Psalms 150 (BOGWICC)
1 Tamandani Yehova. Tamandani Mulungu mʼmalo ake opatulika;mutamandeni ku thambo lake lamphamvu. 2 Mutamandeni chifukwa cha machitidwe ake amphamvu;mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wopambana. 3 Mutamandeni poyimba malipenga,mutamandeni ndi pangwe ndi zeze. 4 Mutamandeni ndi matambolini ndi kuvina,mutamandeni ndi zingwe ndi zitoliro. 5 Mutamandeni ndi ziwaya zolira za malipenga,mutamandeni ndi ziwaya zolira kwambiri. 6 Chamoyo chilichonse chopuma chitamande Yehova. Tamandani Yehova.