2 Chronicles 1 (BOGWICC)

1 Solomoni mwana wa Davide anakhazikika molimbika mu ufumu wake, pakuti Yehova Mulungu wake anali naye ndipo anamukweza kwambiri. 2 Tsono Solomoni anayankhula kwa Aisraeli onse, olamulira a anthu 1,000, olamulira a anthu 100, oweruza ndiponso kwa atsogoleri onse a Israeli ndi atsogoleri amabanja. 3 Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la anthu anapita ku malo ofunika kwambiri pachipembedzo ku Gibiyoni. Tenti ya msonkhano ya Mulungu inali kumeneko, imene Mose mtumiki wa Yehova anayipanga mʼchipululu muja. 4 Davide anabweretsa Bokosi la Mulungu kuchokera ku Kiriyati Yearimu, ndi kulikhazika kumalo kumene analikonzera popeza analimangira tenti mu Yerusalemu. 5 Koma guwa lansembe lamkuwa limene Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huri analipanga linali ku Gibiyoni kutsogolo kwa tenti ya Yehova. Kotero kuti Solomoni ndi gulu lonse anakapembedza kumeneko. 6 Solomoni anapita pamene panali guwa lansembe lamkuwa pamaso pa Yehova mu tenti ya msonkhano ndipo anapereka nsembe zopsereza 1,000. 7 Usiku umenewo Mulungu anaonekera kwa Solomoni ndipo anati kwa iye, “Pempha chilichonse chimene ukufuna ndipo ndidzakupatsa.” 8 Solomoni anayankha Mulungu kuti, “Inu munaonetsa kukoma mtima kwakukulu kwa Davide abambo anga ndipo mwayika ine kukhala mfumu mʼmalo mwake. 9 Tsopano Inu Yehova Mulungu, lolani kuti lonjezo lanu kwa abambo anga Davide likwaniritsidwe, pakuti mwandiyika kukhala mfumu ya anthu anu amene ndi ochuluka ngati fumbi la pa dziko lapansi. 10 Mundipatse nzeru ndi luntha zolamulira anthu awa, pakuti ndani amene angathe kulamulira anthu anu ochulukawa?” 11 Mulungu anati kwa Solomoni, “Popeza izi ndi zokhumba za mtima wako ndipo sunapemphe katundu, chuma kapena ulemu, kapena imfa ya adani ako, ndiponso poti sunapemphe moyo wautali koma nzeru ndi luntha kuti ulamulire anthu anga amene Ine ndakuyika kukhala mfumu yawo, 12 Ine ndidzakupatsa nzeru ndi chidziwitso. Ndipo ndidzakupatsanso katundu, chuma ndi ulemu, zinthu zoti palibe mfumu imene inali nazo iwe usanakhalepo ndipo palibe wina amene adzakhale nazo iweyo ukadzafa.” 13 Kotero Solomoni anabwerera ku Yerusalemu kuchoka kumalo opembedzerako a ku Gibiyoni, ku tenti ya msonkhano ndipo analamulira Israeli. 14 Solomoni anasonkhanitsa magaleta ndi akavalo; anali ndi magaleta 1,400 ndi akavalo 12,000, amene anawayika mʼmizinda yosungira magaleta ndipo ena anali ndi iye mu Yerusalemu. 15 Mfumu inasandutsa siliva ndi golide kukhala ngati miyala wamba mu Yerusalemu. Inasandutsanso mkungudza kukhala wochuluka ngati mitengo ya mkuyu ya ku zigwa. 16 Solomoni amagula akavalo ku Igupto ndi Kuwe pakuti anthu amalonda a mfumu amakawagula ku Kuwe. 17 Anthu ankagula galeta ku Igupto pa mtengo wa masekeli asiliva 600 ndipo kavalo pa mtengo wa ndalama zasiliva 150. Iwo ankazigulitsanso kwa mafumu onse a Ahiti ndi a Aramu.

In Other Versions

2 Chronicles 1 in the ANGEFD

2 Chronicles 1 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 1 in the AS21

2 Chronicles 1 in the BAGH

2 Chronicles 1 in the BBPNG

2 Chronicles 1 in the BBT1E

2 Chronicles 1 in the BDS

2 Chronicles 1 in the BEV

2 Chronicles 1 in the BHAD

2 Chronicles 1 in the BIB

2 Chronicles 1 in the BLPT

2 Chronicles 1 in the BNT

2 Chronicles 1 in the BNTABOOT

2 Chronicles 1 in the BNTLV

2 Chronicles 1 in the BOATCB

2 Chronicles 1 in the BOATCB2

2 Chronicles 1 in the BOBCV

2 Chronicles 1 in the BOCNT

2 Chronicles 1 in the BOECS

2 Chronicles 1 in the BOHCB

2 Chronicles 1 in the BOHCV

2 Chronicles 1 in the BOHLNT

2 Chronicles 1 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 1 in the BOICB

2 Chronicles 1 in the BOILNTAP

2 Chronicles 1 in the BOITCV

2 Chronicles 1 in the BOKCV

2 Chronicles 1 in the BOKCV2

2 Chronicles 1 in the BOKHWOG

2 Chronicles 1 in the BOKSSV

2 Chronicles 1 in the BOLCB

2 Chronicles 1 in the BOLCB2

2 Chronicles 1 in the BOMCV

2 Chronicles 1 in the BONAV

2 Chronicles 1 in the BONCB

2 Chronicles 1 in the BONLT

2 Chronicles 1 in the BONUT2

2 Chronicles 1 in the BOPLNT

2 Chronicles 1 in the BOSCB

2 Chronicles 1 in the BOSNC

2 Chronicles 1 in the BOTLNT

2 Chronicles 1 in the BOVCB

2 Chronicles 1 in the BOYCB

2 Chronicles 1 in the BPBB

2 Chronicles 1 in the BPH

2 Chronicles 1 in the BSB

2 Chronicles 1 in the CCB

2 Chronicles 1 in the CUV

2 Chronicles 1 in the CUVS

2 Chronicles 1 in the DBT

2 Chronicles 1 in the DGDNT

2 Chronicles 1 in the DHNT

2 Chronicles 1 in the DNT

2 Chronicles 1 in the ELBE

2 Chronicles 1 in the EMTV

2 Chronicles 1 in the ESV

2 Chronicles 1 in the FBV

2 Chronicles 1 in the FEB

2 Chronicles 1 in the GGMNT

2 Chronicles 1 in the GNT

2 Chronicles 1 in the HARY

2 Chronicles 1 in the HNT

2 Chronicles 1 in the IRVA

2 Chronicles 1 in the IRVB

2 Chronicles 1 in the IRVG

2 Chronicles 1 in the IRVH

2 Chronicles 1 in the IRVK

2 Chronicles 1 in the IRVM

2 Chronicles 1 in the IRVM2

2 Chronicles 1 in the IRVO

2 Chronicles 1 in the IRVP

2 Chronicles 1 in the IRVT

2 Chronicles 1 in the IRVT2

2 Chronicles 1 in the IRVU

2 Chronicles 1 in the ISVN

2 Chronicles 1 in the JSNT

2 Chronicles 1 in the KAPI

2 Chronicles 1 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 1 in the KBV

2 Chronicles 1 in the KJV

2 Chronicles 1 in the KNFD

2 Chronicles 1 in the LBA

2 Chronicles 1 in the LBLA

2 Chronicles 1 in the LNT

2 Chronicles 1 in the LSV

2 Chronicles 1 in the MAAL

2 Chronicles 1 in the MBV

2 Chronicles 1 in the MBV2

2 Chronicles 1 in the MHNT

2 Chronicles 1 in the MKNFD

2 Chronicles 1 in the MNG

2 Chronicles 1 in the MNT

2 Chronicles 1 in the MNT2

2 Chronicles 1 in the MRS1T

2 Chronicles 1 in the NAA

2 Chronicles 1 in the NASB

2 Chronicles 1 in the NBLA

2 Chronicles 1 in the NBS

2 Chronicles 1 in the NBVTP

2 Chronicles 1 in the NET2

2 Chronicles 1 in the NIV11

2 Chronicles 1 in the NNT

2 Chronicles 1 in the NNT2

2 Chronicles 1 in the NNT3

2 Chronicles 1 in the PDDPT

2 Chronicles 1 in the PFNT

2 Chronicles 1 in the RMNT

2 Chronicles 1 in the SBIAS

2 Chronicles 1 in the SBIBS

2 Chronicles 1 in the SBIBS2

2 Chronicles 1 in the SBICS

2 Chronicles 1 in the SBIDS

2 Chronicles 1 in the SBIGS

2 Chronicles 1 in the SBIHS

2 Chronicles 1 in the SBIIS

2 Chronicles 1 in the SBIIS2

2 Chronicles 1 in the SBIIS3

2 Chronicles 1 in the SBIKS

2 Chronicles 1 in the SBIKS2

2 Chronicles 1 in the SBIMS

2 Chronicles 1 in the SBIOS

2 Chronicles 1 in the SBIPS

2 Chronicles 1 in the SBISS

2 Chronicles 1 in the SBITS

2 Chronicles 1 in the SBITS2

2 Chronicles 1 in the SBITS3

2 Chronicles 1 in the SBITS4

2 Chronicles 1 in the SBIUS

2 Chronicles 1 in the SBIVS

2 Chronicles 1 in the SBT

2 Chronicles 1 in the SBT1E

2 Chronicles 1 in the SCHL

2 Chronicles 1 in the SNT

2 Chronicles 1 in the SUSU

2 Chronicles 1 in the SUSU2

2 Chronicles 1 in the SYNO

2 Chronicles 1 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 1 in the TBT1E

2 Chronicles 1 in the TBT1E2

2 Chronicles 1 in the TFTIP

2 Chronicles 1 in the TFTU

2 Chronicles 1 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 1 in the THAI

2 Chronicles 1 in the TNFD

2 Chronicles 1 in the TNT

2 Chronicles 1 in the TNTIK

2 Chronicles 1 in the TNTIL

2 Chronicles 1 in the TNTIN

2 Chronicles 1 in the TNTIP

2 Chronicles 1 in the TNTIZ

2 Chronicles 1 in the TOMA

2 Chronicles 1 in the TTENT

2 Chronicles 1 in the UBG

2 Chronicles 1 in the UGV

2 Chronicles 1 in the UGV2

2 Chronicles 1 in the UGV3

2 Chronicles 1 in the VBL

2 Chronicles 1 in the VDCC

2 Chronicles 1 in the YALU

2 Chronicles 1 in the YAPE

2 Chronicles 1 in the YBVTP

2 Chronicles 1 in the ZBP