Acts 27 (BOGWICC)
1 Zitatsimikizika kuti tiyenera kupita ku Italiya pa sitima ya pa madzi, anamupereka Paulo pamodzi ndi a mʼndende ena kwa msilikali wolamulira asilikali 100, dzina lake Yuliyo, amene anali wa gulu la asilikali lotchedwa, Gulu la Mfumu. 2 Tinakwera sitima ya pamadzi yochokera ku Adramutiyo imene inali yokonzeka kale kupita ku madooko a ku Asiya, ndipo tinanyamuka. Aristariko, wa ku Makedoniya wa ku mzinda wa Tesalonika, anali nafe. 3 Mmawa mwake tinafika ku Sidoni; ndipo Yuliyo, mokomera mtima Paulo, anamulola kupita kwa abwenzi ake kuti akamupatse zosowa zake. 4 Kuchokera kumeneko tinayambanso ulendo pa nyanja ndipo tinadutsa kumpoto kwa chilumba cha Kupro chifukwa mphepo imawomba kuchokera kumene ife timapita. 5 Titawoloka nyanja mbali ya gombe la Kilikiya ndi Pamfiliya, tinakafika ku Mura, mzinda wa ku Lukia. 6 Kumeneko wolamulira asilikali 100 uja anapeza sitima ya pamadzi ya ku Alekisandriya imene imapita ku Italiya, ndipo anatikweza mʼmenemo. 7 Tinayenda pangʼonopangʼono kwa masiku ambiri ndipo tinakafika kufupi ndi Knido movutikira. Pamene mphepo sinatilole kupitirira ulendo wathu molunjika, tinadzera kummwera kwa chilumba cha Krete, moyangʼanana ndi Salimoni. 8 Timayenda movutikira mʼmbali mwa chilumbacho ndipo tinafika pa malo wotchedwa Madooko Okoma, pafupi ndi mzinda wa Laseya. 9 Tinataya nthawi yayitali, ndipo kuyenda pa nyanja kunali koopsa chifukwa nʼkuti tsopano nthawi yosala kudya itapita kale. Choncho Paulo anawachenjeza kuti, 10 “Anthu inu, ine ndikuona kuti ulendo wathuwu ukhala woopsa ndipo katundu ndi sitima ziwonongeka, ngakhalenso miyoyo yathu.” 11 Koma wolamulira asilikali 100 uja, mʼmalo momvera zimene Paulo amanena, anatsatira malangizo a woyendetsa sitimayo ndiponso mwini wa sitimayo. 12 Popeza kuti dookolo silinali labwino kukhalako nthawi yozizira anthu ambiri anaganiza kuti tichoke. Ife tinkayembekeza kukafika ku Foinikisi ndi kukhala kumeneko nthawi yachisanu. Ili linali dooko la ku Krete, limene limaloza kummwera cha kumadzulo ndiponso kumpoto cha kumadzulo. 13 Mphepo yochokera kummwera itayamba kuwomba pangʼonopangʼono, anthuwo anaganiza kuti apeza chimene amafuna; kotero analowetsa nangula ndipo anayamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba cha Krete. 14 Pasanathe nthawi yayitali, mphepo yamkuntho yotchedwa Eurokulo, inayamba kuwomba kuchokera ku chilumbacho. 15 Mphepo yamkunthoyo inawomba sitima ija ndipo sinathe kulimbana nayo, kotero ife tinayigonjera ndi kuyamba kutengedwa nayo. 16 Tikudutsa mʼmbali mwa kachilumba kakangʼono kotchedwa Kawuda, tinavutika kuti tisunge bwato lopulumukiramo. 17 Anthuwo atakweza bwatolo mʼsitima, anakulunga zingwe sitimayo kuti ayilimbitse. Poopa kuti angakagunde mchenga wa ku Surti, iwo anatsitsa nangula ndi kuyilola sitima kuti idzingoyenda ndi mphepo. 18 Ife tinavutika kwambiri ndi namondwe kotero kuti mmawa mwake tinayamba kuponya katundu mʼmadzi. 19 Pa tsiku lachitatu anaponya mʼnyanja zipangizo za mʼsitima ndi manja awo. 20 Sitinaone dzuwa kapena nyenyezi kwa masiku ambiri ndipo namondwe anapitirira kuwomba kwambiri, pomaliza ife tonse tinalibenso chiyembekezo choti nʼkupulumuka. 21 Anthu aja atakhala nthawi yayitali osadya, Paulo anayimirira pakati pawo ndipo anati, “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga oti tisachoke ku Krete: zonsezi sizikanawonongeka ndi kutayika. 22 Koma tsopano ndikuti limbani mtima, chifukwa palibe aliyense wa inu amene adzataya moyo wake; koma sitima yokhayi idzawonongeka. 23 Usiku wathawu mngelo wa Mulungu, Mulungu amene ine ndili wake ndipo ndimamutumikira, anayima pafupi ndi ine, 24 ndipo iyeyu anati, ‘Usachite mantha, Paulo. Ukuyenera kukayima pamaso pa Kaisara; ndipo Mulungu mwa kukoma mtima kwake wakupatsa miyoyo ya anthu onse amene ukuyenda nawo.’ 25 Tsono limbani mtima, anthu inu, pakuti ine ndili ndi chikhulupiriro mwa Mulungu kuti zichitika monga momwe wandiwuzira. 26 Komabe tiyenera kukatsakamira pa chilumba china chake.” 27 Pakati pa usiku wa tsiku la khumi ndi chinayi tikukankhidwabe ndi mphepo mʼnyanja ya Adriya, oyendetsa sitimayo anazindikira kuti timayandikira ku mtunda. 28 Iwo anatenga choyezera kuzama kwa nyanja ndi kupeza kuti kuzama kwake kunali mamita 36. Atayendanso pangʼono anatenganso choyezera chija napeza kuti kuzama kwake kunali 27. 29 Poopa kuti tingagunde miyala, iwo anatsitsira anangula anayi mʼmadzi kumbuyo kwa sitimayo ndipo tinapemphera kuti kuche. 30 Pofuna kuthawa mʼsitimayo, oyendetsa aja anatsitsira mʼnyanja bwato lopulumukiramo nʼkumachita ngati akufuna kutsitsira anangula mʼnyanjamo kutsogolo kwa sitimayo. 31 Pamenepo Paulo anawuza wolamulira asilikali uja ndi asilikaliwo kuti, “Ngati anthu awa sakhala mʼsitima muno, inu simungapulumuke.” 32 Pamenepo asilikaliwo anadula zingwe za bwatolo ndipo linagwera mʼmadzi. 33 Kutatsala pangʼono kucha, Paulo anawawumiriza anthu onse kuti adye. Iye anati, “Kwa masiku khumi ndi anayi mwakhala mukuda nkhawa ndipo simumadya kanthu kalikonse. 34 Tsopano ine ndikukupemphani kuti mudye. Muyenera kudya kuti mupulumuke. Palibe ndi mmodzi yemwe wa inu adzataye ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pake.” 35 Paulo atanena zimenezi, anatenga buledi nayamika Mulungu pamaso pa onse. Ndipo ananyema bulediyo nayamba kudya. 36 Onse analimba mtima nayamba kudyanso. 37 Tonse pamodzi mʼsitimamo tinalipo anthu 276. 38 Onse atadya, nakhuta anapeputsa sitimayo potaya tirigu mʼnyanja. 39 Kutacha, anthu sanazindikire dzikolo, koma anaona pomwe sitima zimayimapo pamodzi ndi mchenga wa pa gombe. Iwo anaganiza zokocheza sitimayo kumeneko ngati zikanatheka kutero. 40 Atadula anangula aja, nawasiya mʼnyanja, pa nthawi yomweyo anamasula zingwe zimene anamangira zowongolera sitimayo. Kenaka anayimika chinsalu chimene mphepo imakankha kuti sitima iyende, ndipo anayamba kupita ku gombe. 41 Koma sitimayo inagunda mchenga wobisika ndipo inayima. Mbali ya kutsogolo ya sitimayo inakanirira ndipo sinathe kuyendanso, ndipo mbali yakumbuyo inasweka ndi kuwomba kwa mafunde. 42 Asilikali anaganiza za kupha amʼndende onse, kuti angasambire kupita pa mtunda ndi kuthawa. 43 Koma wolamulira asilikali uja anafuna kupulumutsa Paulo ndipo anawaletsa kuchita zimene anakonza. Iye analamulira asilikali kuti amene amatha kusambira kuti adziponye mʼmadzi ndi kuyamba kukafika pa mtunda. 44 Otsalawo anayenera kugwira matabwa kapena tizidutswa ta sitimayo. Motero onse anapulumuka nakafika pa mtunda.