1 Samuel 8 (BOGWICC)
1 Samueli atakalamba anasankha ana ake kuti akhale oweruza Aisraeli. 2 Mwana wake woyamba anali Yoweli, wachiwiri anali Abiya, ndipo ankaweruza ku Beeriseba. 3 Koma ana akewo sanatengere makhalidwe ake abwino. Iwo ankapotokera ku zoyipa namatsata phindu mwachinyengo. Ankalandira ziphuphu ndi kumaweruza mwachinyengo. 4 Tsono akuluakulu onse a Israeli anasonkhana pamodzi ndipo anabwera kwa Samueli ku Rama. 5 Iwo anati kwa iye “Taonani, inu mwakula tsopano ndipo ana anu sakutsata makhalidwe anu abwino. Tsono mutipatse mfumu kuti izitilamulira, monga momwe ikuchitira mitundu ina yonseyi.” 6 Koma mawu oti, “Mutipatse mfumu kuti izitilamulira,” sanakondweretse Samueli. Choncho anapemphera kwa Yehova. 7 Yehova anamuyankha nati, “Mvera zonse zimene anthuwa akukuwuza. Si ndiwe amene akumukana, koma akukana Ine kuti ndikhale mfumu yawo. 8 Kuyambira tsiku limene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto mpaka lero zochita zawo zakhala zondikana Ine nʼkumatumikira milungu ina. Tsopano akukukananso iwe. 9 Tsono amvere zimene akunena, koma uwachenjeze kwambiri ndipo uwawuzitse za khalidwe la mfumu imene idzawalamulire.” 10 Samueli anawawuza anthu amene amamupempha mfumu aja mawu onse a Yehova. 11 Iye anati, “Zimene mfumu imene idzakulamulireniyo idzachite ndi izi: Izidzatenga ana anu aamuna kuti akhale ankhondo ake; ena pa magaleta ake, ena pa akavalo ake ndipo ena othamanga patsogolo pa magaleta akewo. 12 Ena adzawayika kukhala olamulira asilikali 1,000, ena olamulira asilikali makumi asanu, ndi ena otipula minda yake, ndi kukolola ndiponso ena adzakhala osula zida zankhondo ndi zida za magaleta ake. 13 Iyo idzatenga ana anu akazi kuti akhale oyenga mafuta onunkhira, ophika chakudya ndi kupanga buledi. 14 Idzatenga minda yanu yabwino ya mpesa ndi ya mitengo ya olivi ndipo adzayipereka kwa antchito ake. 15 Idzatenga gawo lakhumi la tirigu wanu ndi mphesa zanu ndi kupereka kwa nduna zake ndi akapitawo ake. 16 Mfumuyo idzatenga antchito anu aamuna ndi aakazi. Idzatenganso ngʼombe zanu zabwino ndi abulu anu nʼkumazingwiritsa ntchito. 17 Iyo idzatenga gawo lakhumi la zoweta zanu, ndipo inu eni mudzakhala akapolo ake. 18 Nthawi imeneyo ikadzafika inu mudzalira momvetsa chisoni chifukwa cha mfumu imene mwadzisankhira, koma Yehova sadzakuyankhani.” 19 Koma anthu anakana kumumvera Samueli. Iwo anati, “Ayi! Ife tikufuna mfumu yotilamulira. 20 Kotero ifenso tidzakhala ngati mayiko ena. Mfumu yathu idzatiweruza ndiponso idzatuluka nafe kutitsogolera kukamenya nkhondo.” 21 Samueli atamva zonse zimene anthuwo ananena, iye anakazifotokozanso kwa Yehova. 22 Yehova anamuyankha nati, “Amvere zimene akunena ndipo apatse mfumu.”Ndipo Samueli anati kwa Aisraeli aja, “Bwererani aliyense kwawo.”
In Other Versions
1 Samuel 8 in the ANGEFD
1 Samuel 8 in the ANTPNG2D
1 Samuel 8 in the AS21
1 Samuel 8 in the BAGH
1 Samuel 8 in the BBPNG
1 Samuel 8 in the BBT1E
1 Samuel 8 in the BDS
1 Samuel 8 in the BEV
1 Samuel 8 in the BHAD
1 Samuel 8 in the BIB
1 Samuel 8 in the BLPT
1 Samuel 8 in the BNT
1 Samuel 8 in the BNTABOOT
1 Samuel 8 in the BNTLV
1 Samuel 8 in the BOATCB
1 Samuel 8 in the BOATCB2
1 Samuel 8 in the BOBCV
1 Samuel 8 in the BOCNT
1 Samuel 8 in the BOECS
1 Samuel 8 in the BOHCB
1 Samuel 8 in the BOHCV
1 Samuel 8 in the BOHLNT
1 Samuel 8 in the BOHNTLTAL
1 Samuel 8 in the BOICB
1 Samuel 8 in the BOILNTAP
1 Samuel 8 in the BOITCV
1 Samuel 8 in the BOKCV
1 Samuel 8 in the BOKCV2
1 Samuel 8 in the BOKHWOG
1 Samuel 8 in the BOKSSV
1 Samuel 8 in the BOLCB
1 Samuel 8 in the BOLCB2
1 Samuel 8 in the BOMCV
1 Samuel 8 in the BONAV
1 Samuel 8 in the BONCB
1 Samuel 8 in the BONLT
1 Samuel 8 in the BONUT2
1 Samuel 8 in the BOPLNT
1 Samuel 8 in the BOSCB
1 Samuel 8 in the BOSNC
1 Samuel 8 in the BOTLNT
1 Samuel 8 in the BOVCB
1 Samuel 8 in the BOYCB
1 Samuel 8 in the BPBB
1 Samuel 8 in the BPH
1 Samuel 8 in the BSB
1 Samuel 8 in the CCB
1 Samuel 8 in the CUV
1 Samuel 8 in the CUVS
1 Samuel 8 in the DBT
1 Samuel 8 in the DGDNT
1 Samuel 8 in the DHNT
1 Samuel 8 in the DNT
1 Samuel 8 in the ELBE
1 Samuel 8 in the EMTV
1 Samuel 8 in the ESV
1 Samuel 8 in the FBV
1 Samuel 8 in the FEB
1 Samuel 8 in the GGMNT
1 Samuel 8 in the GNT
1 Samuel 8 in the HARY
1 Samuel 8 in the HNT
1 Samuel 8 in the IRVA
1 Samuel 8 in the IRVB
1 Samuel 8 in the IRVG
1 Samuel 8 in the IRVH
1 Samuel 8 in the IRVK
1 Samuel 8 in the IRVM
1 Samuel 8 in the IRVM2
1 Samuel 8 in the IRVO
1 Samuel 8 in the IRVP
1 Samuel 8 in the IRVT
1 Samuel 8 in the IRVT2
1 Samuel 8 in the IRVU
1 Samuel 8 in the ISVN
1 Samuel 8 in the JSNT
1 Samuel 8 in the KAPI
1 Samuel 8 in the KBT1ETNIK
1 Samuel 8 in the KBV
1 Samuel 8 in the KJV
1 Samuel 8 in the KNFD
1 Samuel 8 in the LBA
1 Samuel 8 in the LBLA
1 Samuel 8 in the LNT
1 Samuel 8 in the LSV
1 Samuel 8 in the MAAL
1 Samuel 8 in the MBV
1 Samuel 8 in the MBV2
1 Samuel 8 in the MHNT
1 Samuel 8 in the MKNFD
1 Samuel 8 in the MNG
1 Samuel 8 in the MNT
1 Samuel 8 in the MNT2
1 Samuel 8 in the MRS1T
1 Samuel 8 in the NAA
1 Samuel 8 in the NASB
1 Samuel 8 in the NBLA
1 Samuel 8 in the NBS
1 Samuel 8 in the NBVTP
1 Samuel 8 in the NET2
1 Samuel 8 in the NIV11
1 Samuel 8 in the NNT
1 Samuel 8 in the NNT2
1 Samuel 8 in the NNT3
1 Samuel 8 in the PDDPT
1 Samuel 8 in the PFNT
1 Samuel 8 in the RMNT
1 Samuel 8 in the SBIAS
1 Samuel 8 in the SBIBS
1 Samuel 8 in the SBIBS2
1 Samuel 8 in the SBICS
1 Samuel 8 in the SBIDS
1 Samuel 8 in the SBIGS
1 Samuel 8 in the SBIHS
1 Samuel 8 in the SBIIS
1 Samuel 8 in the SBIIS2
1 Samuel 8 in the SBIIS3
1 Samuel 8 in the SBIKS
1 Samuel 8 in the SBIKS2
1 Samuel 8 in the SBIMS
1 Samuel 8 in the SBIOS
1 Samuel 8 in the SBIPS
1 Samuel 8 in the SBISS
1 Samuel 8 in the SBITS
1 Samuel 8 in the SBITS2
1 Samuel 8 in the SBITS3
1 Samuel 8 in the SBITS4
1 Samuel 8 in the SBIUS
1 Samuel 8 in the SBIVS
1 Samuel 8 in the SBT
1 Samuel 8 in the SBT1E
1 Samuel 8 in the SCHL
1 Samuel 8 in the SNT
1 Samuel 8 in the SUSU
1 Samuel 8 in the SUSU2
1 Samuel 8 in the SYNO
1 Samuel 8 in the TBIAOTANT
1 Samuel 8 in the TBT1E
1 Samuel 8 in the TBT1E2
1 Samuel 8 in the TFTIP
1 Samuel 8 in the TFTU
1 Samuel 8 in the TGNTATF3T
1 Samuel 8 in the THAI
1 Samuel 8 in the TNFD
1 Samuel 8 in the TNT
1 Samuel 8 in the TNTIK
1 Samuel 8 in the TNTIL
1 Samuel 8 in the TNTIN
1 Samuel 8 in the TNTIP
1 Samuel 8 in the TNTIZ
1 Samuel 8 in the TOMA
1 Samuel 8 in the TTENT
1 Samuel 8 in the UBG
1 Samuel 8 in the UGV
1 Samuel 8 in the UGV2
1 Samuel 8 in the UGV3
1 Samuel 8 in the VBL
1 Samuel 8 in the VDCC
1 Samuel 8 in the YALU
1 Samuel 8 in the YAPE
1 Samuel 8 in the YBVTP
1 Samuel 8 in the ZBP