1 John 3 (BOGWICC)
1 Taonani kukula kwake kwa chikondi chimene Atate anatikonda nacho, kuti titchedwe ana a Mulungu! Ndipo nʼchimene ife tili! Nʼchifukwa chake dziko lapansi silitidziwa chifukwa silinamudziwe Iye. 2 Abale okondedwa, tsopano ndife ana a Mulungu, ndipo sichinaoneke chimene tidzakhala. Koma tikudziwa kuti Yesu akadzaonekera, tidzafanana naye, pakuti tidzamuona Iyeyo monga momwe alili. 3 Aliyense amene ali ndi chiyembekezo ichi mwa Iye adziyeretse yekha, monga Iye ali woyera. 4 Aliyense amene amachimwa amaphwanya lamulo; pakuti tchimo ndi kuphwanya lamulo. 5 Koma inu mukudziwa kuti Yesu anabwera kuti adzachotse machimo athu. Ndipo mwa Iye mulibe tchimo. 6 Aliyense wokhala mwa Khristu sachimwa. Aliyense amene amachimwa sanamuone kapena kumudziwa. 7 Ana okondedwa, musalole kuti aliyense akusocheretseni. Munthu amene amachita chilungamo ndi wolungama, monga Khristu ali wolungama. 8 Iye amene amachimwa ndi wa Satana, chifukwa mdierekezi wakhala akuchimwa kuyambira pa chiyambi. Mwana wa Mulungu anaonekera kuti awononge ntchito za mdierekezi. 9 Aliyense amene ndi mwana wa Mulungu, sachimwirachimwira, popeza mbewu ya Mulungu ili mwa iye, sangathe kuchimwa, chifukwa ndi mwana wa Mulungu. 10 Mmenemu ndi mmene timadziwira ana a Mulungu ndi amene ali ana a mdierekezi. Aliyense amene sachita chilungamo si mwana wa Mulungu; ngakhalenso amene sakonda mʼbale wake. 11 Uthenga umene munawumva kuyambira pachiyambi ndi uwu: Tizikondana wina ndi mnzake. 12 Musakhale ngati Kaini, amene anali wa woyipayo ndipo anapha mʼbale wake. Nanga anamupha chifukwa chiyani? Chifukwa zochita zake zinali zoyipa ndipo zochita za mʼbale wake zinali zolungama. 13 Abale anga, musadabwe ngati dziko lapansi lidana nanu. 14 Ife tikudziwa kuti tinatuluka mu imfa ndi kulowa mʼmoyo, chifukwa timakonda abale athu. Aliyense amene sakonda mʼbale wake akanali mu imfa. 15 Aliyense amene amadana ndi mʼbale wake ndi wakupha, ndipo inu mukudziwa kuti wopha anthu mwa iye mulibe moyo wosatha. 16 Mmene timadziwira chikondi chenicheni ndi umu: Yesu anapereka moyo wake chifukwa cha ife. Ndipo nafenso tiyenera kupereka miyoyo yathu chifukwa cha abale athu. 17 Ngati wina ali ndi chuma ndipo nʼkuona mʼbale wake akusowa, koma wosamvera chisoni, kodi mwa iyeyo muli chikondi cha Mulungu? 18 Ana okondedwa, chikondi chathu chisakhale cha pakamwa pokha koma cha ntchito zathu ndi mʼchoonadi. 19 Pamenepo tidzadziwa kuti tili pa choonadi ndipo tidzakhala okhazikika mtima pamaso pa Mulungu, 20 nthawi zonse pamene mtima wathu utitsutsa. Pakuti Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo Iye amadziwa zonse. 21 Anzanga okondedwa, ngati mitima yathu sikutitsutsa, tili nako kulimbika mtima pamaso pa Mulungu. 22 Ndipo timalandira chilichonse chimene tichipempha kwa Iye, chifukwa timamvera malamulo ake ndi kuchita zimene zimamukondweretsa. 23 Ndipo lamulo lake ndi ili: kukhulupirira dzina la Mwana wake, Yesu Khristu, ndi kukondana wina ndi mnzake monga Iye anatilamulira. 24 Iwo amene amamvera malamulo ake amakhala mwa Iye, ndipo Iye amakhala mwa iwo. Ndipo mmenemu ndi momwe timadziwira kuti Iye akukhala mwa ife. Timadziwa mwa Mzimu Woyera amene anatipatsa.
In Other Versions
1 John 3 in the ANGEFD
1 John 3 in the ANTPNG2D
1 John 3 in the AS21
1 John 3 in the BAGH
1 John 3 in the BBPNG
1 John 3 in the BBT1E
1 John 3 in the BDS
1 John 3 in the BEV
1 John 3 in the BHAD
1 John 3 in the BIB
1 John 3 in the BLPT
1 John 3 in the BNT
1 John 3 in the BNTABOOT
1 John 3 in the BNTLV
1 John 3 in the BOATCB
1 John 3 in the BOATCB2
1 John 3 in the BOBCV
1 John 3 in the BOCNT
1 John 3 in the BOECS
1 John 3 in the BOHCB
1 John 3 in the BOHCV
1 John 3 in the BOHLNT
1 John 3 in the BOHNTLTAL
1 John 3 in the BOICB
1 John 3 in the BOILNTAP
1 John 3 in the BOITCV
1 John 3 in the BOKCV
1 John 3 in the BOKCV2
1 John 3 in the BOKHWOG
1 John 3 in the BOKSSV
1 John 3 in the BOLCB
1 John 3 in the BOLCB2
1 John 3 in the BOMCV
1 John 3 in the BONAV
1 John 3 in the BONCB
1 John 3 in the BONLT
1 John 3 in the BONUT2
1 John 3 in the BOPLNT
1 John 3 in the BOSCB
1 John 3 in the BOSNC
1 John 3 in the BOTLNT
1 John 3 in the BOVCB
1 John 3 in the BOYCB
1 John 3 in the BPBB
1 John 3 in the BPH
1 John 3 in the BSB
1 John 3 in the CCB
1 John 3 in the CUV
1 John 3 in the CUVS
1 John 3 in the DBT
1 John 3 in the DGDNT
1 John 3 in the DHNT
1 John 3 in the DNT
1 John 3 in the ELBE
1 John 3 in the EMTV
1 John 3 in the ESV
1 John 3 in the FBV
1 John 3 in the FEB
1 John 3 in the GGMNT
1 John 3 in the GNT
1 John 3 in the HARY
1 John 3 in the HNT
1 John 3 in the IRVA
1 John 3 in the IRVB
1 John 3 in the IRVG
1 John 3 in the IRVH
1 John 3 in the IRVK
1 John 3 in the IRVM
1 John 3 in the IRVM2
1 John 3 in the IRVO
1 John 3 in the IRVP
1 John 3 in the IRVT
1 John 3 in the IRVT2
1 John 3 in the IRVU
1 John 3 in the ISVN
1 John 3 in the JSNT
1 John 3 in the KAPI
1 John 3 in the KBT1ETNIK
1 John 3 in the KBV
1 John 3 in the KJV
1 John 3 in the KNFD
1 John 3 in the LBA
1 John 3 in the LBLA
1 John 3 in the LNT
1 John 3 in the LSV
1 John 3 in the MAAL
1 John 3 in the MBV
1 John 3 in the MBV2
1 John 3 in the MHNT
1 John 3 in the MKNFD
1 John 3 in the MNG
1 John 3 in the MNT
1 John 3 in the MNT2
1 John 3 in the MRS1T
1 John 3 in the NAA
1 John 3 in the NASB
1 John 3 in the NBLA
1 John 3 in the NBS
1 John 3 in the NBVTP
1 John 3 in the NET2
1 John 3 in the NIV11
1 John 3 in the NNT
1 John 3 in the NNT2
1 John 3 in the NNT3
1 John 3 in the PDDPT
1 John 3 in the PFNT
1 John 3 in the RMNT
1 John 3 in the SBIAS
1 John 3 in the SBIBS
1 John 3 in the SBIBS2
1 John 3 in the SBICS
1 John 3 in the SBIDS
1 John 3 in the SBIGS
1 John 3 in the SBIHS
1 John 3 in the SBIIS
1 John 3 in the SBIIS2
1 John 3 in the SBIIS3
1 John 3 in the SBIKS
1 John 3 in the SBIKS2
1 John 3 in the SBIMS
1 John 3 in the SBIOS
1 John 3 in the SBIPS
1 John 3 in the SBISS
1 John 3 in the SBITS
1 John 3 in the SBITS2
1 John 3 in the SBITS3
1 John 3 in the SBITS4
1 John 3 in the SBIUS
1 John 3 in the SBIVS
1 John 3 in the SBT
1 John 3 in the SBT1E
1 John 3 in the SCHL
1 John 3 in the SNT
1 John 3 in the SUSU
1 John 3 in the SUSU2
1 John 3 in the SYNO
1 John 3 in the TBIAOTANT
1 John 3 in the TBT1E
1 John 3 in the TBT1E2
1 John 3 in the TFTIP
1 John 3 in the TFTU
1 John 3 in the TGNTATF3T
1 John 3 in the THAI
1 John 3 in the TNFD
1 John 3 in the TNT
1 John 3 in the TNTIK
1 John 3 in the TNTIL
1 John 3 in the TNTIN
1 John 3 in the TNTIP
1 John 3 in the TNTIZ
1 John 3 in the TOMA
1 John 3 in the TTENT
1 John 3 in the UBG
1 John 3 in the UGV
1 John 3 in the UGV2
1 John 3 in the UGV3
1 John 3 in the VBL
1 John 3 in the VDCC
1 John 3 in the YALU
1 John 3 in the YAPE
1 John 3 in the YBVTP
1 John 3 in the ZBP