsono mbuye wathu ndani?” 5 “Chifukwa cha kuponderezedwa kwa anthu opanda mphamvundi kubuwula kwa anthu osowa,Ine ndidzauka tsopano,” akutero Yehova,“Ndidzawateteza kwa owazunza.” 6 Ndipo mawu a Yehova ndi angwiromonga siliva oyengedwa mʼngʼanjo yadothi,oyengedwa kasanu nʼkawiri. 7 Inu Yehova mudzatitchinjiriza ndipomudzatiteteza kwa anthu otere kwamuyaya. 8 Oyipa amangoyendayenda ponseponseanthu akamayamikira zochita zawo.