1 Kings 22 (BOGWICC)

1 Kwa zaka zitatu panalibe nkhondo pakati pa Aramu ndi Israeli. 2 Koma pa chaka chachitatu, Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita kukacheza ndi mfumu ya ku Israeli. 3 Mfumu ya ku Israeli nʼkuti itawuza atumiki ake kuti, “Kodi inu simukudziwa kuti Ramoti Giliyadi ndi dera lathu ndipo ife palibe chimene tikuchita kuti tilitenge deralo mʼmanja mwa mfumu ya Aramu?” 4 Tsono iye anafunsa Yehosafati kuti, “Kodi udzapita nane ku nkhondo ku Ramoti Giliyadi?”Yehosafati anayankha mfumu ya ku Israeli kuti, “Ine ndili monga inu, anthu anga monga anthu anu, akavalo anga monga akavalo anu.” 5 Koma Yehosafati anawuzanso mfumu ya ku Israeli kuti, “Poyamba mupemphe nzeru kwa Yehova.” 6 Choncho mfumu ya Israeli inasonkhanitsa pamodzi aneneri okwanira 400, ndipo inawafunsa kuti, “Kodi ndipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena ndileke?”Iwo anayankha kuti, “Pitani, pakuti Ambuye waupereka mzindawo mʼmanja mwa mfumu.” 7 Koma Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi kuno kulibenso mneneri wina wa Yehova kumene ife tingakafunsireko nzeru?” 8 Mfumu ya ku Israeli inayankha Yehosafati kuti, “Alipo munthu mmodzi amene ife tingakafunsire kwa Yehova, koma ndimadana naye chifukwa iyeyo samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa nthawi zonse. Dzina lake ndi Mikaya mwana wa Imula.”Yehosafati anayankha kuti, “Mfumu musatero.” 9 Choncho mfumu ya Israeli inayitana mmodzi mwa atumiki ake ndipo inati, “Kayitane Mikaya mwana wa Imula msangamsanga.” 10 Atavala mikanjo yawo yaufumu, mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anakhala pa mipando yawo yaufumu pabwalo lopondera tirigu pafupi ndi chipata cha Samariya, pamodzi ndi aneneri onse akunenera pamaso pawo. 11 Tsono Zedekiya mwana wa Kenaana nʼkuti atapanga nyanga zachitsulo ndipo iye ananenera kuti, “Yehova akuti, ‘Ndi nyanga izi, inu mudzagunda nazo Aaramu mpaka iwo atawonongeka.’ ” 12 Aneneri ena onse ananenera zomwezonso. Iwo anati, “Kathireni nkhondo Ramoti Giliyadi ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.” 13 Wamthenga amene anapita kukayitana Mikaya anamuwuza kuti, “Taonani, aneneri onse monga munthu mmodzi akunenera za kupambana kwa mfumu. Mawu anunso akhale ogwirizana ndi mawu awo, ndipo mukayankhule zabwino.” 14 Koma Mikaya anati, “Pali Yehova wamoyo, ine ndikawawuza zokhazo zimene Yehova akandiwuze.” 15 Atafika, Ahabu anamufunsa kuti, “Mikaya, kodi tipite kukathira nkhondo Ramoti Giliyadi, kapena tileke?”Iye anayankha kuti, “Pitani ndipo mukapambana, pakuti Yehova adzawupereka mzindawo mʼdzanja la mfumu.” 16 Ahabu anati kwa iye, “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti undiwuze zoona zokhazokha mʼdzina la Yehova?” 17 Pamenepo Mikaya anayankha kuti, “Ndinaona Aisraeli onse atamwazikana pa mapiri ngati nkhosa zopanda mʼbusa, ndipo Yehova anati, ‘Anthu awa alibe mbuye wawo. Aliyense apite kwawo mwamtendere.’ ” 18 Mfumu ya ku Israeli inati kwa Yehosafati, “Kodi ine sindinakuwuzeni kuti ameneyu samanenera kanthu kalikonse kabwino ka ine, koma zoyipa zokhazokha?” 19 Mikaya anapitiriza kuyankhula nati, “Tsono imvani mawu a Yehova: Ine ndinaona Yehova atakhala pa mpando wake waufumu, gulu lonse la kumwamba litayima ku dzanja lake lamanja ndi ku dzanja lake lamanzere. 20 Ndipo Yehova anati, ‘Kodi ndani amene akamukope Ahabu kuti akathire nkhondo Ramoti Giliyadi, nʼkukafera komweko?’ ”“Wina anapereka maganizo ena ndipo winanso maganizo ena. 21 Potsirizira, mzimu wina unabwera ndi kuyima pamaso pa Yehova ndipo unati, ‘Ine ndidzamukopa.’ ” 22 Yehova anafunsa kuti, “Ukamukopa bwanji?”Mzimuwo unati, “Ndidzapita ndi kukakhala mzimu wabodza pakamwa pa aneneri ake onse.”Yehova anati, “ ‘Iwe udzamukopadi. Pita kachite zomwezo.’ 23 “Ndipo tsopano taonani, Yehova wayika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anu onsewa. Yehova waneneratu kuti mukaona mavuto.” 24 Pamenepo Zedekiya mwana wa Kenaana anapita pafupi namenya Mikaya patsaya. Iye anafunsa Mikaya kuti, “Kodi mzimu wa Yehova unadzera njira iti pamene umatuluka mwa ine kuti uziyankhula ndi iwe?” 25 Mikaya anayankha kuti, “Udzaona pa tsiku limene uzikalowa mʼchipinda chamʼkati kuti ukabisale.” 26 Pamenepo mfumu ya ku Israeli inalamula kuti, “Mugwireni Mikaya ndipo mubwerere naye kwa Amoni mkulu wa mzinda, ndi kwa Yowasi mwana wa mfumu 27 ndipo mukanene kuti, ‘Chimene mfumu ikunena ndi ichi; Muyikeni mʼndende munthu uyu ndipo musamupatse chakudya china koma buledi ndi madzi pangʼono mpaka nditabwerera mwamtendere.’ ” 28 Mikaya ananena kuti, “Ngati mudzabwerera mwamtendere, Yehova sanayankhule kudzera mwa ine.” Ndipo iye anapitiriza kunena kuti, “Gwiritsitsani mawu angawa, anthu inu nonse!” 29 Choncho mfumu ya ku Israeli ndi Yehosafati mfumu ya ku Yuda anapita ku Ramoti Giliyadi. 30 Mfumu ya ku Israeli inawuza Yehosafati kuti, “Ine ndidzalowa mu nkhondoyi modzibisa, koma inu muvale zovala zanu zaufumu.” Choncho mfumu ya ku Israeli inadzibisa ndi kupita ku nkhondo. 31 Tsono mfumu ya ku Aramu nʼkuti italamulira anthu ake 32 olamulira magaleta kuti, “Musamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya ku Israeli.” 32 Olamulira magaleta ataona Yehosafati, ankaganiza kuti, “Ndithu iyi ndiye mfumu ya ku Israeli.” Choncho anabwerera kukamenyana naye, koma Yehosafati atafuwula, 33 olamulira akavalo anaona kuti sanali mfumu ya ku Israeli ndipo analeka kumuthamangitsa. 34 Koma munthu wina anaponya muvi wake mwachiponyeponye ndi kulasa mfumu ya ku Israeli polumikizira malaya ake odzitetezera. Mfumu inawuza woyendetsa galeta lake kuti, “Tembenuka ndipo undichotse pa nkhondo pano pakuti ndalasidwa.” 35 Nkhondo inakula kwambiri tsiku limenelo, ndipo mfumu inakhala tsonga mʼgaleta lake moyangʼanana ndi Aaramu. Magazi ake ankayenderera pansi kuchokera mʼgaleta, ndipo pa nthawi ya madzulo inamwalira. 36 Pamene dzuwa linkalowa, kunamveka mfuwu wa nkhondo kuti, “Munthu aliyense apite ku mzinda wa kwawo, aliyense apite ku dziko la kwawo!” 37 Ndipo mfumu ija inafa, nabwera nayo ku Samariya, ndipo anayika mʼmanda kumeneko. 38 Anatsuka galeta lija pa dziwe la ku Samariya (pamene ankasamba akazi achiwerewere) ndipo agalu ananyambita magazi a mfumuyo, monga momwe Yehova ananenera. 39 Tsono ntchito zina za Ahabu, kuphatikiza zonse anazichita, nyumba yaufumu imene anamanga yokutidwa ndi minyanga ya njovu, mizinda yotetezedwa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Israeli? 40 Ahabu anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake. Ndipo Ahaziya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 41 Yehosafati, mwana wa Asa anakhala mfumu ya ku Yuda chaka chachinayi cha Ahabu mfumu ya ku Israeli. 42 Yehosafati anali wa zaka 35 pamene analowa ufumu, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 25. Amayi ake anali Azuba mwana wa Silihi. 43 Pa zinthu zonse, Yehosafati anayenda mʼnjira za Asa abambo ake ndipo sanachite zotsutsana ndi machitidwe a abambo ake. Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova. Komabe, malo azipembedzo sanawawononge, ndipo anthu anapitiriza kupereka nsembe ndi kufukiza lubani kumeneko. 44 Yehosafati anakhala mwamtendere ndi mfumu ya ku Israeli. 45 Ntchito zake zina za Yehosafati, zinthu zimene anachita ndi zamphamvu zimene anaonetsa, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri ya mafumu a ku Yuda? 46 Iye anachotsa mʼdzikomo amuna onse ochita zachiwerewere mwa chipembedzo amene anatsalira pa nthawi ya ulamuliro wa Asa, abambo ake. 47 Nthawi imeneyo kunalibe mfumu ku Edomu, amene ankalamulira anali munthu woyikidwa ndi mfumu ya ku Yuda. 48 Yehosafati anapanga sitima zapamadzi zopita ku Ofiri kukatenga golide, koma sitimazo sizinayende chifukwa zinawonongeka ku Ezioni Geberi. 49 Nthawi imeneyo Ahaziya mwana wa Ahabu anawuza Yehosafati kuti, “Anthu anga ayende pa madzi pamodzi ndi anthu anu,” koma Yehosafati anakana. 50 Ndipo Yehosafati anamwalira nayikidwa mʼmanda pamodzi ndi makolo ake mu mzinda wa Davide. Ndipo Yoramu mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake. 51 Ahaziya mwana wa Ahabu anakhala mfumu ya ku Israeli ku Samariya mʼchaka cha 17 cha Yehosafati mfumu ya ku Yuda, ndipo analamulira Israeli zaka ziwiri. 52 Iye anachita zoyipa pamaso pa Yehova, chifukwa anayenda mʼnjira za abambo ndi amayi ake komanso mʼnjira za Yeroboamu mwana wa Nebati, amene anachimwitsa Israeli. 53 Potumikira ndi kupembedza Baala, iye anakwiyitsa Yehova Mulungu wa Israeli, monga momwe anachitira abambo ake.

In Other Versions

1 Kings 22 in the ANGEFD

1 Kings 22 in the ANTPNG2D

1 Kings 22 in the AS21

1 Kings 22 in the BAGH

1 Kings 22 in the BBPNG

1 Kings 22 in the BBT1E

1 Kings 22 in the BDS

1 Kings 22 in the BEV

1 Kings 22 in the BHAD

1 Kings 22 in the BIB

1 Kings 22 in the BLPT

1 Kings 22 in the BNT

1 Kings 22 in the BNTABOOT

1 Kings 22 in the BNTLV

1 Kings 22 in the BOATCB

1 Kings 22 in the BOATCB2

1 Kings 22 in the BOBCV

1 Kings 22 in the BOCNT

1 Kings 22 in the BOECS

1 Kings 22 in the BOHCB

1 Kings 22 in the BOHCV

1 Kings 22 in the BOHLNT

1 Kings 22 in the BOHNTLTAL

1 Kings 22 in the BOICB

1 Kings 22 in the BOILNTAP

1 Kings 22 in the BOITCV

1 Kings 22 in the BOKCV

1 Kings 22 in the BOKCV2

1 Kings 22 in the BOKHWOG

1 Kings 22 in the BOKSSV

1 Kings 22 in the BOLCB

1 Kings 22 in the BOLCB2

1 Kings 22 in the BOMCV

1 Kings 22 in the BONAV

1 Kings 22 in the BONCB

1 Kings 22 in the BONLT

1 Kings 22 in the BONUT2

1 Kings 22 in the BOPLNT

1 Kings 22 in the BOSCB

1 Kings 22 in the BOSNC

1 Kings 22 in the BOTLNT

1 Kings 22 in the BOVCB

1 Kings 22 in the BOYCB

1 Kings 22 in the BPBB

1 Kings 22 in the BPH

1 Kings 22 in the BSB

1 Kings 22 in the CCB

1 Kings 22 in the CUV

1 Kings 22 in the CUVS

1 Kings 22 in the DBT

1 Kings 22 in the DGDNT

1 Kings 22 in the DHNT

1 Kings 22 in the DNT

1 Kings 22 in the ELBE

1 Kings 22 in the EMTV

1 Kings 22 in the ESV

1 Kings 22 in the FBV

1 Kings 22 in the FEB

1 Kings 22 in the GGMNT

1 Kings 22 in the GNT

1 Kings 22 in the HARY

1 Kings 22 in the HNT

1 Kings 22 in the IRVA

1 Kings 22 in the IRVB

1 Kings 22 in the IRVG

1 Kings 22 in the IRVH

1 Kings 22 in the IRVK

1 Kings 22 in the IRVM

1 Kings 22 in the IRVM2

1 Kings 22 in the IRVO

1 Kings 22 in the IRVP

1 Kings 22 in the IRVT

1 Kings 22 in the IRVT2

1 Kings 22 in the IRVU

1 Kings 22 in the ISVN

1 Kings 22 in the JSNT

1 Kings 22 in the KAPI

1 Kings 22 in the KBT1ETNIK

1 Kings 22 in the KBV

1 Kings 22 in the KJV

1 Kings 22 in the KNFD

1 Kings 22 in the LBA

1 Kings 22 in the LBLA

1 Kings 22 in the LNT

1 Kings 22 in the LSV

1 Kings 22 in the MAAL

1 Kings 22 in the MBV

1 Kings 22 in the MBV2

1 Kings 22 in the MHNT

1 Kings 22 in the MKNFD

1 Kings 22 in the MNG

1 Kings 22 in the MNT

1 Kings 22 in the MNT2

1 Kings 22 in the MRS1T

1 Kings 22 in the NAA

1 Kings 22 in the NASB

1 Kings 22 in the NBLA

1 Kings 22 in the NBS

1 Kings 22 in the NBVTP

1 Kings 22 in the NET2

1 Kings 22 in the NIV11

1 Kings 22 in the NNT

1 Kings 22 in the NNT2

1 Kings 22 in the NNT3

1 Kings 22 in the PDDPT

1 Kings 22 in the PFNT

1 Kings 22 in the RMNT

1 Kings 22 in the SBIAS

1 Kings 22 in the SBIBS

1 Kings 22 in the SBIBS2

1 Kings 22 in the SBICS

1 Kings 22 in the SBIDS

1 Kings 22 in the SBIGS

1 Kings 22 in the SBIHS

1 Kings 22 in the SBIIS

1 Kings 22 in the SBIIS2

1 Kings 22 in the SBIIS3

1 Kings 22 in the SBIKS

1 Kings 22 in the SBIKS2

1 Kings 22 in the SBIMS

1 Kings 22 in the SBIOS

1 Kings 22 in the SBIPS

1 Kings 22 in the SBISS

1 Kings 22 in the SBITS

1 Kings 22 in the SBITS2

1 Kings 22 in the SBITS3

1 Kings 22 in the SBITS4

1 Kings 22 in the SBIUS

1 Kings 22 in the SBIVS

1 Kings 22 in the SBT

1 Kings 22 in the SBT1E

1 Kings 22 in the SCHL

1 Kings 22 in the SNT

1 Kings 22 in the SUSU

1 Kings 22 in the SUSU2

1 Kings 22 in the SYNO

1 Kings 22 in the TBIAOTANT

1 Kings 22 in the TBT1E

1 Kings 22 in the TBT1E2

1 Kings 22 in the TFTIP

1 Kings 22 in the TFTU

1 Kings 22 in the TGNTATF3T

1 Kings 22 in the THAI

1 Kings 22 in the TNFD

1 Kings 22 in the TNT

1 Kings 22 in the TNTIK

1 Kings 22 in the TNTIL

1 Kings 22 in the TNTIN

1 Kings 22 in the TNTIP

1 Kings 22 in the TNTIZ

1 Kings 22 in the TOMA

1 Kings 22 in the TTENT

1 Kings 22 in the UBG

1 Kings 22 in the UGV

1 Kings 22 in the UGV2

1 Kings 22 in the UGV3

1 Kings 22 in the VBL

1 Kings 22 in the VDCC

1 Kings 22 in the YALU

1 Kings 22 in the YAPE

1 Kings 22 in the YBVTP

1 Kings 22 in the ZBP