2 Kings 7 (BOGWICC)

1 Ndipo Elisa anati, “Mverani mawu a Yehova. Yehova akuti, ‘Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.’ ” 2 Mtsogoleri amene mfumu inkamudalira anati kwa munthu wa Mulungu, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?”Elisa anamuyankha kuti, “Taona, iweyo udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.” 3 Tsono pa chipata cholowera mu mzinda wa Samariya pankakhala anthu anayi akhate. Iwo anayankhulana kuti, “Chifukwa chiyani tikungokhala pano kudikira kufa? 4 Ngati tinganene kuti, ‘Tidzalowa mu mzinda,’ njala ili mu mzindamo ndipo tidzafa. Ndipo ngati tikhalebe pano, tidzafa ndithu. Choncho tiyeni tipite ku msasa wa Aaramu ndi kukadzipereka. Ngati sakatipha, tidzakhala ndi moyo, ngati akatipha, basi tikafa.” 5 Iwo ananyamuka ndi kachisisira kupita ku msasa wa Aaramu. Atafika mʼmalire a msasa, taonani, sanapeze munthu ndi mmodzi yemwe, 6 pakuti Ambuye anali atamveketsa phokoso la magaleta ndi akavalo ndiponso mdidi wa gulu lalikulu la ankhondo, kotero anayamba kuwuzana kuti, “Taonani, mfumu ya ku Israeli yalemba ganyu mafumu a Ahiti ndi a Aigupto kuti adzatithire nkhondo!” 7 Choncho ananyamuka nathawa ndi kachisisira ndipo anasiya matenti, akavalo ndi abulu awo. Iwo anasiya msasa wawo momwe unalili nathawa kupulumutsa miyoyo yawo. 8 Anthu akhate aja atafika mʼmalire mwa msasa analowa mʼtenti imodzi. Anadya ndi kumwa, natenga siliva, golide ndi zovala ndipo anachoka kupita kukazibisa. Atabwerera anakalowa mʼtenti ina ndipo anatenga zinthu mʼmenemo nakazibisanso. 9 Kenaka akhate aja anawuzana kuti, “Ife sitikuchita bwino. Lero ndi tsiku la uthenga wabwino ndipo tikungokhala chete. Tikadikira mpaka kucha, tidzalangidwa. Tiyeni msanga tikafotokoze zimenezi ku nyumba yaufumu.” 10 Choncho anapita nakayitana alonda a pa chipata cha mzinda ndi kufotokoza kuti, “Ife tinapita ku msasa wa Aaramu ndipo sitinapezeko munthu, kapena phokoso la wina aliyense koma tinangopeza akavalo okha pamodzi ndi abulu ali chimangire.” 11 Alonda a pa chipata aja analengeza uthengawu kwa okhala mʼnyumba yaufumu. 12 Mfumu inadzuka usiku ndipo inawuza atsogoleri ake a ankhondo kuti, “Ndikukuwuzani zimene Aaramu atichitira ife. Akudziwa kuti tikufa ndi njala; kotero achoka mu msasa wawo kukabisala kuthengo ndi kuti, ‘Iwowa atuluka ndithu, ndipo ife tidzawagwira amoyo ndi kulowa mu mzindamo.’ ” 13 Mmodzi mwa atsogoleri ake ankhondo anayankha kuti, “Chonde uzani anthu ena atenge akavalo asanu amene atsala mu mzinda muno. Taonani, zomwe zingawachitikire zidzakhala zofanana ndi zomwe zingachitikire ena onse amene atsala. Inde iwo adzangokhala ngati Aisraeli ena onse amene awonongeka kale. Choncho tiyeni tiwatume akafufuze zomwe zachitika.” 14 Choncho anasankha magaleta awiri pamodzi ndi akavalo ake, ndipo mfumu inawatuma kuti alondole gulu lankhondo la Aaramu. Mfumuyo inalamula oyendetsa akavalowo kuti, “Pitani kaoneni.” 15 Anthuwa anawalondola mpaka ku Yorodani, ndipo taonani, mʼnjira monse munali zovala zokhazokha ndi zinthu zimene Aaramu ankazitaya pamene ankathawa mofulumira. Ndipo amithengawo anabwerera ndi kudzafotokozera mfumu. 16 Tsono anthu a mu Samariya anatuluka nakafunkha ku msasa wa Aaramu. Kotero kuti makilogalamu atatu a ufa ankawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele ankawagulitsanso pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva, monga momwe ananenera Yehova. 17 Tsono mfumu inayika mtsogoleri amene ankamudalira uja kuti akhale woyangʼanira pa chipata ndipo anthu anamupondaponda ku chipata kuja, ndipo anafa, monga momwe Elisa munthu wa Mulungu ananenera mfumu itapita ku nyumba yake. 18 Zinachitika molingana ndi zomwe ananena munthu wa Mulungu zija kuti “Mawa nthawi ngati yomwe ino, makilogalamu atatu a ufa adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ndipo makilogalamu asanu ndi limodzi a barele adzawagulitsa pa mtengo wa ndalama imodzi yasiliva ku chipata cha Samariya.” 19 Mtsogoleriyu ananena kwa munthu wa Mulungu kuti, “Taona, ngakhale Yehova atatsekula zipata zakumwamba, kodi zimenezi zingachitikedi?” Munthu wa Mulungu anamuyankha kuti, “Iwe udzaziona zimenezi ndi maso ako, koma sudzadyako kanthu.” 20 Ndipo izi ndi zomwe zinamuchitikiradi mtsogoleriyu, pakuti anthu anamupondaponda pa chipata ndipo anafa.

In Other Versions

2 Kings 7 in the ANGEFD

2 Kings 7 in the ANTPNG2D

2 Kings 7 in the AS21

2 Kings 7 in the BAGH

2 Kings 7 in the BBPNG

2 Kings 7 in the BBT1E

2 Kings 7 in the BDS

2 Kings 7 in the BEV

2 Kings 7 in the BHAD

2 Kings 7 in the BIB

2 Kings 7 in the BLPT

2 Kings 7 in the BNT

2 Kings 7 in the BNTABOOT

2 Kings 7 in the BNTLV

2 Kings 7 in the BOATCB

2 Kings 7 in the BOATCB2

2 Kings 7 in the BOBCV

2 Kings 7 in the BOCNT

2 Kings 7 in the BOECS

2 Kings 7 in the BOHCB

2 Kings 7 in the BOHCV

2 Kings 7 in the BOHLNT

2 Kings 7 in the BOHNTLTAL

2 Kings 7 in the BOICB

2 Kings 7 in the BOILNTAP

2 Kings 7 in the BOITCV

2 Kings 7 in the BOKCV

2 Kings 7 in the BOKCV2

2 Kings 7 in the BOKHWOG

2 Kings 7 in the BOKSSV

2 Kings 7 in the BOLCB

2 Kings 7 in the BOLCB2

2 Kings 7 in the BOMCV

2 Kings 7 in the BONAV

2 Kings 7 in the BONCB

2 Kings 7 in the BONLT

2 Kings 7 in the BONUT2

2 Kings 7 in the BOPLNT

2 Kings 7 in the BOSCB

2 Kings 7 in the BOSNC

2 Kings 7 in the BOTLNT

2 Kings 7 in the BOVCB

2 Kings 7 in the BOYCB

2 Kings 7 in the BPBB

2 Kings 7 in the BPH

2 Kings 7 in the BSB

2 Kings 7 in the CCB

2 Kings 7 in the CUV

2 Kings 7 in the CUVS

2 Kings 7 in the DBT

2 Kings 7 in the DGDNT

2 Kings 7 in the DHNT

2 Kings 7 in the DNT

2 Kings 7 in the ELBE

2 Kings 7 in the EMTV

2 Kings 7 in the ESV

2 Kings 7 in the FBV

2 Kings 7 in the FEB

2 Kings 7 in the GGMNT

2 Kings 7 in the GNT

2 Kings 7 in the HARY

2 Kings 7 in the HNT

2 Kings 7 in the IRVA

2 Kings 7 in the IRVB

2 Kings 7 in the IRVG

2 Kings 7 in the IRVH

2 Kings 7 in the IRVK

2 Kings 7 in the IRVM

2 Kings 7 in the IRVM2

2 Kings 7 in the IRVO

2 Kings 7 in the IRVP

2 Kings 7 in the IRVT

2 Kings 7 in the IRVT2

2 Kings 7 in the IRVU

2 Kings 7 in the ISVN

2 Kings 7 in the JSNT

2 Kings 7 in the KAPI

2 Kings 7 in the KBT1ETNIK

2 Kings 7 in the KBV

2 Kings 7 in the KJV

2 Kings 7 in the KNFD

2 Kings 7 in the LBA

2 Kings 7 in the LBLA

2 Kings 7 in the LNT

2 Kings 7 in the LSV

2 Kings 7 in the MAAL

2 Kings 7 in the MBV

2 Kings 7 in the MBV2

2 Kings 7 in the MHNT

2 Kings 7 in the MKNFD

2 Kings 7 in the MNG

2 Kings 7 in the MNT

2 Kings 7 in the MNT2

2 Kings 7 in the MRS1T

2 Kings 7 in the NAA

2 Kings 7 in the NASB

2 Kings 7 in the NBLA

2 Kings 7 in the NBS

2 Kings 7 in the NBVTP

2 Kings 7 in the NET2

2 Kings 7 in the NIV11

2 Kings 7 in the NNT

2 Kings 7 in the NNT2

2 Kings 7 in the NNT3

2 Kings 7 in the PDDPT

2 Kings 7 in the PFNT

2 Kings 7 in the RMNT

2 Kings 7 in the SBIAS

2 Kings 7 in the SBIBS

2 Kings 7 in the SBIBS2

2 Kings 7 in the SBICS

2 Kings 7 in the SBIDS

2 Kings 7 in the SBIGS

2 Kings 7 in the SBIHS

2 Kings 7 in the SBIIS

2 Kings 7 in the SBIIS2

2 Kings 7 in the SBIIS3

2 Kings 7 in the SBIKS

2 Kings 7 in the SBIKS2

2 Kings 7 in the SBIMS

2 Kings 7 in the SBIOS

2 Kings 7 in the SBIPS

2 Kings 7 in the SBISS

2 Kings 7 in the SBITS

2 Kings 7 in the SBITS2

2 Kings 7 in the SBITS3

2 Kings 7 in the SBITS4

2 Kings 7 in the SBIUS

2 Kings 7 in the SBIVS

2 Kings 7 in the SBT

2 Kings 7 in the SBT1E

2 Kings 7 in the SCHL

2 Kings 7 in the SNT

2 Kings 7 in the SUSU

2 Kings 7 in the SUSU2

2 Kings 7 in the SYNO

2 Kings 7 in the TBIAOTANT

2 Kings 7 in the TBT1E

2 Kings 7 in the TBT1E2

2 Kings 7 in the TFTIP

2 Kings 7 in the TFTU

2 Kings 7 in the TGNTATF3T

2 Kings 7 in the THAI

2 Kings 7 in the TNFD

2 Kings 7 in the TNT

2 Kings 7 in the TNTIK

2 Kings 7 in the TNTIL

2 Kings 7 in the TNTIN

2 Kings 7 in the TNTIP

2 Kings 7 in the TNTIZ

2 Kings 7 in the TOMA

2 Kings 7 in the TTENT

2 Kings 7 in the UBG

2 Kings 7 in the UGV

2 Kings 7 in the UGV2

2 Kings 7 in the UGV3

2 Kings 7 in the VBL

2 Kings 7 in the VDCC

2 Kings 7 in the YALU

2 Kings 7 in the YAPE

2 Kings 7 in the YBVTP

2 Kings 7 in the ZBP