2 Peter 1 (BOGWICC)

1 Ndine Simoni Petro, mtumiki ndi mtumwi wa Yesu Khristu.Kwa anthu amene analandira chikhulupiriro cha mtengowapatali chomwe ifenso tinalandira chifukwa cha chilungamo cha Mulungu ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. 2 Chisomo ndi mtendere zochuluka zikhale nanu pomudziwa Mulungu ndi Yesu Ambuye athu. 3 Mulungu mwa mphamvu zake anatipatsa zonse zofunika kukhala moyo opembedza, potidziwitsa za Iyeyo amene anatiyitana ku ulemerero wake ndi ubwino wake. 4 Mwa ulemerero ndi ubwino wakewo, anatipatsa malonjezo opambana kwambiri ndi a mtengowapatali. Amenewa ndi malonjezo amene amakuthandizani kulandira nawo moyo wa Mulungu, titapulumuka ku chiwonongeko chimene chili mʼdziko lapansi chifukwa cha zilakolako zoyipa. 5 Choncho, chitani khama kuwonjezera moyo wabwino pa chikhulupiriro chanu, ndipo pa moyo wabwino muwonjezerepo nzeru. 6 Pa nzeru muwonjezerepo kudziretsa, pa kudziretsa muwonjezerepo chipiriro, ndipo pa chipiriro muwonjezerepo khalidwe lolemekeza Mulungu. 7 Pa khalidwe lolemekeza Mulungu muwonjezerepo chifundo cha ubale, pa chifundo cha ubale muwonjezerepo chikondi. 8 Ngati zonsezi zikhala mwa inu nʼkumachuluka, zidzakuthandizani kuti musakhale aulesi ndi osapindula ndi chidziwitso chanu cha Ambuye athu Yesu Khristu. 9 Koma ngati wina alibe zimenezi, ndi wakhungu sangathe kuona patali, ndipo wayiwala kuti anayeretsedwa machimo ake akale. 10 Nʼchifukwa chake abale anga, funitsitsani kuti mayitanidwe ndi masankhidwe anu akhale otsimikizika. Pakuti ngati muchita zinthu izi, simudzagwa konse. 11 Mudzalandiridwa bwino kwambiri mu ufumu wosatha wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu. 12 Tsono ine ndidzakukumbutsani nthawi zonse za zinthu zimenezi, ngakhale kuti mumazidziwa ndipo kuti munakhazikika mʼchoonadi chimene muli nacho tsopano. 13 Ndikuganiza kuti nʼkoyenera ndikanali mu msasa uno, kuti ndikutsitsimutseni ndi kukukumbutsani, 14 chifukwa ndikudziwa kuti posachedwapa ndikuchoka mu msasa uno, monga Ambuye athu Yesu Khristu anandidziwitsiratu. 15 Ndipo ndidzayesetsa kuti nditachoka, mudzakumbukire nthawi zonse. 16 Ife sitinatsate nkhani zongopeka titakuwuzani za mphamvu zake ndi zakubweranso kwa Ambuye athu Yesu Khristu, koma tinaona ndi maso athu za ukulu wake. 17 Pakuti Iye analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu Atate atamufikira mawu ochokera ku ulemerero wa ukulu akuti, “Uyu ndi mwana wanga amene Ine ndimukonda, amene ndimakondwera naye kwambiri.” 18 Ifeyo tinamva mawuwa akuchokera kumwamba pamene tinali naye pamodzi pa phiri lopatulika lija. 19 Tsono ifenso tili ndi mawu a uneneri amene ndi odalirika kwambiri ndipo inu mudzachita bwino mukawasamalira mawuwa, monga kuwunika kumene kukuwala mu mdima, mpaka tsiku lidzayambe kucha, pamene nthanda idzayambe kuwala mʼmitima mwanu. 20 Kuposa zonse, inu muyenera kuzindikira kuti palibe mawu a uneneri amene amatanthauzidwa pa okha. 21 Pakuti mawu a uneneri sanadze mwa kufuna kwa anthu, koma anthu anayankhula zochokera kwa Mulungu, Mzimu Woyera atawayankhulitsa.

In Other Versions

2 Peter 1 in the ANGEFD

2 Peter 1 in the ANTPNG2D

2 Peter 1 in the AS21

2 Peter 1 in the BAGH

2 Peter 1 in the BBPNG

2 Peter 1 in the BBT1E

2 Peter 1 in the BDS

2 Peter 1 in the BEV

2 Peter 1 in the BHAD

2 Peter 1 in the BIB

2 Peter 1 in the BLPT

2 Peter 1 in the BNT

2 Peter 1 in the BNTABOOT

2 Peter 1 in the BNTLV

2 Peter 1 in the BOATCB

2 Peter 1 in the BOATCB2

2 Peter 1 in the BOBCV

2 Peter 1 in the BOCNT

2 Peter 1 in the BOECS

2 Peter 1 in the BOHCB

2 Peter 1 in the BOHCV

2 Peter 1 in the BOHLNT

2 Peter 1 in the BOHNTLTAL

2 Peter 1 in the BOICB

2 Peter 1 in the BOILNTAP

2 Peter 1 in the BOITCV

2 Peter 1 in the BOKCV

2 Peter 1 in the BOKCV2

2 Peter 1 in the BOKHWOG

2 Peter 1 in the BOKSSV

2 Peter 1 in the BOLCB

2 Peter 1 in the BOLCB2

2 Peter 1 in the BOMCV

2 Peter 1 in the BONAV

2 Peter 1 in the BONCB

2 Peter 1 in the BONLT

2 Peter 1 in the BONUT2

2 Peter 1 in the BOPLNT

2 Peter 1 in the BOSCB

2 Peter 1 in the BOSNC

2 Peter 1 in the BOTLNT

2 Peter 1 in the BOVCB

2 Peter 1 in the BOYCB

2 Peter 1 in the BPBB

2 Peter 1 in the BPH

2 Peter 1 in the BSB

2 Peter 1 in the CCB

2 Peter 1 in the CUV

2 Peter 1 in the CUVS

2 Peter 1 in the DBT

2 Peter 1 in the DGDNT

2 Peter 1 in the DHNT

2 Peter 1 in the DNT

2 Peter 1 in the ELBE

2 Peter 1 in the EMTV

2 Peter 1 in the ESV

2 Peter 1 in the FBV

2 Peter 1 in the FEB

2 Peter 1 in the GGMNT

2 Peter 1 in the GNT

2 Peter 1 in the HARY

2 Peter 1 in the HNT

2 Peter 1 in the IRVA

2 Peter 1 in the IRVB

2 Peter 1 in the IRVG

2 Peter 1 in the IRVH

2 Peter 1 in the IRVK

2 Peter 1 in the IRVM

2 Peter 1 in the IRVM2

2 Peter 1 in the IRVO

2 Peter 1 in the IRVP

2 Peter 1 in the IRVT

2 Peter 1 in the IRVT2

2 Peter 1 in the IRVU

2 Peter 1 in the ISVN

2 Peter 1 in the JSNT

2 Peter 1 in the KAPI

2 Peter 1 in the KBT1ETNIK

2 Peter 1 in the KBV

2 Peter 1 in the KJV

2 Peter 1 in the KNFD

2 Peter 1 in the LBA

2 Peter 1 in the LBLA

2 Peter 1 in the LNT

2 Peter 1 in the LSV

2 Peter 1 in the MAAL

2 Peter 1 in the MBV

2 Peter 1 in the MBV2

2 Peter 1 in the MHNT

2 Peter 1 in the MKNFD

2 Peter 1 in the MNG

2 Peter 1 in the MNT

2 Peter 1 in the MNT2

2 Peter 1 in the MRS1T

2 Peter 1 in the NAA

2 Peter 1 in the NASB

2 Peter 1 in the NBLA

2 Peter 1 in the NBS

2 Peter 1 in the NBVTP

2 Peter 1 in the NET2

2 Peter 1 in the NIV11

2 Peter 1 in the NNT

2 Peter 1 in the NNT2

2 Peter 1 in the NNT3

2 Peter 1 in the PDDPT

2 Peter 1 in the PFNT

2 Peter 1 in the RMNT

2 Peter 1 in the SBIAS

2 Peter 1 in the SBIBS

2 Peter 1 in the SBIBS2

2 Peter 1 in the SBICS

2 Peter 1 in the SBIDS

2 Peter 1 in the SBIGS

2 Peter 1 in the SBIHS

2 Peter 1 in the SBIIS

2 Peter 1 in the SBIIS2

2 Peter 1 in the SBIIS3

2 Peter 1 in the SBIKS

2 Peter 1 in the SBIKS2

2 Peter 1 in the SBIMS

2 Peter 1 in the SBIOS

2 Peter 1 in the SBIPS

2 Peter 1 in the SBISS

2 Peter 1 in the SBITS

2 Peter 1 in the SBITS2

2 Peter 1 in the SBITS3

2 Peter 1 in the SBITS4

2 Peter 1 in the SBIUS

2 Peter 1 in the SBIVS

2 Peter 1 in the SBT

2 Peter 1 in the SBT1E

2 Peter 1 in the SCHL

2 Peter 1 in the SNT

2 Peter 1 in the SUSU

2 Peter 1 in the SUSU2

2 Peter 1 in the SYNO

2 Peter 1 in the TBIAOTANT

2 Peter 1 in the TBT1E

2 Peter 1 in the TBT1E2

2 Peter 1 in the TFTIP

2 Peter 1 in the TFTU

2 Peter 1 in the TGNTATF3T

2 Peter 1 in the THAI

2 Peter 1 in the TNFD

2 Peter 1 in the TNT

2 Peter 1 in the TNTIK

2 Peter 1 in the TNTIL

2 Peter 1 in the TNTIN

2 Peter 1 in the TNTIP

2 Peter 1 in the TNTIZ

2 Peter 1 in the TOMA

2 Peter 1 in the TTENT

2 Peter 1 in the UBG

2 Peter 1 in the UGV

2 Peter 1 in the UGV2

2 Peter 1 in the UGV3

2 Peter 1 in the VBL

2 Peter 1 in the VDCC

2 Peter 1 in the YALU

2 Peter 1 in the YAPE

2 Peter 1 in the YBVTP

2 Peter 1 in the ZBP