1 Samuel 30 (BOGWICC)

1 Pa tsiku lachitatu, Davide ndi anthu ake anakafika ku Zikilagi. Tsono anapeza Aamaleki atawononga kale dera la Negevi ndi Zikilagi. Anathira nkhondo mzinda wa Zikilagi ndi kuwutentha ndi moto. 2 Anatenga akazi ndi onse amene anali mʼmenemo akuluakulu ndi angʼono omwe kuti akakhale akapolo. Sanaphe aliyense koma anawatenga amoyo napita nawo. 3 Davide ndi anthu ake atafika ku Zikilagi anapeza kuti mzindawo watenthedwa ndi moto ndipo akazi awo, ana awo, amuna ndi akazi atengedwa ukapolo. 4 Kotero Davide ndi anthu ake analira mofuwula mpaka analibenso mphamvu zolirira. 5 Akazi awiri a Davide, Ahinoamu wa ku Yezireeli ndi Abigayeli mkazi wa Nabala wa ku Karimeli anatengedwanso. 6 Davide anavutika kwambiri mu mtima mwake chifukwa anthu amakamba zoti amuponye miyala popeza aliyense anali ndi chisoni pokumbukira ana ake aamuna ndi aakazi. Koma Davide anapeza mphamvu mwa Yehova Mulungu wake. 7 Kenaka Davide anawuza wansembe Abiatara, mwana wa Ahimeleki kuti, “Ndipatse efodi ija.” Abiatara anabwera nayo efodiyo. 8 Tsono Davide anapempha nzeru kwa Yehova nati, “Kodi ndilitsatire gulu lankhondoli? Kodi ndidzawapambana?”Yehova anayankha kuti, “Litsatire, iwe udzawapambana ndithu ndipo udzapulumutsa anthu ako.” 9 Davide pamodzi ndi anthu ake 600 aja ananyamuka nafika ku mtsinje wa Besori. Kumeneko anasiyako anthu ena. 10 Davide ndi anthu ake 400 anapitirira kuwalondola Aamaleki aja. Koma anthu ena 200 anatsala popeza anatopa moti sakanatha kuwoloka mtsinje wa Besori uja. 11 Anthu amene anali ndi Davide anapeza Mwigupto mʼmunda wina ndipo anabwera naye kwa Davide. Iwo anamupatsa madzi kuti amwe ndi chakudya kuti adye. 12 Anamupatsanso chidutswa cha keke yankhuyu ndi makeke awiri a mphesa zowumika kuti adye. Atadya anapezanso mphamvu popeza anakhala masiku atatu wosadya kapena kumwa kanthu kalikonse. 13 Davide anafunsa kuti, “Kodi ndiwe yani, ndipo ukuchokera kuti?”Iye anayankha kuti, “Ine ndine Mwigupto, kapolo wa Mwamaleki. Mbuye wanga anandisiya nditayamba kudwala masiku atatu apitawo. 14 Ife tinathira nkhondo dera la kummwera kwa mayiko a Akereti, dera la Yuda, ndi dera la kummwera kwa mayiko a Kalebe. Mzinda wa Zikilagi tinawutentha ndi moto.” 15 Davide anamupempha kuti, “Kodi unganditsogolere kumene kuli gulu lankhondoli?”Iye anayankha kuti, “Mukandilonjeza molumbira kuti simudzandipha kapena kundipereka kwa mbuye wanga, ine ndikulondolerani kumene kuli gululo.” 16 Mwigupto uja anaperekeza Davide. Tsono Aamaleki anali atamwazikana ponseponse. Iwo ankadya, kumwa ndi kuvina chifukwa cha zofunkha zambiri zimene anatenga ku dziko la Afilisti ndi ku dziko la Ayuda. 17 Tsono Davide anawakantha kuyambira madzulo atsikulo mpaka madzulo a tsiku linalo. Palibe anapulumuka kupatula anyamata 400 amene anakwera pa ngamira nʼkuthawa. 18 Choncho Davide analanditsa zinthu zonse zimene Aamaleki aja anatenga. Anapulumutsanso akazi ake awiri aja. 19 Palibe chimene chinasowa anthu onse, kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, mnyamata mpaka mtsikana anapulumutsidwa. Davide anapulumutsa chilichonse chimene anafunkha Aamaleki aja. 20 Anapulumutsanso nkhosa ndi ngʼombe zonse. Tsono anthu ankakusa ziwetozo namati, “Izi ndizo zofunkha za Davide.” 21 Davide anafika ku malo kumene kunali anthu 200 otopa kwambiri aja amene sanathe kutsagana naye koma anangokhala ku mtsinje wa Besori. Tsono ananyamuka kuti akumane ndi Davide pamodzi ndi anthu amene anali naye. Davide anawayandikira nawalonjera. 22 Tsono anthu ena oyipa mtima achabechabe mwa amene anatsagana ndi Davide aja anati, “Popeza awa sanapite nafe, sitiwapatsako zofunkha zimene tapulumutsazi, kupatula kuti aliyense atenge mkazi wake ndi ana ake azipita.” 23 Koma Davide anawayankha kuti, “Ayi, abale anga, musachite zimenezi ndi zinthu zimene Yehova watipatsa. Iye watisunga ndi kupereka mʼmanja mwathu gulu la ankhondo limene linabwera kudzalimbana nafe. 24 Ndani angakumvereni zimene mukunenazi? Gawo la munthu amene anapita kukamenya nkhondo likhale lofanana ndi la munthu amene anatsala pano kuyangʼanira katundu wathu. Pasakhale kusiyana kulikonse.” 25 Choncho Davide anakhazikitsa ngati lamulo mʼchitidwe woterewu pakati pa Aisraeli kuyambira tsiku limenelo mpaka lero. 26 Davide atafika ku Zikilagi, anatumiza zina mwa zofunkhazo kwa akuluakulu a Yuda, amene anali abwenzi ake. Anati, “Nayi mphatso yanu yochokera pa zofunkha za adani a Yehova.” 27 Iye anatumiza mphatsozo kwa anthu a ku Beteli, Ramoti-Negavi, Yatiri, 28 Aroeri, Sifimoti, Esitemowa 29 Rakala, mizinda ya fuko la Ayerahimeeli, mizinda ya fuko la Akeni, 30 a ku Horima, Borasani, Ataki, 31 Hebroni pamodzi ndi onse a kumalo kumene Davide ndi anthu ake anakhala akuyendayendako.

In Other Versions

1 Samuel 30 in the ANGEFD

1 Samuel 30 in the ANTPNG2D

1 Samuel 30 in the AS21

1 Samuel 30 in the BAGH

1 Samuel 30 in the BBPNG

1 Samuel 30 in the BBT1E

1 Samuel 30 in the BDS

1 Samuel 30 in the BEV

1 Samuel 30 in the BHAD

1 Samuel 30 in the BIB

1 Samuel 30 in the BLPT

1 Samuel 30 in the BNT

1 Samuel 30 in the BNTABOOT

1 Samuel 30 in the BNTLV

1 Samuel 30 in the BOATCB

1 Samuel 30 in the BOATCB2

1 Samuel 30 in the BOBCV

1 Samuel 30 in the BOCNT

1 Samuel 30 in the BOECS

1 Samuel 30 in the BOHCB

1 Samuel 30 in the BOHCV

1 Samuel 30 in the BOHLNT

1 Samuel 30 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 30 in the BOICB

1 Samuel 30 in the BOILNTAP

1 Samuel 30 in the BOITCV

1 Samuel 30 in the BOKCV

1 Samuel 30 in the BOKCV2

1 Samuel 30 in the BOKHWOG

1 Samuel 30 in the BOKSSV

1 Samuel 30 in the BOLCB

1 Samuel 30 in the BOLCB2

1 Samuel 30 in the BOMCV

1 Samuel 30 in the BONAV

1 Samuel 30 in the BONCB

1 Samuel 30 in the BONLT

1 Samuel 30 in the BONUT2

1 Samuel 30 in the BOPLNT

1 Samuel 30 in the BOSCB

1 Samuel 30 in the BOSNC

1 Samuel 30 in the BOTLNT

1 Samuel 30 in the BOVCB

1 Samuel 30 in the BOYCB

1 Samuel 30 in the BPBB

1 Samuel 30 in the BPH

1 Samuel 30 in the BSB

1 Samuel 30 in the CCB

1 Samuel 30 in the CUV

1 Samuel 30 in the CUVS

1 Samuel 30 in the DBT

1 Samuel 30 in the DGDNT

1 Samuel 30 in the DHNT

1 Samuel 30 in the DNT

1 Samuel 30 in the ELBE

1 Samuel 30 in the EMTV

1 Samuel 30 in the ESV

1 Samuel 30 in the FBV

1 Samuel 30 in the FEB

1 Samuel 30 in the GGMNT

1 Samuel 30 in the GNT

1 Samuel 30 in the HARY

1 Samuel 30 in the HNT

1 Samuel 30 in the IRVA

1 Samuel 30 in the IRVB

1 Samuel 30 in the IRVG

1 Samuel 30 in the IRVH

1 Samuel 30 in the IRVK

1 Samuel 30 in the IRVM

1 Samuel 30 in the IRVM2

1 Samuel 30 in the IRVO

1 Samuel 30 in the IRVP

1 Samuel 30 in the IRVT

1 Samuel 30 in the IRVT2

1 Samuel 30 in the IRVU

1 Samuel 30 in the ISVN

1 Samuel 30 in the JSNT

1 Samuel 30 in the KAPI

1 Samuel 30 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 30 in the KBV

1 Samuel 30 in the KJV

1 Samuel 30 in the KNFD

1 Samuel 30 in the LBA

1 Samuel 30 in the LBLA

1 Samuel 30 in the LNT

1 Samuel 30 in the LSV

1 Samuel 30 in the MAAL

1 Samuel 30 in the MBV

1 Samuel 30 in the MBV2

1 Samuel 30 in the MHNT

1 Samuel 30 in the MKNFD

1 Samuel 30 in the MNG

1 Samuel 30 in the MNT

1 Samuel 30 in the MNT2

1 Samuel 30 in the MRS1T

1 Samuel 30 in the NAA

1 Samuel 30 in the NASB

1 Samuel 30 in the NBLA

1 Samuel 30 in the NBS

1 Samuel 30 in the NBVTP

1 Samuel 30 in the NET2

1 Samuel 30 in the NIV11

1 Samuel 30 in the NNT

1 Samuel 30 in the NNT2

1 Samuel 30 in the NNT3

1 Samuel 30 in the PDDPT

1 Samuel 30 in the PFNT

1 Samuel 30 in the RMNT

1 Samuel 30 in the SBIAS

1 Samuel 30 in the SBIBS

1 Samuel 30 in the SBIBS2

1 Samuel 30 in the SBICS

1 Samuel 30 in the SBIDS

1 Samuel 30 in the SBIGS

1 Samuel 30 in the SBIHS

1 Samuel 30 in the SBIIS

1 Samuel 30 in the SBIIS2

1 Samuel 30 in the SBIIS3

1 Samuel 30 in the SBIKS

1 Samuel 30 in the SBIKS2

1 Samuel 30 in the SBIMS

1 Samuel 30 in the SBIOS

1 Samuel 30 in the SBIPS

1 Samuel 30 in the SBISS

1 Samuel 30 in the SBITS

1 Samuel 30 in the SBITS2

1 Samuel 30 in the SBITS3

1 Samuel 30 in the SBITS4

1 Samuel 30 in the SBIUS

1 Samuel 30 in the SBIVS

1 Samuel 30 in the SBT

1 Samuel 30 in the SBT1E

1 Samuel 30 in the SCHL

1 Samuel 30 in the SNT

1 Samuel 30 in the SUSU

1 Samuel 30 in the SUSU2

1 Samuel 30 in the SYNO

1 Samuel 30 in the TBIAOTANT

1 Samuel 30 in the TBT1E

1 Samuel 30 in the TBT1E2

1 Samuel 30 in the TFTIP

1 Samuel 30 in the TFTU

1 Samuel 30 in the TGNTATF3T

1 Samuel 30 in the THAI

1 Samuel 30 in the TNFD

1 Samuel 30 in the TNT

1 Samuel 30 in the TNTIK

1 Samuel 30 in the TNTIL

1 Samuel 30 in the TNTIN

1 Samuel 30 in the TNTIP

1 Samuel 30 in the TNTIZ

1 Samuel 30 in the TOMA

1 Samuel 30 in the TTENT

1 Samuel 30 in the UBG

1 Samuel 30 in the UGV

1 Samuel 30 in the UGV2

1 Samuel 30 in the UGV3

1 Samuel 30 in the VBL

1 Samuel 30 in the VDCC

1 Samuel 30 in the YALU

1 Samuel 30 in the YAPE

1 Samuel 30 in the YBVTP

1 Samuel 30 in the ZBP