1 Chronicles 15 (BOGWICC)

1 Davide atadzimangira nyumba zina mu Mzinda wa Davide, iye anakonza malo a Bokosi la Mulungu ndipo analimangira tenti. 2 Pamenepo Davide anati, “Palibe wina ati anyamule Bokosi la Mulungu koma Alevi chifukwa Yehova anawasankha kuti azinyamula Bokosi la Yehova ndi kumatumikira pamaso pake nthawi zonse.” 3 Davide anasonkhanitsa Aisraeli onse mu Yerusalemu kuti abweretse Bokosi la Yehova ku malo amene analikonzera. 4 Iye anayitanitsa pamodzi zidzukulu za Aaroni ndi Alevi: 5 kuchokera ku banja la Kohati,mtsogoleri Urieli ndi abale ake 120. 6 Kuchokera ku banja la Merari,mtsogoleri Asaya ndi abale ake 220; 7 kuchokera ku banja la Geresomu,mtsogoleri Yoweli ndi abale ake 130; 8 kuchokera ku banja la Elizafani,mtsogoleri Semaya ndi abale ake 200; 9 kuchokera ku banja la Hebroni,mtsogoleri Elieli ndi abale ake 80; 10 kuchokera ku banja la Uzieli,mtsogoleri Aminadabu ndi abale ake 112. 11 Kenaka Davide anayitanitsa ansembe Zadoki ndi Abiatara, ndi Alevi awa, Urieli, Asaya, Yoweli, Semaya, Elieli ndi Aminadabu. 12 Iye anawawuza kuti, “Inu ndinu atsogoleri a mabanja a Alevi ndipo inu ndi abale anu Alevi mudziyeretse nokha ndi kubweretsa Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli ku malo amene ine ndalikonzera. 13 Popeza kuti inu Alevi simunalinyamule poyamba paja, Yehova Mulungu wathu anatikantha. Sitinafunse momwe tikanachitira monga mmene Iyeyo anafotokozera.” 14 Kotero ansembe ndi Alevi anadziyeretsa ndi cholinga chakuti akatenge Bokosi la Yehova Mulungu wa Israeli. 15 Ndipo Alevi ananyamula Bokosi la Mulungu pa mapewa awo pa mitengo yake yonyamulira monga momwe Mose analamulira molingana ndi mawu a Yehova. 16 Davide anawuza atsogoleri a Alevi kuti asankhe abale awo kuti akhale oyimba nyimbo zachisangalalo, zoyimba ndi zida: azeze, apangwe ndi ziwaya za malipenga. 17 Kotero Alevi anasankha Hemani mwana wa Yoweli; ndipo mwa abale ake anasankha Asafu mwana wa Berekiya; ndipo mwa ana a Merari, abale awo, anasankha Etani mwana wa Kusaya; 18 ndipo pamodzi ndi iwowa abale awo otsatana nawo: Zekariya, Yaazieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Benaya, Maaseya, Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu ndi Yeiyeli, alonda a pa chipata. 19 Anthu oyimba aja Hemani, Asafu ndi Etani ndiwo ankayimba ziwaya za malipenga zamkuwa; 20 Zekariya, Azieli, Semiramoti, Yehieli, Uni, Eliabu, Maaseya ndi Benaya ankayimba azeze a liwu lokwera; 21 ndipo Matitiya, Elifelehu, Mikineya, Obedi-Edomu, Yeiyeli ndi Azaziya ankayimba apangwe a liwu lotsika. 22 Kenaniya, mtsogoleri wa Alevi anali woyangʼanira mayimbidwe; uwu ndiye unali udindo wake pakuti anali waluso pa zimenezi. 23 Berekiya ndi Elikana anali olondera pa khomo la bokosilo. 24 Ansembe awa; Sebaniya, Yehosafati, Netaneli, Amasai, Zekariya, Benaya ndi Eliezara ndiwo ankayimba malipenga patsogolo pa Bokosi la Mulungu. Obedi-Edomu ndi Yehiya analinso alonda a pa khomo la bokosilo. 25 Choncho Davide pamodzi ndi akuluakulu a Israeli ndiponso asilikali olamulira magulu a anthu 1,000, anapita kukatenga Bokosi la Chipangano la Yehova ku nyumba ya Obedi-Edomu akukondwera. 26 Popeza Mulungu anathandiza Alevi amene ananyamula Bokosi la Chipangano la Yehova, anapereka nsembe ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri ndiponso nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri. 27 Ndipo Davide anali atavala mkanjo wa nsalu yofewa yosalala, monga anavalira Alevi onse amene ananyamula bokosi pamodzi anthu oyimba, ndiponso Kenaniya, amene anali woyangʼanira magulu oyimba. Davide anavalanso efodi ya nsalu yofewa yosalala. 28 Kotero Aisraeli onse anabweretsa Bokosi la Chipangano la Yehova ndi mfuwu, ndiponso akuyimba zitoliro zanyanga zankhosa zazimuna, malipenga ndi maseche ndiponso akuyimba azeze ndi apangwe. 29 Bokosi la Chipangano la Yehova likulowa mu Mzinda wa Davide, Mikala mwana wamkazi wa Sauli ankaona ali pa zenera. Ndipo ataona Mfumu Davide ikuvina ndi kukondwera, iye ananyoza Davideyo mu mtima mwake.

In Other Versions

1 Chronicles 15 in the ANGEFD

1 Chronicles 15 in the ANTPNG2D

1 Chronicles 15 in the AS21

1 Chronicles 15 in the BAGH

1 Chronicles 15 in the BBPNG

1 Chronicles 15 in the BBT1E

1 Chronicles 15 in the BDS

1 Chronicles 15 in the BEV

1 Chronicles 15 in the BHAD

1 Chronicles 15 in the BIB

1 Chronicles 15 in the BLPT

1 Chronicles 15 in the BNT

1 Chronicles 15 in the BNTABOOT

1 Chronicles 15 in the BNTLV

1 Chronicles 15 in the BOATCB

1 Chronicles 15 in the BOATCB2

1 Chronicles 15 in the BOBCV

1 Chronicles 15 in the BOCNT

1 Chronicles 15 in the BOECS

1 Chronicles 15 in the BOHCB

1 Chronicles 15 in the BOHCV

1 Chronicles 15 in the BOHLNT

1 Chronicles 15 in the BOHNTLTAL

1 Chronicles 15 in the BOICB

1 Chronicles 15 in the BOILNTAP

1 Chronicles 15 in the BOITCV

1 Chronicles 15 in the BOKCV

1 Chronicles 15 in the BOKCV2

1 Chronicles 15 in the BOKHWOG

1 Chronicles 15 in the BOKSSV

1 Chronicles 15 in the BOLCB

1 Chronicles 15 in the BOLCB2

1 Chronicles 15 in the BOMCV

1 Chronicles 15 in the BONAV

1 Chronicles 15 in the BONCB

1 Chronicles 15 in the BONLT

1 Chronicles 15 in the BONUT2

1 Chronicles 15 in the BOPLNT

1 Chronicles 15 in the BOSCB

1 Chronicles 15 in the BOSNC

1 Chronicles 15 in the BOTLNT

1 Chronicles 15 in the BOVCB

1 Chronicles 15 in the BOYCB

1 Chronicles 15 in the BPBB

1 Chronicles 15 in the BPH

1 Chronicles 15 in the BSB

1 Chronicles 15 in the CCB

1 Chronicles 15 in the CUV

1 Chronicles 15 in the CUVS

1 Chronicles 15 in the DBT

1 Chronicles 15 in the DGDNT

1 Chronicles 15 in the DHNT

1 Chronicles 15 in the DNT

1 Chronicles 15 in the ELBE

1 Chronicles 15 in the EMTV

1 Chronicles 15 in the ESV

1 Chronicles 15 in the FBV

1 Chronicles 15 in the FEB

1 Chronicles 15 in the GGMNT

1 Chronicles 15 in the GNT

1 Chronicles 15 in the HARY

1 Chronicles 15 in the HNT

1 Chronicles 15 in the IRVA

1 Chronicles 15 in the IRVB

1 Chronicles 15 in the IRVG

1 Chronicles 15 in the IRVH

1 Chronicles 15 in the IRVK

1 Chronicles 15 in the IRVM

1 Chronicles 15 in the IRVM2

1 Chronicles 15 in the IRVO

1 Chronicles 15 in the IRVP

1 Chronicles 15 in the IRVT

1 Chronicles 15 in the IRVT2

1 Chronicles 15 in the IRVU

1 Chronicles 15 in the ISVN

1 Chronicles 15 in the JSNT

1 Chronicles 15 in the KAPI

1 Chronicles 15 in the KBT1ETNIK

1 Chronicles 15 in the KBV

1 Chronicles 15 in the KJV

1 Chronicles 15 in the KNFD

1 Chronicles 15 in the LBA

1 Chronicles 15 in the LBLA

1 Chronicles 15 in the LNT

1 Chronicles 15 in the LSV

1 Chronicles 15 in the MAAL

1 Chronicles 15 in the MBV

1 Chronicles 15 in the MBV2

1 Chronicles 15 in the MHNT

1 Chronicles 15 in the MKNFD

1 Chronicles 15 in the MNG

1 Chronicles 15 in the MNT

1 Chronicles 15 in the MNT2

1 Chronicles 15 in the MRS1T

1 Chronicles 15 in the NAA

1 Chronicles 15 in the NASB

1 Chronicles 15 in the NBLA

1 Chronicles 15 in the NBS

1 Chronicles 15 in the NBVTP

1 Chronicles 15 in the NET2

1 Chronicles 15 in the NIV11

1 Chronicles 15 in the NNT

1 Chronicles 15 in the NNT2

1 Chronicles 15 in the NNT3

1 Chronicles 15 in the PDDPT

1 Chronicles 15 in the PFNT

1 Chronicles 15 in the RMNT

1 Chronicles 15 in the SBIAS

1 Chronicles 15 in the SBIBS

1 Chronicles 15 in the SBIBS2

1 Chronicles 15 in the SBICS

1 Chronicles 15 in the SBIDS

1 Chronicles 15 in the SBIGS

1 Chronicles 15 in the SBIHS

1 Chronicles 15 in the SBIIS

1 Chronicles 15 in the SBIIS2

1 Chronicles 15 in the SBIIS3

1 Chronicles 15 in the SBIKS

1 Chronicles 15 in the SBIKS2

1 Chronicles 15 in the SBIMS

1 Chronicles 15 in the SBIOS

1 Chronicles 15 in the SBIPS

1 Chronicles 15 in the SBISS

1 Chronicles 15 in the SBITS

1 Chronicles 15 in the SBITS2

1 Chronicles 15 in the SBITS3

1 Chronicles 15 in the SBITS4

1 Chronicles 15 in the SBIUS

1 Chronicles 15 in the SBIVS

1 Chronicles 15 in the SBT

1 Chronicles 15 in the SBT1E

1 Chronicles 15 in the SCHL

1 Chronicles 15 in the SNT

1 Chronicles 15 in the SUSU

1 Chronicles 15 in the SUSU2

1 Chronicles 15 in the SYNO

1 Chronicles 15 in the TBIAOTANT

1 Chronicles 15 in the TBT1E

1 Chronicles 15 in the TBT1E2

1 Chronicles 15 in the TFTIP

1 Chronicles 15 in the TFTU

1 Chronicles 15 in the TGNTATF3T

1 Chronicles 15 in the THAI

1 Chronicles 15 in the TNFD

1 Chronicles 15 in the TNT

1 Chronicles 15 in the TNTIK

1 Chronicles 15 in the TNTIL

1 Chronicles 15 in the TNTIN

1 Chronicles 15 in the TNTIP

1 Chronicles 15 in the TNTIZ

1 Chronicles 15 in the TOMA

1 Chronicles 15 in the TTENT

1 Chronicles 15 in the UBG

1 Chronicles 15 in the UGV

1 Chronicles 15 in the UGV2

1 Chronicles 15 in the UGV3

1 Chronicles 15 in the VBL

1 Chronicles 15 in the VDCC

1 Chronicles 15 in the YALU

1 Chronicles 15 in the YAPE

1 Chronicles 15 in the YBVTP

1 Chronicles 15 in the ZBP