Ruth 4 (BOGWICC)

1 Nthawi yomweyo Bowazi anapita ku chipata cha mzinda ndi kukhala pansi kumeneko pabwalo losonkhanira. Tsono anangoona wachibale woyenera kulowa chokolo uja akufika. Ndipo Bowazi anati, “Patukirani kuno, bwenzi langa. Mubwere mudzakhale apa.” Choncho anapatuka nakakhala pansi. 2 Bowazi anayitananso akuluakulu khumi a mu mzindamo nati, “Dzakhaleni pansi apa,” ndipo anadzakhala pansi. 3 Kenaka anamuwuza oyenera kulowa chokolo uja kuti, “Naomi amene wabwera kuchoka ku Mowabu akugulitsa malo amene anali a malemu Elimeleki, mʼbale wathu uja. 4 Choncho ndinaganiza zokuwuza zimenezi kuti ugule mundawu pamaso pa anthu amene ali panowa, ndi pamaso pa akuluakulu mwa abale athu. Ngati ukufuna kuwuwombola, uwombole. Koma ngati sukufuna, undiwuze kuti ndidziwe, pakuti palibe wina angawuwombole koma iweyo, ndipo pambuyo pa iwe pali ine.” Iye anati, “Ine ndidzawuwombola.” 5 Tsono Bowazi anati, “Tsiku limene ukagule mundawo kwa Naomi, udzatenganso Rute Mmowabu, mkazi wamasiye uja, kuti dzina la malemu lisungike pa cholowa chake.” 6 Pamenepo wachibaleyo anati, “Sindingathe kuwuwombola mundawu kuti ukhale wanga, kuopa kuti kutaya cholowa changa. Mugule ndinu. Ine sindingathe.” 7 (Kale mu Israeli zinkatere ngati munthu afuna kuwombola kanthu kapena kusinthana kanthu ndi mnzake kuti chikhale chakechake. Iye ankavula nsapato imodzi namupatsa mnzakeyo. Imeneyo ndiyo inali njira yochitira umboni mu Israeli). 8 Choncho wachibale uja atawuza Bowazi kuti, “Gulani ndinu mundawu.” Iye anavula nsapato yake namupatsa Bowazi. 9 Ndipo Bowazi anawuza akuluakuluwo ndi anthu onse aja kuti, “Nonsenu ndinu mboni lero, kuti ine ndagula kwa Naomi zonse zimene zinali za malemu Elimeleki, zonse zimene zinali za malemu Kiliyoni ndiponso za malemu Maloni. 10 Ndatenganso Rute Mmowabu uja mkazi wa malemu Maloni, kuti akhale mkazi wanga, kuti dzina la malemu Maloni lisungike pa cholowa chake, ndipo lisafafanizike pakati pa abale ake ngakhalenso mʼmudzi mwake. Nonsenu ndinu mboni lero lino.” 11 Ndipo akuluakulu aja ndi anthu onse amene anali pa chipata anati, “Ife ndife mboni, ndipo Yehova amusandutsa mkazi amene akudzalowa mʼnyumba yakoyu kuti akhale ngati Rakele ndi Leya, amene anamanga banja la Israeli. Ukhale munthu wosasowa kanthu mu Efurata ndi munthu wotchuka mu Betelehemu. 12 Ana amene Yehova adzakupatsa mwa mkaziyu adzamange banja lako kukhala la Perezi, amene Tamara anamubalira Yuda.” 13 Choncho Bowazi anakwatira Rute. Yehova anamudalitsa nakhala ndi pakati, ndipo anabereka mwana wamwamuna. 14 Ndipo amayi osiyanasiyana anati kwa Naomi. “Alemekezeke Yehova, amene lero lino sanakusiyeni nokha wopanda wachibale. Mwanayu dzina lake likhale lotchuka mu Israeli. 15 Mwanayo adzakupatseni moyo watsopano ndi kukuthandizani pa ukalamba wanu. Inde, mpongozi wanu amene amakukondani, amenenso waonetsa kuti ali wopambana kwa inu kuposa ana aamuna asanu ndi awiri, ndiye wakubalirani mwanayu.” 16 Kenaka Naomi anatenga mwanayo namufukata ndipo anakhala mlezi. 17 Amayi achinansi ake anati, “Naomi ali ndi mwana wamwamuna.” Ndipo anamutcha dzina lake Obedi. Iye anali abambo a Yese abambo ake a Davide. 18 Izi tsono ndizo zidzukulu za Perezi: Perezi anali abambo a Hezironi. 19 Hezironi anali abambo a Ramu,Ramu anali abambo a Aminadabu, 20 Aminadabu abambo a Naasoni,Naasoni anali abambo a Salimoni, 21 Salimoni abambo a Bowazi,Bowazi abambo a Obedi. 22 Obedi anali abambo a Yese,ndipo Yese anali abambo a Davide.

In Other Versions

Ruth 4 in the ANGEFD

Ruth 4 in the ANTPNG2D

Ruth 4 in the AS21

Ruth 4 in the BAGH

Ruth 4 in the BBPNG

Ruth 4 in the BBT1E

Ruth 4 in the BDS

Ruth 4 in the BEV

Ruth 4 in the BHAD

Ruth 4 in the BIB

Ruth 4 in the BLPT

Ruth 4 in the BNT

Ruth 4 in the BNTABOOT

Ruth 4 in the BNTLV

Ruth 4 in the BOATCB

Ruth 4 in the BOATCB2

Ruth 4 in the BOBCV

Ruth 4 in the BOCNT

Ruth 4 in the BOECS

Ruth 4 in the BOHCB

Ruth 4 in the BOHCV

Ruth 4 in the BOHLNT

Ruth 4 in the BOHNTLTAL

Ruth 4 in the BOICB

Ruth 4 in the BOILNTAP

Ruth 4 in the BOITCV

Ruth 4 in the BOKCV

Ruth 4 in the BOKCV2

Ruth 4 in the BOKHWOG

Ruth 4 in the BOKSSV

Ruth 4 in the BOLCB

Ruth 4 in the BOLCB2

Ruth 4 in the BOMCV

Ruth 4 in the BONAV

Ruth 4 in the BONCB

Ruth 4 in the BONLT

Ruth 4 in the BONUT2

Ruth 4 in the BOPLNT

Ruth 4 in the BOSCB

Ruth 4 in the BOSNC

Ruth 4 in the BOTLNT

Ruth 4 in the BOVCB

Ruth 4 in the BOYCB

Ruth 4 in the BPBB

Ruth 4 in the BPH

Ruth 4 in the BSB

Ruth 4 in the CCB

Ruth 4 in the CUV

Ruth 4 in the CUVS

Ruth 4 in the DBT

Ruth 4 in the DGDNT

Ruth 4 in the DHNT

Ruth 4 in the DNT

Ruth 4 in the ELBE

Ruth 4 in the EMTV

Ruth 4 in the ESV

Ruth 4 in the FBV

Ruth 4 in the FEB

Ruth 4 in the GGMNT

Ruth 4 in the GNT

Ruth 4 in the HARY

Ruth 4 in the HNT

Ruth 4 in the IRVA

Ruth 4 in the IRVB

Ruth 4 in the IRVG

Ruth 4 in the IRVH

Ruth 4 in the IRVK

Ruth 4 in the IRVM

Ruth 4 in the IRVM2

Ruth 4 in the IRVO

Ruth 4 in the IRVP

Ruth 4 in the IRVT

Ruth 4 in the IRVT2

Ruth 4 in the IRVU

Ruth 4 in the ISVN

Ruth 4 in the JSNT

Ruth 4 in the KAPI

Ruth 4 in the KBT1ETNIK

Ruth 4 in the KBV

Ruth 4 in the KJV

Ruth 4 in the KNFD

Ruth 4 in the LBA

Ruth 4 in the LBLA

Ruth 4 in the LNT

Ruth 4 in the LSV

Ruth 4 in the MAAL

Ruth 4 in the MBV

Ruth 4 in the MBV2

Ruth 4 in the MHNT

Ruth 4 in the MKNFD

Ruth 4 in the MNG

Ruth 4 in the MNT

Ruth 4 in the MNT2

Ruth 4 in the MRS1T

Ruth 4 in the NAA

Ruth 4 in the NASB

Ruth 4 in the NBLA

Ruth 4 in the NBS

Ruth 4 in the NBVTP

Ruth 4 in the NET2

Ruth 4 in the NIV11

Ruth 4 in the NNT

Ruth 4 in the NNT2

Ruth 4 in the NNT3

Ruth 4 in the PDDPT

Ruth 4 in the PFNT

Ruth 4 in the RMNT

Ruth 4 in the SBIAS

Ruth 4 in the SBIBS

Ruth 4 in the SBIBS2

Ruth 4 in the SBICS

Ruth 4 in the SBIDS

Ruth 4 in the SBIGS

Ruth 4 in the SBIHS

Ruth 4 in the SBIIS

Ruth 4 in the SBIIS2

Ruth 4 in the SBIIS3

Ruth 4 in the SBIKS

Ruth 4 in the SBIKS2

Ruth 4 in the SBIMS

Ruth 4 in the SBIOS

Ruth 4 in the SBIPS

Ruth 4 in the SBISS

Ruth 4 in the SBITS

Ruth 4 in the SBITS2

Ruth 4 in the SBITS3

Ruth 4 in the SBITS4

Ruth 4 in the SBIUS

Ruth 4 in the SBIVS

Ruth 4 in the SBT

Ruth 4 in the SBT1E

Ruth 4 in the SCHL

Ruth 4 in the SNT

Ruth 4 in the SUSU

Ruth 4 in the SUSU2

Ruth 4 in the SYNO

Ruth 4 in the TBIAOTANT

Ruth 4 in the TBT1E

Ruth 4 in the TBT1E2

Ruth 4 in the TFTIP

Ruth 4 in the TFTU

Ruth 4 in the TGNTATF3T

Ruth 4 in the THAI

Ruth 4 in the TNFD

Ruth 4 in the TNT

Ruth 4 in the TNTIK

Ruth 4 in the TNTIL

Ruth 4 in the TNTIN

Ruth 4 in the TNTIP

Ruth 4 in the TNTIZ

Ruth 4 in the TOMA

Ruth 4 in the TTENT

Ruth 4 in the UBG

Ruth 4 in the UGV

Ruth 4 in the UGV2

Ruth 4 in the UGV3

Ruth 4 in the VBL

Ruth 4 in the VDCC

Ruth 4 in the YALU

Ruth 4 in the YAPE

Ruth 4 in the YBVTP

Ruth 4 in the ZBP