1 Samuel 22 (BOGWICC)

1 Davide anachoka kumeneko nathawira ku phanga la Adulamu. Abale ake ndi banja lonse la abambo ake anamva izi, anapita kumene kunali Davide. 2 Ndipo aliyense amene anali pa mavuto, kapena ndi ngongole kapenanso amene anali wosakondwa anasonkhana kwa iye, ndipo iye anakhala mtsogoleri wawo. Onse pamodzi analipo amuna 400. 3 Kuchokera kumeneko Davide anapita ku Mizipa ku Mowabu ndipo anapempha mfumu ya Mowabu kuti, “Bwanji abambo ndi amayi anga akhale nanu mpaka ine nditadziwa chimene Mulungu adzachite nane?” 4 Choncho iye anawasiya kwa mfumu ya Mowabu ndipo anakhala naye nthawi yonse imene Davide ankabisala ku phanga kuja. 5 Koma mneneri Gadi anawuza Davide kuti, “Usakhale ku phanga kuno. Pita ku dziko la Yuda.” Kotero Davide anachoka ndi kupita ku nkhalango ya Hereti. 6 Tsono Sauli anamva kuti Davide ndi anthu ake apezeka. Nthawiyo nʼkuti Sauli atakhala pansi pa mtengo wa bwemba pa phiri la ku Gibeya, mkondo uli mʼdzanja lake ndi ankhondo ake atayima chomuzungulira. 7 Tsono Sauli anafunsa ankhondo ake aja kuti, “Tamverani inu anthu a fuko la Benjamini! Kodi mwana wa Yese adzakupatsani nonsenu minda ndi minda ya mpesa? Kodi nonsenu adzakuyikani kukhala atsogoleri a magulu ankhondo? 8 Mwinatu nʼchifukwa chake mwagwirizana zondichita chiwembu. Palibe amene anandiwuza pamene mwana wanga ankapanga pangano ndi mwana wa Yese. Palibe aliyense amene ankalabadirako za ine kapena kundiwuza kuti mwana wanga wautsa mtima wa wantchito wanga kuti andiwukire monga wachitira lero.” 9 Koma Doegi Mwedomu anayima pafupi ndi nduna za Sauli nati, “Ine ndinaona mwana wa Yese atabwera kwa Ahimeleki mwana wa Ahitubi ku Nobi. 10 Ahimelekiyo anafunsa kwa Yehova chomwe Davide ayenera kuchita. Iye anamupatsa zakudya ndiponso lupanga la Goliati Mfilisiti uja.” 11 Pamenepo mfumu inayitanitsa wansembe Ahimeleki mwana wa Ahitubi ndi banja lonse la abambo ake, amene anali ansembe ku Nobi. Ndipo onse anabwera kwa mfumu. 12 Sauli anati, “Tsono tamvera, mwana wa Ahitubi.”Iye anayankha kuti, “Inde mbuye wanga.” 13 Sauli anamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani iwe ndi mwana wa Yese mwandiwukira ine? Wamupatsa buledi ndi lupanga. Wafunsiranso kwa Yehova zoti andiwukire ndi kundibisalira monga wachita leromu?” 14 Ahimeleki anayankha mfumu kuti, “Kodi ndani mwa ankhondo anu onse amene ali wokhulupirika monga Davide? Iye uja ndi mkamwini wa mfumu, kapitawo wa asilikali okutetezani ndiponso munthu amene amalemekezedwa mʼbanja lanu? 15 Kodi tsiku limeneli linali loyamba kuti ndimufunsire kwa Yehova? Ayi sichoncho! Mfumu musandinenere kanthu kalikonse koyipa kapena banja la abambo anga, pakuti sindikudziwa kanthu kena kalikonse ka zimenezi.” 16 Koma mfumu inati, “Iwe Ahimeleki ndi banja lonse la abambo ako mudzaphedwa ndithu.” 17 Kenaka mfumu inalamulira alonda amene anali naye kuti, “Iphani ansembe a Yehovawa chifukwa iwo akugwirizana ndi Davide. Iwo amadziwa kuti Davide ankathawa koma sanandiwuze.”Koma antchito a mfumu aja sanasamule dzanja kuti aphe ansembe a Yehova. 18 Kotero mfumu inalamula Doegi kuti, “Uwaphe ndiwe ansembewa.” Choncho Doegi Mwedomu anapita ndi kuwapha. Tsiku limenelo iye anapha amuna 85 amene amavala efodi wa nsalu yofewa. 19 Kunena za Nobi, mzinda wa ansembe, Sauli anapha amuna ndi amayi, ana ndi makanda pamodzi ndi ngʼombe, abulu ndi nkhosa. 20 Koma Abiatara mwana wa Ahimeleki mwana wa Ahitubi anapulumuka ndi kuthawira kwa Davide. 21 Abiatara anawuza Davide kuti Sauli wapha ansembe a Yehova. 22 Ndipo Davide anati kwa Abiatara, “Tsiku lija pamene Doegi Mwedomu anali kumene kuja, ine ndimadziwa kuti salephera kukamuwuza Sauli. Ine ndi amene ndaphetsa banja lonse la abambo ako. 23 Iwe khala ndi ine, usaope munthu amene akufuna moyo wako komanso wanga. Udzatetezeka ukakhala ndi ine.”

In Other Versions

1 Samuel 22 in the ANGEFD

1 Samuel 22 in the ANTPNG2D

1 Samuel 22 in the AS21

1 Samuel 22 in the BAGH

1 Samuel 22 in the BBPNG

1 Samuel 22 in the BBT1E

1 Samuel 22 in the BDS

1 Samuel 22 in the BEV

1 Samuel 22 in the BHAD

1 Samuel 22 in the BIB

1 Samuel 22 in the BLPT

1 Samuel 22 in the BNT

1 Samuel 22 in the BNTABOOT

1 Samuel 22 in the BNTLV

1 Samuel 22 in the BOATCB

1 Samuel 22 in the BOATCB2

1 Samuel 22 in the BOBCV

1 Samuel 22 in the BOCNT

1 Samuel 22 in the BOECS

1 Samuel 22 in the BOHCB

1 Samuel 22 in the BOHCV

1 Samuel 22 in the BOHLNT

1 Samuel 22 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 22 in the BOICB

1 Samuel 22 in the BOILNTAP

1 Samuel 22 in the BOITCV

1 Samuel 22 in the BOKCV

1 Samuel 22 in the BOKCV2

1 Samuel 22 in the BOKHWOG

1 Samuel 22 in the BOKSSV

1 Samuel 22 in the BOLCB

1 Samuel 22 in the BOLCB2

1 Samuel 22 in the BOMCV

1 Samuel 22 in the BONAV

1 Samuel 22 in the BONCB

1 Samuel 22 in the BONLT

1 Samuel 22 in the BONUT2

1 Samuel 22 in the BOPLNT

1 Samuel 22 in the BOSCB

1 Samuel 22 in the BOSNC

1 Samuel 22 in the BOTLNT

1 Samuel 22 in the BOVCB

1 Samuel 22 in the BOYCB

1 Samuel 22 in the BPBB

1 Samuel 22 in the BPH

1 Samuel 22 in the BSB

1 Samuel 22 in the CCB

1 Samuel 22 in the CUV

1 Samuel 22 in the CUVS

1 Samuel 22 in the DBT

1 Samuel 22 in the DGDNT

1 Samuel 22 in the DHNT

1 Samuel 22 in the DNT

1 Samuel 22 in the ELBE

1 Samuel 22 in the EMTV

1 Samuel 22 in the ESV

1 Samuel 22 in the FBV

1 Samuel 22 in the FEB

1 Samuel 22 in the GGMNT

1 Samuel 22 in the GNT

1 Samuel 22 in the HARY

1 Samuel 22 in the HNT

1 Samuel 22 in the IRVA

1 Samuel 22 in the IRVB

1 Samuel 22 in the IRVG

1 Samuel 22 in the IRVH

1 Samuel 22 in the IRVK

1 Samuel 22 in the IRVM

1 Samuel 22 in the IRVM2

1 Samuel 22 in the IRVO

1 Samuel 22 in the IRVP

1 Samuel 22 in the IRVT

1 Samuel 22 in the IRVT2

1 Samuel 22 in the IRVU

1 Samuel 22 in the ISVN

1 Samuel 22 in the JSNT

1 Samuel 22 in the KAPI

1 Samuel 22 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 22 in the KBV

1 Samuel 22 in the KJV

1 Samuel 22 in the KNFD

1 Samuel 22 in the LBA

1 Samuel 22 in the LBLA

1 Samuel 22 in the LNT

1 Samuel 22 in the LSV

1 Samuel 22 in the MAAL

1 Samuel 22 in the MBV

1 Samuel 22 in the MBV2

1 Samuel 22 in the MHNT

1 Samuel 22 in the MKNFD

1 Samuel 22 in the MNG

1 Samuel 22 in the MNT

1 Samuel 22 in the MNT2

1 Samuel 22 in the MRS1T

1 Samuel 22 in the NAA

1 Samuel 22 in the NASB

1 Samuel 22 in the NBLA

1 Samuel 22 in the NBS

1 Samuel 22 in the NBVTP

1 Samuel 22 in the NET2

1 Samuel 22 in the NIV11

1 Samuel 22 in the NNT

1 Samuel 22 in the NNT2

1 Samuel 22 in the NNT3

1 Samuel 22 in the PDDPT

1 Samuel 22 in the PFNT

1 Samuel 22 in the RMNT

1 Samuel 22 in the SBIAS

1 Samuel 22 in the SBIBS

1 Samuel 22 in the SBIBS2

1 Samuel 22 in the SBICS

1 Samuel 22 in the SBIDS

1 Samuel 22 in the SBIGS

1 Samuel 22 in the SBIHS

1 Samuel 22 in the SBIIS

1 Samuel 22 in the SBIIS2

1 Samuel 22 in the SBIIS3

1 Samuel 22 in the SBIKS

1 Samuel 22 in the SBIKS2

1 Samuel 22 in the SBIMS

1 Samuel 22 in the SBIOS

1 Samuel 22 in the SBIPS

1 Samuel 22 in the SBISS

1 Samuel 22 in the SBITS

1 Samuel 22 in the SBITS2

1 Samuel 22 in the SBITS3

1 Samuel 22 in the SBITS4

1 Samuel 22 in the SBIUS

1 Samuel 22 in the SBIVS

1 Samuel 22 in the SBT

1 Samuel 22 in the SBT1E

1 Samuel 22 in the SCHL

1 Samuel 22 in the SNT

1 Samuel 22 in the SUSU

1 Samuel 22 in the SUSU2

1 Samuel 22 in the SYNO

1 Samuel 22 in the TBIAOTANT

1 Samuel 22 in the TBT1E

1 Samuel 22 in the TBT1E2

1 Samuel 22 in the TFTIP

1 Samuel 22 in the TFTU

1 Samuel 22 in the TGNTATF3T

1 Samuel 22 in the THAI

1 Samuel 22 in the TNFD

1 Samuel 22 in the TNT

1 Samuel 22 in the TNTIK

1 Samuel 22 in the TNTIL

1 Samuel 22 in the TNTIN

1 Samuel 22 in the TNTIP

1 Samuel 22 in the TNTIZ

1 Samuel 22 in the TOMA

1 Samuel 22 in the TTENT

1 Samuel 22 in the UBG

1 Samuel 22 in the UGV

1 Samuel 22 in the UGV2

1 Samuel 22 in the UGV3

1 Samuel 22 in the VBL

1 Samuel 22 in the VDCC

1 Samuel 22 in the YALU

1 Samuel 22 in the YAPE

1 Samuel 22 in the YBVTP

1 Samuel 22 in the ZBP