Psalms 98 (BOGWICC)
undefined Salimo. 1 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa;dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyerazamuchitira chipulumutso. 2 Yehova waonetsa chipulumutso chakendipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina. 3 Iye wakumbukira chikondi chakendi kukhulupirika kwake pa Aisraeli;malekezero onse a dziko lapansi aonachipulumutso cha Mulungu wathu. 4 Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi,muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera. 5 Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze,ndi zeze ndi mawu a kuyimba, 6 ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimunafuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu. 7 Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo,dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo. 8 Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo,mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe; 9 izo ziyimbe pamaso pa Yehova,pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo,ndi mitundu ya anthu mosakondera.