Psalms 3 (BOGWICC)
undefined Salimo la Davide. Atathawa mwana wake Abisalomu. 1 Inu Yehova, achulukadi adani anga!Achulukadi amene andiwukira! 2 Ambiri akunena za ine kuti,“Mulungu sadzamupulumutsa.” Sela 3 Koma Inu Yehova, ndinu chishango chonditeteza,Inu mwandiveka ulemerero ndipo mwanditukula. 4 Kwa Yehova, Ine ndilira mofuwulandipo Iye amandiyankha kuchokera ku phiri lake loyera. Sela 5 Ine ndimagona ndi kupeza tulo;ndimadzukanso chifukwa Yehova amandichirikiza. 6 Sindidzaopa adani anga osawerengeka ameneabwera kulimbana nane kuchokera ku madera onse. 7 Dzukani, Inu Yehova!Pulumutseni, Inu Mulungu wanga.Akantheni adani anga onse pa msagwada;gululani mano a anthu oyipa. 8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.Madalitso akhale pa anthu anu. Sela