2 Chronicles 12 (BOGWICC)

1 Rehobowamu atakhazikika monga mfumu nakhaladi wamphamvu, iyeyo pamodzi ndi Aisraeli onse anasiya malamulo a Yehova. 2 Chifukwa anakhala osakhulupirika pamaso pa Yehova, Sisaki mfumu ya dziko la Igupto inathira nkhondo Yerusalemu mʼchaka chachisanu cha mfumu Rehobowamu. 3 Sisakiyo anabwera ndi magaleta 1,200 ndi anthu okwera akavalo 60,000 ndiponso asilikali osawerengeka ochokera ku Libiya, Suki ndi Kusi amene anabwera naye kuchokera ku Igupto. 4 Iye analanda mizinda yotetezedwa ya Yuda ndipo anafika mpaka ku Yerusalemu. 5 Ndipo mneneri Semaya anabwera kwa Rehobowamu ndi kwa atsogoleri a Yuda amene anasonkhana mu Yerusalemu chifukwa cha Sisaki ndipo iye anawawuza kuti, “Yehova akuti, ‘Inu mwandisiya, choncho Inenso ndakusiyani ndi kukuperekani kwa Sisaki.’ ” 6 Atsogoleri a Israeli pamodzi ndi mfumu anadzichepetsa nati, “Yehova ndi wolungama.” 7 Yehova ataona kuti adzichepetsa, anayankhula ndi Semaya kuti, “Pakuti adzichepetsa, Ine sindiwawononga koma posachedwapa ndiwapulumutsa. Sinditsanulira ukali wanga pa Yerusalemu kudzera mwa Sisaki. 8 Komabe iwo adzakhala pansi pa ulamuliro wake, kuti aphunzire kudziwa kusiyanitsa pakati pa kutumikira Ine ndi kutumikira mafumu a mayiko ena.” 9 Sisaki mfumu ya dziko la Igupto atathira nkhondo Yerusalemu, iye anatenga chuma cha mʼNyumba ya Yehova ndi chuma cha mʼnyumba yaufumu. Iye anatenga zinthu zonse kuphatikizapo zishango zagolide zimene Solomoni anapanga. 10 Ndipo mfumu inapereka zishango zamkuwa kwa oyangʼanira mʼmalo mwake ndipo iwo anazipereka kwa oyangʼanira alonda amene amayangʼanira pa chipata cha nyumba yaufumu. 11 Nthawi ina iliyonse imene mfumu ikupita ku Nyumba ya Yehova, alonda amapita nayo atanyamula zishango, ndipo kenaka amakazibwezera ku chipinda cha alonda. 12 Pakuti mfumu Rehobowamu inadzichepetsa, mkwiyo wa Yehova unamuchokera, sanawonongedweretu. Kunena zoona, munali zinthu zina zabwino mu Yuda. 13 Mfumu Rehobowamu anayika maziko a ufumu wake mwamphamvu mu Yerusalemu ndipo anapitirira kukhala mfumu. Iye anali ndi zaka 41 pamene anakhala mfumu, ndipo analamulira zaka 17 mu Yerusalemu, mzinda wa Yehova umene anasankha pakati pa mafuko a Aisraeli mmene Yehova anakhazikikamo. Dzina la amayi ake linali Naama, amene anali Mwamoni. 14 Rehobowamu anachita zoyipa chifuwa mtima wake sunafunefune Yehova. 15 Ntchito za Rehobowamu, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, kodi sizinalembedwe mʼbuku la mbiri la mneneri Semaya ndi mlosi Ido amene amalemba mbiri? Panali nkhondo yosatha pakati pa Rehobowamu ndi Yeroboamu. 16 Rehobowamu anamwalira, ndipo anayikidwa mʼmanda mu mzinda wa Davide. Ndipo mwana wake Abiya analowa ufumu mʼmalo wake.

In Other Versions

2 Chronicles 12 in the ANGEFD

2 Chronicles 12 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 12 in the AS21

2 Chronicles 12 in the BAGH

2 Chronicles 12 in the BBPNG

2 Chronicles 12 in the BBT1E

2 Chronicles 12 in the BDS

2 Chronicles 12 in the BEV

2 Chronicles 12 in the BHAD

2 Chronicles 12 in the BIB

2 Chronicles 12 in the BLPT

2 Chronicles 12 in the BNT

2 Chronicles 12 in the BNTABOOT

2 Chronicles 12 in the BNTLV

2 Chronicles 12 in the BOATCB

2 Chronicles 12 in the BOATCB2

2 Chronicles 12 in the BOBCV

2 Chronicles 12 in the BOCNT

2 Chronicles 12 in the BOECS

2 Chronicles 12 in the BOHCB

2 Chronicles 12 in the BOHCV

2 Chronicles 12 in the BOHLNT

2 Chronicles 12 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 12 in the BOICB

2 Chronicles 12 in the BOILNTAP

2 Chronicles 12 in the BOITCV

2 Chronicles 12 in the BOKCV

2 Chronicles 12 in the BOKCV2

2 Chronicles 12 in the BOKHWOG

2 Chronicles 12 in the BOKSSV

2 Chronicles 12 in the BOLCB

2 Chronicles 12 in the BOLCB2

2 Chronicles 12 in the BOMCV

2 Chronicles 12 in the BONAV

2 Chronicles 12 in the BONCB

2 Chronicles 12 in the BONLT

2 Chronicles 12 in the BONUT2

2 Chronicles 12 in the BOPLNT

2 Chronicles 12 in the BOSCB

2 Chronicles 12 in the BOSNC

2 Chronicles 12 in the BOTLNT

2 Chronicles 12 in the BOVCB

2 Chronicles 12 in the BOYCB

2 Chronicles 12 in the BPBB

2 Chronicles 12 in the BPH

2 Chronicles 12 in the BSB

2 Chronicles 12 in the CCB

2 Chronicles 12 in the CUV

2 Chronicles 12 in the CUVS

2 Chronicles 12 in the DBT

2 Chronicles 12 in the DGDNT

2 Chronicles 12 in the DHNT

2 Chronicles 12 in the DNT

2 Chronicles 12 in the ELBE

2 Chronicles 12 in the EMTV

2 Chronicles 12 in the ESV

2 Chronicles 12 in the FBV

2 Chronicles 12 in the FEB

2 Chronicles 12 in the GGMNT

2 Chronicles 12 in the GNT

2 Chronicles 12 in the HARY

2 Chronicles 12 in the HNT

2 Chronicles 12 in the IRVA

2 Chronicles 12 in the IRVB

2 Chronicles 12 in the IRVG

2 Chronicles 12 in the IRVH

2 Chronicles 12 in the IRVK

2 Chronicles 12 in the IRVM

2 Chronicles 12 in the IRVM2

2 Chronicles 12 in the IRVO

2 Chronicles 12 in the IRVP

2 Chronicles 12 in the IRVT

2 Chronicles 12 in the IRVT2

2 Chronicles 12 in the IRVU

2 Chronicles 12 in the ISVN

2 Chronicles 12 in the JSNT

2 Chronicles 12 in the KAPI

2 Chronicles 12 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 12 in the KBV

2 Chronicles 12 in the KJV

2 Chronicles 12 in the KNFD

2 Chronicles 12 in the LBA

2 Chronicles 12 in the LBLA

2 Chronicles 12 in the LNT

2 Chronicles 12 in the LSV

2 Chronicles 12 in the MAAL

2 Chronicles 12 in the MBV

2 Chronicles 12 in the MBV2

2 Chronicles 12 in the MHNT

2 Chronicles 12 in the MKNFD

2 Chronicles 12 in the MNG

2 Chronicles 12 in the MNT

2 Chronicles 12 in the MNT2

2 Chronicles 12 in the MRS1T

2 Chronicles 12 in the NAA

2 Chronicles 12 in the NASB

2 Chronicles 12 in the NBLA

2 Chronicles 12 in the NBS

2 Chronicles 12 in the NBVTP

2 Chronicles 12 in the NET2

2 Chronicles 12 in the NIV11

2 Chronicles 12 in the NNT

2 Chronicles 12 in the NNT2

2 Chronicles 12 in the NNT3

2 Chronicles 12 in the PDDPT

2 Chronicles 12 in the PFNT

2 Chronicles 12 in the RMNT

2 Chronicles 12 in the SBIAS

2 Chronicles 12 in the SBIBS

2 Chronicles 12 in the SBIBS2

2 Chronicles 12 in the SBICS

2 Chronicles 12 in the SBIDS

2 Chronicles 12 in the SBIGS

2 Chronicles 12 in the SBIHS

2 Chronicles 12 in the SBIIS

2 Chronicles 12 in the SBIIS2

2 Chronicles 12 in the SBIIS3

2 Chronicles 12 in the SBIKS

2 Chronicles 12 in the SBIKS2

2 Chronicles 12 in the SBIMS

2 Chronicles 12 in the SBIOS

2 Chronicles 12 in the SBIPS

2 Chronicles 12 in the SBISS

2 Chronicles 12 in the SBITS

2 Chronicles 12 in the SBITS2

2 Chronicles 12 in the SBITS3

2 Chronicles 12 in the SBITS4

2 Chronicles 12 in the SBIUS

2 Chronicles 12 in the SBIVS

2 Chronicles 12 in the SBT

2 Chronicles 12 in the SBT1E

2 Chronicles 12 in the SCHL

2 Chronicles 12 in the SNT

2 Chronicles 12 in the SUSU

2 Chronicles 12 in the SUSU2

2 Chronicles 12 in the SYNO

2 Chronicles 12 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 12 in the TBT1E

2 Chronicles 12 in the TBT1E2

2 Chronicles 12 in the TFTIP

2 Chronicles 12 in the TFTU

2 Chronicles 12 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 12 in the THAI

2 Chronicles 12 in the TNFD

2 Chronicles 12 in the TNT

2 Chronicles 12 in the TNTIK

2 Chronicles 12 in the TNTIL

2 Chronicles 12 in the TNTIN

2 Chronicles 12 in the TNTIP

2 Chronicles 12 in the TNTIZ

2 Chronicles 12 in the TOMA

2 Chronicles 12 in the TTENT

2 Chronicles 12 in the UBG

2 Chronicles 12 in the UGV

2 Chronicles 12 in the UGV2

2 Chronicles 12 in the UGV3

2 Chronicles 12 in the VBL

2 Chronicles 12 in the VDCC

2 Chronicles 12 in the YALU

2 Chronicles 12 in the YAPE

2 Chronicles 12 in the YBVTP

2 Chronicles 12 in the ZBP