1 Corinthians 11 (BOGWICC)

1 Tsatirani chitsanzo changa, monga inenso nditsatira chitsanzo cha Khristu. 2 Ndikukuyamikani chifukwa chondikumbukira pa zonse ndiponso posunga ziphunzitso monga ndinakuphunzitsirani. 3 Tsopano ndikufuna muzindikire kuti Khristu ndiye mutu wa munthu aliyense, ndipo mwamuna ndiye mutu wamkazi, ndipo mutu wa Khristu ndi Mulungu. 4 Mwamuna aliyense wopemphera kapena kunenera ataphimba mutu wake akunyoza mutu wakewo. 5 Ndipo mkazi aliyense wopemphera kapena kunenera asanaphimbe mutu wake sakulemekeza mutu wakewo. Kuli chimodzimodzi kumeta mutu wake. 6 Ngati mkazi saphimba kumutu kwake, ndiye kuti amete tsitsi lake. Ngati nʼchamanyazi kwa mkazi kungoyepula kapena kumeta mpala, ndiye kuti aphimbe kumutu kwake. 7 Mwamuna sayenera kuphimba kumutu popeza ndi chifaniziro ndi ulemerero wa Mulungu; pamene mkazi ndi ulemerero wa mwamuna. 8 Pakuti mwamuna sachokera kwa mkazi, koma mkazi kwa mwamuna. 9 Ndipo mwamuna sanalengedwe chifukwa cha mkazi, koma mkazi analengedwera mwamuna. 10 Pa chifukwa ichi, ndiponso pa chifukwa cha angelo, mkazi akuyenera kukhala ndi chizindikiro cha ulamuliro wake. 11 Komabe mwa Ambuye, mkazi amadalira mwamuna ndipo mwamuna amadalira mkazi. 12 Pakuti monga mkazi anachokera kwa mwamuna, momwemonso mwamuna anabadwa mwa mkazi. Koma zonse zichokera kwa Mulungu. 13 Dziweruzeni. Kodi nʼchabwino kuti mkazi apemphere kwa Mulungu wopanda chophimba kumutu? 14 Kodi chikhalidwe chathu sichitiphunzitsa kuti nʼchamanyazi kuti mwamuna akhale ndi tsitsi lalitali, 15 koma mkazi akakhala ndi tsitsi lalitali ndi ulemerero wake? Pakuti mkazi anapatsidwa tsitsi lalitali monga chophimba kumutu. 16 Ngati wina akufuna kutsutsapo pa zimenezi, ife ndiponso mipingo ya Mulungu tilibe machitidwe ena apadera koma ndi omwewa. 17 Koma popereka malangizo awa sindikufuna kukuyamikirani popeza mʼmisonkhano yanu mumachita zoyipa kuposa zabwino. 18 Choyamba, ndikumva kuti mukasonkhana mu mpingo mumasankhana ndipo ndikukhulupirira kuti zimenezi kwinaku nʼzoona. 19 Nʼzosakayikitsa kuti pali kugawikana pakati panu kuti adziwike amene ndi ovomerezeka ndi Mulungu. 20 Tsono, mukasonkhana pamodzi, chimene mumadya si Mgonero wa Ambuye. 21 Pakuti mukamadya, aliyense amangodzidyera zomwe anakonza. Wina amakhala ndi njala pamene wina amaledzera. 22 Kodi mulibe nyumba zanu kumene mungamadyere ndi kumwa? Kapena mumapeputsa mpingo wa Mulungu ndi kuchititsa manyazi amene alibe kalikonse? Ndikunena chiyani kwa inu? Moti ndikuyamikireni pa zimenezi? Ayi, pa zinthu izi sindingakuyamikireni. 23 Pakuti zimene ndinalandira kwa Ambuye ndi zomwe ndinakupatsani. Ambuye Yesu, usiku umene anaperekedwa uja, anatenga buledi. 24 Atayamika ndi kumunyema ananena kuti, “Ili ndi thupi langa lomwe laperekedwa kwa inu; muzichita zimenezi pokumbukira Ine.” 25 Chimodzimodzi, atatha kudya, anatenga chikho, nati, “Chikho ichi ndi pangano latsopano la magazi anga; imwani nthawi zonse pokumbukira Ine.” 26 Pakuti nthawi zonse pamene mudya bulediyu ndikumwa chikhochi, mukulalikira imfa ya Ambuye mpaka Iye adzabweranso. 27 Chifukwa chake, aliyense amene adya buledi kapena kumwa chikho cha Ambuye mʼnjira yosayenera adzachimwira thupi ndi magazi a Ambuye. 28 Munthu adzisanthule yekha asanadye buledi kapena kumwa chikhochi. 29 Popeza aliyense amene adya kapena kumwa mosazindikira thupi la Ambuye, amadya ndi kumwa chiweruzo chake chomwe. 30 Nʼchifukwa chake pakati panu ambiri mwa inu ndi ofowoka ndi odwala, ndipo ambirinso agona tulo. 31 Koma tikanadziyesa tokha sitikaweruzidwanso. 32 Pamene tiweruzidwa ndi Ambuye, ndiye kuti akukonza khalidwe lathu kupewa kuti tingatsutsidwe pamodzi ndi anthu osakhulupirira. 33 Ndiye tsono abale anga, pamene musonkhana pa chakudya, mudikirirane. 34 Ngati wina ali ndi njala, adye ku nyumba kwake kuti pamene musonkhana pamodzi zisafike poti muweruzidwe nazo.Ndipo ndikabwera ndidzakupatsani malangizo ena owonjezera.

In Other Versions

1 Corinthians 11 in the ANGEFD

1 Corinthians 11 in the ANTPNG2D

1 Corinthians 11 in the AS21

1 Corinthians 11 in the BAGH

1 Corinthians 11 in the BBPNG

1 Corinthians 11 in the BBT1E

1 Corinthians 11 in the BDS

1 Corinthians 11 in the BEV

1 Corinthians 11 in the BHAD

1 Corinthians 11 in the BIB

1 Corinthians 11 in the BLPT

1 Corinthians 11 in the BNT

1 Corinthians 11 in the BNTABOOT

1 Corinthians 11 in the BNTLV

1 Corinthians 11 in the BOATCB

1 Corinthians 11 in the BOATCB2

1 Corinthians 11 in the BOBCV

1 Corinthians 11 in the BOCNT

1 Corinthians 11 in the BOECS

1 Corinthians 11 in the BOHCB

1 Corinthians 11 in the BOHCV

1 Corinthians 11 in the BOHLNT

1 Corinthians 11 in the BOHNTLTAL

1 Corinthians 11 in the BOICB

1 Corinthians 11 in the BOILNTAP

1 Corinthians 11 in the BOITCV

1 Corinthians 11 in the BOKCV

1 Corinthians 11 in the BOKCV2

1 Corinthians 11 in the BOKHWOG

1 Corinthians 11 in the BOKSSV

1 Corinthians 11 in the BOLCB

1 Corinthians 11 in the BOLCB2

1 Corinthians 11 in the BOMCV

1 Corinthians 11 in the BONAV

1 Corinthians 11 in the BONCB

1 Corinthians 11 in the BONLT

1 Corinthians 11 in the BONUT2

1 Corinthians 11 in the BOPLNT

1 Corinthians 11 in the BOSCB

1 Corinthians 11 in the BOSNC

1 Corinthians 11 in the BOTLNT

1 Corinthians 11 in the BOVCB

1 Corinthians 11 in the BOYCB

1 Corinthians 11 in the BPBB

1 Corinthians 11 in the BPH

1 Corinthians 11 in the BSB

1 Corinthians 11 in the CCB

1 Corinthians 11 in the CUV

1 Corinthians 11 in the CUVS

1 Corinthians 11 in the DBT

1 Corinthians 11 in the DGDNT

1 Corinthians 11 in the DHNT

1 Corinthians 11 in the DNT

1 Corinthians 11 in the ELBE

1 Corinthians 11 in the EMTV

1 Corinthians 11 in the ESV

1 Corinthians 11 in the FBV

1 Corinthians 11 in the FEB

1 Corinthians 11 in the GGMNT

1 Corinthians 11 in the GNT

1 Corinthians 11 in the HARY

1 Corinthians 11 in the HNT

1 Corinthians 11 in the IRVA

1 Corinthians 11 in the IRVB

1 Corinthians 11 in the IRVG

1 Corinthians 11 in the IRVH

1 Corinthians 11 in the IRVK

1 Corinthians 11 in the IRVM

1 Corinthians 11 in the IRVM2

1 Corinthians 11 in the IRVO

1 Corinthians 11 in the IRVP

1 Corinthians 11 in the IRVT

1 Corinthians 11 in the IRVT2

1 Corinthians 11 in the IRVU

1 Corinthians 11 in the ISVN

1 Corinthians 11 in the JSNT

1 Corinthians 11 in the KAPI

1 Corinthians 11 in the KBT1ETNIK

1 Corinthians 11 in the KBV

1 Corinthians 11 in the KJV

1 Corinthians 11 in the KNFD

1 Corinthians 11 in the LBA

1 Corinthians 11 in the LBLA

1 Corinthians 11 in the LNT

1 Corinthians 11 in the LSV

1 Corinthians 11 in the MAAL

1 Corinthians 11 in the MBV

1 Corinthians 11 in the MBV2

1 Corinthians 11 in the MHNT

1 Corinthians 11 in the MKNFD

1 Corinthians 11 in the MNG

1 Corinthians 11 in the MNT

1 Corinthians 11 in the MNT2

1 Corinthians 11 in the MRS1T

1 Corinthians 11 in the NAA

1 Corinthians 11 in the NASB

1 Corinthians 11 in the NBLA

1 Corinthians 11 in the NBS

1 Corinthians 11 in the NBVTP

1 Corinthians 11 in the NET2

1 Corinthians 11 in the NIV11

1 Corinthians 11 in the NNT

1 Corinthians 11 in the NNT2

1 Corinthians 11 in the NNT3

1 Corinthians 11 in the PDDPT

1 Corinthians 11 in the PFNT

1 Corinthians 11 in the RMNT

1 Corinthians 11 in the SBIAS

1 Corinthians 11 in the SBIBS

1 Corinthians 11 in the SBIBS2

1 Corinthians 11 in the SBICS

1 Corinthians 11 in the SBIDS

1 Corinthians 11 in the SBIGS

1 Corinthians 11 in the SBIHS

1 Corinthians 11 in the SBIIS

1 Corinthians 11 in the SBIIS2

1 Corinthians 11 in the SBIIS3

1 Corinthians 11 in the SBIKS

1 Corinthians 11 in the SBIKS2

1 Corinthians 11 in the SBIMS

1 Corinthians 11 in the SBIOS

1 Corinthians 11 in the SBIPS

1 Corinthians 11 in the SBISS

1 Corinthians 11 in the SBITS

1 Corinthians 11 in the SBITS2

1 Corinthians 11 in the SBITS3

1 Corinthians 11 in the SBITS4

1 Corinthians 11 in the SBIUS

1 Corinthians 11 in the SBIVS

1 Corinthians 11 in the SBT

1 Corinthians 11 in the SBT1E

1 Corinthians 11 in the SCHL

1 Corinthians 11 in the SNT

1 Corinthians 11 in the SUSU

1 Corinthians 11 in the SUSU2

1 Corinthians 11 in the SYNO

1 Corinthians 11 in the TBIAOTANT

1 Corinthians 11 in the TBT1E

1 Corinthians 11 in the TBT1E2

1 Corinthians 11 in the TFTIP

1 Corinthians 11 in the TFTU

1 Corinthians 11 in the TGNTATF3T

1 Corinthians 11 in the THAI

1 Corinthians 11 in the TNFD

1 Corinthians 11 in the TNT

1 Corinthians 11 in the TNTIK

1 Corinthians 11 in the TNTIL

1 Corinthians 11 in the TNTIN

1 Corinthians 11 in the TNTIP

1 Corinthians 11 in the TNTIZ

1 Corinthians 11 in the TOMA

1 Corinthians 11 in the TTENT

1 Corinthians 11 in the UBG

1 Corinthians 11 in the UGV

1 Corinthians 11 in the UGV2

1 Corinthians 11 in the UGV3

1 Corinthians 11 in the VBL

1 Corinthians 11 in the VDCC

1 Corinthians 11 in the YALU

1 Corinthians 11 in the YAPE

1 Corinthians 11 in the YBVTP

1 Corinthians 11 in the ZBP