Psalms 128 (BOGWICC)
undefined Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. 1 Odala ndi onse amene amaopa Yehova,amene amayenda mʼnjira zake. 2 Udzadya chipatso cha ntchito yako;madalitso ndi chuma zidzakhala zako. 3 Mkazi wako adzakhala ngati mpesa woberekamʼkati mwa nyumba yako;ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivikuzungulira tebulo lako. 4 Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwaamene amaopa Yehova. 5 Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyonimasiku onse a moyo wako;uwone zokoma za Yerusalemu, 6 ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israeli.