1 Samuel 6 (BOGWICC)

1 Bokosi la Yehova linakhala mʼdziko la Afilisti kwa miyezi isanu ndi iwiri. 2 Tsono Afilisti anayitana ansembe ndi amawula ndipo anati, “Tichite nalo chiyani Bokosi la Yehova? Tiwuzeni momwe tidzalitumizira ku malo ake.” 3 Iwo anayankha kuti, “Ngati mufuna kubweza Bokosi la Mulungu wa Israeli, musalitumize wopanda kanthu, koma muyesetse kulitumiza pamodzi ndi nsembe yopepesera machimo. Mukatero mudzachiritsidwa, ndipo mudzadziwa chifukwa chiyani chilango cha Yehova sichikukuchokani.” 4 Afilisti anafunsanso kuti “Kodi ife tipereke nsembe yanji yopepesera machimo?”Iwo anayankha kuti, “Mupereke zifanizo zagolide za zithupsa zisanu ndi zamakoswe asanu malingana ndi chiwerengero cha akalonga a Afilisti popeza mliri womwewo wagwera inu ndi akalonga anu. 5 Mupange zifanizo za zithupsa zisanu ndi za makoswe asanu amene akuwononga dziko lanu ndipo mupereke ulemu kwa Israeli. Mwina adzaleka kuzunza inu, milungu yanu ndi dziko lanu. 6 Nʼchifukwa chiyani mukuwumitsa mitima monga anachita Aigupto ndi Farao? Mulungu atawalanga anthu a ku Igupto aja kodi suja anawalola Aisraeli kuti azipita ndipo anapitadi? 7 “Tsopano konzani galeta latsopano limodzi ndiponso ngʼombe ziwiri zazikazi zamkaka zimene sizinavalepo goli. Muzimangirire ngʼombezo ku ngoloyo, koma ana awo muwachotse ndi kuwasiya kwanu. 8 Mutenge Bokosi la Yehova ndi kuliyika pa galetapo ndipo pambali pake pakhale Bokosi, mʼmene muyikemonso zinthu zagolide zomwe mukutumiza kwa Iye monga nsembe yopepesera machimo. Kenaka, mulisiye lizipita. 9 Koma muziliyangʼana. Ngati lilondola njira yopita kwawo kwa Bokosilo mpaka ku Beti-Semesi ndiye kuti amene watichita zoyipa zazikulu zoterezi ndi Mulungu wa Israeli. Koma ngati silitero, ife tidzadziwa kuti sanali Mulungu wa Israeli amene watizunza koma kuti zinangochitika mwatsoka.” 10 Anthu aja anachitadi zimenezi. Anatenga ngʼombe zamkaka ziwiri nazimanga ku galeta lija. Koma ana awo anawatsekera mʼkhola. 11 Tsono anayika Bokosi la Yehova pa galeta pamodzi ndi bokosi limene munali makoswe agolide ndi zifanizo zawo za zithupsa. 12 Ngʼombe zija zinapita molunjika kutsata msewu wopita ku Beti Semesi zikulira njira yonse. Sizinakhotere kumanja kapena kumanzere. Akalonga a Afilisti anazitsatira mpaka mʼmalire a Beti-Semesi. 13 Nthawi imeneyi anthu a ku Beti-Semesi amakolola tirigu mʼchigwa ndipo pamene anayangʼana ndi kuona Bokosi la Chipangano likubwera anakondwa. 14 Galeta lija linafika ku munda wa Yoswa ku Beti-Semesi ndipo linayima. Kumeneko kunali mwala waukulu. Tsono anthu anawaza nkhuni galetalo, ndipo anapha ngʼombe zija ndi kuzipereka ngati nsembe zopsereza kwa Yehova. 15 Alevi nʼkuti atatsitsa Bokosi la Yehova, pamodzi ndi bokosi mmene munali zinthu zagolide, ndipo anawayika pa mwala uja waukulu. Tsiku limenelo anthu a ku Beti-Semesi anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Yehova. 16 Atsogoleri asanu a Afilisti ataona izi anabwerera ku Ekroni tsiku lomwelo. 17 Zifanizo zagolide za zithupsa zimene Afilisti anatumiza ngati nsembe zopepesera machimo kwa Yehova zinkayimirira mizinda isanu iyi motere: chimodzi cha ku Asidodi, china cha ku Gaza ndi zina za ku Asikeloni, Gati ndi Ekroni. 18 Ndipo chiwerengero cha zifanizo za makoswe chinali chofanana ndi chiwerengero cha mizinda ya akalonga asanu a Afilisti. Mizindayi inali yotetezedwa bwino ndi ina yapamtetete. Mwala waukulu umene anayikapo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼmunda mwa Yoswa ku Beti-Semesi uli ngati mboni mpaka lero. 19 Yehova anakantha amuna a ku Beti-Semesi 70 chifukwa anasuzumira mʼBokosi la Chipangano cha Yehova. Ndipo anzawo analira chifukwa Yehova anawalanga kwambiri. 20 Tsono anthu a ku Beti-Semesi anafunsa, “Ndani angathe kuyima pamaso pa Yehova Mulungu Woyera? Bokosi la Chipanganoli lipita kuti likachoka pano?” 21 Tsono iwo anatumiza a mithenga kwa anthu a ku Kiriati-Yearimu kuti, “Afilisti atibwezera Bokosi la Yehova. Bwerani kuno mudzalitenge, mupite nalo kwanuko.”

In Other Versions

1 Samuel 6 in the ANGEFD

1 Samuel 6 in the ANTPNG2D

1 Samuel 6 in the AS21

1 Samuel 6 in the BAGH

1 Samuel 6 in the BBPNG

1 Samuel 6 in the BBT1E

1 Samuel 6 in the BDS

1 Samuel 6 in the BEV

1 Samuel 6 in the BHAD

1 Samuel 6 in the BIB

1 Samuel 6 in the BLPT

1 Samuel 6 in the BNT

1 Samuel 6 in the BNTABOOT

1 Samuel 6 in the BNTLV

1 Samuel 6 in the BOATCB

1 Samuel 6 in the BOATCB2

1 Samuel 6 in the BOBCV

1 Samuel 6 in the BOCNT

1 Samuel 6 in the BOECS

1 Samuel 6 in the BOHCB

1 Samuel 6 in the BOHCV

1 Samuel 6 in the BOHLNT

1 Samuel 6 in the BOHNTLTAL

1 Samuel 6 in the BOICB

1 Samuel 6 in the BOILNTAP

1 Samuel 6 in the BOITCV

1 Samuel 6 in the BOKCV

1 Samuel 6 in the BOKCV2

1 Samuel 6 in the BOKHWOG

1 Samuel 6 in the BOKSSV

1 Samuel 6 in the BOLCB

1 Samuel 6 in the BOLCB2

1 Samuel 6 in the BOMCV

1 Samuel 6 in the BONAV

1 Samuel 6 in the BONCB

1 Samuel 6 in the BONLT

1 Samuel 6 in the BONUT2

1 Samuel 6 in the BOPLNT

1 Samuel 6 in the BOSCB

1 Samuel 6 in the BOSNC

1 Samuel 6 in the BOTLNT

1 Samuel 6 in the BOVCB

1 Samuel 6 in the BOYCB

1 Samuel 6 in the BPBB

1 Samuel 6 in the BPH

1 Samuel 6 in the BSB

1 Samuel 6 in the CCB

1 Samuel 6 in the CUV

1 Samuel 6 in the CUVS

1 Samuel 6 in the DBT

1 Samuel 6 in the DGDNT

1 Samuel 6 in the DHNT

1 Samuel 6 in the DNT

1 Samuel 6 in the ELBE

1 Samuel 6 in the EMTV

1 Samuel 6 in the ESV

1 Samuel 6 in the FBV

1 Samuel 6 in the FEB

1 Samuel 6 in the GGMNT

1 Samuel 6 in the GNT

1 Samuel 6 in the HARY

1 Samuel 6 in the HNT

1 Samuel 6 in the IRVA

1 Samuel 6 in the IRVB

1 Samuel 6 in the IRVG

1 Samuel 6 in the IRVH

1 Samuel 6 in the IRVK

1 Samuel 6 in the IRVM

1 Samuel 6 in the IRVM2

1 Samuel 6 in the IRVO

1 Samuel 6 in the IRVP

1 Samuel 6 in the IRVT

1 Samuel 6 in the IRVT2

1 Samuel 6 in the IRVU

1 Samuel 6 in the ISVN

1 Samuel 6 in the JSNT

1 Samuel 6 in the KAPI

1 Samuel 6 in the KBT1ETNIK

1 Samuel 6 in the KBV

1 Samuel 6 in the KJV

1 Samuel 6 in the KNFD

1 Samuel 6 in the LBA

1 Samuel 6 in the LBLA

1 Samuel 6 in the LNT

1 Samuel 6 in the LSV

1 Samuel 6 in the MAAL

1 Samuel 6 in the MBV

1 Samuel 6 in the MBV2

1 Samuel 6 in the MHNT

1 Samuel 6 in the MKNFD

1 Samuel 6 in the MNG

1 Samuel 6 in the MNT

1 Samuel 6 in the MNT2

1 Samuel 6 in the MRS1T

1 Samuel 6 in the NAA

1 Samuel 6 in the NASB

1 Samuel 6 in the NBLA

1 Samuel 6 in the NBS

1 Samuel 6 in the NBVTP

1 Samuel 6 in the NET2

1 Samuel 6 in the NIV11

1 Samuel 6 in the NNT

1 Samuel 6 in the NNT2

1 Samuel 6 in the NNT3

1 Samuel 6 in the PDDPT

1 Samuel 6 in the PFNT

1 Samuel 6 in the RMNT

1 Samuel 6 in the SBIAS

1 Samuel 6 in the SBIBS

1 Samuel 6 in the SBIBS2

1 Samuel 6 in the SBICS

1 Samuel 6 in the SBIDS

1 Samuel 6 in the SBIGS

1 Samuel 6 in the SBIHS

1 Samuel 6 in the SBIIS

1 Samuel 6 in the SBIIS2

1 Samuel 6 in the SBIIS3

1 Samuel 6 in the SBIKS

1 Samuel 6 in the SBIKS2

1 Samuel 6 in the SBIMS

1 Samuel 6 in the SBIOS

1 Samuel 6 in the SBIPS

1 Samuel 6 in the SBISS

1 Samuel 6 in the SBITS

1 Samuel 6 in the SBITS2

1 Samuel 6 in the SBITS3

1 Samuel 6 in the SBITS4

1 Samuel 6 in the SBIUS

1 Samuel 6 in the SBIVS

1 Samuel 6 in the SBT

1 Samuel 6 in the SBT1E

1 Samuel 6 in the SCHL

1 Samuel 6 in the SNT

1 Samuel 6 in the SUSU

1 Samuel 6 in the SUSU2

1 Samuel 6 in the SYNO

1 Samuel 6 in the TBIAOTANT

1 Samuel 6 in the TBT1E

1 Samuel 6 in the TBT1E2

1 Samuel 6 in the TFTIP

1 Samuel 6 in the TFTU

1 Samuel 6 in the TGNTATF3T

1 Samuel 6 in the THAI

1 Samuel 6 in the TNFD

1 Samuel 6 in the TNT

1 Samuel 6 in the TNTIK

1 Samuel 6 in the TNTIL

1 Samuel 6 in the TNTIN

1 Samuel 6 in the TNTIP

1 Samuel 6 in the TNTIZ

1 Samuel 6 in the TOMA

1 Samuel 6 in the TTENT

1 Samuel 6 in the UBG

1 Samuel 6 in the UGV

1 Samuel 6 in the UGV2

1 Samuel 6 in the UGV3

1 Samuel 6 in the VBL

1 Samuel 6 in the VDCC

1 Samuel 6 in the YALU

1 Samuel 6 in the YAPE

1 Samuel 6 in the YBVTP

1 Samuel 6 in the ZBP