2 Samuel 1 (BOGWICC)
1 Atamwalira Sauli, Davide anabwerako kumene anakagonjetsa Aamaleki ndipo anakakhala ku Zikilagi masiku awiri. 2 Pa tsiku lachitatu munthu wina wochokera ku msasa wa Sauli anafika, zovala zake zitangʼambika ndiponso anali atathira dothi pamutu pake. Atafika kwa Davide, anadzigwetsa pansi, kupereka ulemu kwa Davideyo. 3 Davide anamufunsa iye kuti, “Kodi iwe wachokera kuti?”Iye anayankha kuti, “Ine ndathawa ku misasa ya Aisraeli.” 4 Davide anafunsa, “Tandiwuza, chachitika ndi chiyani?”Iye anati, “Anthu athawa ku nkhondo ndipo ambiri aphedwa. Sauli ndi mwana wake Yonatani aphedwa.” 5 Ndipo Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa nkhaniyi, “Ukudziwa bwanji kuti Sauli ndi mwana wake Yonatani afa?” 6 Mnyamatayo anati, “Zinangochitika kuti ndinali pa phiri la Gilibowa, ndipo Sauli anali komweko ataweramira pa mkondo wake, pamodzi ndi magaleta ndi okwera ake atamuyandikira. 7 Pamene anatembenuka ndi kundiona ine, iye anandiyitana, ndipo ndinati, ‘Kodi ndichite chiyani?’ ” 8 Iye anandifunsa, “Iwe ndiwe yani?”Ine ndinayankha kuti, “Ndine Mwamaleki.” 9 “Kenaka iye anati kwa ine, ‘Bwera pafupi ndipo undiphe! Ndikumva ululu kwambiri, koma ndikanali ndi moyo!’ 10 “Kotero ndinabwera pafupi ndi kumupha, chifukwa ndinadziwa kuti mmene anagweramo sakanakhalanso ndi moyo. Ndipo ndatenga chipewa chaufumu chimene chinali pamutu pake ndi khoza la pa dzanja lake ndipo ndazibweretsa kwa inu mbuye wanga.” 11 Apo Davide ndi anthu onse amene anali nawo anangʼamba zovala zawo. 12 Iwo analira maliro ndi kusala zakudya mpaka madzulo chifukwa cha Sauli ndi mwana wake Yonatani, komanso chifukwa cha gulu la ankhondo la Yehova ndi nyumba ya Israeli, chifukwa anaphedwa ndi lupanga. 13 Davide anati kwa mnyamata amene anabweretsa uthengawo, “Iwe umachokera kuti?”Iye anayankha kuti, “Ine ndine mwana wa mlendo Mwamaleki.” 14 Davide anamufunsanso kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunaope kukweza dzanja lako ndi kupha wodzozedwa wa Yehova?” 15 Kenaka Davide anayitana mmodzi mwa anyamata ake ndipo anati, “Pita ukamukanthe!” Kotero iye anapita kukamukantha, ndipo mnyamata uja anafa. 16 Pakuti Davide anali atanena kwa iye kuti, “Iwe wadzipha wekha. Pakamwa pako pakunena zokutsutsa wekha, pamene unanena kuti, ‘Ine ndapha wodzozedwa wa Yehova.’ ” 17 Davide anayimba nyimbo iyi ya maliro, kulira Sauli ndi mwana wake Yonatani. 18 Ndipo analamula kuti anthu a ku Yuda aphunzitsidwe nyimbo ya maliroyi imene yalembedwa mʼbuku la Yasari: 19 “Ulemerero wako iwe Israeli, wagona utaphedwa ku zitunda.Taonani amphamvu agwa kumeneko! 20 “Musakanene zimenezi ku Gati,musazilengeze ku misewu ya ku Asikeloni,kuti ana aakazi a Afilisti angasangalale,ana aakazi a osachita mdulidwe angakondwere. 21 “Inu mapiri a ku Gilibowa,musakhalenso ndi mame kapena mvula,kapena minda yobereka zopereka za ufa.Pakuti kumeneko chishango cha munthu wamphamvu chinadetsedwa,chishango cha Sauli sanachipakenso mafuta. 22 “Pa magazi a ophedwa,pa mnofu wa amphamvu,uta wa Yonatani sunabwerere,lupanga la Sauli silinabwere chabe. 23 “Sauli ndi Yonatani,pa moyo wawo anali okondedwa ndi okoma mtima,ndipo pa imfa yawo sanasiyanitsidwe.Iwo anali ndi liwiro loposa ziwombankhanga,anali ndi mphamvu zoposa mkango. 24 “Inu ana aakazi a Israeli,mulireni Sauli,amene anakuvekani zovala zofiira ndi zofewa,amene anakometsera zovala zanu ndi zokometsera zagolide. 25 “Taonani amphamvu agwa ku nkhondo!Yonatani wagona ataphedwa ku zitunda. 26 Ine ndikuvutika mumtima chifukwa cha iwe mʼbale wanga Yonatani,unali wokondedwa kwambiri kwa ine.Chikondi chako pa ine chinali chopambana,chopambana kuposa chikondi cha akazi. 27 “Taonani amphamvu agwa!Zida zankhondo zawonongeka!”
In Other Versions
2 Samuel 1 in the ANGEFD
2 Samuel 1 in the ANTPNG2D
2 Samuel 1 in the AS21
2 Samuel 1 in the BAGH
2 Samuel 1 in the BBPNG
2 Samuel 1 in the BBT1E
2 Samuel 1 in the BDS
2 Samuel 1 in the BEV
2 Samuel 1 in the BHAD
2 Samuel 1 in the BIB
2 Samuel 1 in the BLPT
2 Samuel 1 in the BNT
2 Samuel 1 in the BNTABOOT
2 Samuel 1 in the BNTLV
2 Samuel 1 in the BOATCB
2 Samuel 1 in the BOATCB2
2 Samuel 1 in the BOBCV
2 Samuel 1 in the BOCNT
2 Samuel 1 in the BOECS
2 Samuel 1 in the BOHCB
2 Samuel 1 in the BOHCV
2 Samuel 1 in the BOHLNT
2 Samuel 1 in the BOHNTLTAL
2 Samuel 1 in the BOICB
2 Samuel 1 in the BOILNTAP
2 Samuel 1 in the BOITCV
2 Samuel 1 in the BOKCV
2 Samuel 1 in the BOKCV2
2 Samuel 1 in the BOKHWOG
2 Samuel 1 in the BOKSSV
2 Samuel 1 in the BOLCB
2 Samuel 1 in the BOLCB2
2 Samuel 1 in the BOMCV
2 Samuel 1 in the BONAV
2 Samuel 1 in the BONCB
2 Samuel 1 in the BONLT
2 Samuel 1 in the BONUT2
2 Samuel 1 in the BOPLNT
2 Samuel 1 in the BOSCB
2 Samuel 1 in the BOSNC
2 Samuel 1 in the BOTLNT
2 Samuel 1 in the BOVCB
2 Samuel 1 in the BOYCB
2 Samuel 1 in the BPBB
2 Samuel 1 in the BPH
2 Samuel 1 in the BSB
2 Samuel 1 in the CCB
2 Samuel 1 in the CUV
2 Samuel 1 in the CUVS
2 Samuel 1 in the DBT
2 Samuel 1 in the DGDNT
2 Samuel 1 in the DHNT
2 Samuel 1 in the DNT
2 Samuel 1 in the ELBE
2 Samuel 1 in the EMTV
2 Samuel 1 in the ESV
2 Samuel 1 in the FBV
2 Samuel 1 in the FEB
2 Samuel 1 in the GGMNT
2 Samuel 1 in the GNT
2 Samuel 1 in the HARY
2 Samuel 1 in the HNT
2 Samuel 1 in the IRVA
2 Samuel 1 in the IRVB
2 Samuel 1 in the IRVG
2 Samuel 1 in the IRVH
2 Samuel 1 in the IRVK
2 Samuel 1 in the IRVM
2 Samuel 1 in the IRVM2
2 Samuel 1 in the IRVO
2 Samuel 1 in the IRVP
2 Samuel 1 in the IRVT
2 Samuel 1 in the IRVT2
2 Samuel 1 in the IRVU
2 Samuel 1 in the ISVN
2 Samuel 1 in the JSNT
2 Samuel 1 in the KAPI
2 Samuel 1 in the KBT1ETNIK
2 Samuel 1 in the KBV
2 Samuel 1 in the KJV
2 Samuel 1 in the KNFD
2 Samuel 1 in the LBA
2 Samuel 1 in the LBLA
2 Samuel 1 in the LNT
2 Samuel 1 in the LSV
2 Samuel 1 in the MAAL
2 Samuel 1 in the MBV
2 Samuel 1 in the MBV2
2 Samuel 1 in the MHNT
2 Samuel 1 in the MKNFD
2 Samuel 1 in the MNG
2 Samuel 1 in the MNT
2 Samuel 1 in the MNT2
2 Samuel 1 in the MRS1T
2 Samuel 1 in the NAA
2 Samuel 1 in the NASB
2 Samuel 1 in the NBLA
2 Samuel 1 in the NBS
2 Samuel 1 in the NBVTP
2 Samuel 1 in the NET2
2 Samuel 1 in the NIV11
2 Samuel 1 in the NNT
2 Samuel 1 in the NNT2
2 Samuel 1 in the NNT3
2 Samuel 1 in the PDDPT
2 Samuel 1 in the PFNT
2 Samuel 1 in the RMNT
2 Samuel 1 in the SBIAS
2 Samuel 1 in the SBIBS
2 Samuel 1 in the SBIBS2
2 Samuel 1 in the SBICS
2 Samuel 1 in the SBIDS
2 Samuel 1 in the SBIGS
2 Samuel 1 in the SBIHS
2 Samuel 1 in the SBIIS
2 Samuel 1 in the SBIIS2
2 Samuel 1 in the SBIIS3
2 Samuel 1 in the SBIKS
2 Samuel 1 in the SBIKS2
2 Samuel 1 in the SBIMS
2 Samuel 1 in the SBIOS
2 Samuel 1 in the SBIPS
2 Samuel 1 in the SBISS
2 Samuel 1 in the SBITS
2 Samuel 1 in the SBITS2
2 Samuel 1 in the SBITS3
2 Samuel 1 in the SBITS4
2 Samuel 1 in the SBIUS
2 Samuel 1 in the SBIVS
2 Samuel 1 in the SBT
2 Samuel 1 in the SBT1E
2 Samuel 1 in the SCHL
2 Samuel 1 in the SNT
2 Samuel 1 in the SUSU
2 Samuel 1 in the SUSU2
2 Samuel 1 in the SYNO
2 Samuel 1 in the TBIAOTANT
2 Samuel 1 in the TBT1E
2 Samuel 1 in the TBT1E2
2 Samuel 1 in the TFTIP
2 Samuel 1 in the TFTU
2 Samuel 1 in the TGNTATF3T
2 Samuel 1 in the THAI
2 Samuel 1 in the TNFD
2 Samuel 1 in the TNT
2 Samuel 1 in the TNTIK
2 Samuel 1 in the TNTIL
2 Samuel 1 in the TNTIN
2 Samuel 1 in the TNTIP
2 Samuel 1 in the TNTIZ
2 Samuel 1 in the TOMA
2 Samuel 1 in the TTENT
2 Samuel 1 in the UBG
2 Samuel 1 in the UGV
2 Samuel 1 in the UGV2
2 Samuel 1 in the UGV3
2 Samuel 1 in the VBL
2 Samuel 1 in the VDCC
2 Samuel 1 in the YALU
2 Samuel 1 in the YAPE
2 Samuel 1 in the YBVTP
2 Samuel 1 in the ZBP