Acts 19 (BOGWICC)

1 Apolo ali ku Korinto, Paulo anadutsa mʼmayiko a ku mtunda ndipo anafika ku Efeso. Kumeneko anapeza ophunzira ena. 2 Iye anawafunsa kuti, “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira?”Iwo anayankha kuti, “Ayi, ife sitinamvepo kuti kuli Mzimu Woyera.” 3 Tsono Paulo anawafunsa kuti, “Nanga munabatizidwa ndi ubatizo wotani?”Iwo anati, “Ubatizo wa Yohane.” 4 Paulo anati, “Ubatizo wa Yohane unali wa kutembenuka mtima. Iye anawuza anthu kuti akhulupirire amene amabwera, ameneyo ndiye Yesu.” 5 Atamva zimenezi, anabatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 6 Pamene Paulo anawasanjika manja, Mzimu Woyera anadza pa iwo ndipo anayankhula mʼmalilime ndipo ananenera. 7 Anthu onsewo analipo khumi ndi awiri. 8 Paulo analowa mʼsunagoge ndipo anayankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa mowakopa za ufumu wa Mulungu. 9 Koma ena anawumitsa mitima; anakana kukhulupirira ndipo ananyoza Njirayo pa gulu la anthu. Kotero Paulo anawasiya. Iye anatenga ophunzirawo ndipo amakambirana tsiku ndi tsiku mʼsukulu ya Turano. 10 Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, kotero kuti Ayuda onse ndi Agriki amene amakhala ku Asiya anamva Mawu a Ambuye. 11 Mulungu anachita zodabwitsa zapadera kudzera mwa Paulo. 12 Kotero kuti mipango yopukutira thukuta ndi yovala pogwira ntchito, zomwe zinakhudza thupi la Paulo amapita nazo kwa odwala ndipo amachiritsidwa ndiponso mizimu yoyipa mwa iwo imatuluka. 13 Ayuda ena amene ankayendayenda kutulutsa mizimu yoyipa anayesa kugwiritsa ntchito dzina la Ambuye Yesu pa amene anali ndi ziwanda. Iwo popemphera amati, “Ine ndikulamulira utuluke, mʼdzina la Yesu amene Paulo amamulalikira.” 14 Amene ankachita zimenezi anali ana asanu ndi awiri a Skeva, mkulu wa ansembe wa Chiyuda. 15 Tsiku lina mzimu woyipa unawayankha kuti, “Yesu ndimamudziwa ndiponso Paulo ndimamudziwa, nanga inu ndinu ndani?” 16 Pamenepo munthu amene anali ndi mzimu woyipa anawalumphira nawagwira onse. Iye anawamenya kwambiri, kotero kuti anathawa mʼnyumbamo ali maliseche, akutuluka magazi. 17 Ayuda ndi Agriki okhala ku Efeso atamva zimenezi, anachita mantha, ndipo anthu anachitira ulemu dzina la Ambuye Yesu koposa. 18 Ambiri a iwo amene tsopano anakhulupirira anafika ndi kuvomereza poyera ntchito zawo zoyipa. 19 Ambiri amene amachita za matsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi nawatentha pamaso pa anthu onse. Atawonkhetsa mtengo wa mabukuwo, unakwanira ndalama zasiliva 50,000. 20 Kotero Mawu a Ambuye anapitirira kufalikira ndipo anagwira ntchito mwamphamvu. 21 Zonsezi zitachitika Paulo anatsimikiza zopita ku Yerusalemu kudzera ku Makedoniya ndi ku Akaya. Iye anati, “Kuchokera kumeneko, ndiyenera kukafikanso ku Roma.” 22 Iye anatuma anthu awiri amene amamuthandiza, Timoteyo ndi Erasto ku Makedoniya, pamene iye anakhalabe ku Asiya kwa kanthawi. 23 Pa nthawi yomweyo panachitika chipolowe chachikulu chifukwa cha Njira ya Ambuye. 24 Mmisiri wantchito zasiliva, dzina lake Demetriyo, amene amapanga mafano asiliva a Atemi ankabweretsa phindu lalikulu kwa amisiri a kumeneko. 25 Iye anasonkhanitsa pamodzi amisiriwo, pamodzinso ndi anthu ena ogwira ntchito yomweyo ndipo anati, “Anthu inu, mukudziwa kuti ife timapeza chuma chathu kuchokera pa ntchito imeneyi. 26 Ndipo inu mukuona ndi kumva kuti munthu uyu Paulo wakopa ndi kusokoneza anthu ambiri a ku Efeso ndiponso pafupifupi dziko lonse la Asiya. Iye akunena kuti milungu yopangidwa ndi anthu si milungu ayi. 27 Choopsa ndi chakuti sikungowonongeka kwa ntchito yathu yokha ayi, komanso kuti nyumba ya mulungu wamkulu wamkazi Atemi idzanyozedwa ndipo mulungu wamkazi weniweniyo amene amapembedzedwa ku Asiya konse ndi dziko lapansi, ukulu wake udzawonongekanso.” 28 Atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndipo anayamba kufuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi.” 29 Nthawi yomweyo mu mzinda wonse munabuka chipolowe. Anthu anagwira Gayo ndi Aristariko, anzake a Paulo a ku Makedoniya, ndipo anathamangira nawo ku bwalo la masewero. 30 Paulo anafuna kulowa pakati pa gulu la anthu, koma ophunzira anamuletsa. 31 Ngakhale olamulira ena aderalo, amene anali abwenzi a Paulo, anatumiza uthenga kumuletsa kuti asayesere kulowa mʼbwalomo. 32 Munali chisokonezo mʼbwalomo pakuti ena amafuwula zina, enanso zina. Anthu ambiri sanadziwe ngakhale chomwe anasonkhanira. 33 Ayuda anamukankhira Alekisandro kutsogolo, ndipo ena anafuwula kumulangiza iye. Iye anatambasula dzanja kuti anthu akhale chete kuti afotokozere anthu nkhaniyo. 34 Koma pamene anthuwo anazindikira kuti ndi Myuda, onse pamodzi kwa maora awiri anafuwula kuti, “Wamkulu ndi Atemi wa ku Efeso!” 35 Mlembi wa mzindawo anakhazikitsa bata gulu la anthuwo ndipo anati, “Anthu a ku Efeso, kodi ndani pa dziko lonse lapansi amene sadziwa kuti mzinda wa Efeso umayangʼanira nyumba ya mulungu wamkulu Atemi ndi fanizo lake, limene linagwa kuchokera kumwamba? 36 Chifukwa chake popeza zinthu izi palibe amene angazikane, inu mukuyenera kukhala chete osachita kanthu kalikonse mofulumira. 37 Inu mwabweretsa anthu awa pano, ngakhale kuti iwo sanabe mʼnyumba zathu zamapemphero kapena kunenera chipongwe mulungu wathu wamkazi. 38 Ngati tsono Demetriyo ndi amisiri anzake ali ndi nkhani ndi munthu wina aliyense, mabwalo a milandu alipo, oweruza aliponso. Akhoza kukapereka nkhaniyo kwa oweruza milanduwo. 39 Ngati mukufuna kubweretsa kanthu kali konse, ziyenera kukatsimikizidwa ndi bwalo lovomerezeka. 40 Monga mmene zililimu, ife titha kuzengedwa mlandu woyambitsa chipolowe chifukwa cha zimene zachitika lerozi. Motero ife sitingathe kufotokoza za chipolowechi popeza palibe nkhani yake.” 41 Iye atatha kunena zimenezi anawuza gulu la anthulo kuti libalalike.

In Other Versions

Acts 19 in the ANGEFD

Acts 19 in the ANTPNG2D

Acts 19 in the AS21

Acts 19 in the BAGH

Acts 19 in the BBPNG

Acts 19 in the BBT1E

Acts 19 in the BDS

Acts 19 in the BEV

Acts 19 in the BHAD

Acts 19 in the BIB

Acts 19 in the BLPT

Acts 19 in the BNT

Acts 19 in the BNTABOOT

Acts 19 in the BNTLV

Acts 19 in the BOATCB

Acts 19 in the BOATCB2

Acts 19 in the BOBCV

Acts 19 in the BOCNT

Acts 19 in the BOECS

Acts 19 in the BOHCB

Acts 19 in the BOHCV

Acts 19 in the BOHLNT

Acts 19 in the BOHNTLTAL

Acts 19 in the BOICB

Acts 19 in the BOILNTAP

Acts 19 in the BOITCV

Acts 19 in the BOKCV

Acts 19 in the BOKCV2

Acts 19 in the BOKHWOG

Acts 19 in the BOKSSV

Acts 19 in the BOLCB

Acts 19 in the BOLCB2

Acts 19 in the BOMCV

Acts 19 in the BONAV

Acts 19 in the BONCB

Acts 19 in the BONLT

Acts 19 in the BONUT2

Acts 19 in the BOPLNT

Acts 19 in the BOSCB

Acts 19 in the BOSNC

Acts 19 in the BOTLNT

Acts 19 in the BOVCB

Acts 19 in the BOYCB

Acts 19 in the BPBB

Acts 19 in the BPH

Acts 19 in the BSB

Acts 19 in the CCB

Acts 19 in the CUV

Acts 19 in the CUVS

Acts 19 in the DBT

Acts 19 in the DGDNT

Acts 19 in the DHNT

Acts 19 in the DNT

Acts 19 in the ELBE

Acts 19 in the EMTV

Acts 19 in the ESV

Acts 19 in the FBV

Acts 19 in the FEB

Acts 19 in the GGMNT

Acts 19 in the GNT

Acts 19 in the HARY

Acts 19 in the HNT

Acts 19 in the IRVA

Acts 19 in the IRVB

Acts 19 in the IRVG

Acts 19 in the IRVH

Acts 19 in the IRVK

Acts 19 in the IRVM

Acts 19 in the IRVM2

Acts 19 in the IRVO

Acts 19 in the IRVP

Acts 19 in the IRVT

Acts 19 in the IRVT2

Acts 19 in the IRVU

Acts 19 in the ISVN

Acts 19 in the JSNT

Acts 19 in the KAPI

Acts 19 in the KBT1ETNIK

Acts 19 in the KBV

Acts 19 in the KJV

Acts 19 in the KNFD

Acts 19 in the LBA

Acts 19 in the LBLA

Acts 19 in the LNT

Acts 19 in the LSV

Acts 19 in the MAAL

Acts 19 in the MBV

Acts 19 in the MBV2

Acts 19 in the MHNT

Acts 19 in the MKNFD

Acts 19 in the MNG

Acts 19 in the MNT

Acts 19 in the MNT2

Acts 19 in the MRS1T

Acts 19 in the NAA

Acts 19 in the NASB

Acts 19 in the NBLA

Acts 19 in the NBS

Acts 19 in the NBVTP

Acts 19 in the NET2

Acts 19 in the NIV11

Acts 19 in the NNT

Acts 19 in the NNT2

Acts 19 in the NNT3

Acts 19 in the PDDPT

Acts 19 in the PFNT

Acts 19 in the RMNT

Acts 19 in the SBIAS

Acts 19 in the SBIBS

Acts 19 in the SBIBS2

Acts 19 in the SBICS

Acts 19 in the SBIDS

Acts 19 in the SBIGS

Acts 19 in the SBIHS

Acts 19 in the SBIIS

Acts 19 in the SBIIS2

Acts 19 in the SBIIS3

Acts 19 in the SBIKS

Acts 19 in the SBIKS2

Acts 19 in the SBIMS

Acts 19 in the SBIOS

Acts 19 in the SBIPS

Acts 19 in the SBISS

Acts 19 in the SBITS

Acts 19 in the SBITS2

Acts 19 in the SBITS3

Acts 19 in the SBITS4

Acts 19 in the SBIUS

Acts 19 in the SBIVS

Acts 19 in the SBT

Acts 19 in the SBT1E

Acts 19 in the SCHL

Acts 19 in the SNT

Acts 19 in the SUSU

Acts 19 in the SUSU2

Acts 19 in the SYNO

Acts 19 in the TBIAOTANT

Acts 19 in the TBT1E

Acts 19 in the TBT1E2

Acts 19 in the TFTIP

Acts 19 in the TFTU

Acts 19 in the TGNTATF3T

Acts 19 in the THAI

Acts 19 in the TNFD

Acts 19 in the TNT

Acts 19 in the TNTIK

Acts 19 in the TNTIL

Acts 19 in the TNTIN

Acts 19 in the TNTIP

Acts 19 in the TNTIZ

Acts 19 in the TOMA

Acts 19 in the TTENT

Acts 19 in the UBG

Acts 19 in the UGV

Acts 19 in the UGV2

Acts 19 in the UGV3

Acts 19 in the VBL

Acts 19 in the VDCC

Acts 19 in the YALU

Acts 19 in the YAPE

Acts 19 in the YBVTP

Acts 19 in the ZBP