2 Kings 11 (BOGWICC)

1 Ataliya amayi ake a Ahaziya ataona kuti mwana wawo wafa, ananyamuka nakawononga banja lonse la mfumu. 2 Koma Yehoseba, mwana wamkazi wa Mfumu Yehoramu, mlongo wake wa Ahaziya, anatenga Yowasi mwana wa Ahaziya, namusunga kutali ndi ana a mfumu amene ankati awaphewo. Anamuyika iye pamodzi ndi mlezi wake mʼchipinda chogona chamʼkati kubisira Ataliya kotero iye sanaphedwe. 3 Mwanayo anakhala mobisala pamodzi ndi mlezi wake mʼnyumba ya Yehova kwa zaka zisanu ndi chimodzi pamene Ataliya ankalamulira dzikolo. 4 Koma mʼchaka chachisanu ndi chiwiri, Yehoyada anatumiza mawu kukayitana atsogoleri olamulira asilikali 100 olondera mfumu ndiponso alonda olonda nyumba yaufumu ndipo anabwera nawo mʼNyumba ya Yehova. Iye anapangana nawo pangano ndipo anawalumbiritsa mʼnyumba ya Yehova. Kenaka anawaonetsa mwana wamwamuna wa mfumu uja. 5 Yehoyada anawalamulira kuti, “Chimene muti muchite ndi ichi: Inu magulu atatu amene muti mudzakhale pa ntchito tsiku la Sabata, gulu loyamba lidzalondera nyumba ya mfumu, 6 gulu lachiwiri lidzalondera Chipata cha Suri, ndipo gulu lachitatu lidzalondera chipata cha kumbuyo kwa asilikali amene amasinthana polondera nyumbayo. 7 Ndipo inu amene muli mʼmagulu ena awiri amene simugwira ntchito pa tsiku la Sabata, nonse mudzalondere mfumu ku nyumbayo. 8 Mudzakhale mozungulira mfumuyo, munthu aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake. Wina aliyense amene adzakuyandikireni adzayenera kuphedwa. Muzikhala pafupi ndi mfumu kulikonse kumene ikupita.” 9 Atsogoleri olamulira asilikali 100 aja anachitadi zonse monga analamulira wansembe Yehoyada. Aliyense anatenga anthu ake, iwo amene amakagwira ntchito pa tsiku la Sabata ndi amene amapita kukapuma ndipo anabwera kwa wansembe Yehoyada. 10 Ndipo wansembeyo anawapatsa asilikaliwo mikondo ndi zishango zimene zinali za mfumu Davide ndipo zinali mʼNyumba ya Yehova. 11 Alondawo, aliyense ali ndi chida mʼmanja mwake, anayima mozungulira mfumu, pafupi ndi guwa lansembe ndi nyumbayo, kuchokera mbali ya kummwera mpaka mbali ya kumpoto kwa nyumbayo. 12 Yehoyada anatulutsa mwana wa mfumuyo namuveka chipewa chaufumu ndipo anamupatsa Buku la Chipangano ndi kumuyika kukhala mfumu. Iwo anamudzoza ndipo anthu anamuwombera mʼmanja akufuwula kuti, “Mfumu ikhale ndi moyo wautali!” 13 Ataliya atamva phokoso limene alonda ndi anthuwo amachita, anapita ku Nyumba ya Yehova kumene kunali anthuwo. 14 Iye anayangʼana naona mfumu itayima pa chipilala, potsata mwambo waufumu. Atsogoleri a asilikali ndi oyimba malipenga anali pafupi ndi mfumuyo, ndipo anthu onse a mʼderalo ankasangalala ndi kuyimba malipenga. Pamenepo Ataliya anangʼamba mkanjo wake nafuwula kuti, “Kuwukira! Kuwukira!” 15 Wansembe Yehoyada analamula atsogoleri a asilikali 100 amene amayangʼanira asilikaliwo kuti, “Mutulutseni ameneyo pakati panu ndipo muphe ndi lupanga aliyense amene adzamutsata.” Pakuti nʼkuti wansembeyo atanena kuti, “Ataliyayo asaphedwere mʼNyumba ya Yehova.” 16 Choncho anamugwira pamene amafika pa malo amene akavalo amalowera ku nyumba ya mfumu ndipo anamuphera pamenepo. 17 Tsono Yehoyada anachititsa pangano pakati pa Yehova ndi mfumu ndi anthu kuti adzakhala anthu a Yehova. Iye anachititsanso pangano pakati pa mfumu ndi anthu. 18 Anthu onse a mʼdzikomo anapita ku nyumba ya Baala nakayigwetsa. Iwo anaphwanya kotheratu maguwa ansembe ndi mafano ake ndipo anapha Matani wansembe wa Baala patsogolo pa maguwa pomwepo.Pamenepo wansembe Yehoyada anasankha oyangʼanira Nyumba ya Yehova. 19 Iye anatenga atsogoleri a asilikali 100 aja, alonda olonda nyumba yaufumu pamodzi ndi anthu onse a mʼdzikomo ndipo onse pamodzi anayitulutsa mfumu mʼNyumba ya Yehova ndi kukalowa ku nyumba yaufumu podzera pa chipata cha alonda. Ndipo mfumuyo inakhala pa mpando wake waufumu. 20 Choncho anthu onse a mʼdzikomo anasangalala. Ndipo mu mzindamo munakhala bata chifukwa Ataliya nʼkuti ataphedwa ndi lupanga ku nyumba ya mfumu. 21 Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziwiri pamene anayamba kulamulira.

In Other Versions

2 Kings 11 in the ANGEFD

2 Kings 11 in the ANTPNG2D

2 Kings 11 in the AS21

2 Kings 11 in the BAGH

2 Kings 11 in the BBPNG

2 Kings 11 in the BBT1E

2 Kings 11 in the BDS

2 Kings 11 in the BEV

2 Kings 11 in the BHAD

2 Kings 11 in the BIB

2 Kings 11 in the BLPT

2 Kings 11 in the BNT

2 Kings 11 in the BNTABOOT

2 Kings 11 in the BNTLV

2 Kings 11 in the BOATCB

2 Kings 11 in the BOATCB2

2 Kings 11 in the BOBCV

2 Kings 11 in the BOCNT

2 Kings 11 in the BOECS

2 Kings 11 in the BOHCB

2 Kings 11 in the BOHCV

2 Kings 11 in the BOHLNT

2 Kings 11 in the BOHNTLTAL

2 Kings 11 in the BOICB

2 Kings 11 in the BOILNTAP

2 Kings 11 in the BOITCV

2 Kings 11 in the BOKCV

2 Kings 11 in the BOKCV2

2 Kings 11 in the BOKHWOG

2 Kings 11 in the BOKSSV

2 Kings 11 in the BOLCB

2 Kings 11 in the BOLCB2

2 Kings 11 in the BOMCV

2 Kings 11 in the BONAV

2 Kings 11 in the BONCB

2 Kings 11 in the BONLT

2 Kings 11 in the BONUT2

2 Kings 11 in the BOPLNT

2 Kings 11 in the BOSCB

2 Kings 11 in the BOSNC

2 Kings 11 in the BOTLNT

2 Kings 11 in the BOVCB

2 Kings 11 in the BOYCB

2 Kings 11 in the BPBB

2 Kings 11 in the BPH

2 Kings 11 in the BSB

2 Kings 11 in the CCB

2 Kings 11 in the CUV

2 Kings 11 in the CUVS

2 Kings 11 in the DBT

2 Kings 11 in the DGDNT

2 Kings 11 in the DHNT

2 Kings 11 in the DNT

2 Kings 11 in the ELBE

2 Kings 11 in the EMTV

2 Kings 11 in the ESV

2 Kings 11 in the FBV

2 Kings 11 in the FEB

2 Kings 11 in the GGMNT

2 Kings 11 in the GNT

2 Kings 11 in the HARY

2 Kings 11 in the HNT

2 Kings 11 in the IRVA

2 Kings 11 in the IRVB

2 Kings 11 in the IRVG

2 Kings 11 in the IRVH

2 Kings 11 in the IRVK

2 Kings 11 in the IRVM

2 Kings 11 in the IRVM2

2 Kings 11 in the IRVO

2 Kings 11 in the IRVP

2 Kings 11 in the IRVT

2 Kings 11 in the IRVT2

2 Kings 11 in the IRVU

2 Kings 11 in the ISVN

2 Kings 11 in the JSNT

2 Kings 11 in the KAPI

2 Kings 11 in the KBT1ETNIK

2 Kings 11 in the KBV

2 Kings 11 in the KJV

2 Kings 11 in the KNFD

2 Kings 11 in the LBA

2 Kings 11 in the LBLA

2 Kings 11 in the LNT

2 Kings 11 in the LSV

2 Kings 11 in the MAAL

2 Kings 11 in the MBV

2 Kings 11 in the MBV2

2 Kings 11 in the MHNT

2 Kings 11 in the MKNFD

2 Kings 11 in the MNG

2 Kings 11 in the MNT

2 Kings 11 in the MNT2

2 Kings 11 in the MRS1T

2 Kings 11 in the NAA

2 Kings 11 in the NASB

2 Kings 11 in the NBLA

2 Kings 11 in the NBS

2 Kings 11 in the NBVTP

2 Kings 11 in the NET2

2 Kings 11 in the NIV11

2 Kings 11 in the NNT

2 Kings 11 in the NNT2

2 Kings 11 in the NNT3

2 Kings 11 in the PDDPT

2 Kings 11 in the PFNT

2 Kings 11 in the RMNT

2 Kings 11 in the SBIAS

2 Kings 11 in the SBIBS

2 Kings 11 in the SBIBS2

2 Kings 11 in the SBICS

2 Kings 11 in the SBIDS

2 Kings 11 in the SBIGS

2 Kings 11 in the SBIHS

2 Kings 11 in the SBIIS

2 Kings 11 in the SBIIS2

2 Kings 11 in the SBIIS3

2 Kings 11 in the SBIKS

2 Kings 11 in the SBIKS2

2 Kings 11 in the SBIMS

2 Kings 11 in the SBIOS

2 Kings 11 in the SBIPS

2 Kings 11 in the SBISS

2 Kings 11 in the SBITS

2 Kings 11 in the SBITS2

2 Kings 11 in the SBITS3

2 Kings 11 in the SBITS4

2 Kings 11 in the SBIUS

2 Kings 11 in the SBIVS

2 Kings 11 in the SBT

2 Kings 11 in the SBT1E

2 Kings 11 in the SCHL

2 Kings 11 in the SNT

2 Kings 11 in the SUSU

2 Kings 11 in the SUSU2

2 Kings 11 in the SYNO

2 Kings 11 in the TBIAOTANT

2 Kings 11 in the TBT1E

2 Kings 11 in the TBT1E2

2 Kings 11 in the TFTIP

2 Kings 11 in the TFTU

2 Kings 11 in the TGNTATF3T

2 Kings 11 in the THAI

2 Kings 11 in the TNFD

2 Kings 11 in the TNT

2 Kings 11 in the TNTIK

2 Kings 11 in the TNTIL

2 Kings 11 in the TNTIN

2 Kings 11 in the TNTIP

2 Kings 11 in the TNTIZ

2 Kings 11 in the TOMA

2 Kings 11 in the TTENT

2 Kings 11 in the UBG

2 Kings 11 in the UGV

2 Kings 11 in the UGV2

2 Kings 11 in the UGV3

2 Kings 11 in the VBL

2 Kings 11 in the VDCC

2 Kings 11 in the YALU

2 Kings 11 in the YAPE

2 Kings 11 in the YBVTP

2 Kings 11 in the ZBP