1 Chronicles 21 (BOGWICC)

1 Satana anafuna kuvutitsa Aisraeli choncho anawutsa mtima wa Davide kuti awerenge Aisraeli. 2 Choncho Davide anati kwa Yowabu pamodzi ndi atsogoleri a ankhondo, “Pitani mukawerenge Aisraeli kuyambira ku Beeriseba mpaka ku Dani. Ndipo mudzandiwuze kuti ndidziwe chiwerengero chawo.” 3 Yowabu anayankha kuti, “Yehova achulukitse ankhondo ake kukhala miyandamiyanda. Mbuye wanga mfumu, kodi anthu onsewa sali pansi panu? Nʼchifukwa chiyani mbuye wanga mukufuna kuchita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukufuna kuchimwitsa Israeli?” 4 Komabe mawu a mfumu anapambana mawu a Yowabu, kotero Yowabu anapita mu Israeli monse ndipo kenaka anabwera ku Yerusalemu. 5 Yowabu anapereka chiwerengero cha anthu ankhondo kwa Davide: Mu Israeli monse munali anthu ankhondo 1,100,000 amene amadziwa kugwiritsa ntchito lupanga, kuphatikizapo anthu 470,000 a fuko la Yuda. 6 Koma Yowabu sanaphatikizepo fuko la Levi ndi fuko la Benjamini pa chiwerengerochi, pakuti lamulo la mfumu linamuyipira. 7 Lamulo limeneli silinakomerenso Mulungu. Kotero Iye analanga Israeli. 8 Choncho Davide anati kwa Mulungu, “Ine ndachimwa kwambiri pa zimene ndachita. Tsono ndikupempha kuti mukhululuke kulakwa kwa mtumiki wanu. Ine ndachita zopusa kwambiri.” 9 Yehova anati kwa Gadi, mlosi wa Davide, 10 “Pita ukamuwuze Davide kuti, ‘Yehova akuti, Ine ndikukupatsa zinthu zitatu izi. Usankhepo chimodzi pa zimenezi choti ndikuchitire.’ ” 11 Choncho Gadi anapita kwa Davide ndipo anati kwa Iye, “Yehova akuti, ‘Musankhepo chimene mungakonde kuti chichitike: 12 mʼdziko mukhale njala zaka zitatu, mukhale mukuthawa adani anu kwa miyezi itatu, akukukanthani ndi lupanga la Yehova, kapena mʼdziko mukhale mliri kwa masiku atatu, mngelo wa Yehova akuwononga Israeli yense.’ Ndipo tsono ganizirani bwino chomwe ndikamuyankhe amene wandituma.” 13 Davide anati kwa Gadi, “Ine ndavutika kwambiri mu mtima mwanga. Ine andilange ndi Yehova, pakuti chifundo chake ndi chachikulu kwambiri; koma ndisalangidwe ndi anthu.” 14 Choncho Yehova anabweretsa mliri pa Aisraeli, ndipo unapha Aisraeli 70,000. 15 Ndipo Mulungu anatumiza mngelo kuti awononge Yerusalemu. Koma pamene mngeloyo amachita zimenezi, Yehova anaona ndipo anavutika mu mtima chifukwa cha zowawazo ndipo anati kwa mngelo amene ankawononga anthu uja, “Basi kwakwanira! Leka kuwononga.” Nthawi imeneyo mngelo wa Yehova anali atayima pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. 16 Davide anakweza maso ake ndipo anaona mngelo wa Yehova atayima pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, mʼdzanja lake muli lupanga lotambalitsa kuloza ku Yerusalemu. Ndipo Davide ndi akuluakulu, atavala ziguduli, anadzigwetsa pansi chafufumimba. 17 Davide anati kwa Mulungu, “Kodi si ine amene ndinalamula kuti ankhondo awerengedwe? Ine mʼbusa ndi amene ndachimwa, ndiye ndachita zoyipa. Anthuwa ali ngati nkhosa zosalakwa. Kodi iwowa achita chiyani? Inu Yehova Mulungu wanga, langani ineyo pamodzi ndi banja langa, koma musalole kuti mliriwu ukhale pa anthu anuwa.” 18 Pamenepo mngelo wa Yehova analamula Gadi kuti awuze Davide kuti akamange guwa lansembe la Yehova pamalo opunthira tirigu a Arauna Myebusi. 19 Ndipo Davide anapita pomvera mawu amene Gadi ananena mʼdzina la Yehova. 20 Pamene Arauna ankapuntha tirigu, anatembenuka ndipo anaona mngelo ndipo ana ake anayi aamuna amene anali naye anabisala. 21 Davide anayandikira, ndipo Arauna atayangʼana ndi kumuona, anachoka popunthira tirigupo ndipo anawerama nagunditsa nkhope yake pansi pamaso pa Davide. 22 Davide anati kwa Arauna, “Undipatse malo ako opunthira tirigu kuti ndimangire Yehova guwa lansembe, kuti mliri uli pa anthuwa usiye. Undigulitse ine pa mtengo woyenera ndithu.” 23 Arauna anati kwa Davide, “Tengani! Mbuye wanga mfumu achite chomukomera. Taonani ine ndidzapereka ngʼombe zazimuna za nsembe yopsereza, zopunthira tirigu zidzakhala nkhuni ndipo tiriguyu adzakhala chopereka chachakudya. Ndidzapereka zonsezi.” 24 Koma mfumu Davide inayankha Arauna kuti, “Ayi, ine ndikuti ndipereka mtengo wathunthu. Sindingatenge chinthu chako ndi kuchipereka kwa Yehova, kapena kupereka nsembe imene sindinayigule.” 25 Choncho Davide analipira Arauna masekeli agolide 600 chifukwa cha malowo. 26 Davide anamangira Yehova guwa lansembe pamenepo ndipo anaperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano. Iye anapemphera kwa Yehova, ndipo Yehova anayankha potumiza moto pa guwa lansembe zopsereza kuchokera kumwamba. 27 Tsono Yehova anayankhula kwa mngelo, ndipo analowetsa lupanga lake mʼchimake. 28 Pa nthawi imeneyo, Davide ataona kuti Yehova wamuyankha pa malo opunthira tirigu a Arauna Myebusi, anapereka nsembe pamenepo. 29 Tenti ya Yehova imene Mose anapanga mʼchipululu, ndi guwa lansembe zopsereza pa nthawi imeneyi zinali pa phiri ku Gibiyoni. 30 Koma Davide sanathe kupita kumeneko kuti akapemphere pamaso pa Yehova, chifukwa amaopa lupanga la mngelo wa Yehova.

In Other Versions

1 Chronicles 21 in the ANGEFD

1 Chronicles 21 in the ANTPNG2D

1 Chronicles 21 in the AS21

1 Chronicles 21 in the BAGH

1 Chronicles 21 in the BBPNG

1 Chronicles 21 in the BBT1E

1 Chronicles 21 in the BDS

1 Chronicles 21 in the BEV

1 Chronicles 21 in the BHAD

1 Chronicles 21 in the BIB

1 Chronicles 21 in the BLPT

1 Chronicles 21 in the BNT

1 Chronicles 21 in the BNTABOOT

1 Chronicles 21 in the BNTLV

1 Chronicles 21 in the BOATCB

1 Chronicles 21 in the BOATCB2

1 Chronicles 21 in the BOBCV

1 Chronicles 21 in the BOCNT

1 Chronicles 21 in the BOECS

1 Chronicles 21 in the BOHCB

1 Chronicles 21 in the BOHCV

1 Chronicles 21 in the BOHLNT

1 Chronicles 21 in the BOHNTLTAL

1 Chronicles 21 in the BOICB

1 Chronicles 21 in the BOILNTAP

1 Chronicles 21 in the BOITCV

1 Chronicles 21 in the BOKCV

1 Chronicles 21 in the BOKCV2

1 Chronicles 21 in the BOKHWOG

1 Chronicles 21 in the BOKSSV

1 Chronicles 21 in the BOLCB

1 Chronicles 21 in the BOLCB2

1 Chronicles 21 in the BOMCV

1 Chronicles 21 in the BONAV

1 Chronicles 21 in the BONCB

1 Chronicles 21 in the BONLT

1 Chronicles 21 in the BONUT2

1 Chronicles 21 in the BOPLNT

1 Chronicles 21 in the BOSCB

1 Chronicles 21 in the BOSNC

1 Chronicles 21 in the BOTLNT

1 Chronicles 21 in the BOVCB

1 Chronicles 21 in the BOYCB

1 Chronicles 21 in the BPBB

1 Chronicles 21 in the BPH

1 Chronicles 21 in the BSB

1 Chronicles 21 in the CCB

1 Chronicles 21 in the CUV

1 Chronicles 21 in the CUVS

1 Chronicles 21 in the DBT

1 Chronicles 21 in the DGDNT

1 Chronicles 21 in the DHNT

1 Chronicles 21 in the DNT

1 Chronicles 21 in the ELBE

1 Chronicles 21 in the EMTV

1 Chronicles 21 in the ESV

1 Chronicles 21 in the FBV

1 Chronicles 21 in the FEB

1 Chronicles 21 in the GGMNT

1 Chronicles 21 in the GNT

1 Chronicles 21 in the HARY

1 Chronicles 21 in the HNT

1 Chronicles 21 in the IRVA

1 Chronicles 21 in the IRVB

1 Chronicles 21 in the IRVG

1 Chronicles 21 in the IRVH

1 Chronicles 21 in the IRVK

1 Chronicles 21 in the IRVM

1 Chronicles 21 in the IRVM2

1 Chronicles 21 in the IRVO

1 Chronicles 21 in the IRVP

1 Chronicles 21 in the IRVT

1 Chronicles 21 in the IRVT2

1 Chronicles 21 in the IRVU

1 Chronicles 21 in the ISVN

1 Chronicles 21 in the JSNT

1 Chronicles 21 in the KAPI

1 Chronicles 21 in the KBT1ETNIK

1 Chronicles 21 in the KBV

1 Chronicles 21 in the KJV

1 Chronicles 21 in the KNFD

1 Chronicles 21 in the LBA

1 Chronicles 21 in the LBLA

1 Chronicles 21 in the LNT

1 Chronicles 21 in the LSV

1 Chronicles 21 in the MAAL

1 Chronicles 21 in the MBV

1 Chronicles 21 in the MBV2

1 Chronicles 21 in the MHNT

1 Chronicles 21 in the MKNFD

1 Chronicles 21 in the MNG

1 Chronicles 21 in the MNT

1 Chronicles 21 in the MNT2

1 Chronicles 21 in the MRS1T

1 Chronicles 21 in the NAA

1 Chronicles 21 in the NASB

1 Chronicles 21 in the NBLA

1 Chronicles 21 in the NBS

1 Chronicles 21 in the NBVTP

1 Chronicles 21 in the NET2

1 Chronicles 21 in the NIV11

1 Chronicles 21 in the NNT

1 Chronicles 21 in the NNT2

1 Chronicles 21 in the NNT3

1 Chronicles 21 in the PDDPT

1 Chronicles 21 in the PFNT

1 Chronicles 21 in the RMNT

1 Chronicles 21 in the SBIAS

1 Chronicles 21 in the SBIBS

1 Chronicles 21 in the SBIBS2

1 Chronicles 21 in the SBICS

1 Chronicles 21 in the SBIDS

1 Chronicles 21 in the SBIGS

1 Chronicles 21 in the SBIHS

1 Chronicles 21 in the SBIIS

1 Chronicles 21 in the SBIIS2

1 Chronicles 21 in the SBIIS3

1 Chronicles 21 in the SBIKS

1 Chronicles 21 in the SBIKS2

1 Chronicles 21 in the SBIMS

1 Chronicles 21 in the SBIOS

1 Chronicles 21 in the SBIPS

1 Chronicles 21 in the SBISS

1 Chronicles 21 in the SBITS

1 Chronicles 21 in the SBITS2

1 Chronicles 21 in the SBITS3

1 Chronicles 21 in the SBITS4

1 Chronicles 21 in the SBIUS

1 Chronicles 21 in the SBIVS

1 Chronicles 21 in the SBT

1 Chronicles 21 in the SBT1E

1 Chronicles 21 in the SCHL

1 Chronicles 21 in the SNT

1 Chronicles 21 in the SUSU

1 Chronicles 21 in the SUSU2

1 Chronicles 21 in the SYNO

1 Chronicles 21 in the TBIAOTANT

1 Chronicles 21 in the TBT1E

1 Chronicles 21 in the TBT1E2

1 Chronicles 21 in the TFTIP

1 Chronicles 21 in the TFTU

1 Chronicles 21 in the TGNTATF3T

1 Chronicles 21 in the THAI

1 Chronicles 21 in the TNFD

1 Chronicles 21 in the TNT

1 Chronicles 21 in the TNTIK

1 Chronicles 21 in the TNTIL

1 Chronicles 21 in the TNTIN

1 Chronicles 21 in the TNTIP

1 Chronicles 21 in the TNTIZ

1 Chronicles 21 in the TOMA

1 Chronicles 21 in the TTENT

1 Chronicles 21 in the UBG

1 Chronicles 21 in the UGV

1 Chronicles 21 in the UGV2

1 Chronicles 21 in the UGV3

1 Chronicles 21 in the VBL

1 Chronicles 21 in the VDCC

1 Chronicles 21 in the YALU

1 Chronicles 21 in the YAPE

1 Chronicles 21 in the YBVTP

1 Chronicles 21 in the ZBP