Psalms 23 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. 1 Yehova ndiye mʼbusa wanga, sindidzasowa kanthu. 2 Amandigoneka pa msipu wobiriwira,amanditsogolera ku madzi akumwa abwino, 3 amatsitsimutsa moyo wanga.Amanditsogolera mʼnjira zachilungamochifukwa cha dzina lake. 4 Ngakhale ndiyendemʼchigwa cha mdima wakuda bii,sindidzaopa choyipa,pakuti Inu muli ndi ine;chibonga chanu ndi ndodo yanuzimanditonthoza. 5 Mumandikonzera chakudyaadani anga akuona.Mumadzoza mutu wanga ndi mafuta;chikho changa chimasefukira. 6 Zoonadi, zokoma ndi chikondi chosasinthika zidzanditsatamasiku onse a moyo wanga,ndipo ndidzakhala mʼNyumba ya Yehovakwamuyaya.