2 Chronicles 28 (BOGWICC)

1 Ahazi anali ndi zaka makumi awiri pamene anakhala mfumu ndipo analamulira mu Yerusalemu kwa zaka 16. Iye sanachite zolungama pamaso pa Yehova, monga momwe anachitira Davide kholo lake. 2 Iye anayenda mʼnjira za mafumu a Israeli ndipo anawumbanso mafano a chipembedzo cha Abaala. 3 Iye amapsereza nsembe ku chigwa cha Hinomu, ndipo anaperekanso ana ake aamuna ngati nsembe yopsereza kutsatira njira zonyansa za mitundu imene Yehova anayithamangitsa pamaso pa Aisraeli. 4 Iyeyo ankapereka nsembe ndi kufukiza lubani pa malo opembedzerapo mafano, pamwamba pa mapiri ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu. 5 Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wake anamupereka mʼmanja mwa mfumu ya Aramu. Aaramu anamugonjetsa ndipo anagwira ukapolo anthu ake ambiri napita nawo ku Damasiko.Yehova anamuperekanso mʼmanja mwa mfumu ya Israeli, imene inamuzunza ndi kumuphera anthu ake ambiri. 6 Pa tsiku limodzi, Peka mwana wa Remaliya anapha asilikali 120,000 mu Yuda chifukwa Yuda anasiya Yehova, Mulungu wa makolo awo. 7 Zikiri msilikali wa ku Efereimu, anapha Maaseya mwana wa mfumu, Azirikamu woyangʼanira nyumba yaufumu, ndi Elikana wachiwiri kwa mfumu. 8 Aisraeli anagwira ukapolo abale awo, akazi, ana aamuna ndi ana aakazi okwanira 200,000. Iwo anafunkhanso katundu wambiri amene anapita naye ku Samariya. 9 Koma kumeneko kunali mneneri wa Yehova dzina lake Odedi, ndipo anapita kukakumana ndi gulu lankhondo pamene linabwerera ku Samariya. Iye anawawuza kuti, “Chifukwa Yehova, Mulungu wa makolo anu anakwiyira Ayuda, Iye anawapereka mʼdzanja lanu. Koma inu mwawapha mwaukali, ukali wake wofika mpaka kumwamba. 10 Ndipo tsopano mukufuna kuti amuna ndi akazi a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akhale akapolo anu. 11 Tsono mvereni! Abwezeni abale anu amene mwawagwira ukapolo, pakuti mkwiyo wa Yehova uli pa inu.” 12 Tsono atsogoleri ena a ku Efereimu, Azariya mwana wa Yehohanani, Berekiya mwana wa Mesilemoti, Yehizikiya mwana wa Salumu, ndi Amasa mwana wa Hadilayi anatsutsana nawo amene ankachokera ku nkhondo kuja. 13 Iwo anati, “Musabweretse akapolowo kuno, pakuti ife tidzakhala olakwa pamaso pa Yehova. Kodi mukufuna kuwonjezera pa machimo athu ndi kulakwa kwathu? Pakuti zolakwa zathu ndi zambiri kale ndipo mkwiyo wake woopsa uli pa Israeli.” 14 Kotero asilikali aja anawasiya akapolowo pamodzi ndi katundu amene analanda ku nkhondo pamaso pa akuluakulu ndi gulu lonse la anthu. 15 Anthu amene atchulidwa mayina aja anatenga akapolowo, ndipo kuchokera pa zolanda ku nkhondo, anawaveka onse amene anali maliseche. Anawapatsa zovala ndi nsapato, chakudya ndi chakumwa ndi mankhwala. Onse amene anali ofowoka anawakweza pa abulu. Choncho anabwera nawo kwa abale awo ku Yeriko, Mzinda wa Migwalangwa, ndipo kenaka anawabweza ku Samariya. 16 Pa nthawi imeneyo mfumu Ahazi inatumiza mawu kwa mfumu ya ku Asiriya kupempha chithandizo. 17 Ankhondo a ku Edomu anabweranso ndi kuthira nkhondo Yuda ndi kugwira akapolo. 18 Pamenepo nʼkuti Afilisti atathira nkhondo mizinda ya mʼmbali mwa phiri ndi ku Negevi ku Yuda. Iwo analanda mizindayo nakhala ku Beti-Semesi, Ayaloni ndi Gederoti, komanso Soko, Timna ndi Gimizo pamodzi ndi midzi yawo yozungulira. 19 Yehova anapeputsa Yuda chifukwa cha mfumu Ahazi ya Israeli, pakuti analimbikitsa zoyipa ku Yuda ndipo anali munthu wosakhulupirika kwambiri pamaso pa Yehova. 20 Tigilati-Pileseri mfumu ya ku Asiriya anabwera kwa iye, ndipo anabweretsa mavuto mʼmalo momuthandiza. 21 Ahazi anatenga zinthu zochokera mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba yaufumu ndi kwa atsogoleri ndipo anazipereka kwa mfumu ya ku Asiriya, koma zimenezo sizinamuthandize. 22 Pa nthawi yake yamavutoyi mfumu Ahazi inapitirira kukhalabe yosakhulupirika pamaso pa Yehova. 23 Ahazi ankapereka nsembe kwa milungu ya ku Damasiko, imene inamugonjetsa. Iye ankaganiza kuti, “Popeza milungu ya mafumu a Aaramu yawathandiza, ine ndidzapereka nsembe kwa iyo kuti indithandize.” Koma iyoyo inakhala kugwa kwake ndi kugwa kwa Aisraeli onse. 24 Ahazi anasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse kuchokera mʼNyumba ya Mulungu ndipo anazitenga. Iye anatseka zitseko za Nyumba ya Yehova ndipo anayimika maguwa ansembe pa ngodya iliyonse ya msewu mu Yerusalemu. 25 Mu mzinda uliwonse wa Yuda anamangamo malo achipembedzo, operekerapo nsembe zopsereza kwa milungu ina ndipo anaputa mkwiyo wa Yehova, Mulungu wa makolo ake. 26 Zochitika zina pa ulamuliro wake ndi machitidwe ake onse, kuyambira pachiyambi mpaka pa mapeto, zalembedwa mʼbuku la mafumu a Yuda ndi Israeli. 27 Ahazi anamwalira ndipo anayikidwa mu mzinda wa Yerusalemu, koma sanamuyike mʼmanda a mafumu a Israeli. Ndipo Hezekiya mwana wake analowa ufumu mʼmalo mwake.

In Other Versions

2 Chronicles 28 in the ANGEFD

2 Chronicles 28 in the ANTPNG2D

2 Chronicles 28 in the AS21

2 Chronicles 28 in the BAGH

2 Chronicles 28 in the BBPNG

2 Chronicles 28 in the BBT1E

2 Chronicles 28 in the BDS

2 Chronicles 28 in the BEV

2 Chronicles 28 in the BHAD

2 Chronicles 28 in the BIB

2 Chronicles 28 in the BLPT

2 Chronicles 28 in the BNT

2 Chronicles 28 in the BNTABOOT

2 Chronicles 28 in the BNTLV

2 Chronicles 28 in the BOATCB

2 Chronicles 28 in the BOATCB2

2 Chronicles 28 in the BOBCV

2 Chronicles 28 in the BOCNT

2 Chronicles 28 in the BOECS

2 Chronicles 28 in the BOHCB

2 Chronicles 28 in the BOHCV

2 Chronicles 28 in the BOHLNT

2 Chronicles 28 in the BOHNTLTAL

2 Chronicles 28 in the BOICB

2 Chronicles 28 in the BOILNTAP

2 Chronicles 28 in the BOITCV

2 Chronicles 28 in the BOKCV

2 Chronicles 28 in the BOKCV2

2 Chronicles 28 in the BOKHWOG

2 Chronicles 28 in the BOKSSV

2 Chronicles 28 in the BOLCB

2 Chronicles 28 in the BOLCB2

2 Chronicles 28 in the BOMCV

2 Chronicles 28 in the BONAV

2 Chronicles 28 in the BONCB

2 Chronicles 28 in the BONLT

2 Chronicles 28 in the BONUT2

2 Chronicles 28 in the BOPLNT

2 Chronicles 28 in the BOSCB

2 Chronicles 28 in the BOSNC

2 Chronicles 28 in the BOTLNT

2 Chronicles 28 in the BOVCB

2 Chronicles 28 in the BOYCB

2 Chronicles 28 in the BPBB

2 Chronicles 28 in the BPH

2 Chronicles 28 in the BSB

2 Chronicles 28 in the CCB

2 Chronicles 28 in the CUV

2 Chronicles 28 in the CUVS

2 Chronicles 28 in the DBT

2 Chronicles 28 in the DGDNT

2 Chronicles 28 in the DHNT

2 Chronicles 28 in the DNT

2 Chronicles 28 in the ELBE

2 Chronicles 28 in the EMTV

2 Chronicles 28 in the ESV

2 Chronicles 28 in the FBV

2 Chronicles 28 in the FEB

2 Chronicles 28 in the GGMNT

2 Chronicles 28 in the GNT

2 Chronicles 28 in the HARY

2 Chronicles 28 in the HNT

2 Chronicles 28 in the IRVA

2 Chronicles 28 in the IRVB

2 Chronicles 28 in the IRVG

2 Chronicles 28 in the IRVH

2 Chronicles 28 in the IRVK

2 Chronicles 28 in the IRVM

2 Chronicles 28 in the IRVM2

2 Chronicles 28 in the IRVO

2 Chronicles 28 in the IRVP

2 Chronicles 28 in the IRVT

2 Chronicles 28 in the IRVT2

2 Chronicles 28 in the IRVU

2 Chronicles 28 in the ISVN

2 Chronicles 28 in the JSNT

2 Chronicles 28 in the KAPI

2 Chronicles 28 in the KBT1ETNIK

2 Chronicles 28 in the KBV

2 Chronicles 28 in the KJV

2 Chronicles 28 in the KNFD

2 Chronicles 28 in the LBA

2 Chronicles 28 in the LBLA

2 Chronicles 28 in the LNT

2 Chronicles 28 in the LSV

2 Chronicles 28 in the MAAL

2 Chronicles 28 in the MBV

2 Chronicles 28 in the MBV2

2 Chronicles 28 in the MHNT

2 Chronicles 28 in the MKNFD

2 Chronicles 28 in the MNG

2 Chronicles 28 in the MNT

2 Chronicles 28 in the MNT2

2 Chronicles 28 in the MRS1T

2 Chronicles 28 in the NAA

2 Chronicles 28 in the NASB

2 Chronicles 28 in the NBLA

2 Chronicles 28 in the NBS

2 Chronicles 28 in the NBVTP

2 Chronicles 28 in the NET2

2 Chronicles 28 in the NIV11

2 Chronicles 28 in the NNT

2 Chronicles 28 in the NNT2

2 Chronicles 28 in the NNT3

2 Chronicles 28 in the PDDPT

2 Chronicles 28 in the PFNT

2 Chronicles 28 in the RMNT

2 Chronicles 28 in the SBIAS

2 Chronicles 28 in the SBIBS

2 Chronicles 28 in the SBIBS2

2 Chronicles 28 in the SBICS

2 Chronicles 28 in the SBIDS

2 Chronicles 28 in the SBIGS

2 Chronicles 28 in the SBIHS

2 Chronicles 28 in the SBIIS

2 Chronicles 28 in the SBIIS2

2 Chronicles 28 in the SBIIS3

2 Chronicles 28 in the SBIKS

2 Chronicles 28 in the SBIKS2

2 Chronicles 28 in the SBIMS

2 Chronicles 28 in the SBIOS

2 Chronicles 28 in the SBIPS

2 Chronicles 28 in the SBISS

2 Chronicles 28 in the SBITS

2 Chronicles 28 in the SBITS2

2 Chronicles 28 in the SBITS3

2 Chronicles 28 in the SBITS4

2 Chronicles 28 in the SBIUS

2 Chronicles 28 in the SBIVS

2 Chronicles 28 in the SBT

2 Chronicles 28 in the SBT1E

2 Chronicles 28 in the SCHL

2 Chronicles 28 in the SNT

2 Chronicles 28 in the SUSU

2 Chronicles 28 in the SUSU2

2 Chronicles 28 in the SYNO

2 Chronicles 28 in the TBIAOTANT

2 Chronicles 28 in the TBT1E

2 Chronicles 28 in the TBT1E2

2 Chronicles 28 in the TFTIP

2 Chronicles 28 in the TFTU

2 Chronicles 28 in the TGNTATF3T

2 Chronicles 28 in the THAI

2 Chronicles 28 in the TNFD

2 Chronicles 28 in the TNT

2 Chronicles 28 in the TNTIK

2 Chronicles 28 in the TNTIL

2 Chronicles 28 in the TNTIN

2 Chronicles 28 in the TNTIP

2 Chronicles 28 in the TNTIZ

2 Chronicles 28 in the TOMA

2 Chronicles 28 in the TTENT

2 Chronicles 28 in the UBG

2 Chronicles 28 in the UGV

2 Chronicles 28 in the UGV2

2 Chronicles 28 in the UGV3

2 Chronicles 28 in the VBL

2 Chronicles 28 in the VDCC

2 Chronicles 28 in the YALU

2 Chronicles 28 in the YAPE

2 Chronicles 28 in the YBVTP

2 Chronicles 28 in the ZBP