2 Timothy 2 (BOGWICC)

1 Tsono iwe, mwana wanga, limbika mʼchisomo chimene chili mwa Khristu Yesu. 2 Ndipo zinthu zimene unamva ine ndikuziyankhula pamaso pa mboni zambiri, uziphunzitse kwa anthu odalirika amene akaphunzitsenso ena. 3 Umve nane zowawa, monga msilikali wa Khristu Yesu. 4 Palibe msilikali amene ali pa ntchito amagwiranso ntchito za anthu wamba, iye amafuna kukondweretsa bwana wolamulira. 5 Chimodzimodzinso, munthu amene ali pa mpikisano waliwiro, salandira mphotho ya wopambana pokhapokha atatsiriza monga mwa malamulo a mpikisanowo. 6 Mlimi wolimbika ndi amene amayembekezereka kukhala woyambirira kulandira gawo la zokolola. 7 Lingalira zimene ndikunenazi, pakuti Ambuye adzakuzindikiritsa zonsezi. 8 Kumbukira Yesu Khristu wochokera ku mtundu wa Davide kuti anauka kwa akufa. Uwu ndiye uthenga wanga wabwino 9 umene ndikuwuvutikira choterewu mpaka kumangidwa ndi maunyolo ngati wakuba. Koma mawu a Mulungu sanamangidwe ndi maunyolo. 10 Choncho ndikupirira chilichonse chifukwa cha osankhidwa, kuti nawonso apulumutsidwe ndi Khristu Yesu ndi kulandira ulemerero wosatha. 11 Mawu oyenera kuwadalira ndi awa:Ngati ife tinafa naye pamodzi,tidzakhalanso moyo pamodzi naye. 12 Ngati tinapirira,tidzalamuliranso naye pamodzi.Ngati ife timukana,Iye adzatikananso. 13 Ngati ndife osakhulupirika,Iye adzakhalabe wokhulupirikapopeza sangathe kudzikana. 14 Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo. 15 Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola. 16 Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera. 17 Chiphunzitso chawo chidzafalikira ngati chilonda. Mwa anthuwa muli Humenayo ndi Fileto. 18 Iwowa apatuka pa choonadi. Iwo amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kunachitika kale, motero amawononga chikhulupiriro cha anthu ena. 19 Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.” 20 Mʼnyumba yayikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Zina zimakhala za ntchito yapamwamba, zina za ntchito wamba. 21 Munthu akadziyeretsa nʼkusiya ntchito za wambazi, adzakhala chiwiya cha ntchito yapamwamba, woyeretsedwa, ndi waphindu kwa Ambuye wake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino. 22 Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa. 23 Ukane matsutsano oyipa ndi opusa, chifukwa amayambitsa mikangano. 24 Ndiponso mtumiki wa Ambuye asamakangane ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa aliyense, wodziwa kuphunzitsa, osati wokalipakalipa. 25 Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi. 26 Motero nzeru zawo zidzabweramo, ndipo adzathawa msampha wa mdierekezi, amene anawagwira ukapolo kuti azichita zofuna zake.

In Other Versions

2 Timothy 2 in the ANGEFD

2 Timothy 2 in the ANTPNG2D

2 Timothy 2 in the AS21

2 Timothy 2 in the BAGH

2 Timothy 2 in the BBPNG

2 Timothy 2 in the BBT1E

2 Timothy 2 in the BDS

2 Timothy 2 in the BEV

2 Timothy 2 in the BHAD

2 Timothy 2 in the BIB

2 Timothy 2 in the BLPT

2 Timothy 2 in the BNT

2 Timothy 2 in the BNTABOOT

2 Timothy 2 in the BNTLV

2 Timothy 2 in the BOATCB

2 Timothy 2 in the BOATCB2

2 Timothy 2 in the BOBCV

2 Timothy 2 in the BOCNT

2 Timothy 2 in the BOECS

2 Timothy 2 in the BOHCB

2 Timothy 2 in the BOHCV

2 Timothy 2 in the BOHLNT

2 Timothy 2 in the BOHNTLTAL

2 Timothy 2 in the BOICB

2 Timothy 2 in the BOILNTAP

2 Timothy 2 in the BOITCV

2 Timothy 2 in the BOKCV

2 Timothy 2 in the BOKCV2

2 Timothy 2 in the BOKHWOG

2 Timothy 2 in the BOKSSV

2 Timothy 2 in the BOLCB

2 Timothy 2 in the BOLCB2

2 Timothy 2 in the BOMCV

2 Timothy 2 in the BONAV

2 Timothy 2 in the BONCB

2 Timothy 2 in the BONLT

2 Timothy 2 in the BONUT2

2 Timothy 2 in the BOPLNT

2 Timothy 2 in the BOSCB

2 Timothy 2 in the BOSNC

2 Timothy 2 in the BOTLNT

2 Timothy 2 in the BOVCB

2 Timothy 2 in the BOYCB

2 Timothy 2 in the BPBB

2 Timothy 2 in the BPH

2 Timothy 2 in the BSB

2 Timothy 2 in the CCB

2 Timothy 2 in the CUV

2 Timothy 2 in the CUVS

2 Timothy 2 in the DBT

2 Timothy 2 in the DGDNT

2 Timothy 2 in the DHNT

2 Timothy 2 in the DNT

2 Timothy 2 in the ELBE

2 Timothy 2 in the EMTV

2 Timothy 2 in the ESV

2 Timothy 2 in the FBV

2 Timothy 2 in the FEB

2 Timothy 2 in the GGMNT

2 Timothy 2 in the GNT

2 Timothy 2 in the HARY

2 Timothy 2 in the HNT

2 Timothy 2 in the IRVA

2 Timothy 2 in the IRVB

2 Timothy 2 in the IRVG

2 Timothy 2 in the IRVH

2 Timothy 2 in the IRVK

2 Timothy 2 in the IRVM

2 Timothy 2 in the IRVM2

2 Timothy 2 in the IRVO

2 Timothy 2 in the IRVP

2 Timothy 2 in the IRVT

2 Timothy 2 in the IRVT2

2 Timothy 2 in the IRVU

2 Timothy 2 in the ISVN

2 Timothy 2 in the JSNT

2 Timothy 2 in the KAPI

2 Timothy 2 in the KBT1ETNIK

2 Timothy 2 in the KBV

2 Timothy 2 in the KJV

2 Timothy 2 in the KNFD

2 Timothy 2 in the LBA

2 Timothy 2 in the LBLA

2 Timothy 2 in the LNT

2 Timothy 2 in the LSV

2 Timothy 2 in the MAAL

2 Timothy 2 in the MBV

2 Timothy 2 in the MBV2

2 Timothy 2 in the MHNT

2 Timothy 2 in the MKNFD

2 Timothy 2 in the MNG

2 Timothy 2 in the MNT

2 Timothy 2 in the MNT2

2 Timothy 2 in the MRS1T

2 Timothy 2 in the NAA

2 Timothy 2 in the NASB

2 Timothy 2 in the NBLA

2 Timothy 2 in the NBS

2 Timothy 2 in the NBVTP

2 Timothy 2 in the NET2

2 Timothy 2 in the NIV11

2 Timothy 2 in the NNT

2 Timothy 2 in the NNT2

2 Timothy 2 in the NNT3

2 Timothy 2 in the PDDPT

2 Timothy 2 in the PFNT

2 Timothy 2 in the RMNT

2 Timothy 2 in the SBIAS

2 Timothy 2 in the SBIBS

2 Timothy 2 in the SBIBS2

2 Timothy 2 in the SBICS

2 Timothy 2 in the SBIDS

2 Timothy 2 in the SBIGS

2 Timothy 2 in the SBIHS

2 Timothy 2 in the SBIIS

2 Timothy 2 in the SBIIS2

2 Timothy 2 in the SBIIS3

2 Timothy 2 in the SBIKS

2 Timothy 2 in the SBIKS2

2 Timothy 2 in the SBIMS

2 Timothy 2 in the SBIOS

2 Timothy 2 in the SBIPS

2 Timothy 2 in the SBISS

2 Timothy 2 in the SBITS

2 Timothy 2 in the SBITS2

2 Timothy 2 in the SBITS3

2 Timothy 2 in the SBITS4

2 Timothy 2 in the SBIUS

2 Timothy 2 in the SBIVS

2 Timothy 2 in the SBT

2 Timothy 2 in the SBT1E

2 Timothy 2 in the SCHL

2 Timothy 2 in the SNT

2 Timothy 2 in the SUSU

2 Timothy 2 in the SUSU2

2 Timothy 2 in the SYNO

2 Timothy 2 in the TBIAOTANT

2 Timothy 2 in the TBT1E

2 Timothy 2 in the TBT1E2

2 Timothy 2 in the TFTIP

2 Timothy 2 in the TFTU

2 Timothy 2 in the TGNTATF3T

2 Timothy 2 in the THAI

2 Timothy 2 in the TNFD

2 Timothy 2 in the TNT

2 Timothy 2 in the TNTIK

2 Timothy 2 in the TNTIL

2 Timothy 2 in the TNTIN

2 Timothy 2 in the TNTIP

2 Timothy 2 in the TNTIZ

2 Timothy 2 in the TOMA

2 Timothy 2 in the TTENT

2 Timothy 2 in the UBG

2 Timothy 2 in the UGV

2 Timothy 2 in the UGV2

2 Timothy 2 in the UGV3

2 Timothy 2 in the VBL

2 Timothy 2 in the VDCC

2 Timothy 2 in the YALU

2 Timothy 2 in the YAPE

2 Timothy 2 in the YBVTP

2 Timothy 2 in the ZBP