2 Corinthians 11 (BOGWICC)

1 Ndikukhulupirira kuti mupirira nako pangʼono kupusa kwanga. Chonde tandipirirani! 2 Nsanje imene ndimakuchitirani ndi yofanana ndi ya Mulungu. Ndinakulonjezani mwamuna mmodzi yekha, mwamunayo ndiye Khristu, kuti ndidzakuperekeni inuyo kwa Iyeyo monga namwali wangwiro. 3 Koma ndikuopa kuti monga Hava ananyengedwa ndi kuchenjera kwa njoka, mitima yanunso ingasocheretsedwe kuleka nʼkudzipereka moona mtima ndi modzipereka kwenikweni kwa Khristu. 4 Pakuti ngati wina abwera kwa inu nalalikira Yesu wina wosiyana ndi Yesu amene tinamulalikira, kapena ngati mulandira mzimu wina wosiyana ndi Mzimu amene munalandira, kapena uthenga wabwino wina wosiyana ndi umene munawuvomereza, inuyo mumangolandira mosavuta. 5 Komatu sindikuganiza kuti ndine wotsika kwambiri kwa “atumwi apamwamba.” 6 Mwina ndikhoza kukhala wosaphunzitsidwa kayankhulidwe, koma ndili ndi chidziwitso. Izi tinakufotokozerani momveka bwinobwino. 7 Kodi linali tchimo kwa ine kudzichepetsa nʼcholinga chakuti ndikukwezeni pamene ndinkalalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu kwa inu mwaulere? 8 Ndinkalanda mipingo ina pomalandira thandizo kwa iwo kuti ndikutumikireni. 9 Ndipo pamene ndinali pakati panu, nditasowa kanthu, sindinalemetse munthu aliyense, pakuti abale ena amene anachokera ku Makedoniya anandipatsa zonse zimene ndinkazisowa. Ndayesetsa kuti ndisakhale cholemetsa kwa inu mʼnjira ina iliyonse, ndipo ndidzapitiriza kutero. 10 Kunena moona mtima molingana ndi chilungamo cha Khristu chimene chili mwa ine, palibe amene angandiletse kudzitamandira mʼzigawo za ku Akaya. 11 Nʼchifukwa chiyani ndikutero? Kodi nʼchifukwa choti sindikukondani? Mulungu akudziwa kuti ndimakukondani! 12 Ndipo ndipitiriza kuchita zomwe ndikuchitazi nʼcholinga chakuti ndisapereke mpata kwa amene akufuna kupezera mwayi woti afanane nafe pa zinthu zimene iwowo amadzitamandira. 13 Pakuti anthu oterewa ndi atumwi onama, antchito achinyengo, odzizimbayitsa ngati atumwi a Khristu. 14 Sizododometsa zimenezi, pakuti Satana mwini amadzizimbayitsa kuoneka ngati mngelo wowunikira anthu. 15 Nʼzosadabwitsa tsono ngati atumiki ake akudzizimbayitsa ngati otumikira chilungamo. Matsiriziro awo adzalandira zoyenerana ndi ntchito zawo. 16 Ndibwereze kunena kuti, wina aliyense asandiyese chitsiru. Koma ngati mutero, mundilandire monga mmene mukhoza kulandirira chitsiru, kuti ndinyadirepo pangʼono. 17 Kudzinyadira kwangaku, sindikuyankhula monga mmene Ambuye akufunira koma ngati chitsiru. 18 Popeza ambiri akudzitama monga dziko lapansi limachitira, inenso ndidzitamanso. 19 Inu mumalolera kukhala ndi zitsiru mokondwera chifukwa mumati ndinu anzeru! 20 Kunena zoona mumangololera aliyense; amene amakusandutsani akapolo, kapena amene amakudyerani masuku pamutu, kapena amene amakupezererani, kapena amene amadzitukumula, kapena amene amakumenyani khofi. 21 Ndikuvomera mwamanyazi kuti ife sitinali olimba mtima kuti nʼkuchita zinthu zimenezi.Ndikuyankhula ngati chitsiru kuti chimene wina aliyense akhoza kudzitama nacho, Inenso ndikhoza kudzitama nachonso. 22 Kodi iwo ndi Ahebri? Inenso ndine Mhebri. Kodi iwo ndi Aisraeli? Inenso ndine Mwisraeli. Kodi iwo ndi zidzukulu za Abrahamu? Inenso ndine mdzukulu wa Abrahamu. 23 Kodi iwo ndi atumiki a Khristu? Ndikuyankhula ngati wamisala. Ine ndine woposa iwowo. Ndagwira ntchito kwambiri kupambana iwo, ndakhala ndikuyikidwa mʼndende kawirikawiri, ndakwapulidwapo kwambiri, kawirikawiri ndinali pafupi kufa. 24 Andikwapulapo kasanu zikoti zija za Ayuda, makumi anayi kuchotsapo chimodzi. 25 Katatu anandimenya ndi ndodo. Kamodzi anandigendapo miyala. Katatu sitima yathu ya panyanja inasweka, ndipo ndinakhala usiku ndi usana ndi kuyandama pa nyanja. 26 Ndakhala ndikuyenda maulendo ataliatali. Moyo wanga wakhala ukukumana ndi zoopsa pa mitsinje, zoopsa za achifwamba, zoopsa zochokera kwa abale anga Ayuda, zoopsa zochokera kwa anthu akunja. Ndinakumana ndi zoopsa mʼmizinda, mʼmidzi, pa nyanja, ndi pakati pa abale onyenga. 27 Ndakhala ndikugwira ntchito molimbika ndipo kawirikawiri ndakhala ndikuchezera usiku wonse osagona. Ndakhala ndikumva njala ndi ludzu ndipo kawirikawiri ndakhala wopanda chakudya. Ndakhala ndi kuzizidwa ndi wosowa zovala. 28 Kuwonjezera pa zonsezi, tsiku ndi tsiku ndimakhala pa chipsinjo cha nkhawa ya mipingo yonse. 29 Ndani ali wofowoka, ine wosakhala naye mʼkufowoka kwakeko? Ndani amene mnzake amuchimwitsa, ine wosavutika mu mtima? 30 Ngati nʼkoyenera kudzitamandira, ndidzadzitamandira pa zinthu zimene zimaonetsa kufowoka kwanga. 31 Mulungu, Atate a Ambuye Yesu, amene tiyenera kumutamanda nthawi zonse, akudziwa kuti sindikunama. 32 Ku Damasiko, bwanamkubwa woyimira Mfumu Areta, anayika alonda kuzungulira mzinda wonse kuti andigwire. 33 Koma abale anandiyika mʼdengu nanditsitsira pa chipupa kudzera pa zenera la mpandawo, motero ndinapulumuka mʼmanja mwake.

In Other Versions

2 Corinthians 11 in the ANGEFD

2 Corinthians 11 in the ANTPNG2D

2 Corinthians 11 in the AS21

2 Corinthians 11 in the BAGH

2 Corinthians 11 in the BBPNG

2 Corinthians 11 in the BBT1E

2 Corinthians 11 in the BDS

2 Corinthians 11 in the BEV

2 Corinthians 11 in the BHAD

2 Corinthians 11 in the BIB

2 Corinthians 11 in the BLPT

2 Corinthians 11 in the BNT

2 Corinthians 11 in the BNTABOOT

2 Corinthians 11 in the BNTLV

2 Corinthians 11 in the BOATCB

2 Corinthians 11 in the BOATCB2

2 Corinthians 11 in the BOBCV

2 Corinthians 11 in the BOCNT

2 Corinthians 11 in the BOECS

2 Corinthians 11 in the BOHCB

2 Corinthians 11 in the BOHCV

2 Corinthians 11 in the BOHLNT

2 Corinthians 11 in the BOHNTLTAL

2 Corinthians 11 in the BOICB

2 Corinthians 11 in the BOILNTAP

2 Corinthians 11 in the BOITCV

2 Corinthians 11 in the BOKCV

2 Corinthians 11 in the BOKCV2

2 Corinthians 11 in the BOKHWOG

2 Corinthians 11 in the BOKSSV

2 Corinthians 11 in the BOLCB

2 Corinthians 11 in the BOLCB2

2 Corinthians 11 in the BOMCV

2 Corinthians 11 in the BONAV

2 Corinthians 11 in the BONCB

2 Corinthians 11 in the BONLT

2 Corinthians 11 in the BONUT2

2 Corinthians 11 in the BOPLNT

2 Corinthians 11 in the BOSCB

2 Corinthians 11 in the BOSNC

2 Corinthians 11 in the BOTLNT

2 Corinthians 11 in the BOVCB

2 Corinthians 11 in the BOYCB

2 Corinthians 11 in the BPBB

2 Corinthians 11 in the BPH

2 Corinthians 11 in the BSB

2 Corinthians 11 in the CCB

2 Corinthians 11 in the CUV

2 Corinthians 11 in the CUVS

2 Corinthians 11 in the DBT

2 Corinthians 11 in the DGDNT

2 Corinthians 11 in the DHNT

2 Corinthians 11 in the DNT

2 Corinthians 11 in the ELBE

2 Corinthians 11 in the EMTV

2 Corinthians 11 in the ESV

2 Corinthians 11 in the FBV

2 Corinthians 11 in the FEB

2 Corinthians 11 in the GGMNT

2 Corinthians 11 in the GNT

2 Corinthians 11 in the HARY

2 Corinthians 11 in the HNT

2 Corinthians 11 in the IRVA

2 Corinthians 11 in the IRVB

2 Corinthians 11 in the IRVG

2 Corinthians 11 in the IRVH

2 Corinthians 11 in the IRVK

2 Corinthians 11 in the IRVM

2 Corinthians 11 in the IRVM2

2 Corinthians 11 in the IRVO

2 Corinthians 11 in the IRVP

2 Corinthians 11 in the IRVT

2 Corinthians 11 in the IRVT2

2 Corinthians 11 in the IRVU

2 Corinthians 11 in the ISVN

2 Corinthians 11 in the JSNT

2 Corinthians 11 in the KAPI

2 Corinthians 11 in the KBT1ETNIK

2 Corinthians 11 in the KBV

2 Corinthians 11 in the KJV

2 Corinthians 11 in the KNFD

2 Corinthians 11 in the LBA

2 Corinthians 11 in the LBLA

2 Corinthians 11 in the LNT

2 Corinthians 11 in the LSV

2 Corinthians 11 in the MAAL

2 Corinthians 11 in the MBV

2 Corinthians 11 in the MBV2

2 Corinthians 11 in the MHNT

2 Corinthians 11 in the MKNFD

2 Corinthians 11 in the MNG

2 Corinthians 11 in the MNT

2 Corinthians 11 in the MNT2

2 Corinthians 11 in the MRS1T

2 Corinthians 11 in the NAA

2 Corinthians 11 in the NASB

2 Corinthians 11 in the NBLA

2 Corinthians 11 in the NBS

2 Corinthians 11 in the NBVTP

2 Corinthians 11 in the NET2

2 Corinthians 11 in the NIV11

2 Corinthians 11 in the NNT

2 Corinthians 11 in the NNT2

2 Corinthians 11 in the NNT3

2 Corinthians 11 in the PDDPT

2 Corinthians 11 in the PFNT

2 Corinthians 11 in the RMNT

2 Corinthians 11 in the SBIAS

2 Corinthians 11 in the SBIBS

2 Corinthians 11 in the SBIBS2

2 Corinthians 11 in the SBICS

2 Corinthians 11 in the SBIDS

2 Corinthians 11 in the SBIGS

2 Corinthians 11 in the SBIHS

2 Corinthians 11 in the SBIIS

2 Corinthians 11 in the SBIIS2

2 Corinthians 11 in the SBIIS3

2 Corinthians 11 in the SBIKS

2 Corinthians 11 in the SBIKS2

2 Corinthians 11 in the SBIMS

2 Corinthians 11 in the SBIOS

2 Corinthians 11 in the SBIPS

2 Corinthians 11 in the SBISS

2 Corinthians 11 in the SBITS

2 Corinthians 11 in the SBITS2

2 Corinthians 11 in the SBITS3

2 Corinthians 11 in the SBITS4

2 Corinthians 11 in the SBIUS

2 Corinthians 11 in the SBIVS

2 Corinthians 11 in the SBT

2 Corinthians 11 in the SBT1E

2 Corinthians 11 in the SCHL

2 Corinthians 11 in the SNT

2 Corinthians 11 in the SUSU

2 Corinthians 11 in the SUSU2

2 Corinthians 11 in the SYNO

2 Corinthians 11 in the TBIAOTANT

2 Corinthians 11 in the TBT1E

2 Corinthians 11 in the TBT1E2

2 Corinthians 11 in the TFTIP

2 Corinthians 11 in the TFTU

2 Corinthians 11 in the TGNTATF3T

2 Corinthians 11 in the THAI

2 Corinthians 11 in the TNFD

2 Corinthians 11 in the TNT

2 Corinthians 11 in the TNTIK

2 Corinthians 11 in the TNTIL

2 Corinthians 11 in the TNTIN

2 Corinthians 11 in the TNTIP

2 Corinthians 11 in the TNTIZ

2 Corinthians 11 in the TOMA

2 Corinthians 11 in the TTENT

2 Corinthians 11 in the UBG

2 Corinthians 11 in the UGV

2 Corinthians 11 in the UGV2

2 Corinthians 11 in the UGV3

2 Corinthians 11 in the VBL

2 Corinthians 11 in the VDCC

2 Corinthians 11 in the YALU

2 Corinthians 11 in the YAPE

2 Corinthians 11 in the YBVTP

2 Corinthians 11 in the ZBP