1 Timothy 4 (BOGWICC)
1 Mzimu akunena momveka bwino kuti mʼmasiku otsiriza anthu ena adzataya chikhulupiriro chawo ndi kutsatira mizimu yonyenga ndi zinthu zophunzitsidwa ndi ziwanda. 2 Ziphunzitso zimenezi zimachokera ku chinyengo cha anthu onama, amene chikumbumtima chawo chinamatidwa ndi chitsulo cha moto. 3 Iwo amaletsa anthu ukwati ndi kuwalamula kuti asamadye zakudya zina, zimene Mulungu analenga kuti amene anakhulupirira ndi kudziwa choonadi, azidye moyamika. 4 Pakuti chilichonse chimene Mulungu analenga ndi chabwino, ndipo chilichonse chisasalidwe, akamachilandira moyamika, 5 pakuti chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndi pemphero. 6 Ngati abale uwalangiza zimenezi, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu, woleredwa mʼchoonadi cha chikhulupiriro ndi mʼchiphunzitso chabwino chimene wakhala ukutsata. 7 Koma upewe nkhani zachabe ndi nthano za amayi okalamba; mʼmalo mwake udziphunzitse kukhala moyo wolemekeza Mulungu. 8 Pakuti kulimbitsa thupi kumapindulitsapo pangʼono, koma moyo woopa Mulungu umapindulitsa pa zonse. Umatilonjeza moyo pa moyo uno ndiponso pa moyo umene ukubwerawo. 9 Amenewa ndi mawu odalirika ndi oyenera kuwalandira kwathunthu. 10 Nʼchifukwa chake timagwira ntchito molimbika ndi kuyesetsa, chifukwa tayika chiyembekezo chathu mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi wa anthu onse, koma makamaka wa amene amakhulupirira. 11 Lamulira ndi kuphunzitsa zinthu zimenezi. 12 Usalole kuti wina akupeputse chifukwa ndiwe wachinyamata, koma khala chitsanzo kwa okhulupirira pa mayankhulidwe, pa makhalidwe, pa chikondi, pa chikhulupiriro ndi pa kuyera mtima. 13 Mpaka nditabwera, udzipereke powerenga mawu a Mulungu kwa anthu, kulalikira ndi kuphunzitsa. 14 Usanyozere mphatso yako yomwe inapatsidwa kwa iwe kudzera mʼmawu auneneri pamene gulu la akulu ampingo linakusanjika manja. 15 Uzichita zimenezi mosamalitsa ndi modzipereka kwathunthu, kuti aliyense aone kuti ukupita mʼtsogolo. 16 Samala kwambiri moyo wako ndi ziphunzitso zako. Uzichitabe zimenezi chifukwa ukatero, udzadzipulumutsa ndiponso udzapulumutsa okumvetsera.
In Other Versions
1 Timothy 4 in the ANGEFD
1 Timothy 4 in the ANTPNG2D
1 Timothy 4 in the AS21
1 Timothy 4 in the BAGH
1 Timothy 4 in the BBPNG
1 Timothy 4 in the BBT1E
1 Timothy 4 in the BDS
1 Timothy 4 in the BEV
1 Timothy 4 in the BHAD
1 Timothy 4 in the BIB
1 Timothy 4 in the BLPT
1 Timothy 4 in the BNT
1 Timothy 4 in the BNTABOOT
1 Timothy 4 in the BNTLV
1 Timothy 4 in the BOATCB
1 Timothy 4 in the BOATCB2
1 Timothy 4 in the BOBCV
1 Timothy 4 in the BOCNT
1 Timothy 4 in the BOECS
1 Timothy 4 in the BOHCB
1 Timothy 4 in the BOHCV
1 Timothy 4 in the BOHLNT
1 Timothy 4 in the BOHNTLTAL
1 Timothy 4 in the BOICB
1 Timothy 4 in the BOILNTAP
1 Timothy 4 in the BOITCV
1 Timothy 4 in the BOKCV
1 Timothy 4 in the BOKCV2
1 Timothy 4 in the BOKHWOG
1 Timothy 4 in the BOKSSV
1 Timothy 4 in the BOLCB
1 Timothy 4 in the BOLCB2
1 Timothy 4 in the BOMCV
1 Timothy 4 in the BONAV
1 Timothy 4 in the BONCB
1 Timothy 4 in the BONLT
1 Timothy 4 in the BONUT2
1 Timothy 4 in the BOPLNT
1 Timothy 4 in the BOSCB
1 Timothy 4 in the BOSNC
1 Timothy 4 in the BOTLNT
1 Timothy 4 in the BOVCB
1 Timothy 4 in the BOYCB
1 Timothy 4 in the BPBB
1 Timothy 4 in the BPH
1 Timothy 4 in the BSB
1 Timothy 4 in the CCB
1 Timothy 4 in the CUV
1 Timothy 4 in the CUVS
1 Timothy 4 in the DBT
1 Timothy 4 in the DGDNT
1 Timothy 4 in the DHNT
1 Timothy 4 in the DNT
1 Timothy 4 in the ELBE
1 Timothy 4 in the EMTV
1 Timothy 4 in the ESV
1 Timothy 4 in the FBV
1 Timothy 4 in the FEB
1 Timothy 4 in the GGMNT
1 Timothy 4 in the GNT
1 Timothy 4 in the HARY
1 Timothy 4 in the HNT
1 Timothy 4 in the IRVA
1 Timothy 4 in the IRVB
1 Timothy 4 in the IRVG
1 Timothy 4 in the IRVH
1 Timothy 4 in the IRVK
1 Timothy 4 in the IRVM
1 Timothy 4 in the IRVM2
1 Timothy 4 in the IRVO
1 Timothy 4 in the IRVP
1 Timothy 4 in the IRVT
1 Timothy 4 in the IRVT2
1 Timothy 4 in the IRVU
1 Timothy 4 in the ISVN
1 Timothy 4 in the JSNT
1 Timothy 4 in the KAPI
1 Timothy 4 in the KBT1ETNIK
1 Timothy 4 in the KBV
1 Timothy 4 in the KJV
1 Timothy 4 in the KNFD
1 Timothy 4 in the LBA
1 Timothy 4 in the LBLA
1 Timothy 4 in the LNT
1 Timothy 4 in the LSV
1 Timothy 4 in the MAAL
1 Timothy 4 in the MBV
1 Timothy 4 in the MBV2
1 Timothy 4 in the MHNT
1 Timothy 4 in the MKNFD
1 Timothy 4 in the MNG
1 Timothy 4 in the MNT
1 Timothy 4 in the MNT2
1 Timothy 4 in the MRS1T
1 Timothy 4 in the NAA
1 Timothy 4 in the NASB
1 Timothy 4 in the NBLA
1 Timothy 4 in the NBS
1 Timothy 4 in the NBVTP
1 Timothy 4 in the NET2
1 Timothy 4 in the NIV11
1 Timothy 4 in the NNT
1 Timothy 4 in the NNT2
1 Timothy 4 in the NNT3
1 Timothy 4 in the PDDPT
1 Timothy 4 in the PFNT
1 Timothy 4 in the RMNT
1 Timothy 4 in the SBIAS
1 Timothy 4 in the SBIBS
1 Timothy 4 in the SBIBS2
1 Timothy 4 in the SBICS
1 Timothy 4 in the SBIDS
1 Timothy 4 in the SBIGS
1 Timothy 4 in the SBIHS
1 Timothy 4 in the SBIIS
1 Timothy 4 in the SBIIS2
1 Timothy 4 in the SBIIS3
1 Timothy 4 in the SBIKS
1 Timothy 4 in the SBIKS2
1 Timothy 4 in the SBIMS
1 Timothy 4 in the SBIOS
1 Timothy 4 in the SBIPS
1 Timothy 4 in the SBISS
1 Timothy 4 in the SBITS
1 Timothy 4 in the SBITS2
1 Timothy 4 in the SBITS3
1 Timothy 4 in the SBITS4
1 Timothy 4 in the SBIUS
1 Timothy 4 in the SBIVS
1 Timothy 4 in the SBT
1 Timothy 4 in the SBT1E
1 Timothy 4 in the SCHL
1 Timothy 4 in the SNT
1 Timothy 4 in the SUSU
1 Timothy 4 in the SUSU2
1 Timothy 4 in the SYNO
1 Timothy 4 in the TBIAOTANT
1 Timothy 4 in the TBT1E
1 Timothy 4 in the TBT1E2
1 Timothy 4 in the TFTIP
1 Timothy 4 in the TFTU
1 Timothy 4 in the TGNTATF3T
1 Timothy 4 in the THAI
1 Timothy 4 in the TNFD
1 Timothy 4 in the TNT
1 Timothy 4 in the TNTIK
1 Timothy 4 in the TNTIL
1 Timothy 4 in the TNTIN
1 Timothy 4 in the TNTIP
1 Timothy 4 in the TNTIZ
1 Timothy 4 in the TOMA
1 Timothy 4 in the TTENT
1 Timothy 4 in the UBG
1 Timothy 4 in the UGV
1 Timothy 4 in the UGV2
1 Timothy 4 in the UGV3
1 Timothy 4 in the VBL
1 Timothy 4 in the VDCC
1 Timothy 4 in the YALU
1 Timothy 4 in the YAPE
1 Timothy 4 in the YBVTP
1 Timothy 4 in the ZBP